-
Kupindula ndi Kukoma Mtima kwa YehovaNsanja ya Olonda—2002 | May 15
-
-
Kukoma Mtima kwa Mulungu Kumapatsa Mpumulo ndi Chitetezo
11, 12. (a) Kodi Yehova anakomera mtima Yosefe pamayesero otani? (b) Kodi Mulungu anamukomera mtima bwanji Yosefe?
11 Tsopano tiyeni tione Genesis chaputala 39. Chaputala chimenechi chikufotokoza za Yosefe, mdzukulutuvi wa Abrahamu, amene anamugulitsa muukapolo ku Igupto. Komabe, “Yehova anali ndi Yosefe.” (Mavesi 1, 2) Ngakhale Potifara, mbuye wa Yosefe wa ku Igupto, anaona kuti Yehova anali naye Yosefeyo. (Vesi 3) Komabe, Yosefe anakumana ndi chiyeso chachikulu. Anamuimba mlandu wabodza woti anafuna kugona ndi mkazi wa Potifara ndipo anamuika m’ndende. (Mavesi 7-20) Pamene anali “m’dzenje [la ndende, NW],” “anapweteka miyendo yake ndi matangadza; anam’goneka m’unyolo.”—Genesis 40:15; Salmo 105:18.
12 Kodi n’chiyani chinachitika nthaŵi yonse ya chiyeso chimenechi? “Yehova anali ndi Yosefe nam’chitira iye zokoma.” (Vesi 21a) Kukoma mtima kumeneku kunachititsa zinthu zosiyanasiyana moti m’kupita kwa nthaŵi Yosefe anapeza mpumulo pa mavuto ake aja. Yehova anam’patsa Yosefe “ufulu pamaso pa woyang’anira kaidi.” (Vesi 21b) Ndipo woyang’anira ndendeyo anam’patsa Yosefe udindo. (Vesi 22) Kenako, Yosefe anakumana ndi munthu amene, patapita nthaŵi, anakam’dziŵitsa kwa Farao, wolamulira wa Igupto. (Genesis 40:1-4, 9-15; 41:9-14) Ndiyeno, mfumuyo inakweza Yosefe n’kukhala wolamulira wachiŵiri m’dziko la Igupto ndipo anagwira ntchito yopulumutsa miyoyo m’dzikolo limene munagwa njala. (Genesis 41:37-55) Yosefe anayamba kuvutika ali ndi zaka 17 ndipo anavutika kwa zaka zoposa 12. (Genesis 37:2, 4; 41:46) Koma zaka zonse zimene anavutikazo, Yehova Mulungu anamukomera mtima Yosefe mwa kum’teteza ku mavuto oopsa ndi kum’pulumutsa kuti achite ntchito yapadera pokwaniritsa cholinga cha Mulungu.
-
-
Kupindula ndi Kukoma Mtima kwa YehovaNsanja ya Olonda—2002 | May 15
-
-
16. Kodi Baibulo limafotokoza zabwino zotani zokhudza Abrahamu ndi Yosefe?
16 Nkhani ya mu Genesis chaputala 24 ikusonyeza bwinobwino kuti Abrahamu anali bwenzi lapamtima la Yehova. Vesi loyamba limati “Yehova anadalitsa Abrahamu m’zinthu zonse.” Mnyamata wa Abrahamu anati Yehova ndi “Mulungu wa mbuyanga Abrahamu.” (Mavesi 12, 27) Ndipo wophunzira Yakobo anati Abrahamu ‘anayesedwa wolungama’ ndipo “anatchedwa bwenzi la Mulungu.” (Yakobo 2:21-23) N’chimodzimodzinso ndi Yosefe. Chaputala 39 chonse cha Genesis chikutsindika kuti Yosefe anali bwenzi lapamtima la Yehova. (Mavesi 2, 3, 21, 23) Ndiponso, wophunzira Stefano ananena za Yosefe kuti: “Mulungu anali naye.”—Machitidwe 7:9.
-