MUTU 15
Sangalalani Chifukwa Chogwira Ntchito Mwakhama
‘Munthu aliyense . . . asangalale ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.’—MLALIKI 3:13.
1-3. (a) Kodi anthu ambiri amaiona bwanji ntchito yawo? (b) Kodi Baibulo limalimbikitsa chiyani pa nkhani ya ntchito, nanga tikambirana mafunso ati?
MASIKU ano anthu ambiri amaona kuti kugwira ntchito si chinthu chosangalatsa. Tsiku lililonse amapita kuntchito asakufuna chifukwa amagwira ntchito yotopetsa kwa maola ambiri. Kodi anthu amenewa angalimbikitsidwe bwanji kuti azikonda ntchito yawo n’kuyamba kusangalala nayo?
2 Baibulo limatilimbikitsa kuti tizigwira ntchito mwakhama. Limanena kuti ntchito ndiponso zimene timapeza chifukwa chogwira ntchito, ndi mphatso. Solomo analemba kuti: “Munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Mlaliki 3:13) Yehova, yemwe amatikonda ndipo nthawi zonse amatifunira zabwino, amafuna kuti tizisangalala ndi ntchito yathu komanso zinthu zimene timapeza chifukwa chogwira ntchito mwakhama. Kuti Mulungu apitirize kutikonda, tiyenera kutsatira maganizo ake ndi mfundo zake pa nkhani ya ntchito.—Werengani Mlaliki 2:24; 5:18.
3 M’mutu uno tikambirana mafunso 4 awa: Kodi tingatani kuti tizisangalala chifukwa chogwira ntchito mwakhama? Kodi ndi ntchito zotani zimene Akhristu oona sayenera kugwira? Kodi tingatani kuti ntchito yathu isamatilepheretse kuchita zinthu zauzimu? Komanso kodi ntchito yofunika kwambiri imene tiyenera kugwira ndi iti? Choyamba, tiyeni tikambirane kaye za Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu, omwe amagwira ntchito mwakhama kuposa wina aliyense m’chilengedwe chonse.
WOLIMBIKIRA NTCHITO KUPOSA ONSE NDI MMISIRI WAKE WALUSO
4, 5. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wolimbikira ntchito?
4 Yehova amagwira ntchito mwakhama kuposa wina aliyense. Lemba la Genesis 1:1 limati: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Mulungu atamaliza ntchito yolenga dziko lapansi ananena kuti zimene analenga “zinali zabwino kwambiri.” (Genesis 1:31) Tinganene kuti iye anakhutira kwambiri ndi ntchito yonse imene anagwira polenga dziko lapansi. Yehova ndi “Mulungu wa chimwemwe,” choncho n’zoonekeratu kuti anasangalala kwambiri chifukwa chogwira ntchito mwakhama.—1 Timoteyo 1:11.
5 Mulungu wathu amalimbikira ntchito ndipo sasiya kugwira ntchito. Patapita zaka zambiri iye atamaliza kulenga zonse zapadziko lapansi, Yesu anati: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano.” (Yohane 5:17) Kodi Atatewa akhala akugwira ntchito yanji? Iwo akhala ali otanganidwa kwambiri potsogolera ndi kusamalira anthu. Analenganso “cholengedwa chatsopano,” omwe ndi Akhristu obadwa ndi mzimu amene adzalamulira ndi Yesu kumwamba. (2 Akorinto 5:17) Komanso akhala akugwira ntchito kuti adzakwaniritse cholinga chimene anali nacho polenga anthu, chakuti adzakhale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano. (Aroma 6:23) Choncho, Yehova amasangalala kwambiri akamaona mmene ntchitoyi ikuyendera. Mulungu akukoka anthu mamiliyoni ambiri ndipo akumvetsera uthenga wa Ufumu n’kusintha moyo wawo kuti iye apitirize kuwakonda.—Yohane 6:44.
6, 7. Kodi Yesu ali ndi mbiri yotani pa nkhani yogwira ntchito mwakhama?
6 Nayenso Yesu wakhala akugwira ntchito mwakhama kwa nthawi yaitali. Asanabwere padziko lapansi pano, iye anatumikira Mulungu ngati “mmisiri wa waluso” polenga zinthu zonse “zakumwamba ndi zapadziko lapansi.” (Miyambo 8:22-31; Akolose 1:15-17) Atabwera padziko lapansi pano, Yesu anapitiriza kugwira ntchito mwakhama. Ali wamg’ono anaphunzira ntchito yamanja ndipo anayamba kudziwika ngati “mmisiri wa matabwa.”a (Maliko 6:3) Ntchito imeneyi imakhala yokhetsa thukuta ndiponso imafunika luso. Ndipo iyenera kuti inali yovuta kwambiri m’nthawi imeneyo chifukwa kunalibe makina ochekera matabwa, masitolo ogulitsa matabwa kapenanso zipangizo zamagetsi. Kodi mungathe kuona m’maganizo anu Yesu akukafuna matabwa, mwina akugwetsa yekha mitengo, kucheka matabwa n’kuwanyamula kupita nawo kumene amagwirira ntchito? Kodi mukutha kumuona akukhoma denga, kukhoma zitseko, ngakhalenso kupanga mipando ndi katundu wina wa m’nyumba? Mosakayikira, Yesu ankasangalala kwambiri chifukwa chogwira ntchito mwakhama komanso mwaluso.
7 Yesu analinso wakhama kwambiri mu utumiki wake. Kwa zaka zitatu ndi hafu anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yofunika kwambiri imeneyi. Pofuna kulalikira kwa anthu onse amene akanatha kuwapeza, iye ankatha tsiku lonse, kuyambira m’mamawa mpaka usiku akulalikira. (Luka 21:37, 38; Yohane 3:2) Ankapita “mu mzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Yesu ankayenda wapansi maulendo ataliatali m’misewu yafumbi pofuna kulalikira uthenga wabwino.
8, 9. Kodi Yesu anasangalala bwanji chifukwa chogwira ntchito mwakhama?
8 Kodi Yesu ankasangalala chifukwa chogwira ntchito mwakhama mu utumiki? Inde. Iye anafesa mbewu za choonadi cha Ufumu ndipo anasiya mbewuzo zitakhwima moti zinali zofunika kukolola. Kugwira ntchito ya Mulungu kunkam’patsa Yesu mphamvu ndiponso kunali ngati chakudya chake moti ankalolera kukhala wosadya pofuna kuti akwaniritse ntchitoyi. (Yohane 4:31-38) Tangoganizani mmene anasangalalira atamaliza utumiki wake padziko lapansi pamene anauza Atate wake moona mtima kuti: “Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa.”—Yohane 17:4.
9 Ndithudi, Yehova ndi Yesu ndi zitsanzo zabwino kwambiri za amene amasangalala chifukwa chogwira ntchito mwakhama. Kukonda Yehova kumatilimbikitsa kuti ‘tizitsanzira Mulungu.’ (Aefeso 5:1) Ndipo kukonda Yesu kumatilimbikitsa ‘kutsatira mapazi ake mosamala kwambiri.’ (1 Petulo 2:21) Choncho, tsopano tiyeni tikambirane zimene tingachite kuti nafenso tizisangalala chifukwa chogwira ntchito mwakhama.
ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA CHIFUKWA CHOGWIRA NTCHITO MWAKHAMA
Kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kungakuthandizeni kuti muzisangalala chifukwa chogwira ntchito mwakhama
10, 11. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tisamadane ndi ntchito imene timagwira?
10 Nawonso Akhristu oona amafunika kugwira ntchito ndipo timafuna kuti tizisangalala komanso tizikhutira ndi ntchito imene timagwira. Komabe, zimenezi zingakhale zovuta kwambiri ngati timagwira ntchito imene sitimaikonda. Kodi zingatheke bwanji kuti tizisangalala ndi ntchito yathu, ngakhale kuti sitimaikonda?
11 Muziona ubwino wa ntchito yanu. Nthawi zambiri sitingathe kusintha mmene zinthu zilili pa ntchito yathu, koma tingathe kusintha maganizo athu okhudza ntchitoyo. Kuganizira mmene Mulungu amaionera ntchito kungatithandize kuona ubwino wa ntchito yathu. Mwachitsanzo, ngati ndinu mutu wa banja dziwani kuti ntchito yanu, kaya ioneke yonyozeka bwanji, imakuthandizani kupezera banja lanu zinthu zofunika pa moyo. Choncho, kusamalira anthu amene mumawakonda ndi nkhani yofunika kwa Mulungu. Mawu ake amanena kuti amene amalephera kusamalira banja lake, amakhala “woipa kuposa munthu wosakhulupirira.” (1 Timoteyo 5:8) Kukumbukira kuti ntchito yanu imakuthandizani kukwaniritsa udindo umene Mulungu anakupatsani, kungakupangitseni kusangalala kwambiri ndi ntchito yanu kusiyana ndi anzanu amene mumagwira nawo ntchito.
12. Kodi kulimbikira ntchito ndiponso kukhala okhulupirika pa ntchito, n’kothandiza bwanji?
12 Muzilimbikira ntchito ndiponso muzikhala wokhulupirika. Zingakuyendereni bwino ngati mumagwira ntchito mwakhama ndiponso ngati mumayesetsa kuwonjezera luso lanu pa ntchitoyo. Nthawi zambiri mabwana amakonda kwambiri anthu olimbikira ntchito ndiponso aluso. (Miyambo 12:24; 22:29) Monga Akhristu oona, tiyenera kukhala okhulupirika pa ntchito. Tisamabere makampani kapena mabwana athu ndalama, katundu kapenanso nthawi. (Aefeso 4:28) Monga tinaonera m’mutu wapita uja, kukhala okhulupirika n’kothandiza kwambiri. Nthawi zambiri mabwana amakhulupirira antchito oona mtima. Ndipo kaya abwana athu adziwe kuti timalimbikira ntchito kapena ayi, tingakhalebe osangalala chifukwa chokhala ndi “chikumbumtima choona” komanso podziwa kuti tikusangalatsa Mulungu amene timam’konda.—Aheberi 13:18; Akolose 3:22-24.
13. Kodi kusonyeza khalidwe labwino kuntchito kungakhale ndi zotsatira zotani?
13 Muzikumbukira kuti khalidwe lanu labwino limalemekeza Mulungu. Anthu amaona tikamasonyeza makhalidwe abwino kwambiri achikhristu kuntchito. Kodi zotsatira zake zimakhala zotani? ‘Timakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu.’ (Tito 2:9, 10) Kusonyeza khalidwe labwino kungathandize ena kuona ubwino wa kulambira kwathu ndipo angakopeke nako. Tangoganizani mmene mungasangalalire ngati mnzanu wakuntchito atayamba kuphunzira choonadi chifukwa cha khalidwe lanu labwino. Koma koposa zonse, khalidwe lanu labwino limalemekeza Yehova ndi kusangalatsa mtima wake. Kodi mukuganiza kuti pali chinthu chinanso chosangalatsa kwambiri kuposa kudziwa kuti Yehova akusangalala nanu?—Werengani Miyambo 27:11; 1 Petulo 2:12.
MUZISANKHA NTCHITO MWANZERU
14-16. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso awiri ofunika ati tisanayambe ntchito ina iliyonse?
14 Baibulo lilibe malangizo atsatanetsatane okhudza ntchito zimene zili zololeka kapena zosaloleka kwa Akhristu. Komatu zimenezi sizikutanthauza kuti tingathe kugwira ntchito ina iliyonse. Malemba angatithandize kusankha ntchito yabwino imene Mulungu angasangalale nayo. Ndiponso angatithandize kupewa kugwira ntchito zimene Mulungu sangasangalale nazo. (Miyambo 2:6) Tikapeza ntchito, tiziyamba tadzifunsa kaye mafunso awiri ofunika kwambiri awa:
15 Kodi kugwira ntchito imeneyi kungakhale kuchita zinthu zimene Baibulo limaletsa? Mawu a Mulungu amaletsa mosapita m’mbali kuba, kunama ndiponso kupanga mafano. (Ekisodo 20:4; Machitidwe 15:29; Aefeso 4:28; Chivumbulutso 21:8) Choncho, tiyenera kupewa ntchito iliyonse imene ingafune kuti tizichita zimenezi. Chifukwa choti timakonda Yehova, sitingalole kugwira ntchito imene ingatipangitse kuswa malamulo ake.—Werengani 1 Yohane 5:3.
16 Kodi ntchito imeneyi ingandipangitse kuthandizira kapena kulimbikitsa zoipa? Taganizirani chitsanzo ichi: Kugwira ntchito yolandira alendo sikulakwa. Koma bwanji ngati Mkhristu atapeza ntchito imeneyi kuchipatala chochotsa mimba? N’zoona kuti ntchito yake siyothandiza mwachindunji kuchotsa mimba. Komabe, kodi kugwira ntchito imeneyi sikungakhale kuthandizira ntchito za chipatala chimene cholinga chake ndi kuchotsa mimba, chinthu chimene Mawu a Mulungu amaletsa? (Ekisodo 21:22-24) Monga anthu amene timakonda Yehova, sitingafune ngakhale pang’ono kuchita zinthu zosemphana ndi Malemba.
17. (a) Kodi tiyenera kuganizira zinthu ziti tisanayambe ntchito ina iliyonse? (Onani bokosi “Kodi Ndiyenera Kulowa Ntchito Imeneyi?”) (b) Kodi mungatani kuti chikumbumtima chanu chizikuthandizani kusankha zinthu zimene zingasangalatse Mulungu?
17 Mafunso ambiri okhudza ntchito angathe kuyankhidwa ngati titaganizira mofatsa mayankho a mafunso awiri ofunika kwambiri amene ali m’ndime 15 ndi 16. Komanso, pali mfundo zina zofunika kuziganizira bwino tisanayambe ntchito iliyonse.b Sitingayembekezere gulu la kapolo wokhulupirika kupereka malamulo okhudza vuto lililonse limene tingakhale nalo pa nkhani ya ntchito. N’chifukwa chake tiyenera kuchita zinthu mwanzeru. ngati mmene tinaphunzirira m’mutu 2, tiyenera kuphunzitsa chikumbumtima chathu pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pa moyo wathu. Tikaphunzitsa ‘mphamvu zathu za kuzindikira,’ chikumbumtima chathu chidzatithandiza kusankha ntchito zimene zingakondweretse Mulungu ndiponso zimene zingachititse kuti apitirize kutikonda.—Aheberi 5:14.
NTCHITO YATHU ISAMATILEPHERETSE KUCHITA ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI
18. Kodi n’chifukwa chiyani n’zovuta kupitiriza kuchita zinthu zimene zingapangitse kuti Yehova azitikonda?
18 ‘M’masiku otsiriza’ komanso ‘m’nthawi yovuta’ ino, n’kovuta kwambiri kuti nthawi zonse tizichita zinthu zimene zingapangitse kuti Yehova apitirize kutikonda. (2 Timoteyo 3:1) Kupeza ntchito ndiponso kukhalabe pa ntchitoyo n’kovuta kwambiri. Monga Akhristu oona, timadziwa kufunika kogwira ntchito mwakhama kuti tizipeza zofunika pa banja lathu. Koma ngati sitingasamale, kuchuluka kwa ntchito kapena maganizo a dzikoli okonda kwambiri chuma zingasokoneze zochita zathu zauzimu. (1 Timoteyo 6:9, 10) Tiyeni tikambirane zimene tingachite kuti ntchito yathu isamatilepheretse kuchita “zinthu zofunika kwambiri.”—Afilipi 1:10.
19. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse, ndipo zimenezi zingatithandize kupewa chiyani?
19 Khulupirirani Yehova ndi mtima wonse. (Werengani Miyambo 3:5, 6.) Yehova ndi woyenera kumukhulupirira. Ndipotu, amatisamalira. (1 Petulo 5:7) Iye amadziwa bwino zimene timafunikira kuposa mmene ifeyo timadziwira, ndipo dzanja lake si lalifupi moti n’kulephera kutithandiza. (Salimo 37:25) Choncho, n’kofunika kumvera Mawu ake amene amatikumbutsa kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’” (Aheberi 13:5) Atumiki ambiri a nthawi zonse angavomereze kuti Mulungu amapereka zinthu zofunika pa moyo. Ngati timakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova amatisamalira, timapewa kudera nkhawa kwambiri za mmene tingapezere zinthu zofunika pa banja lathu. (Mateyu 6:25-32) Sitingalole kuti ntchito imene tikugwira itilepheretse kuchita zinthu zauzimu, monga kulalikira uthenga wabwino ndi kusonkhana.—Mateyu 24:14; Aheberi 10:24, 25.
20. Kodi kukhala ndi diso lolunjika pa chinthu chimodzi kumatanthauza chiyani, nanga tingatani kuti tikhalebe ndi diso limeneli?
20 Muzikhala ndi diso lolunjika pa chinthu chimodzi. (Werengani Mateyu 6:22, 23.) Kukhala ndi diso lolunjika pa chinthu chimodzi kumatanthauza kukhala ndi moyo wosalira zinthu zambiri. Mkhristu amene ali ndi diso lolunjika pa chinthu chimodzi amaika maganizo ake onse pochita chifuniro cha Mulungu. Ngati diso lathu lili lotere, sitingatanganidwe ndi kufuna ntchito ya malipiro apamwamba ndiponso sitingafune zinthu zambiri pa moyo wathu. Komanso, sitingakhale ndi mtima womangofuna zinthu zilichonse zimene zangotuluka kumene zomwe otsatsa malonda amafuna kuti tizikhulupirira kuti n’zimene zingatipangitse kukhala osangalala. Kodi mungatani kuti mukhalebe ndi diso lolunjika pa chinthu chimodzi? Pewani kutenga ngongole popanda zifukwa zomveka. Musadziunjikire katundu amene angakutengereni nthawi yambiri kumusamalira. Tsatirani malangizo a m’Baibulo akuti tizikhala okhutira ndi “chakudya, zovala ndi pogona.” (1 Timoteyo 6:8) Yesetsani mmene mungathere kuti muzikhala moyo wosalira zambiri.
21. N’chifukwa chiyani tiyenera kuika zinthu zofunika kwambiri pa malo oyamba, ndipo kodi zinthu zakezo ndi ziti?
21 Nthawi zonse muziika zinthu zauzimu patsogolo ndipo musalole china chilichonse kukusokonezani. Popeza pa tsiku timakhala ndi nthawi yochepa, tiziyamba kuchita zinthu zomwe n’zofunika kwambiri. Popanda kutero, zinthu zosafunika kwenikweni zingatidyere nthawi yathu yamtengo wapatali, n’kutilepheretsa kuchita zinthu zofunika kwambiri. Kodi n’chiyani chimene tiyenera kuika pamalo oyamba m’moyo wathu? Anthu ambiri m’dzikoli amaika maganizo awo onse pa maphunziro apamwamba n’cholinga choti adzapeze ntchito yabwino kwambiri. Komabe, Yesu analimbikitsa otsatira ake ‘kupitiriza kufuna ufumu choyamba.’ (Mateyu 6:33) Choncho, monga Akhristu oona, timaika Ufumu wa Mulungu patsogolo. Moyo wathu, zimene timasankha kuchita, ndiponso zolinga zathu ziyenera kusonyeza kuti zinthu za Ufumu komanso kuchita chifuniro cha Mulungu n’zofunika kwambiri kwa ife kuposa kupeza chuma kapena ntchito.
MUZILIMBIKIRA UTUMIKI
Tingasonyeze kuti timakonda Yehova tikamaika patsogolo ntchito yolalikira
22, 23. (a) Kodi ntchito yofunika kwambiri kwa Akhristu oona ndi iti, ndipo tingasonyeze bwanji kuti timaona ntchito imeneyi kukhala yofunika kwambiri? (Onani bokosi “Zimene Ndinasankha Kuchita Zandithandiza Kukhala Wosangalala.”) (b) Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani pa nkhani ya ntchito?
22 Popeza kuti tili kumapeto kwenikweni kwa masiku otsiriza, ife Akhristu oona tiyenera kuika maganizo athu onse pa ntchito yathu yeniyeni, yomwe ndi kulalikira komanso kuphunzitsa anthu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Potsatira zimene Yesu anachita, ifenso tiyenera kumatanganidwa kwambiri ndi ntchito yopulumutsa miyoyo imeneyi. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona ntchito imeneyi kukhala yofunika kwambiri? Atumiki a Mulungu ambiri amadzipereka ndi mtima wonse pogwira ntchito yolalikira monga ofalitsa mumpingo. Ena asintha zinthu zina pa moyo wawo kuti athe kuchita upainiya kapena umishonale. Pozindikira kufunika kwa zolinga zauzimu, makolo ambiri amalimbikitsa ana awo kuchita utumiki wa nthawi zonse. Kodi amene amalalikira za Ufumu mwakhama amasangalala chifukwa chochita utumikiwu? Inde, amasangalala kwambiri. Kutumikira Yehova ndi mtima wonse ndi njira yokhayo imene ingatipangitse kukhala osangalala komanso kupeza madalitso ochuluka.—Werengani Miyambo 10:22.
23 Ambirife timagwira ntchito nthawi yaitali kuti tipeze zinthu zofunika pa banja lathu. Kumbukirani kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala chifukwa chogwira ntchito mwakhama. Tingathe kukhala osangalala ndi ntchito yathu ngati maganizo ndi zochita zathu pa ntchito zili zogwirizana ndi maganizo komanso mfundo za Mulungu. Ndipo tiyenera kutsimikiza mtima kuti ntchito isatilepheretse kugwira ntchito yofunika kwambiri, yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Tikamaika patsogolo ntchito imeneyi, timasonyeza kuti timakonda Yehova ndipo nayenso adzapitiriza kutikonda.
a Buku lina linanena kuti mawu Achigiriki amene anamasuliridwa kuti “mmisiri wa matabwa,” “amatanthauza ntchito zosiyanasiyana zimene mmisiriyo angagwire, kaya kukhoma denga la nyumba, kupanga katundu wa m’nyumba kapenanso china chilichonse chamatabwa.”
b Kuti mudziwe mfundo zambiri zoyenera kuziganizira posankha ntchito, onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1999, patsamba 28 mpaka 30, ndiponso ya Chingelezi ya July 15, 1982, patsamba 26.