Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 5/8 tsamba 26-29
  • Kodi Tingakhale kwa Utali Wotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingakhale kwa Utali Wotani?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anapangidwa Kukhala ndi Moyo, Osati Kufa
  • “Monga Masiku a Mtengo”
  • Mmene Mungakhalire ndi Moyo Kosatha
    Galamukani!—1995
  • Kodi Moyo Wosatha Ndi Wothekadi?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • N’zotheka Ndithu Kuti Amene Ali Kumanda Adzakhalenso ndi Moyo
    Galamukani!—2008
  • Yesu Anafa Ndi Kuukitsidwa—Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 5/8 tsamba 26-29

Kodi Tingakhale kwa Utali Wotani?

“ANTHU AMBIRI amene ali ndi moyo lerolino adzakhala ndi mwaŵi wamoyo wotalikitsidwa kwambiri. Ngakhale kusakhoza kufa kukuwoneka kukhala kotheka tsopano.”

“Mamiliyoni Amene Ngamoyo Tsopano Sangamwalire Konse.”

Kodi pali kusiyana kotani pakati pa ndemanga ziŵirizi? Yoyambayo ndi ndemanga yopangidwa ndi Dr. Lawrence E. Lamb, wolemba nkhani zamankhwala m’danga la nyuzipepala ndiponso profesala, m’bukhu lake lakuti Get Ready for Immortality, lofalitsidwa mu 1975. Yachiŵiriyo iri mutu wa nkhani yapoyera ndi wa bukhu lolembedwa ndi J. F. Rutherford, prezidenti wachiŵiri wa Watch Tower Society. Nkhani yapoyerayo inaperekedwa choyamba mu Los Angeles, California, mu 1918.

Komabe, ndemanga ziŵiri zowoneka zofananazo zinasiyana kwambiri m’kulingalira ndi kufufuza kumene kunatsogolera ku izo. Mawu a Dr. Lamb alidi ofanana ndi a anthu ambiri otchedwa okhulupirira kusakhoza kufa. Anthu ameneŵa amalingalira kuti kupita patsogolo kwa sayansi ya mankhwala, kuphatikizapo kufufuza kwa kukalamba, posachedwapa zidzathetsa chinsinsi cha chifukwa chimene timakalambira ndipo m’kupita kwa nthaŵi kudzagonjetsa imfa yeniyeniyo. Komabe, mosasamala kanthu za zipambano za sayansi yamakono m’kutalikitsa avareji ya moyo ndi kuthandiza ambiri kusangalala ndi miyoyo yabwinopo, zoneneratu za kusakhoza kufa zidakali zomwezo—kuneneratu kotsimikiza.

J. F. Rutherford, kumbali ina, sanali kuneneratu mozika pasayansi kapena mankhwala. Kukambitsirana kwake kunazikidwa pa Baibulo. Iye anasonyeza mwakukwaniritsidwa kwa maulosi a Baibulo kuti dziko la mtundu wa anthu linali litaloŵa mu “nthaŵi [yake] ya chimaliziro.” (Danieli 12:4) Iye kenaka anasonya ku chiyembekezo chozikidwa pa Baibulo chakuti mongadi mmene Nowa ndi banja lake anapulumuka mapeto a dziko la tsiku lawo, mamiliyoni adzapulumuka mapeto a dziko lino ndi kupitiriza kukhala ndi moyo m’dziko latsopano lolungama kusangalala ndi moyo pa dziko lapansi la paradaiso.—Mateyu 24:37-39; Chibvumbulutso 21:3, 4.

Kwa ambiri a awo amene anali m’khamu lake, mawu a Rutherford anali odabwitsa. Ngakhale lerolino, anthu ambiri amapeza nkhani yoteroyo yonena zokhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu kusakhala yeniyeni ndipo yosakhulupiririka. (Salmo 37:10, 11, 29) Koma kodi zimene Baibulo limanena ponena za chifukwa chimene timakalambira ndi kufa nzosakhulupiririkadi? Kwenikwenidi, kodi limanenanji pa nkhaniyo?

Anapangidwa Kukhala ndi Moyo, Osati Kufa

Mwanzeru, Baibulo limayamba ndi mbiri ya chiyambi cha moyo wa munthu. M’mutu woyamba wa Genesis, timaŵerenga kuti pambuyo polenga anthu aŵiri oyambirira, “Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.”—Genesis 1:28.

Kwa anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava, kuchita ntchito imeneyo, kukatanthauza kuti akhale ndi moyo kwa nthaŵi yaitali, ndiponso mbadwa zawo. Koma kodi kwa utali wotani? Kuŵerengabe bukhu la Baibulo la Genesis, tikupeza kuti palibe pamene pakutchulidwa utali wachindunji wa moyo wa Adamu ndi Hava. Mosasamala kanthu za izo, panali mkhalidwe umodzi umene anayenera kuufikira ngati anati apitirizebe kukhala ndi moyo. Mulungu anati kwa Adamu: “Koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.”—Genesis 2:17.

Chotero, imfa ikawadzera kokha ngati samvera lamulo la Mulungu. Kupanda apo, iwo adali ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi Laparadaiso limenelo lotchedwa Edeni. Mwachiwonekere, anthu anapangidwa kuti akhale ndi moyo, osati kufa.

Komabe, mbiri ya Genesis ikupitiriza kulongosola kuti anthu aŵiri oyambirirawo anasankha kunyalanyaza lamulo lomvekera bwino la Mulungu ndipo chotero anachimwa. Njira yawo yopanda chimvero inawabweretsera iwo, ndiponso mbadwa zawo, chiweruzo cha imfa. Zaka mazana ambiri pambuyo pake, mtumwi Paulo analongosola kuti: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”—Aroma 5:12.

Lamulo la choloŵa nlakuti Adamu ndi Hava angangopatsira ana awo kokha zimene iwo anali nazo. Monga olengedwa, iwo anali okhoza kupatsira moyo wangwiro, wosatha kwa mibadwo yamtsogolo. Koma popeza tsono miyoyo yawo inakhala yoipitsidwa ndi chimo ndi imfa, iwo sakanathanso kupereka choloŵa chabwino chimenecho. Chimo, kupanda ungwiro, ndi imfa zakhala zotulukapo za anthu chiyambire nthaŵi imeneyo, mosasamala kanthu za zoyesayesa za kutalikitsa utali wa moyo wa munthu.

M’lingaliro lina, zimenezi zingayerekezedwe ndi programu ya kompyuta imene iri ndi chophophonya, kapena cholakwa. Kokha ngati cholakwacho chadziŵidwa ndi kuwongoleredwa, programuyo singagwire bwino ntchito, ndipo zotulukapo zake zingakhale zangozi. Munthu wakhala wosakhoza kupeza, ndipo kutalitali kuwongolera, chophophonya chachibadwa chimene chimatulukapo kugwira ntchito koipa kwa matupi athu aumunthu, kotulukapo ukalamba ndi imfa. Komabe, Mlengi wa munthu, Yehova Mulungu, wapanga makonzedwe a kuwongolera icho. Kodi yankho lake nchiyani?

Mulungu wapereka moyo wamunthu wangwiro wa Mwana wake, Yesu Kristu, “Adamu wotsirizayo,” yemwe kwenikwenidi akuloŵa m’malo Adamu woyamba monga tate wathu ndi mpatsi wa moyo. Chotero, m’malo mokhala oweruzidwa ku imfa monga ana a Adamu wochimwa, anthu omvera angaŵerengedwe kukhala oyenera kulandira moyo wosatha monga ana a “Atate [wawo] Wosatha,” Yesu Kristu. Yesu iyemwini analongosola kuti: “Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang’ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nawo moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.”—1 Akorinto 15:45; Yesaya 9:6; Yohane 3:16; 6:40.

Pamapeto pa uminisitala wake wapadziko lapansi, m’pemphero kwa Atate wake wakumwamba, Yesu Kristu analengeza chiyeneretso chachikulu chopezera mphotho yaikulu ya moyo imeneyi mwakunena kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.

“Monga Masiku a Mtengo”

Tangolingalirani mukubzala mbewu ya mtengo wa sequoia ndikuona ukukula mapazi mazanamazana m’mwamba, kusangalala ndi kukula kwake kwa moyo wake wonse. Kenaka tangolingalirani mukuupitirira ndi kubzala wina zaka zikwizikwi pambuyo pake ndipo kachiŵirinso kusangalala ndi kukula ndi kukongola kwake.

Kodi kulingalira koteroko kuli kwenikweni? Ndithudi, popeza kuti kwazikidwa pa lonjezo la Mlengi wake wa munthu, Yehova Mulungu, amene akuti: “Monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga.” (Yesaya 65:22) Lonjezo limeneli limathandiza kuyankha funso lakuti, Kodi munthu angakhale kwa utali wotani? Yankho nlakuti: mpaka mtsogolo mosadziŵika, inde, kosathadi.—Salmo 133:3.

Chiitano chikuperekedwa tsopano, chakuti: “Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chibvumbulutso 22:17) Chimenechi ndicho chiitano chimene Yehova Mulungu akupereka kwa onse owona mtima. Chiitanocho chiri cha kugwiritsira ntchito makonzedwe auzimu a Mulungu kaamba ka moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso.

Kodi mudzasankha kuvomereza chiitanocho? Ziyembekezo zanu za moyo wautaliko, moyo wosatha, zimadalira pa chosankha chanu tsopano!

[Bokosi patsamba 27]

CHIYEMBEKEZO CHA MOYO

Winawake wobadwira mu North America kapena Kumadzulo kwa Europe kumapeto kwa zaka za zana la 18 angayembekezere kukhala ndi moyo kwa msinkhu wa zaka 35 kapena 40. Lerolino, amuna ndi akazi mu United States angayembekezere kukhala ndi moyo kwa chifupifupi zaka 71 ndi 78 mosiyana, ndipo kuwongokera kofananako kwapangidwa m’maiko ena. Tikuzindikira kwambiri za kuthekera kwathu kwa kukhala ndi moyo wautali. Koma kodi pali malire ku mmene chiyembekezo cha moyo chingafutukukire?

Palibe aliyense m’mbiri yaposachedwapa amene wakhala kapena kuyembekezera kukhala kwa zaka 500, 300, kapena ngakhale 200. Mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwa sayansi yamankhwala, chiyembekezo cha moyo lerolino chidakali pansi pa 80. Komabe pali malipoti a anthu okhala ndi zaka 140 kapena ngakhale 150 zakubadwa. Ndipo mu nthaŵi za Baibulo, anthu anakhala ndi zaka mazana zakubadwa. Kodi zimenezo ziri kokha nthano kapena nthanthi?

Mosangalatsa, The New Encyclopœdia Britannica ikulongosola kuti “utali weniweni wa moyo wa munthu ngosadziŵika.” Monga mmene nkhaniyo ikulongosolera, kulingalira kuti anthu ena anakhala ndi zaka 150, “palibe chifukwa chokwanira chokanira kuthekera kwakuti munthu wina angakhale ndi zaka 150 ndi mphindi imodzi. Ndipo ngati zaka 150 ndi mphindi imodzi zikulandiridwa, bwanji osati zaka 150 ndi mphindi ziŵiri, nkupitirizabe?” Nkhaniyo ikupitiriza kuti: “Kuzikidwa pa chidziŵitso chimene chiripo cha moyo wautali, chiŵerengero chotsimikizirika cha utali wa moyo wa munthu sichingaperekedwe.”

Kodi tingamalizenji kuchokera ku zimenezi? Kuti zimene sayansi yamankhwala yaphunzira ponena za kukalamba ndi imfa zazikidwa pa mkhalidwe wa anthu umene tikuwona lerolino. Funso lalikulu liri lakuti kaya mkhalidwe wa anthu nthaŵi zonse wakhala umodzimodzi kapena udzakhalabe umodzimodzi. Lonjezo la Mulungu nlakuti: “Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.” M’dziko latsopano lomayandikira mofulumiralo, “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chibvumbulutso 21:4, 5.

[Chithunzi pamasamba 28, 29]

‘Mtsinje wa madzi a moyo, wonyezemira ngati krustalo, otuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu.’—Chibvumbulutso 22:1

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena