-
Tingaphunzire ku Banja Loyamba la AnthuNsanja ya Olonda—2000 | November 15
-
-
MULUNGU analiyang’ana Dziko Lapansi. Anali kulikonza kuti anthu akhalemo. Iye anaona kuti chilichonse chimene anali kupanga chinali chabwino. Inde, pamene ntchito imeneyi inatha, iye ananena kuti inali ‘yabwino ndithu.’ (Genesis 1:12, 18, 21, 25, 31) Komabe, asanamalize kwenikweni, Mulungu ananena za chinthu chinachake chimene sichinali ‘bwino.’ Inde, Mulungu sanapange chinachake chosakhala bwino. Kungoti chabe anali asanamalize kulenga. “Si kwabwino kuti munthu akhale yekha,” anatero Yehova. “Ndidzam’pangira wom’thangatira iye.”—Genesis 2:18.
-
-
Tingaphunzire ku Banja Loyamba la AnthuNsanja ya Olonda—2000 | November 15
-
-
Mwamuna anafunika “wom’thangatira.” Anali naye tsopano amene anali woyenereradi. Hava anali woyenera bwino ndithu kukhala wom’kwaniritsa Adamu—posamalira munda wa mudzi wawo ndi nyama, pobala ana, ndiponso monga bwenzi lenileni lom’thandiza kuganiza mwanzeru ndi kum’chirikiza.—Genesis 1:26-30.
-