Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 4/15 tsamba 4-9
  • Kodi Moyo Wosatha Ndi Wothekadi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Moyo Wosatha Ndi Wothekadi?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tinapangidwa Kuti Tikhale ndi Moyo Kosatha
  • Chikhumbo cha Kukhala ndi Moyo Kosatha
  • Kodi Tiyenera Kukhulupirira Yani?
  • Kodi Chilidi Chifuno cha Mulungu?
  • Chifuno cha Mulungu Sichinasinthe
  • Tingakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kukhala ndi Moyo Kosatha Siloto Chabe
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Mmene Mungakhalire ndi Moyo Kosatha
    Galamukani!—1995
  • N’zotheka Ndithu Kuti Amene Ali Kumanda Adzakhalenso ndi Moyo
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 4/15 tsamba 4-9

Kodi Moyo Wosatha Ndi Wothekadi?

“Mphunzitsi, chabwino n’chiti ndichichite, kuti ndikhale nawo moyo wosatha?”​—MATEYU 19:16.

1. Kodi tinganenenji pa kutalika kwa moyo wa munthu?

MFUMU Xerxes I ya Perisiya, yodziŵika m’Baibulo monga Ahaswero, inali kuyendera asilikali ake asanayambe nkhondo m’chaka cha 480 B.C.E. (Estere 1:1, 2) Malinga ndi kunena kwa Mgiriki wolemba mbiri, Herodotus, mfumuyo inagwetsa misozi poona anyamata ake. Chifukwa? Xerxes anati: “Ndimamva chisoni ndikamaganiza za kufupika kwa moyo wa munthu. Pakuti amuna onseŵa, palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakhala ndi moyo zaka zana limodzi kuchokera lero.” Inunso mwina mwaona kuti moyo ndi waufupi momvetsa chisoni ndi kuti palibe amene amafuna kukalamba, kudwala, kapena kufa. Oo, bwenzi tikukhala ndi moyo wachinyamata, wathanzi ndi wachimwemwe!​—Yobu 14:1, 2.

2. Kodi anthu ambiri ali ndi chiyembekezo chotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

2 The New York Times Magazine ya September 28, 1997, inali ndi chifukwa chabwino pamene inafalitsa nkhani yakuti “Akufuna Kukhala ndi Moyo.” Inagwira mawu wofufuza wina amene anati: “Ndikukhulupiriradi kuti mbadwo wathu ndiwo ungakhale woyamba kukhala ndi moyo kosatha”! Mwina inunso mukukhulupirira kuti moyo wosatha ndi wotheka. Mungaganize motero chifukwa Baibulo limalonjeza kuti tidzakhala ndi moyo kosatha pano padziko lapansi. (Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4) Komabe, anthu ena amakhulupirira kuti moyo wosatha uli wotheka pazifukwa zina zosakhala za m’Baibulo. Kukambirana zingapo za zifukwa zimenezo kudzatithandiza kuzindikira kuti moyo wosatha ulidi wotheka.

Tinapangidwa Kuti Tikhale ndi Moyo Kosatha

3, 4. (a) Kodi n’chifukwa chiyani anthu ena amakhulupirira kuti tiyenera kukhala okhoza kukhala ndi moyo kosatha? (b) Kodi Davide anati chiyani pa za mmene anapangidwira?

3 Chifukwa china chimene anthu ambiri amakhulupirira kuti anthu ayenera kukhala ndi moyo kosatha chikukhudza njira yodabwitsa imene tinalengedwera. Mwachitsanzo, n’zozizwitsadi mmene tinaumbidwira m’mimba ya mayi wathu. Katswiri wotchuka wodziŵa zaukalamba analemba kuti: “Mphamvu ya chilengedwe itachita zozizwitsa zochokera pa kutenga mimba mpaka kubadwa ndiyeno kufika pakukhwima kwa mphamvu ya kugonana ndi pauchikulire, sinasankhe kukonza limene likanaoneka kukhala dongosolo wamba kuti lipitirize zozizwitsa zimenezo kosatha.” Inde, polingalira za mmene tinapangidwira modabwitsa, funso limakhalapo lakuti, Kodi n’chifukwa chiyani timafa?

4 Zaka zikwi zochuluka zapitazo, wolemba Baibulo Davide anasinkhasinkha pa zozizwitsa zimenezi, ngakhale kuti sanathe kuona m’mimba mwenimwenimo monga momwe asayansi lerolino amachitira. Davide anafatsa kulingalira za mmene anapangidwira pamene, monga momwe analembera, anali ‘kuumbidwa asanabadwe iye.’ Iye anati panthaŵi imeneyo ‘imso zake zinalengedwa.’ Ananenanso za kupangidwa kwa “mafupa” ake pamene, monga mmene iye analingalirira, “ndinali kupangidwa mobisika.” Davide kenako ananena za “mluza wanga” ndipo anati ponena za mluza umenewo uli m’mimba mwa mayi ake: “Ziŵalo zake zonse zinalembedwa.”​—Salmo 139:13-16, NW.

5. Kodi ndi zozizwitsa ziti zimene zimachitika pamene tikupangidwa m’mimba?

5 Ndithudi, panalibe buku lenileni lolembedwa ndi manja la kupangidwa kwa Davide m’mimba mwa mayi ake. Koma pamene Davide anali kusinkhasinkha za kupangidwa kwa “imso” zake, “mafupa” ake, ndi ziŵalo zina za thupi lake, anali kuona ngati kuti kupangidwa kwa ziŵalozi kunali kochita kulinganizidwa​—kuti chilichonse chinali, kunena kwake titero, ‘chitalembedwa.’ Kunali ngati kuti dzira lokhwima m’mimba mwa mayi ake linali ndi chipinda chachikulu chodzaza ndi mabuku okhala ndi malangizo onse a kuumba mwana wamunthu, ndiyeno malangizo ocholowana ameneŵa anaperekedwa kwa selo lililonse limene linatuluka. Ndicho chifukwa chake magazini ya Science World inagwiritsa ntchito fanizo la ‘selo lililonse la mluza womakulawo lokhala ndi kachipinda kodzaza bwino ka mabuku a malangizo.’

6. Kodi pali umboni wotani wakuti, monga mmene Davide analembera, ‘tinapangidwa modabwitsa’?

6 Kodi munayamba mwaganizapo za kagwiridwe ka ntchito kodabwitsa ka matupi athu? Katswiri wa sayansi ya zinthu za moyo Jared Diamond anati: “Kamodzi masiku oŵerengeka alionse, maselo a mkati mwa matumbo athu amachoka ndipo pamabwera atsopano, a mkati mwa chikodzero kamodzi miyezi iŵiri iliyonse, ndipo maselo athu ofiira a magazi kamodzi miyezi inayi iliyonse.” Iye anafika ponena kuti: “Chilengedwe chimatiswa ndi kutilumikizanso masiku onse.” Kodi zimenezo zikutanthauzanji kwenikweni? Zikutanthauza kuti mosasamala kanthu za zaka zimene tili nazo​—kaya ndi 8, 80, kapena ngakhale 800​—thupi lathu limakhalabe lanthete. Panthaŵi ina wasayansi wina anayerekezera kuti: “Pachaka, pafupifupi 98 peresenti ya maatomu amene ali mwa ife tsopano amachoka ndipo maatomu amene timaloŵetsa popuma, m’zakudya, ndi zakumwa, amatenga malo ake.” Zoonadi, ‘chipangidwe chathu ndi chodabwitsa,’ monga mmene Davide ananenera.​—Salmo 139:14.

7. Chifukwa cha mmene matupi athu anapangidwira, kodi anthu ena afika ponena chiyani?

7 Chifukwa cha mmene matupi athu anapangidwira, katswiri wina wa zaukalamba anati: “N’kovuta kudziŵa chimene timakalambira.” Zikuonekadi kuti tiyenera kukhala ndi moyo kosatha. Ndipo ndicho chifukwa chake anthu akuyesa kukwaniritsa cholinga chimenechi mwa tekinoloji yawo. Osati kale kwambiri, Dr. Alvin Silverstein, m’buku lake lakuti Conquest of Death, analemba motsimikiza kuti: “Tidzatulukira maziko enieni a moyo. Tidzamvetsa . . . mmene munthu amakalambira.” Ndiye zotsatira zake? Analosera kuti: “Sikudzakhalanso anthu ‘okalamba,’ pakuti chidziŵitso chimene chidzatilola kugonjetsa imfa chidzadzetsanso unyamata wamuyaya.” Polingalira za zofufuza zamakono za asayansi pa chipangidwe cha munthu, kodi kukuoneka kuti ndi kusalingalira bwino kuganiza za moyo wosatha? Palinso chifukwa china chachikulu chokhulupirira kuti moyo wosatha ndi wotheka.

Chikhumbo cha Kukhala ndi Moyo Kosatha

8, 9. Kodi anthu m’mbiri yonse akhala ndi chikhumbo chachibadwa chotani?

8 Kodi munaona kuti kukhala ndi moyo kosatha ndi chikhumbo chachibadwa cha anthu? Dokotala wina analemba m’magazini achijeremani kuti: “Chikhumbo cha moyo wosatha ndi chakalekale mwina mofanana ndi anthu.” Pofotokoza zikhulupiriro za Azungu ena akale, The New Encyclopædia Britannica ikuti: “Anthu oyenerera adzakhala kosatha m’nyumba yoŵala yofolera ndi golidi.” Ndipo, ee! Anthu afika patali ndi khama lawo lofuna kukhutiritsa chikhumbo chawo cha moyo wosatha.

9 The Encyclopedia Americana inati zaka zoposa 2,000 zapitazo ku China, “mafumu ndi anthu [wamba] omwe, motsogozedwa ndi ansembe achitao, anasiya ntchito nakafunafuna mankhwala a moyo”​—otchedwa kasupe wa unyamata. Indedi, anthu m’mbiri yonse akhulupirira kuti mwa kumwa mankhwala amitundumitundu kapena ngakhale kumwa madzi ena ake, sangakalambe.

10. Kodi ndi kuyesayesa kwamakono kotani kumene kukuchitika kuti moyo wautali ukhale wotheka?

10 Khama la anthu amakono poyesa kukhutiritsa chikhumbo chamunthu cha moyo wosatha nalonso n’lochititsa kaso. Chitsanzo chodziŵika bwino ndicho mchitidwe woumitsa mtembo wa munthu amene anafa ndi matenda. Zimenezi zikuchitika ndi cholinga chodzabwezeretsa moyo nthaŵi ina yake m’tsogolo akadzapeza mankhwala a matendawo. Munthu wina wolimbikitsa mchitidwe umenewu, umene umatchedwa kuti cryonics, analemba kuti: “Ngati chiyembekezo chathu chikhala choona ndipo tapeza njira yochiritsira kapena kukonzanso zowonongedwa zonse​—kuphatikizapo zofooka za ukalamba​—ndiye kuti aja amene ‘akufa’ tsopano adzakhala ndi moyo wautali wosatha m’tsogolo.”

11. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amafuna kukhala ndi moyo kosatha?

11 Mungafunse kuti, kodi n’chifukwa chiyani chikhumbo chimenechi cha moyo wosatha chili cholimba m’maganizo mwathu? Kodi ndi chifukwa chakuti “[Mulungu] waika umuyaya m’maganizo a munthu”? (Mlaliki 3:11, Revised Standard Version) Imeneyi ndi nkhani yofuna kuilingalira kwambiri! Tangoganizirani: Kodi tikanakhumbiranji mwachibadwa kukhalako kwamuyaya​—kosatha​—ngati Mlengi wathu sanafune kuti chikhumbo chimenechi chikhutiritsidwe? Ndipo kodi iye akanakhala wachikondi ngati anatilenga ndi chikhumbo cha moyo wosatha kenako n’kutigwiritsa mwala mwa kusatilola kukhutiritsa chikhumbocho?​—Salmo 145:16.

Kodi Tiyenera Kukhulupirira Yani?

12. Kodi anthu ena ali ndi chidaliro chotani, koma kodi inuyo mukukhulupirira kuti ndi zoona?

12 Kodi ndi kuti, kapena ndi ndani amene tiyenera kukhulupirira kuti tikapeze moyo wosatha? Tekinoloji ya anthu ya m’zaka za zana la 20 kapena 21? Nkhani ya mu The New York Times Magazine yakuti “Akufuna Kukhala ndi Moyo” inasimba za “mulungu: tekinoloji” ndi za “chidwi m’mphamvu ya tekinoloji.” Ndipo akuti wofufuza wina anali ndi “chikhulupiriro chonse . . . chakuti posapita nthaŵi kudzakhala njira zogwiritsa ntchito majini kupulumutsa [ifeyo] mwa kuletsa ukalamba, mwinamwake kuubwereretsa m’mbuyo.” Koma kunena zoona, zoyesayesa za anthu zalephereratu kuletsa kukalamba kapena kugonjetsa imfa.

13. Kodi kapangidwe ka ubongo wathu kamasonyeza motani kuti tinalengedwa kuti tikhale ndi moyo kosatha?

13 Kodi izi zikutanthauza kuti palibe njira yopezera moyo wosatha? Kutalitali! Njira ilipo! Kapangidwe ka ubongo wathu wodabwitsawo, pamodzi ndi mphamvu yake ya kuphunzira yopanda malire, ziyenera kutikhutiritsa maganizo pa zimenezi. Katswiri wa sayansi ya mamolekiyu a zinthu zamoyo James Watson anatero kuti ubongo wathu ndiwo “chinthu chocholoŵana koposa chimene tapeza m’chilengedwe chathu chonse.” Ndipo katswiri wa zaminyeŵa Richard Restak anati: “Kulibe kulikonse m’chilengedwe chodziŵika kumene tingapeze chinthu chofanana nawo mpang’ono pomwe.” Ngati sitinalengedwe kuti tisangalale ndi moyo wosatha, kodi n’chifukwa chiyani tili ndi ubongo umene uli ndi mphamvu yosunga chidziŵitso chopanda malire n’kumachikumbukira ndiponso thupi limene linalengedwa kukhala kosatha?

14. (a) Kodi olemba Baibulo anagamula zotani ponena za moyo wamunthu? (b) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Mulungu ndipo osati munthu?

14 Chifukwa cha zimenezi, kodi tingafike pogamula zotani zimene zilidi zanzeru ndi zoona? Kodi sizakuti tinalengedwa ndi Mpangi wanzeru ndi wamphamvu yonse kuti tikhale ndi moyo kosatha? (Yobu 10:8; Salmo 36:9; 100:3; Malaki 2:10; Machitidwe 17:24, 25) Motero, kodi sitiyenera kulabadira mwanzeru lamulo louziridwa la wamasalmo wa m’Baibulo lakuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye”? Chifukwa chiyani sitiyenera kukhulupirira munthu? Chifukwa chakuti, monga momwe wamasalmoyo analembera, “mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” Inde, mosasamala kanthu kuti angakhale ndi moyo kosatha, anthu amasoŵa chochita imfa itafika. Wamasalmoyo anagamula kuti: “Wodala munthu amene . . . chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.”​—Salmo 146:3-5.

Kodi Chilidi Chifuno cha Mulungu?

15. Kodi ndi chiyani chikusonyeza kuti chili chifuno cha Mulungu kuti tikhale ndi moyo kosatha?

15 Koma mungafunse kuti, Kodi n’zoona kuti chili chifuno cha Mulungu kuti tikhale ndi moyo wosatha? Inde! Mawu ake amalonjeza za moyowo nthaŵi zambirimbiri. “Mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha,” Baibulo limatitsimikizira motero. Mtumiki wa Mulungu Yohane analemba kuti: “Ili ndi lonjezano [Mulungu] anatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha.” Ndi zosadabwitsa kuti mnyamata wina anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi, chabwino n’chiti ndichichite, kuti ndikhale nawo moyo wosatha?” (Aroma 6:23; 1 Yohane 2:25; Mateyu 19:16) Ndiponsotu, mtumwi Paulo analemba za ‘chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthaŵi zosayamba.’​—Tito 1:2.

16. Kodi ndi m’lingaliro lotani limene Mulungu angakhale atalonjeza moyo wosatha “zisanayambe nthaŵi zosayamba”?

16 Kodi zikutanthauzanji kuti Mulungu analonjeza moyo wosatha “zisanayambe nthaŵi zosayamba”? Ena amaganiza kuti mtumwi Paulo anali kutanthauza kuti anthu aŵiri oyambawo, Adamu ndi Hava, asanalengedwe, Mulungu anafuna kuti anthu akhale ndi moyo kosatha. Komabe, ngakhale ngati Paulo anali kunena za nthaŵi ina pambuyo pa kulengedwa kwa anthu pamene Yehova anatchula za chifuno chake, ndi zomvekabe kuti chifuno cha Mulungu chikuphatikizapo moyo wosatha kwa anthu.

17. Kodi ndi chifukwa chiyani Adamu ndi Hava anapitikitsidwa m’munda wa Edene, nanga ndi chifukwa chiyani makerubi anaikidwa pakhomo la mundawo?

17 Baibulo limanena kuti m’munda wa Edene, “Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka . . . mtengo wa moyo.” Chifukwa chimene chinaperekedwa chopitikitsira Adamu m’mundawo chinali chakuti “asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthaŵi zonse”​—inde, kosatha! Adamu ndi Hava atapitikitsidwa m’munda wa Edene, Yehova anaika “Makerubi . . . ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.”​—Genesis 2:9; 3:22-24.

18. (a) Kodi kudya za mtengo wa moyo kukanatanthauzanji kwa Adamu ndi Hava? (b) Kodi kudya mtengo umenewo kunaimira chiyani?

18 Ngati Adamu ndi Hava akanadya za mtengo wa moyo umenewo, kodi zikanatanthauzanji kwa iwo? Eya, akanakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso! Katswiri wina wa Baibulo analingalira kuti: “Mtengo wa moyowo uyenera kuti unali ndi mphamvu inayake imene ikanachotsa zofooka za ukalamba m’thupi la munthu, kapena chivundi chimene chimadzetsa imfa.” Anafika ngakhale ponena kuti “m’paradaiso munali mankhwala azitsamba okhoza kuletsa zotsatirapo” za ukalamba. Komabe, Baibulo silinena kuti mtengo wa moyowo pawokha unali ndi mphamvu zopatsa moyo. M’malo mwake, mtengowo unangoimira chitsimikizo cha Mulungu cha kupatsa moyo wosatha kwa munthu amene iye akanamulola kudya zipatso zake.​—Chivumbulutso 2:7.

Chifuno cha Mulungu Sichinasinthe

19. Kodi n’chifukwa chiyani Adamu anafa, nanga n’chifukwa chiyani ifeyo, ana ake, timafanso?

19 Adamu atachimwa, anataya ufulu wake wokhala ndi moyo kosatha ndi wa ana ake onse amene anali asanabadwe. (Genesis 2:17) Pamene anakhala wochimwa chifukwa cha kusamvera kwake, analemala, anakhala wopanda ungwiro. Kuyambira nthaŵi imeneyo kumka m’tsogolo, tingati thupi la Adamu linalinganizidwa kuti lidzafe. Malinga ndi zimene Baibulo limanena, “mphotho yake ya uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Ndiponso, ana opanda ungwiro a Adamu nawonso tingati analinganizidwa kuti azifa, osati kukhala ndi moyo kosatha. Baibulo limafotokoza kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”​—Aroma 5:12.

20. Kodi ndi chiyani chikusonyeza kuti anthu analinganizidwa kukhala ndi moyo wosatha padziko lapansi?

20 Nanga bwanji ngati Adamu akanapanda kuchimwa? Bwanji ngati anamvera Mulungu ndiyeno kuloledwa kudya za ku mtengo wa moyo? Kodi mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha akanailandirira kuti? Kumwamba? Ayi! Mulungu sananenepo zoti adzatengera Adamu kumwamba. Anapatsidwa ntchito yochita pano padziko lapansi. Baibulo limanena kuti “Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya,” ndiponso limati: “Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m’munda wa Edene kuti aulime nauyang’anire.” (Genesis 2:9, 15) Hava atalengedwa kukhala mkazi wa Adamu, aŵiriwo anapatsidwanso ntchito zina pompano padziko lapansi. Mulungu anawauza kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwaŵa padziko lapansi.”​—Genesis 1:28.

21. Kodi anthu oyambirirawo anali ndi chiyembekezo chosangalatsa chotani?

21 Talingalirani za chiyembekezo chosangalatsa cha padziko lapansi chimene malangizo amenewo a Mulungu anapereka kwa Adamu ndi Hava! Anali kudzalera ana aamuna ndi aakazi athanzi langwiro m’Paradaiso wa padziko lapansi. Pokula ana awo okondedwawo, iwonso akanabala ana ndi kuchita ntchito yosangalatsa ya m’munda kuti asamalire Paradaiso ameneyo. Pokhala kuti nyama zonse zikanawamvera, anthu akanakhala okhutira kwambiri. Taganizani za chimwemwe chomwe akanakhala nacho cha kufutukula malire a munda wa Edene kotero kuti pomaliza pake dziko lonse lapansi likhale paradaiso! Kodi mukanakonda kukhala ndi moyo muli ndi ana angwiro m’mudzi wa padziko lapansi wokongola chotere, popanda nkhaŵa iliyonse ya ukalamba ndi imfa? Lekani chilakolako cha mtima wanu chiyankhe funso limenelo.

22. Kodi ndi chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Mulungu sanasinthe chifuno chake cha dziko lapansi?

22 Tsopano, Adamu ndi Hava atakana kumvera ndipo n’kuthamangitsidwa m’munda wa Edene, kodi Mulungu anasintha chifuno chake chakuti anthu akhale ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi? Kutalitali! Mulungu akanachita zimenezo, zikanatanthauza kuti iye akuvomereza kuti walephera kuchita chifuno chake choyamba. Tikutsimikiza kuti Mulungu amachita zimene walonjeza, monga momwe iye mwini ananenera kuti: “Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:11.

23. (a) Kodi n’chiyani chimene chikutsimikiziranso kuti chili chifuno cha Mulungu kuti olungama akhale ndi moyo kosatha padziko lapansi? (b) Kodi nthaŵi yotsatira tidzakambirana chiyani?

23 Kuti chifuno cha Mulungu cha dziko lapansi sichinasinthe zikusonyezedwa bwino m’Baibulo, mmene Mulungu akulonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Ngakhale Yesu Kristu ananena mu Ulaliki wake wa pa Phiri kuti ofatsa adzalandira dziko lapansi. (Salmo 37:29; Mateyu 5:5) Komabe, kodi moyo wosatha tingaupeze bwanji, ndipo kodi tiyenera kuchitanji kuti tikhale ndi moyo woterewo? Nkhani yotsatira idzalongosola zimenezi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

◻ Kodi ndi chifukwa chiyani anthu ambiri amakhulupirira kuti moyo wosatha ndi wotheka?

◻ Kodi ndi chiyani chimene chiyenera kutikhutiritsa maganizo kuti tinalengedwa kuti tikhale ndi moyo kosatha?

◻ Kodi chifuno cha Mulungu choyambirira cha anthu ndi dziko lapansi chinali chotani?

◻ Kodi n’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Mulungu adzakwaniritsa chifuno chake choyambirira?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena