Mulungu Akulinganiza Kuti Munthu Asangalale ndi Moyo M’paradaiso
“Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m’munda wa Edene kuti aulime nauyang’anire.”—GENESIS 2:15.
1. Nchiyani chomwe chinali chifuno choyambirira cha Mlengi ponena za anthu omvera?
CHINALI chifuno choyambirira cha Mlengi, ndipo chidakali chifuno chake, kuti anthu omvera asangalale ndi moyo wosakalamba, nthaŵi zonse wodzala ndi thanzi lauchichepere, wopanda kusungulumwa konse, nthaŵi zonse wokhala ndi chifuno chophulapo kanthu choti achikwaniritse, moyo wokonda ndi wokondedwa m’njira yowona, yopanda dyera, yangwiro—m’paradaiso!—Genesis 2:8; yerekezani ndi Luka 23:42, 43.
2. (a) Nchiyani chomwe chiyenera kukhala chinachitika pamene mwamuna woyamba anakhala wozindikira? (b) Ndi liti pamene mwamuna woyamba analengedwa, kuti, ndipo pa nthaŵi yanji ya chaka?
2 Kuti muzindikire chimenecho, yang’anani kumbuyo pa Adamu wolengedwa chatsopanoyo pamene iye choyamba analandira kuzindikira, pamene anasanthula thupi lake la iyemwini ndi zonse zimene iye anawona ndi kumva ndi kudzimva momuzungulira, pamene iye anazindikira poyambirirapo kuti anali wamoyo! Ichi chinachitika zaka zina 6,000 zapitazo, m’chaka cha 4,026 Nyengo yathu Yachisawawa isadakhale, mogwirizana ndi kuŵerengera kwa nthaŵi kopatsidwa m’Baibulo Lopatulika. Icho chinachitika m’dera la dziko lomwe lerolino likudziŵika monga Turkey, kapena mbali ya kum’mwera cha kumadzulo kwa imene tsopano ikutchedwa Asia, kwinakwake chapafupi ndi Mtsinje wa Firate ndi Mtsinje wa Tigrisi, ndipo mwakutero ku theka la kumpoto kwa chiwunda chathu cha dziko lapansi. Nthaŵiyo ikakhala chifupifupi October 1, popeza kuti makalenda ochulukira a mtundu wa anthu anayamba kuŵerengera nthaŵi pafupi ndi deti limenelo.
3. (a) Ndi mu mkhalidwe wotani mmene mwamuna woyamba anakhala ndi moyo? (b) Nchiyani chimene dzina la mwamuna woyamba linadzakhala, ndipo nchiyani chomwe chinali kupatulika kwake?
3 Mwamuna woyamba anakhala ndi moyo atakula kale, wopangidwa mwangwiro, waumoyo wangwiro, wa makhalidwe angwiro. Dzina lomwe limapatsidwa kwa iye mobwerezabwereza m’zolembera za Baibulo limaitanira chisamaliro chathu ku zinthu zimene iye anapangidwirako. Dzina lake linali ‘A·dhamʹ.a Dziko lapansi, kapena nthaka, kuchokera ku limene iye anapangidwa linatchedwa ‘a·dha·mahʹ. Chotero dzina lake linganenedwe bwino lomwe kutanthauza “Munthu wa pa Dziko Lapansi.” Iri linadzakhala dzina laumwini la mwamuna woyambirira ameneyu—Adamu. Ndi kuzindikira kotani nanga mmene iko kunakhalira kwa Adamu pamene anakhala wamoyo, kukhala munthu wozindikira, waluntha!
4. Ndi kudzutsidwa kwachilendo kotani ku moyo kumene mwamuna woyamba sanakhale nako, chotero iye sanali mwana wa chiyani?
4 Pamene mwamuna woyambirira ameneyu, Adamu, anakhala ndi moyo, kudzuka ku kuzindikira kwa luntha, ndi kutsegula maso ake, iye sanadzipeze iyemwini aligone pamiyendo yaubweya, wofukatiridwa ndi mikono yaitali yamphamvu ya cholengedwa chachikazi chonga nyani, akumamamatira kwa icho ndi kuyang’ana m’maso mwake ndipo ndi kudzimva kwachikondi kuchitcha icho Amayi. Mwamuna woyambayo, Adamu, analibe kudzutsidwa kwachilendo koteroko ku moyo. Iye sanadzimve unansi wakuthupi uliwonse kwa nyani, osati ngakhale pambuyo pake pamene iye anawona mmodzi. Pa tsiku la kulengedwa kwake, panalibe chirichonse cholingalira kuti iye anali mbadwa, mwana wapatali, wa nyani kapena cholengedwa china chirichonse chofanana ndi chimenecho. Komabe, kodi mwamuna woyambayo, Adamu, anafunikira kukhalabe wozizwitsidwa ponena za mmene iye anadzakhalirako? Ayi.
5. Nchiyani chomwe Adamu anadziŵa motsimikizirika ponena za munda wake wonga paki ndi ponena za iyemwini?
5 Momvetsetseka, iye ayenera kukhalanso anali wozizwitsidwa ponena za mmene zinthu zonse zokongola pa zimene iye anayang’ana zinakhalirako. Anadzipeza iyemwini ali m’munda wofanana ndi paki, paradiso yomwe sinakonzedwe ndi iye, kapangidwe, ndi kakonzekeretsedwe. Kodi zonsezi zinadza motani? Pokhala mwamuna waluntha mwangwiro, wolingalira, iye akafuna kudziŵa. Iye analibe chokumana nacho cha poyambirirapo. Iye anadziŵa kuti sanali munthu wodzipanga yekha, wodziyambitsa yekha. Iye sanauke ku mkhalidwewu ndi kuyesayesa kwa iyemwini.—Yerekezani ndi Salmo 100:3; 139:14.
6. Ndimotani mmene Adamu mwachidziŵikire akavomerezera ku kukhala wamoyo m’mudzi wangwiro wa pa dziko lapansi?
6 Mwamuna woyambayo, Adamu, poyambirirapo angakhale anali wokondweretsedwa kwenikweni ponena za chokumana nacho choyambirira chimenechi cha kukhala wamoyo mosangalala m’nyumba yangwiro ya dziko lapansi kuganizira za kumene iye anachokera ndi chifukwa chake. Iye sakakhoza kuthandiza mpang’ono pomwe koma kupanga kufuula kwachimwemwe. Iye anapeza mawu akutuluka m’kamwa mwake. Anadzimva iyemwini akulankhula chinenero cha munthu, kupanga ndemanga ponena za zinthu zokondeka zomwe iye anawona ndi kumva. Chinali chabwino chotani nanga kukhala wamoyo muno m’munda wa Paradaiso uwu! Koma pamene anadzidzaza iyemwini mosangalatsa ndi chidziŵitso chochokera ku zowoneka zonse, mawu, kununkhira, ndi kumva zinthu, iye akanasonkhezeredwa kuchita kulingalira kwinakwake. Kwa ife, tikanaikidwa mu mkhalidwe wake, pakanakhala chinsinsi ponena za chinthu chonsecho, chinsinsi chomwe sitikanachithetsa ife eni.
Palibe Chinsinsi Ponena za Kukhalapo kwa Munthu
7. Nchifukwa ninji Adamu sanazizwitsidwe kwa nthaŵi yaitali ponena za kudzipeza iyemwini wamoyo ndipo m’munda wa paradaiso?
7 Mwamuna woyambirirayo, Adamu, sanazizwitsidwe kwa nthaŵi yaitali ponena za mkhalidwe mu umene iye anadzipeza iyemwini wamoyo ndipo ali yekha, popanda wina aliyense wofanana ndi iye wowonekera m’munda wa Paradaiso. Iye anamva liwu, winawake akulankhula. Mwamunayo analimvetsetsa ilo. Koma kodi mlankhuliyo anali kuti? Mwamunayo sanawone aliyense akulankhula. Liwulo linachokera kosawoneka, m’bwalo losawoneka, ndipo linali kulankhula kwa iye. Linali liwu la Mpangi wa mwamunayo, Mlengi wake! Ndipo mwamunayo akakhoza kumuyankha iye mu mtundu wofananawo wa kalankhulidwe. Iye anadzipeza iyemwini akulankhula ndi Mulungu, Mlengi. Mwamunayo sanafunikire cholandirira cha wailesi yamakono ya usayansi kuti amve liwu laumulungulo. Mulungu analankhula naye mwachindunji monga cholengedwa chake.
8, 9. (a) Ndi mafunso otani omwe Adamu akapeza mayankho, ndipo ndi chisamaliro chautate chotani ndi chikondwerero chomwe chinasonyezedwa kwa iye? (b) Ndi yankho lotani limene Adamu analandira kuchokera kwa Atate wake wakumwamba?
8 Tsopano mwamunayo anadziŵa kuti sanali yekha, ndipo kaamba ka ichi iye afunikira kukhala anadzimva bwinopo. Maganizo ake anali odzaza ndi mafunso. Iye akafunsa ponena za iwo kwa Wosawonekayo wolankhula kwa iye. Ndani yemwe anampanga iye ndi munda wachisangalalo? Nchifukwa ninji iye anaikidwa kumeneko, ndipo nchiyani chomwe iye akachita ndi moyo wake? Kodi panali chifuno chirichonse m’kukhala ndi moyo? Chisamaliro ndi chikondwerero cha utate zinasonyezedwa kwa mwamuna woyamba ameneyu, Adamu, popeza kuti mafunso ake anapatsidwa yankho lomwe linakhutiritsa maganizo ake ofunsa. Ndi chisangalalo chotani nanga momwe chinakhalira kwa Mpangi wake, Mpatsi wake wa Moyo, Atate wake wakumwamba, kumva mwamunayo akuyamba kulankhula ndi kunena mawu ake oyambirira! Ndi chimwemwe chotani nanga chimene icho chinapereka kwa Atate wakumwamba kumva mwana wake akulankhula kwa iye! Funso lachibadwa loyambirira likakhala lakuti, “Ndimotani mmene ndinakhalirako?” Atate wakumwamba anali wosangalatsidwa kuyankha ichi ndipo mwakutero kuvomereza kuti mwamuna woyamba ameneyu anali mwana Wake. Iye anali “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Yehova anadzidziŵitsa iyemwini kukhala Atate wa mwamuna woyamba ameneyu, Adamu. Kuchokera kwa Atate wake wa kumwamba, pano pali nsonga ya yankho limene Adamu analandira ku funso lake ndi limene analipereka ilo kwa mbadwa zake:
9 “Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nawuzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo. Ndipo Yehova Mulungu anabzala m’munda ku Edene chakum’mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo. Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pa mundapo, ndi mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa. Ndipo unatuluka m’Edene mtsinje wakuthirira m’mundamo, mmenemo ndipo unalekana nuchita miyendo inayi.”—Genesis 2:7-10.b “Dzina la wakuyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, mmene muli golidi; golidi wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu. Dzina la mtsinje wachiŵiri ndi Gihoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Kusi. Dzina la mtsinje wachitatu ndi Hidikeli: umenewo ndiwo wakuyenda cha kum’mawa kwake kwa Asuri. Mtsinje wachinayi ndi Firate.”—Genesis 2:11-14.
10, 11. (a) Ndi nsonga zotani zimene Adamu anaphunzira momvekera, koma kodi ndi mafunso ena otani omwe iye anafuna kuti ayankhidwe? (b) Ndi mayankho otani amene Atate wakumwamba anapereka kwa Adamu?
10 Maganizo owala a Adamu, atsopano anatenga mofunitsitsa chidziŵitso chokhutiritsa chimenechi. Tsopano iye anadziŵa kuti sanachokere ku bwalo losawoneka limenelo kuchokera kumene Mpangi wake ndi Wolinganiza anali kulankhula. M’malomwake, iye analinganizidwa kuchokera ku dziko lapansi pamene iye anali kukhala ndi moyo ndipo chotero anali wa pa dziko lapansi. Mpatsi wake wa Moyo ndi Atate anali Yehova Mulungu. Iye anali “wamoyo.” Pokhala atalandira moyo wake kuchokera kwa Yehova Mulungu, iye anali “mwana wa Mulungu.” Mitengo yomuzungulira m’munda wa Edene inatulutsa zipatso zomwe zinali zabwino kaamba ka kudya, kuti iye adye ndi kukhala ndi moyo monga wamoyo. Ndipo komabe, nchifukwa ninji iye akafunikira kukhala ndi moyo, ndipo nchifukwa ninji iye anaikidwa pa dziko lapansi, m’munda wa Edene umenewu? Iye anali mwamuna wolinganizidwa mokwanira wa luntha wokhala ndi kuthekera kwakuthupi, ndipo anafunikira kudziŵa. Ndimotani, kupanda apo, momwe akanakwaniritsira chifuno chake m’moyo ndipo mwakutero kukondweretsa Mpangi wake ndi Atate mwa kuchita chifuniro chaumulungu? Mayankho ku mafunso oyenera amenewa anaperekedwa m’chidziŵitso chotsatirachi:
11 “Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m’munda wa Edene kuti aulime nauyang’anire. Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.”—Genesis 2:15-17.
12. Ndi ponena za chiyani chimene Adamu afunikira kukhala anayamikira Mlengi wake, ndipo ndimotani mmene munthu mwakutero analemekezera Mulungu?
12 Adamu ayenera kukhala anayamikira Mlengi wake chifukwa chopatsidwa chinachake cha kumusunga iye kukhala wotanganitsidwa mwachangu m’munda wokongola umenewu wa Edene. Tsopano iye anadziŵa chifuno cha Mlengi wake, ndipo akanachita chinachake pa dziko lapansi kaamba ka Iye. Iye tsopano anali ndi thayo lokhala pa iye, lija la kulima munda wa Edene ndi kuwusamalira, koma chimenecho chikakhala chinthu chosangalatsa kuchichita. Mwa kuchita chimenechi, iye akasunga munda wa Edene kukhala ukuwoneka m’njira yoteroyo yopereka ulemerero ndi chitamando kwa Mpangi wake, Yehova Mulungu. Nthaŵi iriyonse pamene Adamu anamva njala chifukwa chogwira ntchito, iye akanakhoza kudya ku chikhutiritso kuchokera ku mitengo ya m’mundayo. Mwanjirayi iye akapanganso yatsopano nyonga yake ndi kusungabe moyo wake wachimwemwe ku nthaŵi zonse—kosatha.—Yerekezani ndi Mlaliki 3:10-13.
Chiyembekezo cha Moyo Wosatha
13. Ndi chiyembekezo chotani chimene mwamuna woyamba anali nacho, ndipo nchifukwa ninji tero?
13 Kosatha? Ndi chifupifupi lingaliro losakhulupirika chotani nanga lomwe iri linakhalira kwa munthu wangwiro! Nkulekeranji? Mlengi wake analibe lingaliro lirilonse kapena chifuno cha kuwononga munda wa Edene wolinganizidwa mwaluso umenewo. Nchifukwa ninji iye akawononga ntchito yakeyake, pamene iyo inali yabwino kwambiri ndipo yolongosola kupanga kwake kwa luso? Mwanzeru, iye sakalingalira kuchita tero. (Yesaya 45:18) Ndipo popeza kuti munda wosayerekezeka umenewu unafunikira kukhala pansi pa kulimidwa, iwo ukafunikira mlimi ndi wosamalira wofanana ndi mwamuna wangwiroyo, Adamu. Ndipo ngati munthu wosamalirayo sanadye konse chipatso cha mtengo woletsedwa “wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa,” iye sakanafa konse. Mwamuna wangwiroyo akanakhala ndi moyo kosatha!
14. Ndimotani mmene Adamu akakhalira ndi moyo wosatha m’Paradaiso?
14 Moyo wosatha m’munda wa Paradaiso wa Edene unakhazikitsidwa pamaso pa Adamu! Iwo ukasangalalidwa kosatha, malinga ngati iye anakhala womvera mwangwiro kwa Mlengi wake, osadya chipatso chomwe chinaletsedwa ndi Mlengi wa munthu. Chinali chikhumbo Chake kuti mwamuna wangwiroyo akhale womvera ndi kukhala ndi moyo kosatha. Kuletsedwa kwa chipatso cha “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa” sikunali chirichonse chochititsa imfa. Chinali kokha chiyeso cha chimvero changwiro cha munthu kwa Atate wake. Icho chinapereka mwaŵi kwa mwamunayo kutsimikizira chikondi chake kaamba ka Mulungu, Mlengi wake.
15. Nchifukwa ninji Adamu akayang’ana kutsogolo ku mtsogolo mowala, mokhala ndi zabwino pa manja a Mlengi wake?
15 Pokhala ndi mtima wokhutiritsidwa wakuti iye sanali osati kokha ngozi yosayembekezeredwa koma anali ndi Atate wakumwamba, pokhala ndi maganizo ake owunikiridwa ndi kumvetsetsa kwa chifuno chake m’moyo, kukhala ndi lingaliro la moyo wosatha m’Paradaiso, munthu wangwiroyo akayang’ana kutsogolo kuloŵa mtsogolo mowala. Iye anadya za mitengo yomwe inali yabwino kaamba ka zakudya, akumapewa “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa.” Iye anafuna kudziŵa zabwino pa manja a Mlengi wake. Ntchito, osati ya mtundu wowononga, koma yolima munda wa Edene inali yabwino, ndipo munthu wangwiroyo anagwira ntchito.
Panalibe Thayo Lomvedwa la Kulongosola Zinthu
16-18. Ndi zotchedwa zinsinsi zotani zimene Adamu sanadzimve wofunikira kuthetsa, ndipo nchifukwa ninji?
16 Masana owala anazimiririka monga chowunikira chachikulu cha usana, chomwe iye akakhoza kuwona m’kayendedwe kake modutsa mlengalenga, kufikira kuloŵa. Mdima unadza, usiku, ndipo mwezi unawonekera kwa iye. Sichinamdzaze iye ndi lingaliro la mantha; chinali chowunikira chaching’ono chimene chinalamulira usiku. (Genesis 1:14-18) Mwachidziŵikire, zipanipani zinawuluka uku ndi uko m’mundawo, zikumayatsa ndi kuzima kuwunika kwawo kosatenthako mofanana ndi nyali zazing’ono.
17 Pamene usiku unafika ndipo mdima unamkuta, iye anamva chifuno cha kugona mofanana ndi zinyama zomzinga iye. Pamene anagalamuka anayamba kumva njala, ndipo anadya ndi chilakolako chabwino kuchokera ku mitengo ya zipatso yovomerezedwa, kuti akhale ndi chomwe chingatchdwe kufisula.
18 Atakhalanso ndi mphamvu ndi kutsitsimulidwa bwino lomwe ndi kupuma kwausiku, iye anatembenuzira chisamaliro chake ku ntchito ya tsikulo. Pamene iye anawona kubiriŵira konseko komuzungulira, iye sanadzimve kuti anafunikira kukumba m’chinsinsi cha chomwe anthu zaka zikwi zingapo pambuyo pake akatcha photosynthesis, kugwira ntchito kodabwitsa kumeneku mwa kumene mtundu wobiriŵira wa zomera, kubiriŵira kwake, kumamwererera mphamvu ya kuwala kwa dzuŵa kuti kutulutse zakudya kaamba ka munthu ndi nyama kuti zidye, pa nthaŵi imodzimodziyo kutenga carbon dioxide mpweya womwe munthu ndi nyama zimatulutsa ndi kutulutsa oxygen (mpweya womwe timapumira mkati) kaamba ka iwo kuti azipuma. Munthu angakutche iko chinsinsi, koma panalibe kufunika kaamba ka Adamu kuchithetsa icho. Chinali chozizwitsa cha Mlengi wa munthu. Iye anachimvetsetsa icho ndipo anachipanga kuti chigwire ntchito kaamba ka phindu la zolengedwa zamoyo pa dziko lapansi. Ndiponso, chinali chokwanira kaamba ka luntha la mwamuna woyambirira wangwiro kuti Mulungu, Mlengi, anapanga zinthu kuti zizikula, ndipo ntchito ya munthu yopatsidwa ndi Mulungu inali kusamalira kaamba ka mitundu imeneyi ya zomera zamoyo zomakula m’munda wa Edene.—Onani Genesis 1:12.
Yekha—Koma Wosasoŵa Chisangalalo
19. Ngakhale kuti anazindikira kuti anali yekha, popanda wina aliyense wofanana ndi iye pa dziko lapansi, nchiyani chomwe Adamu sanachite?
19 Maphunziro a munthu pa manja a Atate wake wakumwamba sanathe. Munthu anasamalira munda wa Edene popanda aliyense wofanana ndi iye pa dziko lapansi kutsagana naye kapena kumuthandiza. Malinga ndi mtundu wake, mmene mtundu wa munthu, unakhuzidwira, iye anali yekha. Iye sanapite kukafufuza kukapeza winawake wofanana ndi iye kwa amene akafunikira kukhala ndi unansi wa pa dziko lapansi. Iye sanafunse Mulungu, Atate wake wakumwamba, kumpatsa iye mbale kapena mlongo. Kukhala kwake yekha monga mwamuna sikunamtenge iye potsirizira kukhala wofuntha ndi kumlanda chisangalalo cha kukhala ndi moyo ndi kugwira ntchito. Iye anali ndi ubwenzi ndi Mulungu.—Yerekezani ndi Salmo 27:4.
20. (a) Nchiyani chomwe chinali kuya kwa chimwemwe ndi chisangalalo cha Adamu? (b) Nchifukwa ninji kupitiriza mwanjira imeneyi ya moyo sikukakhala kutopetsa kwakupha kwa Adamu? (c) Nchiyani chomwe nkhani yotsatira idzakambitsirana?
20 Adamu anadziŵa kuti iye ndi ntchito yake zinali pansi pa chiyang’aniro cha Atate wake wakumwamba. Kuya kwa chisangalalo chake kunali m’kukondweretsa Mulungu wake ndi Mlengi, amene kudabwitsa kwake kunavumbulidwa ndi ntchito zokongola zonse za chilengedwe pozungulira ponse pa munthu. (Yerekezani ndi Chibvumbulutso 15:3.) Kupitiriza m’njira imeneyi ya moyo sikukakhala kutopetsa kwakupha kapena ntchito yosungulumwitsa kaamba ka mwamuna wolinganizika mwangwiro amenewu yemwe akakhoza kukambitsirana ndi Mulungu wake. Ndipo Mulungu anali atakhazikitsa pamaso pa Adamu ntchito yokondweretsa, yosangalatsa, yomwe ikambweretsera iye chikhutiritso chachikulu ndi chisangalalo. Nkhani yotsatira idzanena zambiri ponena za madalitso ndi ziyembekezo za Paradaiso zimene Adamu anasangalala nazo pa manja a Mlengi wake wachikondi.
[Mawu a M’munsi]
a Iri ndi liwu la m’chinenero choyambirira cha cholembera cha chilengedwe m’Baibulo Lopatulika.—Genesis 1:26, New World Translation Reference Bible, mawu am’munsi.
b Mneneri Mose, yemwe analemba chidziŵitsocho m’bukhu la Genesis m’zana la 16 Nyengo yathu Yachisawawa isadakhale, anawonjezera chidziŵitso chotsatirachi ponena za mtsinje wa mu Edene umenewu, mogwirizana ndi chidziŵitso cha m’tsiku lake:
Ndi Ati Omwe Ali Mayankho Anu?
◻ Nchifukwa ninji Adamu sanazizwitsidwe kwa nthaŵi yaitali ponena za kukhalapo kwake?
◻ Ndi ntchito yotani imene Mulungu anapatsa Adamu, ndipo ndimotani mmene iye angakhale anavomerezera?
◻ Ndi chiyembekezo chotani chimene mwamuna wangwiroyo anasangalala nacho, ndipo nchifukwa ninji?
◻ Nchifukwa ninji Adamu sanachipange icho kukhala ntchito yake ya moyo kuthetsa zinsinsi?
◻ Nchifukwa ninji kukhala yekha kwa Adamu monga mwamuna sikunalande chisangalalo m’kukhala ndi moyo?
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
NASA photo