Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 1/1 tsamba 30-31
  • Kukhululukira Ena Kutsegula Njira ya Chipulumutso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhululukira Ena Kutsegula Njira ya Chipulumutso
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifundo Kenako Chilanditso
  • Yosefe Wamkulu
  • Phunziro kwa Ife
  • “Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kupulumutsa Moyo mu Nthawi ya Njala
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Yehova Sanamuiwale Yosefe
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • “Tamverani Maloto Amene Ine Ndinalota”
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 1/1 tsamba 30-31

Anachita Chifuniro cha Yehova

Kukhululukira Ena Kutsegula Njira ya Chipulumutso

ANA khumiwo a Yakobo amene anaima pamaso pa nduna yaikulu ya Igupto anali ndi chinsinsi china choopsa. Zaka zambiri kalelo iwo anagulitsa mbale wawo wamimba ina Yosefe mu ukapolo nati atate wawo akawauza kuti Yosefe anaphedwa ndi chilombo.​—Genesis 37:18-35.

Tsopano, patapita zaka ngati 20, njala yaikulu inapangitsa amunawa kupita ku Igupto kukagula chakudya. Koma zinthu sizinayende bwino. Nduna yaikulu, imenenso inali kutumikira monga woyang’anira chakudya, inawaimba mlandu wa kuzonda dziko. Anaponya mmodzi wa iwo m’ndende nati otsalawo abwerere kwawo ndi kubwera ndi mbale wawo womalizira, Benjamini. Atabwera naye, nduna yaikuluyo inachita machenjera ena kuti Benjamini amangidwe.​—Genesis 42:1–44:12.

Yuda, mmodzi mwa ana a Yakobowo, anadandaula. ‘Tikabwerera kunyumba popanda Benjamini,’ iye anatero, ‘atate wathu adzamwalira.’ Ndiyeno chinachake chinachitika chimene Yuda kapena anzake onse amene anayenda naye paulendowo sanayembekeze. Atalamula onse kuti atuluke m’chipindacho kusiyapo ana a Yakobo, nduna yaikuluyo inalira mofuula. Kenako, itatonthola, inawauza kuti: “Ine ndine Yosefe.”​—Genesis 44:18–45:3.

Chifundo Kenako Chilanditso

“Kodi akali ndi moyo atate wanga?” Yosefe anawafunsa motero abale akewo. Sanayankhe. Ndithudi, abale a Yosefewo analibe chonena. Kodi akondwere kapena aope? Ndi iko komwe, zaka 20 zapitazo iwo anagulitsa mwamunayu kuti akhale kapolo. Yosefe anali ndi mphamvu yowaponya m’ndende, kuwamana chakudya, kapena​—choopsa kwambiri​—kuwanyonga! Pachifukwa chabwino, abale a Yosefe “sanakhoza kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye.”​—Genesis 45:3.

Mwamsanga Yosefe anawapangitsa kukhala omasuka. “Muyandikiretu kwa ine,” iye anatero. Anamyandikira. Kenako anati: “Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndiloŵe m’Aigupto. Tsopano musaphwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsira ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo.”​—Genesis 45:4, 5.

Yosefe sanasonyeze chifundo popanda maziko ake. Anali ataona kale umboni wa kulapa kwawo. Mwachitsanzo, Yosefe atawaimba mlandu abale ake kuti ndi azondi, anawamva akunena pakati pawo kuti: “Tachimwiratu mbale wathu . . . Chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira.” (Genesis 42:21) Ndiponso Yuda anadzipereka kuti akhale kapolo m’malo mwa Benjamini kuti mnyamatayo abwerere kwa atate wake.​—Genesis 44:33, 34.

Ndiye chifukwa chake Yosefe anali ndi chifukwa chabwino chosonyezera chifundo. Ndithudi, anadziŵa kuti kutero kungapulumutse banja lake lonse. Choncho, Yosefe anauza abale ake kuti abwerere kwa atate wawo, Yakobo, ndi kumuuza kuti: “Chotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Aigupto lonse: tsikirani kwa ine, musachedwe. Ndipo mudzakhala m’dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoŵeta zanu, ndi zonse muli nazo; ndipo ndidzachereza inu komweko.”​—Genesis 45:9-11.

Yosefe Wamkulu

Tingatche Yesu Kristu kuti Yosefe Wamkulu, popeza amuna aŵiriwa akufanana m’zambiri. Monga Yosefe, Yesu anasautsidwa ndi abale ake, mbadwa zinzake za Abrahamu. (Yerekezerani ndi Machitidwe 2:14, 29, 37.) Komabe, amuna onse aŵiriwa anaona zotsatirapo zodabwitsa. M’kupita kwa nthaŵi, Yosefe anasintha kuchoka paukapolo kukhala nduna yaikulu, wachiŵiri kwa Farao. Momwemonso, Yehova anaukitsa Yesu kwa akufa ndi kumkweza kukhala pamalo apamwamba ‘kudzanja lamanja la Mulungu.’​—Machitidwe 2:33; Afilipi 2:9-11.

Monga nduna yaikulu, Yosefe anali kupereka chakudya kwa onse amene anabwera ku Igupto kudzagula chakudya. Lerolino, Yosefe Wamkulu ali ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru padziko lapansi mwa amene akuperekera chakudya chauzimu “panthaŵi yake.” (Mateyu 24:45-47; Luka 12:42-44) Inde, awo amene amabwera kwa Yesu “sadzamvanso njala, kapena ludzu . . . chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaŵeta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo.”​—Chivumbulutso 7:16, 17.

Phunziro kwa Ife

Yosefe akupereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kusonyeza chifundo. Chilungamo cholimba chidakafuna kuti awakhaulitse onse amene anamgulitsa kuukapolo. Komanso, kutengeka maganizo kukadamsonkhezera kungonyalanyaza tchimo lawo. Yosefe sanachite zonse ziŵirizi. M’malo mwake, iye anayesa abale akewo kuti aone ngati analapa. Kenako, ataona kuti anali ndi chisoni chenicheni, anawakhululukira.

Tingatsanzire Yosefe. Pamene winawake amene watilakwira asonyeza kuti wasinthadi mtima wake, tiyenera kumkhululukira. Inde, sitiyenera kulola kutengeka maganizo kutipangitsa kusaona kulakwa kwakukulu. Komanso, sitiyenera kulola kunyansidwa kutipangitsa kusaona zochita zosonyeza kulapa koona. Choncho tiyeni ‘[tipitirizebe] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni tokha.’ (Akolose 3:13) Tikamatero, tidzakhala tikutsanzira Mulungu wathu, Yehova, amene ali “wokhululukira.”​—Salmo 86:5; Mika 7:18, 19.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena