Mutu 5
Ufulu Womwe Olambira Yehova Amakhala Nawo
YEHOVA atalenga mwamuna ndi mkazi oyambirira, iwo anali ndi ufulu woposa ufulu uliwonse umene anthu ali nawo lerolino. Anali kukhala m’Paradaiso, m’munda wokongola wa Edene. Sanalephere kusangalala ndi moyo chifukwa cha matenda, popeza maganizo awo ndi matupi awo anali angwiro. Sanali kuyembekezera kufa monga mmene wina aliyense amachitira kuchokera nthaŵi imeneyo. Ndiponso, sanali anthu ongochita zinthu mosaganiza, koma anali ndi mphatso yapamwamba kwambiri ya ufulu wosankha, nzeru yosankha zoti achite. Komabe, iwo anafunika kumvera malamulo a Mulungu kuti akhalebe ndi ufulu wapamwamba umenewo.
2 Mwachitsanzo, talingalirani malamulo amene chilengedwe chimayendera omwe Mulungu anakhazikitsa. Inde, sikuti malamulo ameneŵa angakhale oti anachita kuwauza, koma Adamu ndi Hava anapangidwa m’njira yakuti aziwatsatira mwachibadwa. Njala inali kuwadziŵitsa kuti afunika kudya; ludzu linawadziŵitsa kuti afunika kumwa madzi; kuloŵa kwa dzuŵa kunawadziŵitsa kuti afunika kugona. Yehova anawapatsanso ntchito yoti azigwira. Ntchito imeneyo tingati inali lamulo chifukwa inali kudzalamulira zochita zawo. Anafunika kubala ana, kulamulira zinthu zamoyo za mitundu yambirimbiri padziko lapansi, ndi kufutukula malire a Paradaiso mpaka atakuta dziko lonse. (Genesis 1:28; 2:15) Limeneli linalitu lamulo labwino ndi lopindulitsa kwambiri! Linawapatsa ntchito yosangalatsa kwambiri, yomwe inawapatsa mwayi wogwiritsa ntchito nzeru zawo zonse m’njira zopindulitsa zedi. Ndiponso, anali aufulu kusankha mmene agwirire ntchito yawoyo. N’chiyaninso china chomwe akanafuna?
3 Zoonadi, pamene Adamu ndi Hava anapatsidwa mwayi wosankha zochita, sizinatanthauze kuti chilichonse chimene akanasankha chikanawakhalira bwino. Ufulu wawo wosankha anayenera kuugwiritsa ntchito mosapitirira malire a malamulo a Mulungu ndi mfundo zake za makhalidwe abwino. Kodi malamulo ndi mfundo zimenezi akanazidziŵa bwanji? Mwa kumvera Mlengi wawo ndiponso mwa kupenda ntchito zake. Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava nzeru zofunika pogwiritsa ntchito zimene anaphunzira. Popeza kuti analengedwa angwiro, mwachibadwa iwo anayenera kukhala ofuna kuonetsa makhalidwe a Mulungu posankha zochita. Indedi, chimene chikanawathandiza kusamala pochita zimenezo ndi kuyamikira kwawo ndi mtima wonse zimene Mulungu anawachitira ndiponso kufuna kwawo kumukondweretsa iyeyo.—Genesis 1:26, 27; Yohane 8:29.
4 Ndiye mpake kuti Mulungu anasankha kuwayesa kuti aone ngati iwo anali odzipereka kwa iye monga Wowapatsa Moyo ndiponso ngati anali kufuna kuchita zinthu mosapitirira malire amene iye anaika. Yehova analamula Adamu kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Hava atalengedwa, iyenso anadziŵitsidwa za lamuloli. (Genesis 3:2, 3) Kodi lamulo limeneli linawalanda ufulu? Ayi. Anali ndi chakudya chabwino cha mitundu yonse ndiponso chochuluka chomwe akanadya popanda kudya chipatso cha mtengo umodzi umenewo. (Genesis 2:8, 9) Linali loyenera ndithu kuti iwo azindikire kuti dziko lapansi n’la Mulungu, chifukwa ndiye analilenga. Motero iye ali ndi ufulu wopanga malamulo ogwirizana ndi cholinga chake ndiponso opindulitsa anthu.—Salmo 24:1, 10.
5 Koma kodi chinachitika n’chiyani? Chifukwa chofuna mpando, mngelo wina anagwiritsa ntchito molakwa ufulu wake wosankha ndipo anakhala Satana, mawu amene amatanthauza kuti “Wotsutsa.” Ananyenga Hava pomulonjeza zinthu zosiyana ndi chifuniro cha Mulungu. (Genesis 3:4, 5) Adamu naye anachitanso zomwe anachita Hava zophwanya lamulo la Mulungu. Mwa kutenga chimene sichinali chawo, iwo anataya ufulu wawo wa ulemerero. Uchimo unayamba kuwalamulira, ndipo monga momwe Mulungu anawachenjezera, iwo anafa pomaliza pake. Choloŵa chimene anasiyira ana awo chinali uchimo, umene umaonekera m’chibadwa chawo chokonda kuchita zolakwa. Chifukwa cha uchimo matupi a anthu anayambanso kufooka kenako kudwala, kukalamba, ndi kufa. Maganizo ofuna kuchita zoipa, amene amakula chifukwa cha mphamvu ya Satana, achititsa kuti mbiri ya anthu ikhale yodzala ndi chidani, upandu, kuponderezana, ndiponso nkhondo zomwe zapha anthu mamiliyoni ambiri. Izi ndi zosiyanatu kwambiri ndi ufulu umene Mulungu anapatsa anthu pachiyambipo!—Deuteronomo 32:4, 5; Yobu 14:1, 2; Aroma 5:12; Chivumbulutso 12:9.
Kumene Ufulu Ungapezeke
6 Poona zinthu zoipa zimene zili ponseponse masiku ano, n’zosadabwitsa kuti anthu amalakalaka atakhala ndi ufulu wochuluka. Koma kodi ufulu weniweni tingaupeze kuti? Yesu anati: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:31, 32) Ufulu umenewu si uja umene anthu amayembekezera pamene akusintha wolamulira posankha wina kapena boma posankha lina. Koma ufulu umenewu umakhudza gwero lake lenileni la mavuto a anthu. Yesu anali kunena za kumasuka ku ukapolo wa uchimo. (Yohane 8:24, 34-36) Choncho, munthu akakhala wophunzira woona wa Yesu Kristu, moyo wake umasintha kwambiri, amapeza ufulu.
7 Izi sizikutanthauza kuti pakali pano Akristu oona savutikanso ndi chibadwa chawo chokonda kuchita tchimo. Popeza analandira uchimo monga choloŵa chawo, amavutikabe chifukwa cha uchimowo. (Aroma 7:21-25) Komabe, ngati munthu akuchitadi zimene Yesu anaphunzitsa, sakhalanso kapolo wa uchimo. Kwa iye uchimo sukhalanso monga wolamulira wopondereza amene amapereka malamulo oti munthuyo azitsatira mosaŵiringula. Sadzaloŵerera m’moyo wotayirira umene ungawononge chikumbumtima chake. Adzakhala ndi chikumbumtima choyera kwa Mulungu pokhala machimo ake akale akhululukidwa chifukwa chokhulupirira nsembe ya Kristu. Maganizo ofuna kuchita tchimo angakhalepo, koma pamene iye akana kuwatsatira chifukwa chokumbukira ziphunzitso zoyera za Kristu, amasonyeza kuti uchimo sukumulamuliranso.—Aroma 6:12-17.
8 Talingalirani ufulu umene tili nawo popeza ndife Akristu. Tamasulidwa ku ziphunzitso zonyenga, ku goli la kukhulupirira zamizimu, ndiponso ku ukapolo wa uchimo. Mfundo za choonadi chapamwamba kwambiri zokhudza mmene akufa alili ndi kuuka kwa akufa zatimasula ku mantha opanda pake a imfa. Kudziŵa kuti posachedwapa Ufumu wolungama wa Mulungu udzaloŵa m’malo mwa maboma a anthu opanda ungwiro kumatimasula kuti tisakhale opanda chiyembekezo. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Komabe, ufulu woterewu si chifukwa choti ife tinyozere akuluakulu a boma ndi malamulo awo.—Tito 3:1, 2; 1 Petro 2:16, 17.
9 Yehova sangotisiyira kuti tiyese tokha njira zosiyanasiyana mpaka titapeza njira yabwino yokhalira moyo ayi. Amadziŵa mmene tinapangidwira. Amadziŵanso zomwe zimatisangalatsadi, ndiponso zomwe tingapindule nazo kosatha. Amazindikira maganizo a munthu ndi khalidwe lake zomwe zingawononge ubwenzi wa munthuyo ndi Mulungu komanso ndi anthu anzake, mwinanso ngakhale kumulepheretsa kukhala m’dziko latsopano. Koma chifukwa chotikonda, Yehova amatiuza zonsezi kudzera m’Baibulo ndi gulu lake looneka. (Marko 13:10; Agalatiya 5:19-23; 1 Timoteo 1:12, 13) Ndiyeno zili kwa ife kugwiritsa ntchito ufulu wathu wosankha umene Mulungu anatipatsa posankha kuti tilabadira bwanji. Mosiyana ndi Adamu, ngati talabadira zimene Baibulo limatiuza, tidzasankha zanzeru. Tidzasonyeza kuti kukhala ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova ndicho chinthu chachikulu pa moyo wathu.
Kufuna Ufulu wa Mtundu Wina
10 Nthaŵi zina achinyamata amene ndi Mboni za Yehova, ngakhalenso ena amene ndi achikulire ndithu, angaganize kuti akufunika ufulu wa mtundu wina. Dzikoli lingaoneke kukhala n’zinthu zopatsa chidwi, ndipo akamaganiza kwambiri za zinthu zimenezo, amayamba kulakalaka kwambiri kuchita zinthu zoipa zotchuka m’dzikoli. Otereŵa sangalingalire zogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa kwambiri, kapenanso kuchita dama. Koma amayamba kugwirizana ndi anthu amene si Akristu oona pofuna kuti aziwaona ngati anzawo. Angayambenso kutengera ngakhale kalankhulidwe ndi khalidwe lawo.—3 Yohane 11.
11 Nthaŵi zina munthu yemwe amanyengerera ena kutengera khalidwe loipa angakhale amene amadzinenera kuti akutumikira Yehova. Zoterezi zinawachitikira Akristu ena oyambirira, ndipo zikhozanso kuchitika masiku ano. Anthu oterowo nthaŵi zambiri amafuna kuchita zimene akuona kuti zidzawakondweretsa, koma zinthuzo zimasemphana ndi malamulo a Mulungu. Amalimbikitsa ena kuti “azisangalala.” ‘Amalonjeza ufulu, pokhala iwo ali akapolo a chivundi.’—2 Petro 2:19.
12 Zimene ambiri amati ndi ufulu zimangodzetsa mavuto nthaŵi zonse, chifukwa ndi kusamvera malamulo a Mulungu. Mwachitsanzo, chiwerewere chingachititse munthu kuvutika maganizo, kudwala, kufa, kukhala ndi mimba ya pathengo, ndiponso banja lake likhoza kutha. (1 Akorinto 6:18; 1 Atesalonika 4:3-8) Kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kungachititse munthu kukhala wamtima wapachala, kulankhula zosamveka bwino, kusaona bwino, kuchita chizungulire, kubanikabanika popuma, kuona zideruderu, ndi kufa kumene. Munthu angakhale chidakwa cha mankhwala osokoneza bongo, ndipo angamachite zaupandu kuti azipeza mankhwalawo. Zofanana ndi zomwezi zimachitikiranso chidakwa cha mowa. (Miyambo 23:29-35) Amene ali ndi khalidwe ngati limeneli angaganize kuti ali ndi ufulu, komano amazindikira mochedwa kuti ali akapolo a uchimo. Tingaonetu kuti uchimo ndi wolamulira wankhanza kwambiri! Kulingalira nkhaniyi tsopanoli kungatiteteze kuti zoterozo zisatichitikire.—Agalatiya 6:7, 8.
Pamene Pamayambira Mavuto
13 Taganizirani pamene mavuto amayambira kaŵirikaŵiri. Baibulo limafotokoza kuti: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimukokera, nichimunyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.” (Yakobo 1:14, 15) Kodi chilakolakochi chimayamba bwanji? Chimayamba ndi zimene zimaloŵa m’maganizo. Kaŵirikaŵiri izi zimachitika chifukwa chogwirizana ndi anthu amene sagwiritsa ntchito mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo. Inde, tonse timadziŵa kuti tiyenera kupewa “mayanjano oipa.” (1 Akorinto 15:33) Koma kodi ndi mayanjano ati amene ali oipa? Kodi nkhaniyi Yehova amaiona motani? Kulingalira mafunso otsatiraŵa ndi kuŵerenga m’Baibulo malemba osonyezedwawo kuyenera kutithandiza kukhala ndi mayankho olondola.
Ngakhale kuti anthu ena amaoneka olemekezeka, kodi iwo angakhale mabwenzi abwino? (Genesis 34:1, 2, 18, 19)
Kodi zokamba zawo, mwina nthabwala zawo, zimasonyeza kuti akhoza kukhala anzathu? (Aefeso 5:3, 4)
Kodi Yehova amamva bwanji ngati tisankha kuyanjana kwambiri ndi anthu amene samukonda? (2 Mbiri 19:1, 2)
Ngakhale kuti tikhoza kugwira ntchito kapena kupita kusukulu limodzi ndi anthu amene sakhulupirira zimene ife timakhulupirira, n’chifukwa chiyani tifunika kukhala ochenjera? (1 Petro 4:3, 4)
Timayanjananso ndi ena mwa kuonerera wailesi yakanema ndi mafilimu, kugwiritsa ntchito Intaneti (njira yotumizirana mauthenga pa kompyuta), ndiponso kuŵerenga mabuku, magazini, ndi nyuzipepala. Pamene tikuchita zimenezi, kodi tiyenera kusamala zinthu ziti? (Miyambo 3:31; Yesaya 8:19; Aefeso 4:17-19)
Kodi Yehova timamuuza kuti ndife anthu otani ndi mabwenzi amene timasankha? (Salmo 26:1, 4, 5; 97:10)
14 Patsogolo pathu pompa pali dziko latsopano la Mulungu. Boma la kumwamba la Ufumu wa Mulungu lidzamasula anthu ku mphamvu ya Satana ndi dziko lake lonse loipali. Mavuto onse obwera chifukwa cha uchimo adzachotsedwa mwapang’onopang’ono pa anthu omvera, ndipo tidzakhala ndi maganizo angwiro ndi matupi angwiro kotero kuti tidzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Pamapeto pake chilengedwe chonse chidzakhala ndi ufulu umene uli wogwirizana kwambiri ndi ‘mzimu wa Ambuye.’ (2 Akorinto 3:17) Kodi zingakhale zomveka kuti munthu ataye zonse zimenezi chifukwa chosamvera uphungu wa m’Mawu a Mulungu tsopano lino? Mwa kugwiritsa ntchito mwanzeru ufulu wathu wachikristu lerolino, tonse tionetsetu kuti chomwe timafuna kwenikweni ndi “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.
Bwerezani Zomwe Mwakambirana
• Kodi anthu aŵiri oyambirira anali ndi ufulu wotani? Kodi zimenezo tingaziyerekeze motani ndi zimene anthu akukumana nazo lerolino?
• Kodi Akristu oona ali ndi ufulu wotani? Kodi ufulu umenewu umasiyana motani ndi ufulu umene dzikoli limati ndiwo ufulu?
• N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kupeŵa mayanjano oipa? Kodi ife, kusiyana ndi Adamu, timamvera ndani amene ndi udindo wake kutiuza kuti choipa ndi ichi?
[Mafunso]
1, 2. (a) Kodi ndi ufulu wotani umene Mulungu anapatsa anthu aŵiri oyambirira? (b) Tchulani ena mwa malamulo amene anali kulamulira zochita za Adamu ndi Hava.
3. Kodi Adamu ndi Hava akanaphunzira motani kugwiritsa ntchito mwanzeru ufulu wawo wosankha?
4. (a) Kodi lamulo limene Adamu ndi Hava anapatsidwa lakuti asadye chipatso cha mtengo umodzi linawalanda ufulu? (b) N’chifukwa chiyani lamuloli linali loyenera?
5. (a) Kodi Adamu ndi Hava anataya motani ufulu waulemerero umene anali nawo? (b) Kodi n’chiyani chomwe chinaloŵa m’malo mwa ufulu umene Adamu ndi Hava anali nawo, nanga zimenezi zatikhudza motani?
6. (a) Kodi ufulu weniweni tingaupeze kuti? (b) Kodi Yesu analankhula za ufulu wotani?
7. (a) Kodi ndi motani mmene timamasukira ku uchimo panopo? (b) Kodi tiyenera kuchitanji kuti tikhale ndi ufulu umenewo?
8. (a) Kodi Chikristu choona chimatipatsa ufulu wotani? (b) Kodi olamulira a dzikoli tiyenera kuwaona motani?
9. (a) Kodi Yehova potikonda amatithandiza bwanji kukhala ndi ufulu wapamwamba kwambiri womwe anthu angathe kukhala nawo masiku ano? (b) Kuti tisankhe zanzeru, tifunika kuchita chiyani?
10. Kodi ena amene ndi Mboni za Yehova afuna ufulu wotani?
11. Kodi nthaŵi zina ndani amanyengerera ena kuchita zoipa?
12. Kodi khalidwe losemphana ndi malamulo a Mulungu ndiponso mfundo zake za makhalidwe abwino limakhala ndi mavuto otani?
13. (a) Kodi kaŵirikaŵiri zilakolako zimene zimabweretsa mavuto zimayamba bwanji? (b) Kuti tizindikire kuti aŵa ndi “mayanjano oipa,” kodi tifunikira maganizo a ndani? (c) Pamene mukuyankha mafunso amene ali m’ndime 13, tsindikani amene ali maganizo a Yehova.
14. Kodi anthu amene panopo akugwiritsa ntchito mokhulupirika uphungu wa m’Mawu a Mulungu adzakhala ndi ufulu wotani wapamwamba m’tsogolo muno?
[Zithunzi patsamba 46]
Mawu a Mulungu amachenjeza kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma”