-
Mdani Wathu Womalizira AdzawonongedwaNsanja ya Olonda—2014 | September 15
-
-
3, 4. (a) Kodi Mulungu anapereka lamulo liti kwa Adamu ndi Hava? (b) N’chifukwa chiyani iwo anayenera kumvera lamulolo?
3 Ngakhale kuti Adamu ndi Hava akanakhala ndi moyo wosatha, sikuti anali ndi moyo wosakhoza kufa. Iwo anayenera kupuma, kumwa, kugona ndiponso kudya kuti apitirize kukhala ndi moyo. Koma chofunika kwambiri kuti akhalebe ndi moyo chinali kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Deut. 8:3) Anayenera kutsatira malangizo ake kuti asafe komanso kuti azisangalala. Mulungu anaonetsetsa kuti Adamu adziwe zimenezi Hava asanalengedwe. Kodi anachita bwanji zimenezi? Baibulo limanena kuti: “Yehova Mulungu anapatsa munthuyo lamulo lakuti: ‘Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.’”—Gen. 2:16, 17.
4 “Mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa” unkasonyeza kuti Mulungu ndi amene ali ndi udindo wonena kuti ichi ndi chabwino, ichi ndi choipa. N’zoona kuti Adamu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu komanso anali ndi chikumbumtima choncho akanatha kudziwa kuti izi ndi zabwino, izi ndi zoipa. Koma mtengowu unkasonyeza kuti nthawi zonse Adamu ndi Hava ankafunika kutsatira malangizo a Mulungu. Kudya zipatso za mtengowu kukanasonyeza kuti anthuwo sakufuna kuti Mulungu aziwalamulira. Kuchita zimenezi kukanabweretsa mavuto aakulu kwambiri kwa iwowo ndiponso ana awo ndipo malinga ndi zimene Mulungu anawachenjeza, akanafa.
-
-
Mdani Wathu Womalizira AdzawonongedwaNsanja ya Olonda—2014 | September 15
-
-
7 Mulungu anali atauza Adamu kuti: “Tsiku limene udzadya [zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa], udzafa ndithu.” N’kutheka kuti Adamu ankaganiza kuti ‘tsikulo’ linali tsiku lenileni la maola 24. Atadya chipatso choletsedwacho, mwina ankaganiza kuti Yehova adzapereka chilangocho tsiku lomwelo dzuwa lisanalowe. Ndiyeno Yehova analankhula nawo madzulo ake kapena kuti “nthawi ya kamphepo kayeziyezi.” (Gen. 3:8) Iye anayamba kuwafunsa mafunso ngati ali m’khoti kuti adziwe bwinobwino maganizo awo. (Gen. 3:9-13) Kenako Mulungu anapereka chiweruzo choti adzafadi. (Gen. 3:14-19) Koma ngati Mulungu akanawawononga nthawi yomweyo, cholinga chake chokhudza ana a Adamu ndi Hava sichikanakwaniritsidwa. (Yes. 55:11) Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anayamba nthawi yomweyo kuvutika chifukwa cha uchimowo, Mulungu anawalola kubereka ana omwe anali ndi mwayi wodzalandira madalitso. Choncho pa tsiku lenilenilo limene anachimwa, zinali ngati Adamu ndi Hava anafa pa maso pa Mulungu. Komanso tinganene kuti anafadi pa tsikulo chifukwa anamwalira pasanathe “tsiku” limodzi la zaka 1,000.—2 Pet. 3:8.
-