Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 8/1 tsamba 15-21
  • Ziyembekezo Zazikulu za Anthu M’paradaiso ya Chisangalalo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ziyembekezo Zazikulu za Anthu M’paradaiso ya Chisangalalo
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulenga Mkazi Woyamba wa Munthu
  • Ziyembekezo Kutsogolo kwa Okwatirana Aŵiri Aumunthu Oyambirira
  • Mulungu Apuma Ku Ntchito Zake Zolenga
  • Mulungu Akulinganiza Kuti Munthu Asangalale ndi Moyo M’paradaiso
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Ziyembekezo za Paradaiso Ziri Zotsimikizirika Mosasamala Kanthu za Kusamvera kwa Anthu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mlengi Aika Okhala pa “Chombo cha m’Mlengalenga Dziko Lapansi”
    Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Moyo Uli ndi Chifuno Chachikulu
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 8/1 tsamba 15-21

Ziyembekezo Zazikulu za Anthu M’paradaiso ya Chisangalalo

“Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuruke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.”​—GENESIS 1:28.

1, 2. Ndi ku utali wotani umene Yehova akugwira ntchito mwachikondi m’chigwirizano ndi anthu, ndipo ndi ntchito yotani yogawiridwa imene anapereka kwa Adamu?

“MULUNGU ndiye chikondi,” tikuwuzidwa tero m’Baibulo Lopatulika. Iye ali wokondweretsedwa mwachikondi ndi mopanda dyera mu mtundu wa anthu ndi kugwira ntchito mosaleka kotero kuti iwo angasangalale kosatha ndi umoyo, miyoyo ya mtendere m’paradaiso ya pa dziko lapansi yosangalatsa. (1 Yohane 4:16; yerekezani ndi Salmo 16:11.) Mwamuna woyambayo, Adamu wangwiro, anali ndi moyo wa mtendere ndi ntchito yokondweretsa, yosangalatsa. Mlengi wa munthu anamgaŵira iye kulima munda wosangalatsa wa Edene. Mlengi wa munthu tsopano anampatsa iye ntchito ina, yapadera, ntchito yokhala ndi chitokoso, monga mmene cholembera cha zomwe zinachitika chikuvumbulira kuti:

2 “Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m’thengo, ndi mbalame zonse za m’mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti awone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina awo. Adamu ndipo anazitcha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m’mlengalenga ndi zamoyo zonse za m’thengo.”​—Genesis 2:19, 20.

3. Nchifukwa ninji panalibe mantha kumbali ya Adamu ndi zolengedwa za nyama?

3 Mwamunayo anatcha kavalo sus, bulu shohr, nkhosa seh, mbuzi ʽez, mbalame ʽohph, njiwa yoh·nahʹ, mbalame ya chitsukwa chachitali yamawangamawanga tuk·kiʹ, mkango ʼar·yehʹ kapena ʼariʹ, kasenye dov, nyani qohph, galu keʹlev, njoka na·chashʹ, ndi kupitirizabe.a Pamene iye anapita ku mtsinje womwe madzi ankayenda kutuluka m’munda wa Edene, iye anawona nsomba. Ku nsomba iye anapatsa dzina lakuti da·gahʹ. Mwamuna wopanda chidayo sanadzimve wamantha ndi zinyama zimenezi, zam’mudzi ndi zakuthengo, kapena ndi mbalame, ndipo sizinamve mantha ndi iye, amene zinamzindikira mwachibadwa kukhala wokulira pa izo, wa mtundu wapamwamba wa moyo. Izo zinali zolengedwa za Mulungu, zopatsidwa mphatso ya moyo ndi Iye, ndipo mwamunayo analibe chikhumbo kapena chikhoterero cha kuzivulaza izo kapena kuchotsa moyo wawo.

4. Nchiyani chomwe tingaganizire ponena za kutcha maina kochitidwa ndi Adamu kwa nyama zonse ndi mbalame, ndipo ndi mtundu wotani wa chokumana nacho umene chimenechi chinali?

4 Ponena za kaya ndi utali wotani umene munthu anasonyezedwa nyama za m’mudzi ndi zakuthengo ndi zolengedwa zowuluka m’mlengalenga, cholemberacho sichimatiuza ife. Zonsezo zinali pansi pa chitsogozo ndi kakonzedwe kaumulungu. Adamu mwachidziŵikire anatenga nthaŵi kuphunzira nyama iriyonse yosiyana, kuwona zizoloŵezi zake zapadera ndi kapangidwe; kenaka iye akakhoza kusankha dzina lomwe likakhala loyenera mwapadera kaamba ka iyo. Ichi chikatanthauza kupita kwa unyinji wolingalirika wa nthaŵi. Chinali chokumana nacho chosangalatsa kwenikweni kwa Adamu mwakutero kukhala wozoloŵerana ndi moyo wa zolengedwa za dziko lapansi limeneli mu mtundu wake wochulukira, ndipo chinaitanira kaamba ka kuthekera kokulira kwa maganizo ndi mphamvu za kulankhula kwa iye kuti asiyanitse uliwonse wa mitundu imeneyi ya zolengedwa za moyo ndi dzina loyenerera.

5-7. (a) Ndi mafunso otani omwe akabuka mwachidziŵikire? (b) Ndi mtundu wotani wa mayankho omwe anaperekedwa m’cholembera cha chilengedwe pa Genesis 1:1-25?

5 Koma kodi nchiyani chomwe chinali dongosolo la kulenga la zolengedwa zamoyo zonsezi? Kodi nyama za pa mtunda zinalengedwa mbalame zisanakhale kapena ayi, ndipo ndi kuti m’nthaŵi ndi m’ndandanda kumene mwamuna amapezeka m’chigwirizano ndi zolengedwa zamoyo zonsezi za mtundu wochepera? Ndimotani mmene Mulungu anakonzekera nkhope ya dziko lapansi kaamba ka kusiyanasiyana kochulukira koteroko kwa zolengedwa zamoyo, kupereka mpweya mu umene mbalame zikakhoza kuwuluka kutali koteko, kupereka madzi akumwa ndi moyo wa zomera zamasamba kutumikira monga zakudya, kupanga chowunikira chachikulu kuwalitsa masana ndi kutheketsa munthu kuwona, ndi kupanga chowunikira chaching’ono kukongoletsa usiku? Nchifukwa ninji mphepo inali yodekha chotero ndi yofunda kotero kuti mwamuna akakhoza kuyendayenda ndi kugwira ntchito ndi kugona wopanda kanthu ndipo wamaliseche?

6 Mwamunayo sanasiidwe kuti alote mayankho. Maganizo ake ofunsa anafunikira mayankho a luntha kuchokera ku magwero a ulamuliro omwe anadziŵa molongosoka. Iye sanasiidwe monga mwana waumbuli wa Mulungu, koma kuzama kwake kwa luntha lapamwamba mwachidziŵikire kunazindikiridwa ndi mbiri yakale yodabwitsa ya chilengedwe monga momwe yaperekedwera pa Genesis 1:1-25.

7 Ponena za cholembera chosangalatsa cha chilengedwe chimenecho, Adamu akakhoza kukhala woyamikira kwenikweni. Icho chinalongosola zinthu zambiri. Kuchokera m’njira imene ichi chinalembedwera, iye anamvetsetsa kuti panali nyengo zitatu zazitali za nthaŵi zimene Mulungu anatcha masiku mogwirizana ndi njira Yake ya kuyesera nthaŵi, nyengo yachinayi yolenga isadakhale mu imene Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziŵiri kuwonekera m’thambo la miyamba kuzindikiritsa tsiku lofupikirako la maora 24 la munthu. Tsiku lofupikirako limeneli la munthu pa dziko lapansi linali nthaŵi kuchokera pa kuzimiririka kwa chowunikira chachikulu kufika pa kutuluka kwake kotsatira. Adamu anadziŵanso kuti panafunikira kukhala zaka za nthaŵi kaamba ka iye, ndipo iye mosakaikira anayamba mwamsanga kuŵerenga zaka zake za moyo. Chowunikira chachikulu m’thambo la miyamba chikamtheketsa iye kuchita chimenechi. Koma ponena za masiku otalikirako a Mulungu a chilengedwe, mwamuna woyambayo anazindikira kuti iye panthaŵiyo anali kukhala ndi moyo m’tsiku lachisanu ndi chimodzi la ntchito yolenga dziko lapansi ya Mulungu. Palibe mapeto omwe anali atatchulidwa kwa iye onena za tsiku lachisanu ndi chimodzi limenelo kaamba ka kulenga nyama za pa mtunda zonsezo ndipo kenaka kaamba ka kulenga mwamuna mosiyana. Tsopano iye akakhoza kumvetsetsa dongosolo la kulenga moyo wa zomera, moyo wa za m’nyanja, moyo wa mbalame, ndi nyama za pa mtunda. Koma pokhala yekha m’munda wa Edene, Adamu sanali kulongosola kokwanira, kwathunthu kwa chifuno chachikondi cha Mulungu kaamba ka munthu m’Paradaiso yake ya pa dziko lapansi.

Kulenga Mkazi Woyamba wa Munthu

8, 9. (a) Nchiyani chimene mwamuna wangwiro anawona ponena za chilengedwe cha nyama, koma nchiyani chomwe iye anamaliza ponena za iyemwini? (b) Nchifukwa ninji chinali choyenerera kuti munthu wangwiro sanafunse Mulungu kaamba ka mnzake? (c) Ndimotani mmene cholembera cha Baibulo chimalongosolera kulengedwa kwa mkazi woyambirira waumunthu?

8 Mwamuna woyambayo, wokhala ndi maganizo ake angwiro ndi mphamvu za kuyang’ana, anawona kuti mu ufumu wa mbalame ndi nyama, panali yaimuna ndi yaikazi ndipo kuti pakati pawo zinabala mitundu yawo. Koma ponena za munthu iyemwini, sizinali tero. Ngati kawonedweka kanakhotetsa iye kukhala ndi lingaliro la kusangalala ndi bwenzi, iye sanapeze mnzake woyenerera pakati pa ufumu wa nyama uliwonse, osati ngakhale pakati pa anyani. Adamu akakhoza kumaliza kuti panalibe mnzake chifukwa chakuti ngati panali mmodzi, kodi Mulungu sakanambweretsa mnzake ameneyo kwa iye? Mwamuna anali atalengedwa mosiyana ndi mitundu ya nyama yonseyo, ndipo iye anatanthauzidwa kukhala wosiyana! Iye sanakhoterere kugamulapo nkhani kaamba ka iyemwini ndi kukhala wopulupudza ndi kufunsa Mulungu Mlengi wake kaamba ka mnzake. Chinali cholondola kuti mwamuna wangwiro alekere nkhani yonseyo mwa Mulungu, popeza kuti mwamsanga pambuyo pake iye anapeza kuti Mulungu anali atapanga malekezero a Iyemwini ponena za mkhalidwewo. Ponena za ichi ndi chimene tsopano chinachitika, cholemberacho chikutiwuza kuti:

9 “Koma kwa Adamu sanapezedwa womthangatira iye. Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikuru, ndipo anagona: ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake: ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu. Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzatchedwa Mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna. Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi. Onse aŵiri ndipo anali amaliseche, mwamuna ndi mkazi wake, ndipo analibe manyazi.”​—Genesis 2:20-25.

10. Ndimotani mmene mwamuna wangwiro anachitira pamene mkazi wangwiro anaperekedwa kwa iye, ndipo nchiyani chimene mawu ake angakhale anasonyeza?

10 Panali kukhutiritsidwa kokwanira kosonyezedwa m’mawu ake pamene mkazi wangwiro anaperekedwa kwa iye monga wothandizira ndi wothangatira: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga.” M’chiyang’aniro cha mawu amenewa pamene iye potsirizira pake anawona mkazi wake wolengedwa chatsopano, chingakhale chifukwa chakuti iye anali atayembekezera kwa nthaŵi yaitali kulandira mnzake wosangalatsa waumunthu. Kulongosola womthangatira wake, Adamu anamtcha iye “Mkazi” (ʼish·shahʹ kapena, m’chenicheni, “mwamuna wachikazi”), “chifukwa chakuti mwa mwamuna ameneyo anatengedwa.” (Genesis 2:23, New World Translation Reference Bible, mawu am’munsi) Adamu sanadzimve kukhala chiŵalo cha zolengedwa zowuluka ndi nyama za pa mtunda zimene Mulungu anazidziŵitsa papitapo kwa iye kuti azitche maina. Mnofu wake unali wosiyana ndi izo. Koma mkazi ameneyu mowonadi anali wa mtundu wa mnofu wake. Fupa la nthiti lotengedwa kuchokera ku mbali kwake linapanga mtundu wofananawo wa mwazi womwe unali m’thupi lake. (Onani Mateyu 19:4-6.) Tsopano iye anali ndi winawake kwa amene iye akachita monga mneneri wa Mulungu ndi kwa amene akakhoza kugaŵana naye zolembera zozizwitsa za chilengedwe.

11-13. (a) Pokhala ndi kulandiridwa kwa mkazi kochitidwa ndi Adamu, ndi mafunso otani omwe angabuke? (b) Nchiyani chomwe chinali chifuno cha Mulungu kaamba ka okwatirana aumunthu aŵiri oyambirira? (c) Nchiyani chomwe chikatumikira monga chakudya kaamba ka banja laumunthu langwiro?

11 Nchiyani, ngakhale ndi tero, chimene chinali chifuno cha Mlengi wa munthu m’kumpatsa iye mkazi? Kodi chinali kokha kumpatsa iye wothandizira ndi wothangatira, bwenzi la mtundu wake kumusunga iye kusakhala wosungulumwa? Cholemberacho chikulongosola chifuno cha Mulungu pamene chikusimba kwa ife dalitso la Mulungu lomwe linanenedwa pa ukwati wawo:

12 “Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa ng’ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi. Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuruke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.

13 “Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbewu liri pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse mmene muli chipatso cha mtengo wakubala mbewu; chidzakhala chakudya cha inu: ndiponso ndapatsa zinyama zonse za m’mlengalenga, ndi zakukwawa zonse za dziko lapansi mmene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero.”​—Genesis 1:26-30.

Ziyembekezo Kutsogolo kwa Okwatirana Aŵiri Aumunthu Oyambirira

14. Ndi dalitso la Mulungu, ndi mtsogolo motani momwe munakhala pamaso pa mwamuna ndi mkazi angwiro, ndipo nchiyani chomwe iwo molondola akawona m’masomphenya?

14 Ndi chinthu chabwino kwambiri chotani nanga mmene icho chinaliri kaamba ka mwamuna wangwiro ameneyo ndi mkazi wake wangwiro kumva liwu la Mulungu likulankhula ndi iwo, kuwawuza iwo chomwe akafunikira kuchita ndi kuwadalitsa iwo! Ndi dalitso la Mulungu, moyo sukakhala wachabe, koma iwo akatheketsedwa kuchita chimene iwo anawuzidwa kuchita. Ndi mtsogolo motani nanga momwe munali patsogolo pawo! Pamene okwatirana mwachimwemwe aŵiriwo anaima pamenepo m’mudzi wawo, munda wa Edene, iwo mwachidziŵikire anasinkhasinkha pa chimene chikachitika pamene iwo anachita chifuno cha Mulungu kaamba ka iwo. Pamene maso awo a maganizo anayang’ana kutsogolo motalikira, iwo anawona, osati kokha “munda wa Edene, kum’mawa,” koma dziko lonse lapansi lodzazidwa ndi amuna ndi akazi a nkhope zowala. (Genesis 2:8) Mtima wa mwamunayo ndi mkazi ukadumpha pa lingaliro lakuti onsewa anali ana awo, mbadwa zawo. Onse akakhala angwiro, opanda zophophonya mu mkhalidwe wakuthupi ndi kapangidwe, okhala ndi uchichepere wopitirizabe womwe ukadzala ndi umoyo wabwino ndi chisangalalo cha kukhala ndi moyo, onsewo akumasonyeza chikondi changwiro kaamba ka wina ndi mnzake, onsewo ogwirizana m’kulambira Mlengi wawo wamkulu, Atate wawo wakumwamba, akumachita chimenechi limodzi ndi atate ndi amayi aumunthu oyambirira. Mtima wa mwamuna ndi mkazi woyambirira unadzazidwa ndi chikondwerero chotani nanga pa lingaliro la kukhala ndi banja loterolo!

15, 16. (a) Nchifukwa ninji pakakhala zakudya zambiri kaamba ka banja la munthu? (b) Pamene banja lachimwemwe linakula m’chiŵerengero, ndi ntchito yotani yomwe ikakhalapo kaamba ka iwo kunja kwa munda wa Edene?

15 Pakakhala zakudya zambiri kaamba ka chiŵalo chirichonse cha banja la munthu limeneli lomwe linadzaza dziko lonse lapansi. Panali zakudya zambiri zoyamba nazo, mmenemo m’munda wa Edene. Mulungu anali atapereka kaamba ka iwo ndi kuwapatsa zomera zonse zotulutsa mbewu kutumikira monga zakudya zaumoyo, zosungilira moyo, limodzi ndi mitengo yobala zipatso.​—Yerekezani ndi Salmo 104:24.

16 Pamene banja lawo lachimwemwe linakula m’chiŵerengero, iwo akakhoza kufutukula mundawo ku maiko opyola malire a Edene, popeza kuti mawu a Mulungu amasonyeza kuti kunja kwa munda wa Edene, dziko lapansi linali mu mkhalidwe wosakonzekeredwa. Linali chifupifupi, losasamaliridwa ndipo silinabweretsedwe ku mlingo wapamwamba wofananawo wa kulimidwa womwe unazindikiritsa munda wa Edene. Chimenecho ndicho chifukwa chake Mlengi wawo anawauza “kugonjetsa” dziko lapansi pamene analidzaza ilo.​—Genesis 1:28.

17. Nchifukwa ninji pakakhala zakudya zambiri kaamba ka chiŵerengero chomakulakulacho, ndipo nchiyani chomwe potsirizira pake chikafalikira pamene munda unakulitsidwa?

17 Pamene mundawo unafutukulidwa ndi alimi angwiro ndi osamalira, dziko lapansi logonjetsedwa likakhala lotulutsa zochuluka kaamba ka chiŵerengero chomakulakulacho. Potsirizira pake, munda wofutukulika mokhazikikawo ukakuta dziko lonse lapansi, ndipo paradaiso ya pa dziko lapansi ikafalikira, kukula monga mudzi wosatha wa mtundu wa anthu. Likakhala dontho lokongola kuliwona kuchokera kumwamba, ndipo Mlengi wakumwamba akakhoza kulinena ilo kukhala labwino.​—Yerekezani ndi Yobu 38:7.

18. Nchifukwa ninji munda wa Edene wa chiwunda chonse ukakhalira waufulu ku kusokonezedwa, ndipo kodi ndi mtendere wotani womwe ukafalikira?

18 Zonsezo zikakhala za mtendere ndi zopanda kusokonezedwa monga munda wa Edene umenewo mu umene okwatirana chatsopanowo mwamuna ndi mkazi anadzipeza iwo eni. Sikukakhala kufunika kwa kuwopa ngozi kapena kuvulala kuchokera ku nyama zonsezo ndi zolengedwa zowuluka zimene mwamuna woyambirira, Adamu, anazisanthula ndi kuzitcha maina. Mofanana ndi atate ndi amayi awo aumunthu oyambirira, nzika zangwiro za Paradaiso ya pa dziko lapansi zimenezo zikakhala m’kugonjetseredwa kwawo nsomba za m’nyanja, zolengedwa zowuluka zakumwamba, ndi chamoyo chirichonse choyendayenda pa dziko lapansi, ngakhale nyama zakuthengo. Ndi lingaliro lachibadwa la kugonjetsera kwa mwamuna, yemwe analengedwa “m’chifanizo cha Mulungu,” zolengedwa zamoyo zochepera zimenezi zikakhala pa mtendere ndi iye. Ambuye awo abwino, angwiro aumunthu, pokhala ndi zolengedwa zokhala ndi moyo zochepera zimenezi m’kugonjetseredwa kwawo, akapereka mkhalidwe wa mtendere pakati pa chilengedwe cha nyama. Chisonkhezero cha mtendere cha ambuye onga mulungu aumunthu amenewa chikafalikira motetezera pa zolengedwa zokhutiritsidwa zokhala ndi moyo zochepera zimenezi. Pamwamba pa zonse, mtundu wa anthu wangwiro ukakhala pa mtendere ndi Mulungu, amene dalitso lake silikachotsedwa konse pa iwo.​—Yerekezani ndi Yesaya 11:9.

Mulungu Apuma Ku Ntchito Zake Zolenga

19. (a) M’chigwirizano ndi chifuno cha Mulungu, nchiyani chomwe mwamuna woyamba ndi mkazi afunikira kukhala anazindikira? (b) Nchiyani chomwe Mulungu anasonyeza m’chigwirizano ndi nthaŵi?

19 Pamene okwatirana aŵiri aumunthu angwiro akalingalira malo otsirizidwa a pa dziko lapansi mogwirizana ndi chifuno cha Mulungu, iwo akazindikira chinachake. Kwa iwo kuti achite ntchito yodabwitsa imeneyi yochokera kwa Mulungu kukafunikira nthaŵi. Nthaŵi yochulukira motani? Mlengi ndi Atate wawo wakumwamba anadziŵa. Iye anasonyeza kwa iwo kuti mpambo waukulu wa masiku a kulenga tsopano unali utafika pamapeto pena ndikuti iwo ankaimirira pa “madzulo,” mbali yoyambirira ya tsiku latsopano mogwirizana ndi kuzindikiritsa kwake kwa Mulungu kwa masiku a kulenga. Linafunikira kukhala tsiku lodalitsidwa ndi loyeretsedwa ku chifuno chake choyera, cholungama cha Mulungu. Mwamuna wangwiroyo, mneneri wa Mulungu, anadziŵa chimenechi. Kusimba kowuziridwa kumatiwuza ife kuti:

20. Nchiyani chomwe cholembera cha Baibulo chimanena ponena za “tsiku lachisanu ndi chiŵiri”?

20 “Ndipo anaziwona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, tawonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m’mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi. Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lawo lonse. Pofika tsiku lachisanu ndi chiŵiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ku ntchito yake yonse. Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, naliyeretsa limenelo: chifukwa limenelo adapuma ku ntchito yake yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga. Imeneyo ndiyo mibadwo yawo ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.”​—Genesis 1:31–2:4.

21. (a) Kodi Baibulo limanena kuti Mulungu anatsiriza tsiku lake la kupuma ndipo linali labwino ndithu? Longosolani. (b) Ndi mafunso otani omwe amabuka?

21 Cholemberacho sichikunena kuti Mulungu anatsiriza tsiku lake la kupuma ndi kuwona kuti zinali zabwino ndithu ndi kuti panali madzulo ndi m’mawa, tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Kuti lilingane ndi masiku apitawo asanu ndi limodzi akulenga, tsiku lachisanu ndi chiŵiri likufunikirabe kulengezedwa kukhala labwino ndithu, popeza kuti silinathebe. Kodi Yehova Mulungu angalengeze tsikulo kukhala labwino ndithu? Kodi ilo lakhala tsiku la kupuma kwa mtendere kaamba ka iye kufika pano? Bwanji ponena za chiyembekezo chopumitsa mtima chimene mwamuna ndi mkazi oyamba anachiwona kwa iwo eni pa tsiku lawo la ukwati m’Paradaiso? Tiyeni tiwone pamene zochitikazo zikufutukulidwa m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Awa ndi maina opezeka m’lemba la Chihebri la Genesis ndi mabukhu ena owuziridwa a Malemba a Chihebri.

Kodi Mukayankha Motani?

◻ Ndi ntchito yotani imene Mulungu anapatsa Adamu kuwonjezera ku kusamalira kaamba ka mundawo, ndipo kodi ichi chinaphatikizapo chiyani?

◻ Nchiyani chomwe cholembera cha chilengedwe pa Genesis 1:1-25 chinavumbula?

◻ Ndimotani mmene mkazi waumunthu woyambirira analengedwera, ndipo ndimotani mmene Adamu anavomerezera pa tsiku lawo la ukwati?

◻ Ndi ziyembekezo zotani zomwe zinali kutsogolo kwa okwatirana aŵiri aumunthu oyambirira?

◻ Ndimotani mmene Mulungu anasonyezera kuti mpambo waukulu wa masiku olenga unafikira mapeto ena?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena