Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 7 tsamba 69-75
  • Chifukwa Chake Tiri Pano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Tiri Pano
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHITSINTHIKO KAPENA CHILENGEDWE?
  • MMENE MULUNGU ANALENGERA MUNTHU
  • CHIFUKWA CHAKE MULUNGU ANAIKA MUNTHU PANO
  • CHIFUKWA CHAKE TIMAKALAMBA NDI KUFA
  • Yesu Anafa Ndi Kuukitsidwa—Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • M’pomveka Kukhulupirira Kuti Dzikoli Lidzakhala Paradaiso
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Cifukwa Cace Timakalamba ndi Kufa
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Mulungu Analenga Anthu Awiri Oyamba
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 7 tsamba 69-75

Mutu 7

Chifukwa Chake Tiri Pano

1.Kodi ndilingaliro lotani limene anthu oganiza alifikira?

ANTHU kwa nthawi yaitali adabwa ponena za tanthauzo la moyo padziko lapansi. Iwo ayang’ana kuthambo lalikulu lodzaza nyenyezi. Iwo achita kaso ndi kulowa kwadzuwa kokongola ndi kukongola kwa dziko. Anthu oganiza alingalira kuti payenera kukhala chifuno china chabwino kwambiri ku zinthu zonsezi. Koma kawirikawiri iwo adabwa pamene iwo akuloweramo.—Salmo 8:3, 4.

2. Kodi ndimafunso otani amene anthu afunsa?

2 Pa nthawi ina m’moyo anthu ochuluka amafunsa kuti: Kodi ife tiyenera kukhala ndi moyo nthawi yaifupi chabe, kupeza zimene tingathe m’moyo, ndi kenako kumwalira? Kodi nkuti kwenikweni kumene ife tikupita? Kodi pali zina zimene tingayembekezere koposa nyengo yaifupi ya kubadwa, moyo ndi imfa? (Yobu 14:1, 2) Chimene chidzatithandiza kumvetsetsa nkhani imeneyi ndicho yankho la funsolo: Kodi tinafika pano motani?

CHITSINTHIKO KAPENA CHILENGEDWE?

3. Kodi chiphunzitso cha chisinthiko nchotani?

3 M’mbali zina kumaphunzitsidwa mofala kuti chinthu chirichonse chimene tikuwona chinangokhalako chokha, kuti chinachitika mwamwayi kapena ngozi. Koposa mamiliyoni ambiri a zaka, amatero, moyo unasinthika, kapena unabuka, kuchokera ku mipangidwe yotsikirapo kufikira potsirizira pake anthu anakhalako. M’mbali zambiri za dziko lapansi chiphunzitso cha chisinthiko chimenechi chimaphunzitsidwa monga chowona. Koma kodi nzowona kuti ife tinachokera ku chinyama chonga dzimwe chimene chinakhalako zaka mamiliyoni ambiri zapitazo? Kodi chilengedwe chachikulu chimenechi chinangokhalako mwangozi?

4. Kodi nchifukwa ninji tingakhulupirire kuti “Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi”?

4 Baibulo limati: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Ndipo maumboni a sayansi amavomereza kuti kumwamba, limodzi ndi mabiliyoni ake a nyenyezi, ndi dziko lathu lapansi zinali ndi chiyambi. Zinalengedwa. Kuyenda kwa nyenyezi ndi mapulaneti kuli kokhazikika kwambiri chakuti ngakhale zaka zambiri pasadakhale malo awo angadziwidwe molondola kwambiri. Nyenyezi ndi mapulaneti zimayenda m’mlengalenga mogwirizana ndi malamulo ndi njira zamasamu. Polofesala wina wa masamu wa ku University of Cambridge, P. Dirac, anati, m’magaziniwo Scientific American: “Munthu mwina mwake angafotokoze mkhalidwewo mwa kunena kuti Mulungu ndiye mwini masamu a mtundu wapamwamba kwambiri, ndipo Iye anagwiritsira ntchito masamu apamwamba kwambiri m’kupanga chilengedwe.”

5. Kodi ndimotani thupi lathu limasonyezera kuti tinalengedwa koposa ndi kukhala chotulukapo cha chisinthiko?

5 Baibulo limafotokoza kuti: “Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu. Ndiye amene anatilenga, ndipo osati ife eni.” (Salmo 100:3, NW) Thupi lathu laumunthu limasonyeza kupangidwa kodabwitsa koteroko chakuti wolemba Baibulo wina anasonkhezereka kunena kwa Mulungu kuti: “Ndidzakuyamikani chifukwa chakuti ndapangidwa modabwitsa m’njira yochititsa mantha. . . . Mafupa anga sanabisike kwa inu pamene ndinapangidwa mobisika . . . Maso anu anawona ngakhale mluza wanga, ndipo m’bukhu mwanu mbali zake zonse zinalembedwa.” (Sakmo 139:14-16, NW) Khanda limakula m’mimba mwa mayi wake m’njira yodabwitsa. Ponena za zimenezi magazini a Newsweek anati: “Ndiko, kwenikwenidi, chozizwitsa.” Ndiyeno anatinso: “Palibe njira imene ingasonye molunjika nthawi yeniyeni ya kukhala ndi pakati. Palibe wasayansi amene angathe kutchula mphamvu zodabwitsa zimene pa nthawi imeneyo zimapitiriza kukulitsa ziwalo ndi cholowanecholowane wa minyewa yochuluka ya mluza wamunthu.”

6. Kodi nchifukwa ninji kumamvekera kwa ife kukhulupirira kulengedwa koposa ndi chisinthiko?

6 Taganizirani chilengedwe chathu chachikulu, kuphatikizapo thupi lathu la ife eni limodzi ndi kumangidwa ndi kulinganizidwa kwake kodabwitsa. Kulingalira bwino kuyenera kutiuza kuti zinthu zimenezi sizinangosandulika kapena kudza zokha. Izo zinafunikira kukhala ndi Wolinganiza, Mlengi. Lingalirani zinthu zina zimene timaziwona motizinga. Pamene muli m’nyumba mwanu, dzifunseni kuti: Kodi desiki langa, nyali, bedi, mpando, thebulo, makoma, kapena ngakhale nyumba yeniyeniyo, zinasinthika? Kapena kodi izo zinafunikira wopanga? Ndithudi anthu anzeru adazipanga! Pamenepa, kodi ndi m’njira yotani, kunganenedwe kuti chilengedwe chathu chocholowanacholowana kwambirimbiri ndi ife eni sitinafunikire wopanga? Ndipo ngati Mulungu anatiika pano, ndithudi iye anali ndi chifukwa chochitira motero.

7. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti anakhulupirira kulengedwa? (b) Kodi pali umboni wowonjezereka wotani wakuti Adamu anali munthu weniweni?

7 Yesu Kristu mwiniyo ponena za mwamuna ndi mkazi woyambayo anati: “Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.” (Mateyu 19:4, 5) Panopa Yesu anagwira mawu m’Genesis 1:27 ndi 2:24 ponena za kulengedwa kwa Adamu ndi Hava. Iye motero anali kusonyeza cholembedwa cha Baibulo chimenechi kukhala chowona. (Yohane 17:17) Ndiponso, Baibulo limatcha Enoke “wachisanu ndi chiwiri kuyambira kwa Adamu.” (Yuda 14) Ngati Adamu sadaali munthu weniweni, Baibulo silikanamdziwikitsa m’njira yotsimikizirika imeneyi.—Luke 3:37, 38.

8. Kodi ndilingaliro lotani la chiyambi cha munthu limene Baibulo silimaphunzitsa?

8 Anthu ena amanena kuti Mulungu anagwiritsira ntchito njira ya chisinthiko kulenga munthu. Iwo amanena kuti Mulungu analola munthu kusinthika, ndipo pamene iye anafika pakutipakuti Iye anaika moyo mwa iye. Koma palibe kulikonse m’Baibulo kumene lingaliro limeneli limapezeka. M’malo mwake, Baibulo limanena kuti zomera ndi zinyama zinalengedwa “monga mwa mitundu yawo.” (Genesis 1:11, 21, 24) Ndipo maumboni amasonyeza kuti mtundu umodzi wa chomera kapena chinyama, m’kupita kwanthawi, sumasanduka kukhala mtundu wina. Chidziwitso chowonjezereka chotsimikizira kuti sindife chotulukapo cha chisinthiko chingapezedwe m’bukhu Lachingelezilo Life—How Did It Ger Here? By Evolution or by Creation?

MMENE MULUNGU ANALENGERA MUNTHU

9. (a) Kodi ndimotani mmene Baibulo limafotokozerera kulengedwa kwa munthu? (b) Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Mulungu anauzira m’mphuno mwa munthu “mphweya wa moyo”?

9 Mulungu analenga munthu kuchokera m’nthaka kuti akhale padziko lapansi, monga momwe Baibulo limanenera: “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mphweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” (Genesis 2:7) Mwa zimenezi tingathe kuwona kuti munthu anali cholengedwa chachindunji cha Mulungu. M’kachitidwe kapadera ka kulenga, Mulungu anapanga mwamunayo kukhala munthu wokwanira ndi wamphumphu. Pamene Mulungu anauzira “mpweya wa moyo” m’mphuno wa munthuyo, mapapu a munthuyo anadzaza mpweya. Koma choposa chimenecho chinachitidwa. Mulungu mwa zimenezo anapereka umoyo kuthupi la munthuyo. Mphamvu ya moyo imeneyi imachirikizidwa, kapena kuchititsidwa kupitiriza, mwa kupuma.

10. Kodi moyo wa munthu nchiyani, ndipo kodi unalengedwa motani?

10 Komabe, wonani kuti Baibulo silikunena kuti Mulungu anapatsa munthu moyo. M’malo mwake, limanena kuti Mulungu atayambitsa munthu kupuma “munthuyo nakhala wamoyo.” Motero munthu anali moyo, monga momwedi munthu amene amakhala dokotala aliri dokotala. (1 Akorinto 15:45) “Dothi lapansi,” m’mene thupi likuumbidwa sindilo moyo. Ndiponso Baibulo silimanena kuti “mpweya wa moyo” ndiwo moyo. M’malo mwake, Baibulo limasonyeza kuti kuphatikizidwa kwa zinthu ziwiri zimenezi ndiko kumene kunachititsa ‘kukhala kwa munthu wamoyo.’

11. Kodi ndimaumboni Abaibulo otani onena za moyo wamunthu amene amasonyeza kuti sungakhale chinthu chosawoneka bwino chimene chingapitirize kukhalapo popanda munthu?

11 Popeza kuti moyo wamunthu ndiwo munthu mwiniyo, pamenepo sungakhale chinthu china chosawonekera bwino chimene chimakhala mkati mwa thupi kapena chimene chingasiye thupi. Kunena mosavutika, Baibulo limaphunzitsa kuti moyo wanu ndiwo inu. Mwa chitsanzo, Baibulo limatchula kufuna kwa moyo kudya chakudya chenicheni, kuti: “Moyo wanu ukhumba kudya nyama.” (Deuteronomo 12:20, NW) Limanenanso kuti miyoyo iri ndi mwazi woyenda m’mitsempha mwawo, pakuti limatchula “mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa.”—Yeremiya 2:34.

CHIFUKWA CHAKE MULUNGU ANAIKA MUNTHU PANO

12. Kodi chifuno cha Mulungu chinali chotani kaamba ka anthu padziko lapansi?

12 Sichinali chifuno cha Mulungu kuti Adamu ndi Hava afe pambuyo pa kanthawi ndi kukhala ndi moyo kwina kwakenso. Iwo anayenera kukhala pano kuti asamalire dziko lapansi ndi zamoyo zake zonse. Monga momwe Baibulo likunenera: “Mulungu . . . anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa padziko lapansi.” (Genesis 1:28; 2:15) Adamu ndi Hava, kuphatikizapo ana onse amene iwo akabala, akanakhala okondwa padziko lapansi kosatha, akumachita zinthu zimene Mulungu anafuna kuti iwo achite.

13. (a) Kodi tingakhale okondwa motani? (b) Kodi nchiyani chimene chidzapereka tanthauzo lenileni ku miyoyo yathu?

13 Wonani kuti “Mulungu . . . anadalitsa iwo.” Iye anasamaliradi ana ake apadziko lapansi. Motero monga Atate wachikondi anawapatsa malangizo amene anali kaamba ka ubwino wawo. Iwo akanapeza chimwemwe m’kuwamvera. Yesu anadziwa zimenezi ndipo motero anati pambuyo pake: “Odala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga!” (Luka 11:28) Yesu anasunga mawu a Mulungu. “Ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse,” iye anatero. (Yohane 8:29) Kumeneku ndiko mfungulo ya chifukwa chenichenicho ife tiri pano. Ndicho chakuti tikhale ndi miyoyo yokwanira ndi yachimwemwe mwa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Kudzapereka tanthauzo lenileni ku miyoyo yathu tsopano kutumikira Yehova. Ndipo mwa kutero tidzakhala tikudziyeneretsa kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi.—Salmo 37:11, 29.

CHIFUKWA CHAKE TIMAKALAMBA NDI KUFA

14. Mwa kusamvera lamulo la Mulungu, kodi nchiyani chimene Adamu ndi Hava anachita?

14 Koma tsopano ife tonse timakalamba ndi kufa. Kodi nchifukwa ninji? Monga momwe kwawonedwera m’mutu wapitawo, nchifukwa cha kupanduka kwa Adamu ndi Hava. Yehova adaika pa iwo chiyeso chimene chinasonyeza kufunika kwa kukhala kwawo omvera Mulungu. Iye anati kwa Adamu: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Mwa kudya mtengo umenewu, Adamu ndi Hava anafulatira Atate wawo wakumwamba nakana chitsogozo chake. Iwo sanamvere ndipo anatenga chimene sichinali chawo. Iwo akanatha kukhala ndi moyo mokondwa m’paradaiso kosatha popanda umphawi kapena mavuto, koma tsopano iwo anadzidzetsera chilango cha uchimo. Chilango chimenechi ndicho kupanda ungwiro ndi imfa.—Aroma 6:23.

15. Kodi tinalandira motani uchimo wathu kuchokera kwa Adamu?

15 Kodi mukudziwa mmene tinapezera tchimo lathu kuchokera kwa Adamu? Adamu atakhala wopanda ungwiro, iye anapatsira ana ake onse kupanda ungwiro kumeneko ndi imfa. (Yobu 14:4; Aroma 5:12) Monga chithandizo m’kumvetsetsa kwanu mkhalidwewo, ganizirani chimene chimachitika pamene wophika buledi amaphikira buledi m’chiwaya chimene chiri ndi kutiwanizika. Chizindikiro chidzawoneka pabuledi yense amene aphikidwa m’chiwaya chimenecho. Adamu anakhala ngati chiwaya chimenecho, ndipo ife tiri ngati buledi. Iye anakhala wopanda ungwiro pamene anaswa lamulo la Mulungu. Kunali monga ngati kuti analandira kutiwanizika kapena chizindikiro choipa. Motero pamene anabala ana iwo onse analandira chizindikiro cha uchimo kapena kupanda ungwiro chimodzimodzicho.

16, 17. Kodi ndimotani mmene chimodzi cha zozizwitsa za Yesu chimasonyezera kuti kudwala kwafika pa banja la anthu chifukwa cha uchimo?

16 Timadwala ndi kukalamba tsopano chifukwa cha uchimo umene tonsefe talandira kuchokera kwa Adamu. Chimodzi cha zozizwitsa zimene Yesu anachita chimasonyeza zimenezi. Pamene Yesu anali kuphunzitsa m’nyumba imene anali kukhala, khamu lalikulu linasonkhana kotero kuti panalibenso anatha kulowa m’chipindacho. Pamene amuna anai anadza ndi munthu wamanjenje wogona pamachira, iwo anawona kuti sakanatha kulowa. Motero iwo anakwera padenga, nalisasula, natsitsa machira limodzi ndi munthu wamanjenje pa iwo kufikira pansi pafupi ndi Yesu.

17 Pamene Yesu anawona chikhulupiriro chimene iwo anali nacho, iye anati kwa munthu wamanjenjeyo: “Machimo ako akhululukidwa.” Koma ena a anthu okhalapowo sanaganize kuti Yesu akanatha kukhulukira machimo. Motero Yesu anati: “Kuti anthuni mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu ya kukhululukira machimo padziko lapansi,’—iye anati kwa wamanjenjeyo: ‘Ndinena ndi iwe, Dzuka, tenga machira ako, nupite kwanu.’ Atatero iye anadzuka, ndipo nthawi yomweyo anatenga machira ake natuluka pamaso pa iwo onse.”—Marko 2:1-12, NW.

18. Kodi atumiki a Mulungu angayembekezere mtsogolo mwa mtundu wotani?

18 Tangoganizirani chimene mphamvu ya Yesu imeneyi ingatanthauze kwa ife! Mu ulamuliro wa ufumu wa Mulungu, Kristu adzakhala wokhoza kukhululukira machimo a anthu onse amene amakonda ndi kutumikira Mulungu. Zimenezi zikutanthauza kuti zowawa zonse ndi zopweteka ndi matenda zidzachotsedwa. Palibe adzafunikira kukalamba ndi kufa! Ha, ndichiyembekezo chabwino kwambiri chotani nanga mmene chimenechi chiliri kaamba ka mtsogolo! Inde, palidi zina zambiri zimene tingayembekezere koposa ndi kubadwa, kukhala ndi moyo nthawi yaifupi ndi kenako kufa. Mwa kupitiriza kuphunzira ponena za Mulungu ndi mwa kumtumikira, tingakhaledi ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi.

[Chithunzi patsamba 69]

Ambiri amadabwa ponena za tanthauzo la moyo

[Chithunzi patsamba 70]

Kodi zinthu zimenezi zinasinthika, kapena kodi zinapangidwa?

[Chithunzi patsamba 75]

Cholembedwa Chabaibulo cha kuchiritsa kwa Yesu wamanjenje chimasonyeza kuti anthu amadwala chifukwa cha uchimo wa Adamu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena