Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 10/1 tsamba 15-20
  • Kuchirikiza Mokhulupirika Mawu a Mulungu Ouziridwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchirikiza Mokhulupirika Mawu a Mulungu Ouziridwa
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchiyani Chachitikira Dzina la Mulungu?
  • Pamene Zokhulupirira Zamunthu Zikhudza Katembenuzidwe
  • Kuchirikiza Mawu a Mulungu Mokhulupirika
  • New World Translation
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Chochitika Chosaiŵalika kwa Okonda Mawu a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Dzina la Mulungu ndi Otembenuza Baibulo
    Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
  • Kodi Mungadziwe Bwanji Baibulo Lomasuliridwa Bwino?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 10/1 tsamba 15-20

Kuchirikiza Mokhulupirika Mawu a Mulungu Ouziridwa

“Takaniza zobisika zamanyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga.” ​—2 AKORINTO 4:2.

1. (a) Kodi nchiyani chafunika kuti ntchito yotchulidwa pa Mateyu 24:14 ndi 28:19, 20 ichitike? (b) Pamene masiku otsiriza anayamba, kodi Baibulo linalipo m’zinenero za anthu zochuluka motani?

MU ULOSI wake waukuluwo wonena za kukhalapo kwake monga mfumu ndi chimaliziro cha dongosolo lakaleli la zinthu, Yesu Kristu ananeneratu kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” Analangizanso otsatira ake kuti: “Phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewo kumaloŵetsapo ntchito yaikulu yotembenuza ndi kusindikiza Baibulo, kuphunzitsa anthu zimene limatanthauza, ndi kuwathandiza kulitsatira m’moyo wawo. Ndi mwaŵi waukulu chotani nanga kukhala ndi mbali pantchito imeneyi! Podzafika 1914 Baibulo kapena mbali yake ina linali litafalitsidwa kale m’zinenero 570. Koma kuyambira pamenepo zinenero mazana ambiri ndi malankhulidwe ambiri zawonjezedwapo, ndipo zinenero zambiri zakhala ndi matembenuzidwe ambiri.a

2. Kodi ndi zolinga zosiyanasiyana zotani zimene zasonkhezera ntchito ya otembenuza ndi ofalitsa Baibulo?

2 Nkovuta kwa wotembenuza aliyense kutenga nkhani ya m’chinenero china ndi kuimveketsa kwa awo amene amamva ndi kuŵerenga chinenero chinanso. Otembenuza Baibulo ena achita ntchito yawo mosamala kwambiri podziŵa kuti akutembenuza Mawu a Mulungu. Ena angokopeka ndi maphunziro okhudza ntchitoyo. Mwina anaona nkhani za m’Baibulo monga kuti zangokhala mwambo wabwino wa makolo akale. Kwa ena, chipembedzo ndicho malonda awo, ndipo kufalitsa buku lokhala ndi dzina lawo monga wotembenuza kapena wofalitsa kuli mbali yopezera zofunika za moyo. Mosakayikira zolinga zawo zimakhudza mmene amachitira ntchito yawoyo.

3. Kodi a New World Bible Translation Committee anaiona motani ntchito yawo?

3 Mawu otsatirawa a New World Bible Translation Committee ngochititsadi chidwi: “Kutembenuza Malemba Opatulika kumatanthauza kutembenuzira malingaliro ndi zonena za Yehova Mulungu m’chinenero china . . . Lingaliro limenelo limachititsa kuganiza mozama. Otembenuza Baibuloli, amene amaopa ndi kukonda Mlembi Wamkulu Waumulungu wa Malemba Opatulika, akudzimva kuti ayenera kumchitira Iye ntchito yapadera yopereka malingaliro ake ndi zilengezo zake molongosoka koposa monga momwe angathere. Amamvanso kuti ali ndi ntchito yochitira oŵerenga ofuna kudziŵa zinthu amene amadalira pa Mawu ouziridwa a Mulungu Wam’mwambamwamba otembenuzidwa kuti akapeze chipulumutso chosatha. Anali malingaliro amenewo a kuona kufunika kwa ntchitoyi amene anachititsa komiti ya amuna odziperekawa kutulutsa New World Translation of the Holy Scriptures pambuyo pa zaka zambiri.” Cholinga cha komitiyi chinali kukhala ndi matembenuzidwe a Baibulo olunjika ndi omveka ndipo amene adzamamatira kwambiri ku Chihebri ndi Chigiriki choyambirira kwakuti adzakhala maziko a kukula kosalekeza m’chidziŵitso cholongosoka.

Kodi Nchiyani Chachitikira Dzina la Mulungu?

4. Kodi dzina la Mulungu nlofunika motani m’Baibulo?

4 Chimodzi cha zolinga zazikulu za Baibulo ndicho kuthandiza anthu kudziŵa Mulungu woona. (Eksodo 20:2-7; 34:1-7; Yesaya 52:6) Yesu Kristu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti dzina la Atate wake “liyeretsedwe,” likhale lopatulika, kapena lionedwe loyera. (Mateyu 6:9) Mulungu anachititsa dzina lake kulembedwa m’Baibulo nthaŵi zoposa 7,000. Akufuna kuti anthu adziŵe dzinalo ndi mikhalidwe ya Mwini wake.​—Malaki 1:11.

5. Kodi otembenuza osiyanasiyana alitchula motani dzina la Mulungu?

5 Otembenuza Baibulo ambiri asonyeza ulemu weniweni padzina la Mulungu limenelo ndipo aligwiritsira ntchito mosalekeza m’zotembenuza zawo. Otembenuza ena amakonda dzina lakuti Yahweh. Ena asankha mtundu wa dzina la Mulungu umene amagwiritsira ntchito m’chinenero chawo umene mosakayikira konse umatanthauzabe zimene zili m’malemba achihebri, mwinamwake kalembedwe kodziŵika bwino chifukwa chakuti kagwiritsidwa ntchito kwa nthaŵi yaitali. New World Translation of the Holy Scriptures imagwiritsira ntchito “Jehovah” nthaŵi 7,210 m’malemba ake.

6. (a) M’zaka zaposachedwa, kodi otembenuza atani nawo mawu onena za dzina la Mulungu? (b) Kodi zimenezi nzofala motani?

6 M’zaka zaposachedwa, ngakhale kuti otembenuza Baibulo agwiritsira ntchito maina a milungu yachikunja monga Baala ndi Moleki, iwo akuchotsa dzina lake la Mulungu woona pamalo owonjezereka m’matembenuzidwe a Mawu ake ouziridwa. (Eksodo 3:15; Yeremiya 32:35) M’malemba monga Mateyu 6:9 ndi Yohane 17:6, 26, kope lina lofala lachialubaniya limatembenuza mawu achigiriki otanthauza “dzina lanu” (kunena dzina la Mulungu) kungokhala “inu,” monga kuti malemba amenewo sakunenapo za dzina. Pa Salmo 83:18, ma Baibulo a The New English Bible ndi Today’s English Version anachotsa ponse paŵiri dzina laumwini la Mulungu ndi mawu alionse osonyeza kuti Mulungu ali ndi dzina. Ngakhale kuti dzina la Mulungu linaonekera m’matembenuzidwe akale a Malemba Achihebri m’zinenero zambiri, matembenuzidwe atsopano nthaŵi zambiri amalichotsamo kapena amalilemba m’manoti a m’mbali. Ndi mmene zakhalira m’Chingelezi, ndi m’zinenero zambiri za ku Afirika, India, South America, Ulaya, ndi zisumbu za m’nyanja ya Pacific.

7. (a) Kodi otembenuza ma Baibulo ena a m’Afirika achita nalo motani dzina la Mulungu? (b) Inuyo mukumva nazo bwanji zimenezi?

7 Otembenuza Baibulo m’zinenero zina za mu Afirika akuchitanso zina zowonjezereka. M’malo mongochotsa dzina la Mulungu ndi kuikapo dzina laulemu la m’Malemba, monga Mulungu kapena Ambuye, iwo akuikapo maina otengedwa m’zikhulupiriro zachipembedzo zakumaloko. M’Baibulo la The New Testament and Psalms in Zulu (lotembenuzidwa mu 1986), dzina laulemu lakuti Mulungu (uNkulunkulu) analigwiritsira ntchito moligwirizanitsa ndi dzina laumwini (uMvelinqangi) limene Azulu amalidziŵa kuti limatanthauza ‘kholo lalikulu lolambiridwa kudzera mwa makolo akufa a anthu.’ Nkhani ina m’magazini akuti The Bible Translator, ya October 1992, inanena kuti pokonza Baibulo lachicheŵa limene lidzatchedwa kuti Buku Loyera, otembenuza anagwiritsira ntchito Chauta monga dzina laumwini loloŵa m’malo mwa dzina la Yehova. Chauta, nkhaniyo inafotokoza motero, ndiye “Mulungu amene amamdziŵa ndi kumlambira nthaŵi zonse.” Komabe, ambiri mwa anthu ameneŵa amalambiranso zimene amakhulupirira kukhala mizimu ya anthu akufa. Kodi nzoona kuti ngati anthu apereka mapemphero awo kwa “Chamoyo Chapamwamba,” ndiye kuti dzina lililonse limene adzagwiritsira ntchito potchula “Chamoyo Chapamwamba” chimenecho ndi lolingana ndi dzina laumwini lakuti Yehova, mosasamala kanthu kuti kulambira kwawo kumaphatikizaponso chiyani? Kutalitali! (Yesaya 42:8; 1 Akorinto 10:20) Kuchotsa dzina laumwini la Mulungu ndi kuikapo lina limene lipangitsa anthu kuona monga kuti zikhulupiriro zawo zamwambo zili bwino kwambiri sikumawathandiza kuyandikira kwa Mulungu woona.

8. Kodi nchifukwa ninji chifuno cha Mulungu chodziŵikitsa dzina lake sichinasokonezedwe?

8 Zonsezi sizinasinthe kapena kusokoneza chifuno cha Yehova chodziŵikitsa dzina lake. Zinenero za ku Ulaya, Afirika, maiko a ku Amereka, Kummaŵa, ndi zisumbu za m’nyanja, zikali ndi ma Baibulo ambiri amene ali ndi dzina la Mulungu. M’maiko ndi magawo 233 mulinso Mboni za Yehova zoposa 5,400,000 zimene zonse pamodzi zimathera maola oposa 100,000,000 pachaka kuuza ena za dzina ndi chifuno cha Mulungu woona. Zimasindikiza ndi kufalitsa ma Baibulo​—amene amagwiritsira ntchito dzina la Mulungu​—m’zinenero zolankhulidwa ndi anthu pafupifupi 3,600,000,000 mwa anthu onse padziko lapansi, kuphatikizapo Chidatchi, Chifrenchi, Chingelezi, Chipwitikizi, Chirasha, Chisipanya, ndi Chitchaina. Zimasindikizanso zothandiza kuphunzira Baibulo m’zinenero zodziŵidwa ndi anthu ambirimbiri padziko lapansi. Posachedwapa Mulungu iyemwini adzachitapo kanthu m’njira imene idzakwaniritsa motsimikizika chilengezo chake chakuti amitundu “adzadziŵa kuti [iye ndi] Yehova.”​—Ezekieli 38:23.

Pamene Zokhulupirira Zamunthu Zikhudza Katembenuzidwe

9. Kodi Baibulo limasonyeza motani ukulu wa udindo wa ogwiritsira ntchito Mawu a Mulungu?

9 Otembenuza pamodzi ndi ophunzitsa Mawu a Mulungu ali ndi udindo waukulu. Ponena za utumiki wake ndi wa anzake, mtumwi Paulo anati: “Takaniza zobisika zamanyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga [“kusukulutsa mawu a Mulungu,” NW]; koma ndi maonekedwe a choonadi tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.” (2 Akorinto 4:2) Kusukulutsa kumatanthauza kuipitsa chinthu mwa kuchisanganiza ndi china cha mtundu wina kapena chosafunika. Mtumwi Paulo sanali ngati abusa osakhulupirika a Israyeli a m’tsiku la Yeremiya amene Yehova anawadzudzula chifukwa cholalikira za m’mutu mwawo m’malo mwa zimene Mulungu ananena. (Yeremiya 23:16, 22) Koma kodi nchiyani chachitika m’nthaŵi zamakonozi?

10. (a) Kodi zolinga zina zosiyana ndi kukhala wokhulupirika kwa Mulungu zasonkhezera motani otembenuza ena amakono? (b) Kodi iwo molakwitsa anali kukhala pamalo ati?

10 M’Nkhondo Yadziko II, komiti ya akatswiri a zaumulungu ndi apasitala inagwirizana ndi boma la Nazi ku Germany kuti itulutse “Chipangano Chatsopano” chokonzedwanso chimene chinasiya mawu onse abwino onena za Ayuda ndi mawu onse osonyeza kuti Yesu Kristu anabadwa kwa makolo achiyuda. Chaposachedwapa, otembenuza amene anatulutsa The New Testament and Psalms: An Inclusive Version anatsata njira yawo, nayesetsa kuchotsa mawu onse osonyeza kuti Ayuda anali ndi liwongo pa imfa ya Kristu. Otembenuza amenewo anaganizanso kuti oŵerenga ochirikiza zoyenera za akazi adzakondwa ngati Mulungu sanamutche Atate, koma Atate-Amayi ndipo ngati Yesu anamutcha Mwana wa Mulungu [God’s Child], osati Mwana wa Wamwamuna wa Mulungu [God’s Son]. (Mateyu 11:27, NW) Pochita zimenezo, iwo anachotsa pulinsipulo lakuti akazi azigonjera amuna awo ndi kuti ana azimvera makolo awo. (Akolose 3:18, 20) Otembenuza zimenezo ndithudi sanali otsimikiza mtima monga mtumwi Paulo pa ‘kusasukulutsa mawu a Mulungu.’ Iwo anaiŵala ntchito ya wotembenuza, nakhala pamalo a wolemba, kupanga mabuku amene anagwiritsira ntchito mbiri ya Baibulo kukhala njira yochirikizira za m’mutu mwawo.

11. Kodi ziphunzitso za Dziko Lachikristu zimasiyana motani ndi zimene Baibulo limanena pankhani ya sou ndi imfa?

11 Matchalitchi ambiri a m’Dziko Lachikristu amaphunzitsa kuti sou ya munthu ndi mzimu, kuti imachoka m’thupi paimfa, ndi kuti siikufa. Mosiyana ndi zimenezo, matembenuzidwe akale a Baibulo amanena momveka kuti anthu ndiwo sou, kuti nyama ndi sou, ndi kuti sou imafa. (Genesis 12:5; 36:6; Numeri 31:28; Yakobo 5:20) Zimenezo zavutitsa malingaliro a atsogoleri achipembedzo.

12. Kodi matembenuzidwe ena aposachedwa amabisa motani choonadi chofunika kwambiri cha Baibulo?

12 Tsopano matembenuzidwe ena atsopano amabisa choonadi chimenechi. Motani? Amangopeŵa kutembenuza mwachindunji nauni yachihebri yakuti neʹphesh (sou) m’malemba ena. Pa Genesis 2:7, amanena kuti munthu woyamba “anakhala wamoyo” (m’malo mwakuti “anakhala sou yamoyo”). Mwina amanena kuti “cholengedwa” m’malo mwa “sou” potchula nyama. (Genesis 1:21) Pamalemba ena monga Ezekieli 18:4, 20 amanena za “munthuyo” kapena “ameneyo” (m’malo mwa “sou”) kuti ndiye amafa. Mwinamwake, katembenuzidwe kameneka nkoyenera kwa wotembenuzayo. Koma kodi ndi thandizo lotani limene kamapereka kwa wofunafuna choonadi moona mtima amene maganizo ake anapotozedwa kale ndi ziphunzitso za Dziko Lachikristu zosakhala za m’Malemba?b

13. Kodi ma Baibulo ena abisa motani chifuno cha Mulungu chokhudza dziko lapansi?

13 Poyesayesa kuchirikiza chikhulupiriro chawo chakuti anthu onse abwino amapita kumwamba, otembenuza​—kapena akatswiri a zaumulungu amene amapenda zotembenuza zawo​—amayesetsa kubisanso zimene Baibulo limanena pankhani ya chifuno cha Mulungu chokhudza dziko lapansi. Pa Salmo 37:11, matembenuzidwe angapo amangoti ofatsa adzalandira “dziko.” Liwu lakuti “dziko” ndi matembenuzidwe oyenerera a liwu logwiritsiridwa ntchito m’lemba lachihebri (ʼeʹrets). Komabe, Baibulo la Today’s English Version (limene lakhala maziko a matembenuzidwe a zinenero zina zambiri) limawonjezeranso zina. Ngakhale kuti Baibulo limeneli limatembenuza liwu lachigiriki ge kukhala “dziko lapansi” nthaŵi 17 mu Uthenga Wabwino wa Mateyu, pa Mateyu 5:5 limachotsapo liwu lakuti “dziko lapansi” ndi kuikapo mawu akuti “chimene Mulungu walonjeza.” Mamembala atchalitchi amangoganiza za kumwamba basi. Sakuuzidwa moona mtima kuti, pa Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu Kristu ananena kuti odekha, ofatsa, kapena odzichepetsa “adzalandira dziko lapansi.”

14. Kodi ncholinga chadyera chotani chimene chimaonekera m’ma Baibulo ena?

14 Katembenuzidwe kena ka Malemba mosakayikira anakachita ncholinga chothandiza alaliki kukhala ndi malipiro abwino. Nzoona kuti Baibulo limati: “Wogwira ntchito ayenera kulipira kwake.” (1 Timoteo 5:18) Koma pa 1 Timoteo 5:17, pamene pamanena kuti akulu akuweruza bwino “ayesedwe oyenera ulemu woŵirikiza,” ulemu wokha umene ena amaona monga woyenera kutchulidwa ndi wokhudza ndalama. (Yerekezerani ndi 1 Petro 5:2.) Choncho, Baibulo la The New English Bible limanena kuti akulu ameneŵa “ali oyenerera malipiro oŵirikiza,” ndipo Baibulo la Contemporary English Version limanena kuti “ayenera kulipidwa moŵirikiza.”

Kuchirikiza Mawu a Mulungu Mokhulupirika

15. Kodi tingadziŵe bwanji ma Baibulo amene tingagwiritsire ntchito?

15 Kodi zonsezi zimatanthauzanji kwa odziŵerengera okha Baibulo ndi kwa ogwiritsira ntchito Baibulo kuphunzitsa ena? Zinenero zambiri zazikulu zili ndi matembenuzidwe ambiri a Baibulo amene mungasankhepo. Sonyezani kuzindikira posankha Baibulo logwiritsira ntchito. (Miyambo 19:8) Ngati Baibulo silitchula momveka kuti Mulungu iyemwini ndani​—kuchotsa dzina lake m’Mawu ake ouziridwa pachifukwa chilichonse​—kodi otembenuzawo angakhale atasinthanso mbali zina za malemba a m’Baibulo? Ngati mwakayikira kulondola kwa katembenuzidwe kena, yesetsani kukayerekezera ndi matembenuzidwe akale. Ngati ndinu mphunzitsi wa Mawu a Mulungu, sankhani matembenuzidwe omamatira kwambiri ku zimene zili m’malemba oyambirira achihebri ndi achigiriki.

16. Kodi aliyense wa ife angasonyeze motani kukhulupirika pa kugwiritsira ntchito kwathu Mawu ouziridwa a Mulungu?

16 Tonsefe aliyense payekha tiyenera kukhala okhulupirika ku Mawu a Mulungu. Timachita zimenezo mwa kusamaladi zimene amanena moti, ngati nkotheka, tsiku lililonse nkumakhala ndi nthaŵi yoŵerenga Baibulo. (Salmo 1:1-3) Timachita zimenezo mwa kutsatira mosamalitsa m’moyo wathu zimene amanena, kuphunzira kugwiritsitsira ntchito mapulinsipulo ake ndi zitsanzo zake monga maziko opangira zosankha zabwino. (Aroma 12:2; Ahebri 5:14) Timasonyeza kuti ndife ochirikiza okhulupirika a Mawu a Mulungu mwa kuwalalikira kwa ena mwachangu. Timachitanso zimenezo monga aphunzitsi mwa kugwiritsira ntchito Baibulo mosamala, osalipotoza kapena kuwonjezera zimene limanena kuti zigwirizane ndi malingaliro athu. (2 Timoteo 2:15) Zimene Mulungu waneneratu zidzachitika mosalephereka. Iye amakwaniritsa Mawu ake mokhulupirika. Tiyenitu tiwachirikize mokhulupirika.

[Mawu a M’munsi]

a United Bible Societies mu 1997 inandandalika zinenero ndi malankhulidwe 2,167 m’zimene Baibulo, lathunthu kapena mbali yake, lafalitsidwa. Chiŵerengero chimenechi chikuphatikizapo malankhulidwe ambiri a zinenero zina.

b Nkhani ino ikunena kwambiri za zinenero zomwe zingafotokoze bwino lomwe nkhaniyi koma otembenuza a zinenerozo amalekera dala kutero. Chifukwa cha kuchepa kwa mawu m’zinenero zina, otembenuza amalephera kuchita zambiri. Choncho, alangizi oona mtima achipembedzo adzafotokoza kuti ngakhale kuti wotembenuza anagwiritsira ntchito mawu osiyanasiyana kapena ngakhale kuti anagwiritsira ntchito liwu lokhala ndi matanthauzo ena osakhala a m’Malemba, liwu la m’chinenero choyambirira, neʹphesh, limagwira ntchito kwa anthu ndi nyama zomwe ndipo limatanthauza chinthu chimene chimapuma, kudya, ndipo chimene chingafe.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi nzolinga zotani zimene zasonkhezera ntchito ya otembenuza Baibulo m’nthaŵi zamakono?

◻ Kodi nchifukwa ninji katembenuzidwe kamakonoka sikanasokoneze chifuno cha Mulungu chokhudza dzina lake?

◻ Kodi matembenuzidwe ena amabisa motani choonadi cha Baibulo chonena za sou, imfa ndi dziko lapansi?

◻ Kodi kuchirikiza kwathu mokhulupirika Mawu a Mulungu tingakusonyeze m’njira zotani?

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi muyenera kugwiritsira ntchito Baibulo liti?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena