-
Kodi Moyo Unayamba Bwanji?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
1. Kodi zinthu zam’chilengedwechi zinakhalako bwanji?
Baibulo limanena kuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Asayansi ambiri amavomereza kuti zinthu zam’chilengedwechi zili ndi chiyambi. Kodi Mulungu anazilenga bwanji? Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera, womwe ndi “mphamvu ya Mulungu” yogwira ntchito, kuti alenge zinthu zonse m’chilengedwechi, kuphatikizapo milalang’amba, nyenyezi ndi mapulaneti.—Genesis 1:2.
-
-
Kodi Moyo Unayamba Bwanji?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
5. Nkhani ya m’Baibulo yokhudza kulengedwa kwa zinthu ndi yoona
Mu Genesis chaputala 1, Baibulo limafotokoza mmene dziko lapansi komanso zinthu zamoyo zinayambira. Kodi inuyo mumakhulupirira nkhani imeneyi, kapena mumaona kuti ndi yongopeka? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti dziko lapansi ndiponso zamoyo zonse zinalengedwa m’masiku 6 a maola 24?
Kodi inuyo mumaona kuti nkhani ya m’Baibulo yokhudza kulengedwa kwa zinthu ndi yomveka komanso yoona? N’chifukwa chiyani mukutero?
Werengani Genesis 1:1, kenako mukambirane funso ili:
Asayansi amanena kuti chilengedwechi chili ndi chiyambi. Kodi zimene amanenazi zikugwirizana bwanji ndi zimene mwawerenga m’Baibulo?
Anthu ena amaganiza kuti polenga zinthu, Mulungu anangochititsa kuti zisinthe kuchokera ku zinthu zina. Werengani Genesis 1:21, 25, 27, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu anapanga zinthu zing’onozing’ono zomwe zinasintha n’kukhala nsomba, zinyama ndiponso anthu? Kapena kodi analenga zamoyo za “mitundu” yosiyanasiyana?b
-