Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 74-tsamba 78
  • Chilengedwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilengedwe
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Tingadziŵire Kuti Mulungu Aliko
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Kulenga
    Galamukani!—2014
  • Mzimu Woyera Unagwira Ntchito Polenga Zinthu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 74-tsamba 78

Chilengedwe

Tanthauzo: Chilengedwe, monga momwe chalongosoledwera m’Baibulo chimatanthauza kuti Mulungu Wamphamvuyonse analinganiza ndi kuchititsa chilengedwe kukhalako, kuphatikizapo anthu ena auzimu ndi mitundu yonse yaikulu ya zamoyo padziko lapansi.

M’dziko lamakono, lasayansi limeneli, kodi nkwanzeru kukhulupirira chilengedwe?

“Malamulo a chilengedwe chonse ngotsimikizirika kwambiri kotero kuti sitimakhala ndi vuto kumanga chombo cha m’mlengalenga kuulukira pamwezi ndipo tingalinganize nthaŵi ya kuulukayo motsimikizirika kwambirimbiri kufikira kukamphindi. Malamulo amenewa ayenera kukhala atakhazikitsidwa ndi munthu wina.”—Mawu ogwidwa kwa Wernher von Braun, amene anali ndi mbali yaikulu m’kutumiza opita kutali m’mlengalenga kumwezi a ku Amereka.

Chilengedwe chakuthupi: Ngati munapeza koloko yosunga nthaŵi bwino koposa, kodi mukananena kuti inakhalapo yokha mwa kuuluka ndi kugwirizana kwa fumbi? Mwachiwonekere, munthu waluntha anaipanga. Pali “koloko” yodabwitsadi kwambiri. Maplaneti ozungulira dzuŵa lathu, ndiponso nyenyezi m’chilengedwe chonse, zimayenda paliŵiro limene liri lolunjika kwambiri kuposa makoloko ambiri olinganizidwa ndi kupangidwa ndi anthu. Khamu lanyenyezi mu limene maplaneti ozungulira dzuŵa lathu ali limaphatikizapo nyenyezi zoposa mabiliyoni 100, ndipo akatswiri odziŵa za m’mlengalenga amayerekezera kuti pali makamu a nyenyezi otero mabiliyoni 100 m’chilengedwe chonse. Ngati koloko iri umboni wa kulinganiza kwaluntha, koposa kotani nanga chilengedwe chachikulu kwambirimbiri ndi chocholoŵana! Baibulo limalongosola Mlinganizi wake monga “Mulungu wowona, Yehova, . . . Mlengi wakumwamba ndi Wamkulukulu wozifunyulula.”—Yes. 42:5, NW; 40:26; Sal. 19:1.

Planeti Dziko Lapansi: Podutsa chipululu chamchenga chouma, ngati munafika panyumba yokongola, yokonzedwa bwino mwanjira iriyonse ndi yodzala ndi zakudya, kodi mukanakhulupirira kuti inafikapo yokha mwa kuphulika? Ayi; mukanazindikira kuti munthu wina wokhala ndi luntha lalikulu anaimanga. Eya, asayansi sanapezebe moyo pamaplaneti ena alionse ozungulira dzuŵa lathu kusiyapo padziko lapansi; umboni wopezeka ukusonyeza kuti enawo ngopanda moyo. Planeti limeneli, monga momwe bukhu lotchedwa The Earth limanenera, ndiro “chozizwitsa cha chilengedwe, malo apadera.” (New York, 1963, Arthur Beiser, p. 10) Iro liri pamtunda woyenereradi kuchokera kudzuŵa kaamba ka moyo wa anthu, ndipo limayenda paliŵiro loyenereradi kuti ligwidwe pozungulira. Mpweya, umene umapezeka kokha kuzungulira dziko lapansi wopangidwa ndi nsanganizo yoyenerera ya mpweya wochirikiza moyo. Modabwitsa, kuunika kuchokera kudzuŵa, kalaboni dayokosayidi wochokera mu mpweya, ndi madzi ndi zokumbidwa m’nthaka yachonde zimagwirizana kutulutsa chakudya cha zamoyo za padziko lapansi. Kodi zonsezi zinangochitika mwa kuphulika kwina kosalamulirika m’mlengalenga? Science News imavomereza kuti: “Kukuwonekera ngati kuti mikhalidwe yeniyeni imeneyi ndi kulondola sizikanachitika konse mwa malunji.” (August 24 ndi 31, 1974, p. 124) Kunena kwa Baibulo nkwanzeru pamene limafotokoza kuti: “Pakuti nyumba iriyonse iri naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.”—Aheb. 3:4.

Ubongo wamunthu: Makompyutala amakono apangidwa pambuyo pa mafufuzidwe aakulu ndi uinjiniya wosamalitsa. Iwo “sanangokhalako mwa iwo okha.” Bwanji ponena za ubongo wamunthu? Mosafanana ndi ubongo wanyama iriyonse, ubongo wakhanda laumunthu umaŵirikiza nthaŵi zitatu mu ukulu mkati mwa chaka chake choyamba. Kuti umagwira ntchito motani kukali chikhalirebe chinsinsi chachikulu kwa asayansi. Mwa anthu, muli mlingo waukulu wobadwa nawo wa kuphunzira zilankhulidwe zocholoŵana, kuyamikira kukongola, kupanga nyimbo, kusinkhasinkha chiyambi cha moyo ndi tanthauzo lake. Dokotala wa opareshoni ya ubongo Robert White anati: “Ndimasiyidwa ndiri wopanda chosankha kusiyapo kuvomereza kukhalako kwa Waluntha Wamkulu, amene analinganiza ndi kupanga unansi wodabwitsa umene uli pakati pa maganizo ndi ubongo—chinthu chimene chiri chosayerekezeka kwambiri kunzeru za munthu.” (The Reader’s Digest, September 1978, p. 99) Kukula kwa chozizwitsa chimenechi kumayambira paselo laling’onong’ono logwirizanitsidwa ndi ubwamuna m’mimba. Mwachidziŵitso chapadera, wolemba Baibulo Davide anati kwa Yehova: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwiza; ntchito zanu nzodabwiza; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.”—Sal. 139:14.

Selo lamoyo: Selo limodzi lamoyo nthaŵi zina limatchedwa mpangidwe “wosacholoŵana” wa moyo. Koma cholengedwa chaselo limodzi chingagwire chakudya, kuchipukusa, kuchotsa zinyansi, kudzimangira nyumba ndi kuphatikizidwa m’machitachita a kukwerana. Selo lirilonse la thupi lamunthu layerekezeredwa ndi mzinda walinga, wokhala ndi boma lalikulu losungitsa bata, makina amagetsi opangira magetsi, mafakitale opanga maprotini, dongosolo locholoŵana lazamtengatenga, ndi alonda olamulira zololedwa kuloŵa. Ndipo thupi limodzi lamunthu lapangidwa ndi maselo ochuluka kufikira matriliyoni 100. Ha ngoyenerera chotani nanga mawu a Salmo 104:24 akuti: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonsezi mwanzeru”!

Kodi Baibulo limapereka mpata wa lingaliro lakuti Mulungu anagwiritsira ntchito chisinthiko kutulutsa mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zamoyo?

Genesis 1:11, 12 imanena kuti maudzu ndi mitengo zinapangidwa kuti chirichonse chitulutse “monga mwa mtundu yake.” Mavesi 21, 24, 25 amawonjezera kuti Mulungu analenga zolengedwa za m’nyanja, zolengedwa zouluka ndi zinyama za pamtunda, iriyonse “monga mwa mtundu wake.” Panopa sipakupereka mpata wakuti mtundu waukulu umodzi usinthike kapena kusinthira kumtundu wina.

Ponena za munthu, Genesis 1:26 ikusimba kuti Mulungu anati: “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwachikhalidwe chathu.” Chotero anali kudzakhala ndi mikhalidwe yofanana ndi ya Mulungu, osati mikhalidwe imene inali kokha kuwongoleredwa kwa yochokera m’zanyama. Genesis 2:7 amawonjezera kuti: “Yehova Mulungu anaumba munthu [osati kuchokera m’moyo umene unaliko kale koma] ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake.” Panopa palibe lingaliro la chisinthiko, koma, mmalo mwake, malongosoledwe a cholengedwa chatsopano.

Kodi Mulungu analenga mamiliyoni ambiri azamoyo zosiyanasiyana zonsezo zimene ziri padziko lapansi lerolino?

Genesis chaputala 1 amangonena kuti Mulungu analenga chirichonse “monga mwamtumdu wake.” (Gen. 1:12, 21, 24, 25) Pokonzekera Chigumula chadziko lonse m’tsiku la Nowa, Mulungu analamula kuti ziŵalo zoimira chirichonse cha “mtundu” wa cholengedwa cha nyama zapamtunda ndi zouluka chiloŵetsedwe m’chingalaŵa. (Gen. 7:2, 3, 14) “Mtundu” uliwonse uli ndi kuthekera kwa kutulutsa majini osiyanasiyana kwambiri. Chotero kwasimbidwa kuti pali mitundu yosiyanasiyana ya agalu yoposa 400 ndi mitundu yoposa 250 ya akavalo. Mitundu yokhoza kubalitsana yonseyo ya nyama iriyonse iri “mtundu” umodzi wokha wa Genesis. Mofananamo, mitundu yonse ya anthu—Achikasu akummaŵa, Achiafirika, ndi Achicaucasia, kuphatikizapo Adinka otalika mapazi asanu ndi aŵiri a ku Sudan ndi Apigime aafupi kufikira mapazi anayi ndi mainchi anayi—amachokera kwa aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava.—Gen. 1:27, 28; 3:20.

Kodi nchiyani chimene chimachititsa kufanana kwakukulu mu mpangidwe wa zinthu zamoyo?

“Mulungu wolenga zonse.” (Aef. 3:9) Chotero zonse ziri ndi Wolinganiza Wamkulu mmodzi.

“Zonse zinalengedwa ndi iye [Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, amene anadzakhala Yesu Kristu pamene anali padziko lapansi], ndipo kopanda iye sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa.” (Yoh. 1:3) Chotero panali Mmisiri mmodzi mwa amene Yehova anachita ntchito zake zachilengedwe.—Miy. 8:22, 30, 31.

Kodi nchiyani chimene chiri magwero a zipangizo zimene chilengedwe chapangidwa nazo?

Asayansi aphunzira kuti chinthu ndicho mpangidwe wa nsanganizo za nyonga. Zimenezi zachitiridwa chitsanzo ndi kuphulika kwa zida zanyukliya. Katswiri wa zinthu zowoneka za m’mwamba Josip Kleczek akufotokoza kuti: “Nsanganizo zambiri ndipo mwinamwake zoyambirira zonse zingakhale zitalengedwa mwa kuumbika kwa nyonga.”—The Universe (Boston, 1976), Vol. 11, p. 17.

Kodi nkuti kumene nyonga yotero ingachokere? Pambuyo pa kufunsa kuti, ‘Ndani amene analenga zinthu izi [nyenyezi ndi maplaneti]?’ Baibulo limafotokoza za Yehova Mulungu, kuti “popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.” (Yes. 40:26) Chotero Mulungu mwiniyo ndiye Magwero a ‘nyonga yonse yamphamvuyo’ imene inali yofunika kupangira chilengedwe.

Kodi chilengedwe chonse chosawoneka chinamalizidwa m’masiku asanu ndi aŵiri okha nthaŵi ina mkati mwa zaka 6 000 mpaka 10 000 zapitazo?

Maumboni akutsutsa malankhulidwe otero: (1) Kuunika kochokera ku mlalang’amba wotchedwa Andromeda kungawonedwe pausiku wopanda mitambo kuchigawo cha kumpoto kwa dziko lapansi. Kumatengera pafupifupi zaka 2 000 000 kuti kuunikako kufike padziko lapansi, kusonyeza kuti chilengedwe chiyenera kukhala ndi usinkhu wa zaka zokwanira mamiliyoni ambiri. (2) Zotulukapo za kuvunda kwa mathanthwe kochititsidwa ndi mpweya wovunditsa kumachitira umboni kuti kupangidwa kwa mathanthwe ena m’nthaka kwakhala kosadodometsedwa kwa zaka mabiliyoni angapo.

Genesis 1:3-31 sakulongosola za chiyambi cha chilengedwe cha zinthu kapena makamu akumwamba. Akufotokoza kukonzekeretsedwa kwa dziko lapansi limene linaliko kale monga malo okhala anthu. Zimenezi zinaphatikizapo kulengedwa kwa mitundu yaikulu ya zomera, zamoyo za m’madzi, zolengdwa zouluka, nyama za pamtunda, ndi anthu aŵiri oyambirira. Zonsezi zikunenedwa kukhala zitachitidwa mkati mwa nyengo ya “masiku” asanu ndi limodzi. Komabe, liwu Lachihebri lotembenuzidwa “tsiku” liri ndi matanthauzo osiyanasiyana, kuphatikizapo ‘nthaŵi yaitali; nthaŵi yoloŵetsamo nyengo yaikulu mwapadera.’ (Old Testament Word Studies, Grand Rapids, Mich.; 1978, W. Wilson, p. 109) Liwu logwiritsiridwa ntchito limasiya mpata wa lingaliro lakuti “tsiku” lirilonse lingakhale linali lotalika zaka zingapo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena