Kugwira Ntchito ndi Yehova Mokhulupirika
“Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwiza zanu.”—SALMO 71:17.
1. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti ntchito ndimphatso yochokera kwa Yehova?
NTCHITO nchimodzi cha mphatso za Mulungu kwa munthu. Kwa makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, Yehova anati: “Mudzaze dziko lapansi . . . muligonjetse.” Iyi inali ntchito yobweretsa chitokoso koma yokhozadi kuchitidwa ndi nyonga yawo. Kuyesayesa kwakuthupi ndi kwamaganizo kofunikira kukawonjezera chisangalalo chawo cha kukhala ndi moyo, chinthu chosakumanidwapo ndi nyama zimene zinagawana nawo mudzi wawo wa dziko lapansiwo.—Genesis 1:28.
2, 3. (a) Kodi ntchito yakhala chiyani kwa ambiri lerolino, ndipo nchifukwa ninji? (b) Kodi ndimwaŵi wa kuchita ntchito yapadera uti umene tiyenera kulingalira?
2 Ngakhale mumkhalidwe wathu wopanda ungwiro, ‘ntchito yolimba’ yotulukapo “zabwino” ndi “mtulo wa Mulungu,” monga mmene munthu wanzeru Solomo analembera. (Mlaliki 3:13) Munthu amafunikirabe kukhala ndi nyonga yozindikira ya maganizo ake ndi thupi. Kukhala wopanda ntchito kumachititsa tondovi. Komabe, sintchito zonse zimene ziri zabwino kapena zophulapo kanthu. Kwa ambiri, ntchito njogwetsa ulesi, yongogwirira kupeza zakudya basi.
3 Komabe, iripo ntchito yodzetsadi mphotho imene anthu onse akuitanidwa kukhalamo ndi phande. Koma kwa omwe amakhalamo ndi phande kumakhala otsutsa ndi mavuto ambiri ofunikira kulaka. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti tiyenerere kaamba ka ntchito imeneyi? Kodi tingayenerere motani? Tisanayankhe mafunsowa, choyamba tiyeni tilingalire ichi:
Kodi Tikugwirira Ntchito Yani?
4. Kodi ndi mtundu wa ntchito yanji imene inabweretsa chisangalalo ndi chikhutiritso kwa Yesu?
4 Yesu Kristu anati: ‘Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.’ (Yohane 4:34) Kugwirira ntchito Yehova mokhulupirika kunasangalatsa kwambiri ndi kukhutiritsa Yesu. Iko kunampatsa chifuno m’moyo wake, ndipo pamapeto pa uminisitala wake wa zaka zitatu ndi theka, iye mowonadi akanena kwa Atate wake wakumwamba kuti: ‘Ine ndalemekeza inu padziko lapansi, mmene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.’ (Yohane 17:4) Mongadi mmene ziriri kuti chakudya chakuthupi chimachilikiza, irinso tero ntchito yodzala ndi zauzimu. Yesu anagogomezera ichi panthaŵi ina pamene analangiza kuti: ‘Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitaika koma cha chakudya chimene chitsalira ku moyo wosatha.’ (Yohane 6:27) Mosiyana ndi iyi, ntchito imene iri yosabala zipatso mwauzimu imatsogolera ku kugwiritsiridwa mwala ndi imfa.
5. Kodi ndani yemwe anatsutsa ntchito yabwino imene Yesu anaichita, ndipo nchifukwa ninji?
5 ‘Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, inenso ndigwira ntchito.’ Yesu anafotokoza mawuwa kwa Ayuda amene ankamusuliza chifukwa chakuti patsiku la Sabata iye anachiritsa munthu amene anadwala kwa zaka 38. (Yohane 5:5-17) Ngakhale kuti Yesu ankachita ntchito ya Yehova, otsutsa achipembedzo anakana kuvomereza nsonga imeneyo ndipo anachita chirichonse chothekera kumuletsa iye. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anali ochokera kwa atate wawo, Satana Mdyerekezi, amene nthaŵi zonse watsutsa ntchito ya Yehova. (Yohane 8:44) Popeza kuti Satana ‘angadzionetse ngati mngero wa kuunika,’ mwa kugwiritsira ntchito ‘chinyengo chonse cha chosalungama,’ ife tifunikira kuzindikira kwauzimu ndi kuganiza kwabwino kuzindikira mawonekedwe a ntchito zake. Apo phuluzi, tingadzipeze kukhala tikuchita motsutsana ndi Yehova.—2 Akorinto 11:14; 2 Atesalonika 2:9, 10.
Kugwira Ntchito kwa Otsutsa
6. Kodi nchifukwa ninji ampatuko akutchedwa ‘ochita ochenjerera?’ Fotokozani mwa fanizo.
6 Ena, mofanana ndi ampatuko ena lerolino, akugwira ntchito mosakhulupirika monga atifitifi a Satana kuti adodometse chikhulupiriro cha ziŵalo zatsopano zosonkhana ndi mpingo Wachikristu. (2 Akorinto 11:13) Mmalo mwa kugwiritsira ntchito Baibulo lokha monga maziko a ziphunzitso zowona, iwo amasumika pa kuyesera kugwetsa New World Translation of the Holy Scriptures, ngati kuti Mboni za Yehova zimadalira kotheratu pa iyo kaamba ka chirikizo. Koma ichi sichiri tero. Kwa nyengo yaitali ya pafupifupi zaka zana limodzi, Mboni choyambirira zinagwiritsira ntchito King James Version, Douay Version ya Roma Katolika, kapena matembenuzidwe aliwonse omwe analipo m’chinenero chawo, kuphunzira chowonadi cha Yehova ndi zifuno zake. Ndipo izo zinagwiritsira ntchito matembenuzidwe akalekalewa polengeza chowonadi chonena za mkhalidwe wa akufa, unansi wa Mulungu ndi Mwana wake, ndi chifukwa chimene kagulu kankhosa kokha kamapita kumwamba. Anthu anzeru amadziŵanso kuti Mboni za Yehova zimapitirizabe kugwiritsira ntchito matembenuzidwe ambiri a Baibulo m’ntchito yawo ya kulengeza kwa padziko lonse. Komabe, chiyambire 1961, izo zasangalala mowonjezereka kugwiritsira ntchito New World Translation, yokhala ndi matembenuzidwe ake atsopano, olongosoka ndi oŵerengeka bwino.
7. (a) Kodi nchifukwa ninji Yesu akukana ambiri amene amati ali ndi chikhulupiriro mwa iye? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kulabadira uphungu wa pa 1 Yohane 4:1?
7 Yesu anati akakana ambiri amene anati amukhulupirira iye. Iye anavomereza kuti awa angakhale akunenera, kutulutsa ziŵanda, ndi ‘kuchita ntchito zazikulu’ (NW) m’dzina lake. Chikhalirechobe, iye anawazindikira awa kukhala “osayeruzika.” (Mateyu 7:21-23) Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti sakuchita chifuniro cha Atate wake wakumwamba ndipo ngachabechabe pamaso pa Yehova Mulungu. Ntchito zachilendo, ngakhale zowoneka kukhala zozizwitsa lerolino, zingakhale zoyambitsidwa ndi wonyenga wamkulu, Satana. Mtumwi Yohane, polemba kalata yake yoyamba yachisawawa zaka zoposa 60 zapitazo pambuyo pa imfa ndi kuukitsidwa kwa Yesu, analangiza kuti Akristu sakayenera ‘kukhulupirira mzimu uli wonse, koma kuyesa mizimu ngati ichokera mwa Mulungu.’ Ife tifunikira kuchita chofananacho.—1 Yohane 4:1.
Ntchito Zosapatsa Mphotho
8. Kodi tiyenera kulingaliranji ponena za ntchito zathupi?
8 Ngakhale ngati sitimachita ntchito yosabala zipatso zauzimu, ntchito zathu zimakhala zachabe ngati zipitirizabe kusamalira zilakolako za thupi lochimwa. Mtumwi Petro anati tinathera nthaŵi yaikulu tikugwirira ntchito ‘chifuno cha amitundu . . . m’kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka.’ (1 Petro 4:3, 4) Ndithudi, ichi sichikutanthauza kuti anthu onse amene tsopano ndi Akristu odzipereka anachitapo ntchito zoterezi, koma chimatanthauzadi kuti mkhalidwe wa anthu omwe adachitapo tero udafunikira kusintha mofulumira pamene kuzindikira kwawo kwauzimu kunakula. Dziko lidzawanyoza iwo chifukwa cha kutembenuka kwawo; ichi chiyenera kuyembekezeredwa. Komabe, iwo afunikira kusintha ngati ati akhale antchito okhulupirika muutumiki wa Yehova.—1 Akorinto 6:9-11.
9. Kodi timaphunziranji m’chokumana nacho cha Mboni imene inayamba kuphunzira kukhala woimba nyimbo wa poyera?
9 Yehova watipatsa mphatso zambiri zotisangalatsa, pakati pa izi pali nyimbo. Komabe, popeza kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi, kodi ili silimaphatikiza nyimbo? (1 Yohane 5:19) Inde, nyimbo zingakhale msampha woipa, monga mmene Sylvana anapezera. Donayu anali ndi mwaŵi wa kuphunzirira mu Falansa monga woimbira poyera. “Ndinali nachobe chikhumbo champhamvu cha kutumikira Yehova,” akutero. “Ndinasangalala ndi upainiya wothandiza ndipo ndinayembekezera kugwirizanitsa zinthu ziŵirizi m’moyo wanga. Koma vuto loyamba limene ndinafunikira kuyang’anizana nayo posamalira ntchito yanga linali chisembwere. Pachiyambi, mabwenzi anga anandilingalira ine kukhala bulutu pamene sindinagwirizane nawo m’kukambirana kwawo kwa chisembwere ndi chitsanzo. Pambuyo pake, mayendedwe oipawa anayamba kupha chikumbumtima changa, ichi chinandipangitsa kulekerera zinthu zimene Yehova amada. Mmodzi wa aphunzitsi anga anandisonkhezera kuti ndipange kuimbako kukhala chipembedzo changa, ndipo ndinaphunzitsidwa kuchita mwauchinyama papulatifomu ndikudzilingalira kuti ndinali wopambana aliyense. Zinthu zonsezi zinandipangitsa kukhala wosakhazikika. Pambuyo pake, ndinafunikira kukonzekera kaamba ka kuimba kwapadera kwapoyera. Ndinapemphera kwa Yehova kundiunikira njira yomwe ndikafunikira kuyendamo. Chinkana kuti ndinaimba mwa myaa ndi kudzidalira, sindinakhale mmodzi wa omwe anasankhidwa. Pambuyo pake, ndinadzazindikira chifukwa chake—zotulukapo zinagamulidwa kale mwachinsinsi mpikisanowo usanayambike. Koma ndinali ndi yankho lomvekera ku pemphero langa ndipo ndinasankhapo kuleka kuimbira papulatifomu ndikukaphunzitsira kuimba kunyumba.” Mlongoyu pambuyo pake anakwatidwa ndi mkulu mumpingo Wachikristu, mmene onse aŵiriwa akutumikira mokhulupirika kupititsa patsogolo zikondwerero za Ufumu.
10. Kodi mumalingalira bwanji ndi mawu a Yesu a pa Yohane 3:19-21?
10 Yesu anati: ‘Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.’ Kumbali ina, ‘wochita chowonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.’ (Yohane 3:19-21) Ndidalitso lotani nanga kumagwira ntchito mogwirizana ndi chifuniro ndi cholinga cha Yehova! Koma kuti ichi chichitidwe mwachipambano, nthaŵi zonse tiyenera kulola ntchito zathu kusanthulidwa m’chiunikiro cha Mawu a Mulungu. Sitiri okalamba kwambiri ndipo sikumakhalpo kuchedwa kusintha njira yathu ya moyo ndi kuvomereza chiitano cha kutenga utumiki wabwino wa Yehova.
Kuchita “Ntchito Zabwino” Lerolino
11. Kodi nziti zimene ena amazilondola kukhala “ntchito zabwino,” ndipo kodi nchifukwa ninji zoterezi zingatsogolere ku kugwiritsidwa mwala?
11 Ntchito imene iri yabwino kwambiri lerolino iyenera kusonyeza kufulumira kwa nthaŵi zathu. Anthu owona mtima ambiri amadzitanganitsa ndi kuvomerezana okha ndi ntchito zimene kaŵirikaŵiri zimafotokozedwa kukhala “ntchito zabwino,” zochitidwa kaamba ka kupindulitsa anthu onse kapena kaamba ka chinthu chimodzi chenicheni. Komabe, ntchito ya mtundu umenewu imakhala yogwiritsa mwala chotani nanga! Mu Briteni, CAFOD (Catholic Fund for Overseas Development), pochitira lipoti ndawala yake kaamba ka dzinthu dzothandizira anjala, inati: “Zaka zitatu zapitazo . . . mapaundi mamiliyoni ambiri anapezedwa kaamba ka dzinthu dzothandizira. Anthu zikwi zambiri anapulumutsidwa. Tsopano anthu amenewo alinso pangozi . . . Koma kodi nchifukwa ninji? Kodi chinalakwika nchiyani?” Popitiriza ndi nkhani yakeyo, CAFOD Journal yalongososla kuti mavuto okhalirira sanathetsedwe ndikuti “chuma chofunika kwambiri cha kutukula anthu chagwiritsiridwa ntchito kusonkhezera kupikisana [nkhondo ya chiweniweni].” Mosakaikira, inu munamvapo mawu ofanana ndi awa ofuulidwa ndi magulu osonkhanitsa zopereka ochita ntchito yofananayi.
12. Kodi ndiliti limene liri yankho lokha ku mavuto oyang’anizana ndi dziko lerolino?
12 Njala ndivuto lofunikira thandizo lamwamsanga. Komabe, kodi ndani omwe akudziŵa kuti masoka a lerolino a njala ndi nkhondo monga momwe akukwaniritsa ulosi wa Yesu Kristu, akusonya ku mapeto a dongosolo lamakonoli la zinthu? (Mateyu 24:3, 7) Kodi ndani omwe afalitsa umboni wogwirizanitsa zochitikazi ndi kukwera kwa apakavalo anayi osonyezedwa mowonekera m’bukhu la Baibulo la Chibvumbulutso, mutu 6? Mosasemphana mawu, Mboni za Yehova zachita tero mokhulupirika m’magazine ano. Chifukwa ninji? Kuti asonyeze kuti sikwamunthu kubweretsa zothetsera zokhalitsa. Ichi sichikutanthauza kuti Akristu sakusamala ndi mavuto a dziko iri. Kutalitali. Iwo ngachifundo ndipo adzachita zomwe angathe kuthetsa kusauka. Chikhalirechobe, iwo mowonadi amakumbukira nsonga yakuti popanda kuloŵereramo kwa Mulungu, mavuto adzikowa sadzathetsedwa. Mofanana ndi osauka, mavutowa adzakhalapobe malinga ngati Satana aloledwa kukhala wolamulira wa dziko lino.—Marko 14:7; Yohane 12:31.
Ntchito ya Phindu Lalikulu
13. Kodi ndiiti imene iri ntchito yofulumira kwenikweni lerolino, ndipo kodi akuichita ndani?
13 Chofunika chofulumira lerolino nchakulalikira mbiri yabwino yakuti Ufumu wa Yehova Mulungu posachedwapa udzalowa mmalo maboma onse adziko ndikubweretsa mpumulo umene anthu owopa Mulungu amaulakalaka. (Danieli 2:44; Mateyu 24:14) Yesu Kristu anapanga kulalikira Ufumu wakumwamba kukhala chifuno chake chachikulu m’moyo, ngakhale kuti kulalikira kwake kunali kolekezera ku dziko la Palestina. Lerolino, ukulu wa kulalikiraku ngwapadziko lonse, mongadi mmene Yesu ananenera kuti ukakhalira. (Yohane 14:12; Machitidwe 1:8) Kukhalamo ndi phande, ngakhale pang’ono, m’ntchito ya Mulungu, kuli mwaŵi wosayerekezeka. Amuna ndi akazi, okalamba ndi achichepere mofananamo, omwe nthaŵi ina sanalingalirepo kukhala alaliki a mbiri yabwino ali kutsogolo kwa ntchito yolengeza yokwaniritsidwa ndi Mboni za Yehova lerolino. Mofanana ndi Nowa ndi banja lake, iwo akuchita ntchito ya Mulungu mokhulupirika mwa kutumidwa ndi Iye, ndipo motero akuchita ichi ndi nyonga Yake, monga kalambula bwalo wa mapeto a dongosolo ili la zinthu.—Afilipi 4:13; Ahebri 11:7.
14. Kodi kulalikira nkopulumutsa moyo ndipo panthaŵi imodzimodziyo kotetezera motani?
14 Ntchito yochitira umboni yochitidwa ndi Mboni za Yehova m’masiku ano otsiriza njopulumutsa moyo kwa oimvetsera ndi kuchitapo kanthu pa mbiri yabwino imene akuimva. (Aroma 10:11-15) Iyo imawatetezeranso oilalikirawo. Mwa kukhala okondwerera mowona mtima m’kuthandiza anthu amene ali ndi mavuto aakulu kuposa athu, sitidzadetsedwadi nkhaŵa ndi mavuto amene tingakhale nawo. Timazindikira kuti dziko ili lokhala ndi miyezo yonyonyotsoka ingatikole kuti tigwirizane ndi njira zake. Chotero kudzaza maganizo athu ndi malingaliro a Mulungu m’kulalikira kwathu nkoposadi kulimbikitsa chikhulupiriro chokha; nchikondwerero chathu chabwino. Monga mmene Mboni ina inanenera kuti: “Ngati sindiyesa kusintha anthu amene ndimakumana nawo, iwo angandisinthe ine!”—Yerekezerani ndi 2 Petro 2:7-9.
Kugwirira Limodzi ndi Mpingo
15. Kodi ndi mathayo ati omwe ngaabusa aang’ono lerolino, ndipo kodi ndimotani mmene ziŵalo zachimuna za mpingo ziyenera kulingalira ponena za 1 Timoteo 3:1?
15 Pamene okondwerera atsopano abwera kumpingo, iwo amadza pansi pa chisamaliro cha Mbusa Wamkulu, Yehova Mulungu, ndi Mbusa wake Wabwino, Yesu Kristu. (Salmo 23:1; Yohane 10:11) Abusa akumwambawa akuimiridwa ndi abusa aang’ono okhulupirika ankhosa pano padziko lapansi, amuna oikidwa m’mipingo. (1 Petro 5:2, 3) Kukhala ndi ntchitoyi ndimwaŵi wosagulika ndi ndalama m’masiku otsiriza ano. Ntchito ya abusawo njaikulu, yophatikiza osati kutsogolera kokha m’kuphunzitsa mumpingo ndi polengeza komanso kuchinjiriza nkhosa kwa adani auzimu ndi mkuntho wa mkhalidwe wonga namondwe wa dziko lomwe tikukhalamo. Palibe ntchito yabwinopo imene ziŵalo zachimuna za mpingo zingafikire kuposa yothandizira kusamalira mkhalidwe wabwino wauzimu wa ziŵalo za mpingo Wachikristu womakulakula.—1 Timoteo 3:1; yerekezerani ndi Yesaya 32:1, 2.
16. Kodi ndi m’njira ziti zimene abusa Achikristu amathandizirana?
16 Komabe, sitiyenera kuiwala kuti, abusawa ndi anthu, okhala ndi umunthu ndi zophophonya zosiyanasiyana mofanana ndi nkhosa zonsezo. Pamene kuli kwakuti munthu wina angapambane pambali yakutiyakuti ya ntchito yaubusa, mphatso za winanso zidzapindulitsa mpingo pamfundo yosiyana ndi iyi. Ntchito zawo monga akulu Achikristu zimathandizirana kulimbitsa mpingo. (1 Akorinto 12:4, 5) Mzimu wopikisana suyenera kuwaloŵerera. Iwo chapamodzi amagwirira ntchito kutetezera ndi kupititsa patsogolo zikondwerero za Ufumu, “kukweza manja okhulupirika” mpemphero kwa Yehova, kufunafuna dalitso ndi chitsogozo chake pamakambitsirano ndi zosankha zawo zonse.—1 Timoteo 2:8, NW.
17. (a) Kodi tiri ndi thayo lotani? (b) Kodi tifunikira kupeŵa zinthu ziti ngati titi tisamalire mathayo athu mokwanira?
17 Ntchito yolalikira tsopano ikupeza kufulumira kowonjezereka pamene mapeto a ufumu wa Satana akuyandikira. Pokhala ndi chowonadi cha Mawu a Yehova Mulungu, monga Mboni zake, tiri ndi thayo la kufalitsa mbiri yabwino pa mwaŵi uliwonse. Ntchito yomwe tili nayo njokwaniradi kutitanganitsa, kufikira kumapeto. Sitiyenera kudzilola tokha kupatutsidwa ndi maseŵera, kulondola zosangulutsa zachisembwere kapena kufooketsedwa ndi chuma chakuthupi. Sitiyenera kudziphatikiza m’maloto, ndikuchita makani, pakuti kutero kungatsimikizire kukhala kosapindulitsa ndi kwakutha nthaŵi. (2 Timoteo 2:14; Tito 1:10; 3:9) Pamene ophunzira anamfunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” Yesu anatsogozanso malingaliro awo ku ntchito yofunika yomwe inalipo, nati: ‘Mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.’ Ntchito imeneyi ikufika mpaka lero.—Machitidwe 1:6-8.
18. Kodi nchifukwa ninji kugwirira ntchito ndi Yehova kuli kopindulitsa kwenikweni?
18 Kugwira ntchito ndi Yehova, kulalikira ndi mpingo wake wa padziko lonse lerolino, kumabweretsa chimwemwe, chikhutiro, ndi chifuno chenicheni m’miyoyo yathu. Uli mwaŵi kwa wokonda Yehova aliyense kusonyeza kudzipereka ndi kukhulupirika kwa iye. Ntchito yonseyi sidzabwerezedwanso. Pokhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha patsogolo pathu, tiyeni tipitirizebe mokhulupirika ‘kutumikira Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha,’ ku chitamando chake ndi chipulumuko chathu.—Ahebri 12:28.
Kodi Yankho Lanu Nlotani?
◻ Kodi Yesu anapeza chisangalalo ndi chikhutiro m’ntchito iti?
◻ Kodi ndani yemwe amatsutsa ntchito ya Yehova, ndipo nchifukwa ninji?
◻ Kodi zomwe ziri “ntchito zabwino” kudziko zimayerekezera motani ndi mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu?
[Chithunzi patsamba 18]
Yesu anatuma ophunzira ake kupita kukalalikira