Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 9/1 tsamba 8-13
  • Mosasamala Kanthu za Kupangidwa ndi Fumbi, Pitanibe Patsogolo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mosasamala Kanthu za Kupangidwa ndi Fumbi, Pitanibe Patsogolo!
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusintha kwa Mikhalidwe
  • Nawonso Anapangidwa ndi Fumbi
  • Kodi Kukhala Opangidwa ndi Fumbi Kumatanthauzanji kwa Ife Aliyense Payekha?
  • Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira??
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Anthu Akafa Amapita Kudziko la Mizimu?
    Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Limbikitsanani Pamene Tsiku Likuyandikira
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 9/1 tsamba 8-13

Mosasamala Kanthu za Kupangidwa ndi Fumbi, Pitanibe Patsogolo!

“Adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.”​—SALMO 103:14.

1. Kodi Baibulo nlolondola mwasayansi ponena kuti anthu n’ngopangidwa ndi fumbi? Fotokozani.

M’LINGALIRO lakuthupi, ife ndife fumbi. “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” (Genesis 2:7) Malongosoledwe achilengedwe cha munthu osavuta ameneŵa ali ogwirizana ndi choonadi cha sayansi. Ma element onse amene thupi la munthu lapangidwa nawo amapezeka mu “dothi lapansi.” Panthaŵi ina katswiri wa chemistry ananena kuti thupi la munthu wachikulire nlopangidwa ndi 65 peresenti ya oxygen, 18 peresenti ya carbon, 10 peresenti ya hydrogen, 3 peresenti ya nitrogen, 1.5 peresenti ya calcium, ndi 1 peresenti ya phosphorus, ndipo mbali yotsalayo ikumapangidwa ndi ma element ena. Kaya kuyerekezera kumeneku nkolondola kwambiri kapena ayi zimenezo sizofunika kwambiri. Choonadi nchakuti: “Ife ndife fumbi”!

2. Kodi mumamva motani ponena za njira imene Mulungu analengera nayo anthu, ndipo chifukwa ninji?

2 Kodi ndaninso wina, kusiyapo Yehova, amene akanalenga zolengedwa zocholoŵana zotero ndi fumbi chabe? Ntchito za Mulungu nzangwiro ndi zopanda banga, chotero kusankha kwake kulenga munthu m’njira imeneyi kulidi chochititsa kusaŵiringula. Ndithudi, kukhoza kwa Mlengi Wamkulu kulenga munthu kuchokera m’fumbi la padziko lapansi m’njira yowopsa ndi yodabwitsa kumawonjezera chiyamikiro chathu kaamba ka mphamvu Yake yopanda malire, luso, ndi nzeru yothandiza.​—Deuteronomo 32:4, NW, mawu amtsinde; Salmo 139:14.

Kusintha kwa Mikhalidwe

3, 4. (a) Kodi nchiyani chimene Mulungu sanalinganize polenga munthu kuchokera m’fumbi? (b) Kodi nchiyani chimene Davide anali kusonyeza pa Salmo 103:14, ndipo kodi ndimotani mmene nkhani yakeyo imatithandizira kuzindikira tanthauzo limeneli?

3 Zolengedwa za fumbi zili ndi zinthu zimene sizikhoza kuchita. Komabe, Mulungu sanafune konse kuti zimenezi zikhale zovutitsa kapena zoletsa kwambiri. Sizinalinganizidwire kukhala zolefulitsa kapena zochititsa kupanda chimwemwe. Komabe, monga momwe nkhani ya mawu a Davide pa Salmo 103:14 imasonyezera, zinthu zimene anthu sakhoza kuchita zingalefulitse maganizo ndipo zingathe kuchititsa kupanda chimwemwe. Chifukwa ninji? Pamene Adamu ndi Hava anapandukira Mulungu, anadzetsa mkhalidwe wosintha ku banja lawo lamtsogolo. Pamenepo kukhala opangidwa ndi fumbi kunatenga lingaliro latsopano.a

4 Davide sanali kulankhula, za zinthu zimene mwachibadwa ngakhale anthu angwiro opangidwa ndi fumbi sakanakhoza kuchita, koma zophophonya zochititsidwa chifukwa cha choloŵa cha kupanda ungwiro. Akanatanthauza zimenezo sibwenzi atanena za Yehova kuti: “Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse; amene awombola moyo wako ungawonongeke; [amene] sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.” (Salmo 103:2-4, 10) Mosasamala kanthu za kukhala opangidwa ndi fumbi, anthu angwiro akanapitiriza kukhala okhulupirika, sakanachita cholakwa konse, sakanachimwa, kotero kuti afunikire kukhululukidwa; ndiponso sakanakhalanso ndi nthenda zofuna kuchiritsidwa. Koposa zonsezo, sakanatsikira kudzenje la imfa kumene angawomboledweko kokha mwanjira ya chiukiriro.

5. Kodi nchifukwa ninji kuli kosavuta kwa ife kumvetsetsa mawu a Davide?

5 Pokhala opanda ungwiro, tonsefe takumana ndi zinthu zimene Davide ananena. Nthaŵi zonse timakumbukira za zimene sitikhoza kuchita chifukwa cha kupanda ungwiro. Timachita chisoni pamene nthaŵi zina zimenezi zimaonekera kukhala zikuwononga unansi wathu ndi Yehova kapena ndi abale athu Achikristu. Timamva chisoni kuti kupanda ungwiro kwathu ndi zitsenderezo za dziko la Satana panthaŵi ndi nthaŵi zimatilepheretsa kuchita kanthu. Popeza kuti ulamuliro wa Satana ukuyandikira mapeto ake mofulumira, dziko lake likupereka chitsenderezo chokulira nthaŵi zonse pa anthu onse ndipo makamaka pa Akristu.​—Chivumbulutso 12:12.

6. Kodi nchifukwa ninji Akristu ena angalefulidwe, ndipo kodi ndimotani mmene Satana angagwiritsirire ntchito kumva mwa mtundu umenewu?

6 Kodi mumaona kuti kukhala ndi moyo Wachikristu kukukhala kovuta mowonjezereka? Akristu ena amvedwa akumanena kuti pamene amakhalitsa m’choonadi mpamenenso amaonekera kukhala opanda ungwiro mowonjezereka. Komabe, mwachionekere, kuli chabe kuti iwo afikira kukhala ozindikira mowonjezereka za kupanda ungwiro kwawo ndi kusakhoza kwawo kugwirizana ndi miyezo yangwiro ya Yehova m’njira imene iwo akakonda. Komabe, kwenikweni chimenechi mwachionekere ndicho chotulukapo cha kupitirizabe kukula m’chidziŵitso ndi m’kuzindikira zofunika zolungama za Yehova. Nkofunika kuti tisalole kuzindikira kotero kulikonse kutilefula maganizo kufikira pamlingo wa kuloŵa m’manja mwa Mdyerekezi. Kwa zaka mazana onse apitawo iye mobwerezabwereza wayesa kugwiritsira ntchito kulefula maganizo kotero kuti achititse atumiki a Yehova kuleka kulambira koona. Komabe, chikondi choona pa Mulungu, ndiponso “udani weniweni” pa Mdyerekezi, zatetezera ochuluka a iwo pa kuchita motero.​—Salmo 139:21, 22; Miyambo 27:11.

7. Kodi ndimotani mmene ife nthaŵi zina tingakhalire ngati Yobu?

7 Komabe, atumiki a Yehova kwanthaŵi ndi nthaŵi angaone kukhala olefulidwa. Kusakhutira ndi zipambano za ife eni kungakhalenso chifukwa chake. Matenda kapena maunansi ovuta ndi ziŵalo za banja, mabwenzi, kapena antchito anzathu zingaloŵetsedwemo. Yobu wokhulupirikayo anakhala wolefulidwa maganizo kwambiri kwakuti anachonderera Mulungu kuti: “Ha! mukadandibisa kumanda, mukadandisunga mtseri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthaŵi, ndi kundikumbukira.” Tsopano, ngati mikhalidwe yovuta inatha kutsendereza Yobu, “munthu [wosalakwa, NW] ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa,” kukhala ndi nyengo za kulefulidwa, mposadabwitsa kuti zofananazo zingachitike kwa ife.​—Yobu 1:8, 13-19; 2:7-9, 11-13; 14:13.

8. Kodi nchifukwa ninji kulefulidwa kwa panthaŵi ndi nthaŵi kungakhale chizindikiro chabwino?

8 Nkotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti Yehova amayang’ana m’mitima ndipo samanyalanyaza zolinga zabwino! Sadzataya konse awo amene amayesayesa ndi kuona mtima konse kumkondweretsa. Kwenikweni, kulefulidwa kwa panthaŵi ndi nthaŵi, kungakhale chizindikiro chabwino, chosonyeza kuti sitikupeputsa utumiki wathu kwa Yehova. Polingaliridwa motere, munthu amene samayesa kulimbana ndi kulefulidwa maganizo angakhale wosazindikira mwauzimu za zofooka zake monga momwe ena akuchitira ndi zawo. Kumbukirani: “Iye wakuyesa kuti ali chiriri, ayang’anire kuti angagwe.”​—1 Akorinto 10:12; 1 Samueli 16:7; 1 Mafumu 8:39; 1 Mbiri 28:9.

Nawonso Anapangidwa ndi Fumbi

9, 10. (a) Kodi ndi chikhulupiriro cha yani chimene Akristu angachite bwino kuchitsanzira? (b) Kodi ndimotani mmene Mose anachitira ndi gawo lake?

9 Ahebri chaputala 11 amandandalika mboni za Yehova zambiri zokhalako Chikristu chisanadze zimene zinasonyeza chikhulupiriro champhamvu. Akristu a m’zaka za zana loyamba ndi a m’nthaŵi zamakono achita chimodzimodzi. Maphunziro oti aphunziridwe kwa iwo n’ngamtengo wapatali. (Yerekezerani ndi Ahebri 13:7.) Mwachitsanzo, kodi nchikhulupiriro cha yaninso chimene Akristu angachite bwino kutsanzira kuposa chija cha Mose? Iye anapemphedwa kukalengeza uthenga wachiweruzo kwa wolamulira wamphamvu koposa padziko lonse wa m’nthaŵi yake, Farao wa Igupto. Lerolino, Mboni za Yehova ziyenera kulengeza mauthenga achiweruzo ofananawo pa chipembedzo chonyenga ndi magulu ena amene akutsutsa Ufumu wa Kristu wokhazikitsidwa.​—Chivumbulutso 16:1-15.

10 Kuchita ntchito imeneyi kuli gawo lovuta, monga momwe Mose anasonyezera. “Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israyeli m’Aigupto?” iye anafunsa motero. Tingamvetsetse malingaliro ake a kukhala wosakhoza. Iye anavutikanso mtima ndi mmene Aisrayeli anzake akachitira: “Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mawu anga.” Pamenepo Yehova anamfotokozera mmene akasonyezera kuti analamulidwa ndi iye, koma Mose anali ndi vuto linanso. Iye anati: “Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosoŵa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa mkamwa molemera.”​—Eksodo 3:11; 4:1, 10.

11. Kodi ndimotani mmene ife tingachitire ndi mathayo ateokratiki mofanana ndi Mose, koma mwa kusonyeza chikhulupiriro, kodi tingadalire chiyani?

11 Nthaŵi zina, tingamve monga momwe Mose anachitira. Ngakhale kuti timazindikira mathayo athu ateokratiki, tingakayikire za mmene tingawakwaniritsire. ‘Kodi ndine yani kuti ndifikire anthu, ena a iwo okhala ndi malo apamwamba m’chitaganya, m’zachuma, ndi m’maphunziro, ndi kuyesa kuwaphunzitsa njira za Mulungu? Kodi abale anga auzimu adzachita motani pamene ndipereka ndemanga pamisonkhano Yachikristu kapena pamene ndipereka maulaliki pa pulatifomu m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki? Kodi sadzaona zolephera zanga?’ Komatu kumbukirani, Yehova anali ndi Mose ndipo anamkonzekeretsa kuchita ntchito yake chifukwa chakuti Mose anasonyeza chikhulupiriro. (Eksodo 3:12; 4:2-5, 11, 12) Ngati titsanzira chikhulupiriro cha Mose, Yehova adzakhala nafe ndi kutikonzekeretsa kaamba ka ntchito yathunso.

12. Kodi chikhulupiriro cha Davide chingatilimbikitse motani poyang’anizana ndi kulefulidwa chifukwa cha machimo kapena zophophonya?

12 Aliyense amene amaona kukhala wogwiritsidwa mwala kapena wolefulidwa chifukwa cha machimo kapena zophophonya angakumbukiredi Davide pamene anati: “Ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire.” Pochonderera Yehova, Davide anatinso: “Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.” Komabe, iye sanalole konse kulefulidwa maganizo kumubera chikhumbo chake cha kutumikira Yehova. “Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera.” Davide analidi “fumbi,” koma Yehova sanamsiye, pakuti Davide anasonyeza chikhulupiriro m’lonjezo la Yehova la kusanyalanyaza “mtima wosweka ndi wolapa.”​—Salmo 38:1-9; 51:3, 9, 11, 17.

13, 14. (a) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhala akutsata anthu? (b) Kodi ndimotani mmene zitsanzo za Paulo ndi Petro zimasonyezera kuti ngakhale iwonso anapangidwa ndi fumbi?

13 Komabe, onani kuti ngakhale kuti tiyenera kuona “mtambo waukulu wotere wa mboni” monga chilimbikitso cha ‘kuthamanga mwachipiriro makaniwo adatiikira,’ sitikuuzidwa kukhala otsatira awo. Tikuuzidwa kutsatira mapazi a “woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu,” osati anthu opanda ungwiro​—osati ngakhale atumwi okhulupirika a m’zaka za zana loyamba.​—Ahebri 12:1, 2; 1 Petro 2:21.

14 Mtumwi Paulo ndi Petro, mizati ya mpingo Wachikristu, nthaŵi zina anakhumudwa. “Chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita,” analemba motero Paulo. “Munthu wosauka ine.” (Aroma 7:19, 24) Ndipo Petro pokhala ndi chidaliro chopambanitsa anauza Yesu kuti: “Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthaŵi zonse.” Pamene Yesu anachenjeza Petro kuti akakana Iye katatu, Petro modzikuza anatsutsa Mbuye wake, akumadzitamandira kuti: “Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iyayi.” Komabe iye anakanadi Yesu, cholakwa chimene chinamchititsa kulira mopwetekedwa mtima kwambiri. Inde, Paulo ndi Petro anapangidwa ndi fumbi.​—Mateyu 26:33-35.

15. Mosasamala kanthu kuti ndife opangidwa ndi fumbi, kodi nchisonkhezero chotani chimene tili nacho cha kupitirizabe patsogolo?

15 Komabe, mosasamala kanthu za zophophonya zawo, Mose, Davide, Paulo, Petro, ndi enanso ofanana nawo anapambana. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anasonyeza chikhulupiriro champhamvu mwa Yehova, anamkhulupirira kotheratu, ndi kumamatira kwa iye mosasamala kanthu za zokhumudwitsazo. Anadalira pa iye kuwapatsa “ukulu woposa wamphamvu.” Ndipo iye anatero, osawalola konse kugwa ndi kuwonongekeratu. Ngati tipitirizabe kusonyeza chikhulupiriro, tingakhale otsimikiza kuti pamene chiweruzo chiperekedwa kwa ife, chidzakhala chogwirizana ndi mawu akuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” Zimenezi zimatipatsa chisonkhezero chotani nanga kuti tipitirizebe patsogolo mosasamala kanthu kuti ndife opangidwa ndi fumbi!​—2 Akorinto 4:7; Ahebri 6:10.

Kodi Kukhala Opangidwa ndi Fumbi Kumatanthauzanji kwa Ife Aliyense Payekha?

16, 17. Pamene tifika pankhani ya kuweruza, kodi Yehova amagwiritsira ntchito motani lamulo lofotokozedwa pa Agalatiya 6:4?

16 Zochitika zaphunzitsa makolo ndi aphunzitsi ambiri nzeru ya kuweruza ana kapena ophunzira molingana ndi kukhoza kwa munthu mwini, osati pamaziko a kuyerekezera ndi abale ake kapena a m’kalasi anzake. Zimenezi nzogwirizana ndi lamulo la mkhalidwe la Baibulo limene Akristu auzidwa kutsatira: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.”​—Agalatiya 6:4.

17 Mogwirizana ndi lamulo limeneli, ngakhale kuti Yehova amachita ndi anthu ake monga gulu lolinganizidwa, iye amawaweruza aliyense payekha. Aroma 14:12 amati: “Munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.” Yehova amadziŵa bwino mpangidwe wa majini wa aliyense wa atumiki ake. Amadziŵa mpangidwe wawo wakuthupi ndi wamaganizo, zokhoza zawo, nyonga zawo ndi zofooka zawo zachibadwa, zothekera zimene ali nazo, ndiponso mlingo umene amagwiritsira ntchito zothekera zimenezi kuti abale zipatso Zachikristu. Mawu a Yesu onena za mkazi wamasiye amene anaponya tindalama tiŵiri mosungiramo zopereka za m’kachisi ndi fanizo lake la mbewu zobzalidwa panthaka yabwino zili zitsanzo zabwino kwa Akristu amene angadzione kukhala opsinjika maganizo chifukwa cha kudziyerekezera iwo eni ndi ena kosayenera.​—Marko 4:20; 12:42-44.

18. (a) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kudziŵa chimene kukhala fumbi kwa ife eni kumatanthauza? (b) Kodi nchifukwa ninji kudzipenda koona mtima sikuyenera kutichititsa kutaya mtima?

18 Nkofunika kuti tidziŵe chimene kukhala fumbi kuli kwa ife enife kotero kuti titumikire monga momwe tingathere. (Miyambo 10:4; 12:24; 18:9; Aroma 12:1) Kuli kokha mwa kukhala ozindikira kwambiri zophophonya zathu ndi zifooko kuti tingathe kukhala ogalamuka pa kufunikira ndi kuthekera kwa kuwongolera. Podzipenda, tiyeni tisanyalanyaze nyonga ya mzimu woyera m’kutithandiza kuwongolera. Mwa uwo, chilengedwe chinalengedwa, Baibulo linalembedwa, ndipo, pakati pa dziko lomafali, chitaganya cha dziko latsopano chamtendere chabadwa. Chotero mzimu woyera wa Mulungu ulidi wamphamvu mokwanira kupatsa awo amene amaupempha nzeru ndi nyonga zofunikira m’kusunga umphumphu.​—Mika 3:8; Aroma 15:13; Aefeso 3:16.

19. Kodi kukhala kwathu opangidwa ndi fumbi sikuli chodzikhululukira cha chiyani?

19 Nkotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti Yehova amakumbukira kuti ife ndife fumbi! Komabe, sitiyenera kulingalira konse kuti chimenecho chili chodzikhululukira chololedwa chochitira ulesi kapena ngakhale chochitira cholakwa. Kutalitali! Kukumbukira kwa Yehova kuti ife ndife fumbi ndiko chisonyezero cha kukoma mtima kwake kwapadera. Koma ife sitikufuna kukhala “anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, [ndi kukaniza] Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Kristu.” (Yuda 4) Kukhala opangidwa ndi fumbi sikuli chodzikhululukira chokhalira osapembedza. Mkristu amayesayesa kulimbana ndi zikhoterero zolakwa, kupumphuntha thupi lake ndi kuliyesa kapolo, kotero kuti apeŵe ‘kumvetsa chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu.’​—Aefeso 4:30; 1 Akorinto 9:27.

20. (a) Kodi ndi m’mbali ziŵiri ziti zimene tili ndi “zambiri zochita m’ntchito ya Ambuye”? (b) Kodi nchifukwa ninji tili ndi chifukwa chokhalira ndi chitsimikizo?

20 Tsopano, mkati mwa zaka zomaliza za dongosolo la dziko la Satana, sili nthaŵi ya kuyamba kuleka​—ngati tikunena za kulalikira Ufumu ndiponso ngati tikunena za kukulitsa mokwanira zipatso za mzimu wa Mulungu. Kumbali zonsezo tili ndi “zambiri zochita.” (NW) Tsopano ndiyo nthaŵi ya kupitabe patsogolo chifukwa chakuti tikudziŵa kuti ‘kuchititsa kwathu sikuli chabe.’ (1 Akorinto 15:58) Yehova adzatilimbitsa, popeza kuti ponena za iye Davide anati: “Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Nchisangalalo chotani nanga kudziŵa kuti Yehova akulola ife mwachindunji kukhala ndi phande m’ntchito yaikulu koposa iliyonse imene inapatsidwa ku zolengedwa zaumunthu zopanda ungwiro kuti ziichite​—ndipo wachita zimenezi mosasamala kanthu za kukhala kwathu opangidwa ndi fumbi!

[Mawu a M’munsi]

a Buku lothirira ndemanga pa Baibulo lakuti Herders Bibelkommentar, ponena za Salmo 103:14, limati: “Adziŵa bwino kuti analenga anthu ndi fumbi la pansi, ndipo adziŵa zofooka ndi mkhalidwe wa kusakhalitsa kwa moyo wawo, kumene kumawatsendereza kwambiri chiyambire pa uchimo woyambirira.”​—Kanyenye ngwathu.

Kodi Mungafokoze?

◻ Kodi ndimotani mmene Genesis 2:7 ndi Salmo 103:14 amasiyanirana ponena za anthu kukhala opangidwa ndi fumbi?

◻ Kodi nchifukwa ninji Ahebri chaputala 11 ali magwero achilimbikitso kwa Akristu lerolino?

◻ Kodi nchifukwa ninji timakhala anzeru pogwiritsira ntchito lamulo la mkhalidwe loperekedwa pa Agalatiya 6:4?

◻ Kodi ndimotani mmene Ahebri 6:10 ndi 1 Akorinto 15:58 angathandizire kuletsa kulefulidwa?

[Zithunzi patsamba 10]

Akristu amatsanzira chikhulupiriro cha olambira anzawo, koma amatsatira Womaliza wa chikhulupiriro chawo, Yesu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena