-
Ziyembekezo Zazikulu za Anthu M’paradaiso ya ChisangalaloNsanja ya Olonda—1989 | August 1
-
-
2 “Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m’thengo, ndi mbalame zonse za m’mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti awone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina awo. Adamu ndipo anazitcha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m’mlengalenga ndi zamoyo zonse za m’thengo.”—Genesis 2:19, 20.
3. Nchifukwa ninji panalibe mantha kumbali ya Adamu ndi zolengedwa za nyama?
3 Mwamunayo anatcha kavalo sus, bulu shohr, nkhosa seh, mbuzi ʽez, mbalame ʽohph, njiwa yoh·nahʹ, mbalame ya chitsukwa chachitali yamawangamawanga tuk·kiʹ, mkango ʼar·yehʹ kapena ʼariʹ, kasenye dov, nyani qohph, galu keʹlev, njoka na·chashʹ, ndi kupitirizabe.a Pamene iye anapita ku mtsinje womwe madzi ankayenda kutuluka m’munda wa Edene, iye anawona nsomba. Ku nsomba iye anapatsa dzina lakuti da·gahʹ. Mwamuna wopanda chidayo sanadzimve wamantha ndi zinyama zimenezi, zam’mudzi ndi zakuthengo, kapena ndi mbalame, ndipo sizinamve mantha ndi iye, amene zinamzindikira mwachibadwa kukhala wokulira pa izo, wa mtundu wapamwamba wa moyo. Izo zinali zolengedwa za Mulungu, zopatsidwa mphatso ya moyo ndi Iye, ndipo mwamunayo analibe chikhumbo kapena chikhoterero cha kuzivulaza izo kapena kuchotsa moyo wawo.
4. Nchiyani chomwe tingaganizire ponena za kutcha maina kochitidwa ndi Adamu kwa nyama zonse ndi mbalame, ndipo ndi mtundu wotani wa chokumana nacho umene chimenechi chinali?
4 Ponena za kaya ndi utali wotani umene munthu anasonyezedwa nyama za m’mudzi ndi zakuthengo ndi zolengedwa zowuluka m’mlengalenga, cholemberacho sichimatiuza ife. Zonsezo zinali pansi pa chitsogozo ndi kakonzedwe kaumulungu. Adamu mwachidziŵikire anatenga nthaŵi kuphunzira nyama iriyonse yosiyana, kuwona zizoloŵezi zake zapadera ndi kapangidwe; kenaka iye akakhoza kusankha dzina lomwe likakhala loyenera mwapadera kaamba ka iyo. Ichi chikatanthauza kupita kwa unyinji wolingalirika wa nthaŵi. Chinali chokumana nacho chosangalatsa kwenikweni kwa Adamu mwakutero kukhala wozoloŵerana ndi moyo wa zolengedwa za dziko lapansi limeneli mu mtundu wake wochulukira, ndipo chinaitanira kaamba ka kuthekera kokulira kwa maganizo ndi mphamvu za kulankhula kwa iye kuti asiyanitse uliwonse wa mitundu imeneyi ya zolengedwa za moyo ndi dzina loyenerera.
-
-
Ziyembekezo Zazikulu za Anthu M’paradaiso ya ChisangalaloNsanja ya Olonda—1989 | August 1
-
-
7 Ponena za cholembera chosangalatsa cha chilengedwe chimenecho, Adamu akakhoza kukhala woyamikira kwenikweni. Icho chinalongosola zinthu zambiri. Kuchokera m’njira imene ichi chinalembedwera, iye anamvetsetsa kuti panali nyengo zitatu zazitali za nthaŵi zimene Mulungu anatcha masiku mogwirizana ndi njira Yake ya kuyesera nthaŵi, nyengo yachinayi yolenga isadakhale mu imene Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziŵiri kuwonekera m’thambo la miyamba kuzindikiritsa tsiku lofupikirako la maora 24 la munthu. Tsiku lofupikirako limeneli la munthu pa dziko lapansi linali nthaŵi kuchokera pa kuzimiririka kwa chowunikira chachikulu kufika pa kutuluka kwake kotsatira. Adamu anadziŵanso kuti panafunikira kukhala zaka za nthaŵi kaamba ka iye, ndipo iye mosakaikira anayamba mwamsanga kuŵerenga zaka zake za moyo. Chowunikira chachikulu m’thambo la miyamba chikamtheketsa iye kuchita chimenechi. Koma ponena za masiku otalikirako a Mulungu a chilengedwe, mwamuna woyambayo anazindikira kuti iye panthaŵiyo anali kukhala ndi moyo m’tsiku lachisanu ndi chimodzi la ntchito yolenga dziko lapansi ya Mulungu. Palibe mapeto omwe anali atatchulidwa kwa iye onena za tsiku lachisanu ndi chimodzi limenelo kaamba ka kulenga nyama za pa mtunda zonsezo ndipo kenaka kaamba ka kulenga mwamuna mosiyana. Tsopano iye akakhoza kumvetsetsa dongosolo la kulenga moyo wa zomera, moyo wa za m’nyanja, moyo wa mbalame, ndi nyama za pa mtunda. Koma pokhala yekha m’munda wa Edene, Adamu sanali kulongosola kokwanira, kwathunthu kwa chifuno chachikondi cha Mulungu kaamba ka munthu m’Paradaiso yake ya pa dziko lapansi.
Kulenga Mkazi Woyamba wa Munthu
8, 9. (a) Nchiyani chimene mwamuna wangwiro anawona ponena za chilengedwe cha nyama, koma nchiyani chomwe iye anamaliza ponena za iyemwini? (b) Nchifukwa ninji chinali choyenerera kuti munthu wangwiro sanafunse Mulungu kaamba ka mnzake? (c) Ndimotani mmene cholembera cha Baibulo chimalongosolera kulengedwa kwa mkazi woyambirira waumunthu?
8 Mwamuna woyambayo, wokhala ndi maganizo ake angwiro ndi mphamvu za kuyang’ana, anawona kuti mu ufumu wa mbalame ndi nyama, panali yaimuna ndi yaikazi ndipo kuti pakati pawo zinabala mitundu yawo. Koma ponena za munthu iyemwini, sizinali tero. Ngati kawonedweka kanakhotetsa iye kukhala ndi lingaliro la kusangalala ndi bwenzi, iye sanapeze mnzake woyenerera pakati pa ufumu wa nyama uliwonse, osati ngakhale pakati pa anyani. Adamu akakhoza kumaliza kuti panalibe mnzake chifukwa chakuti ngati panali mmodzi, kodi Mulungu sakanambweretsa mnzake ameneyo kwa iye? Mwamuna anali atalengedwa mosiyana ndi mitundu ya nyama yonseyo, ndipo iye anatanthauzidwa kukhala wosiyana! Iye sanakhoterere kugamulapo nkhani kaamba ka iyemwini ndi kukhala wopulupudza ndi kufunsa Mulungu Mlengi wake kaamba ka mnzake. Chinali cholondola kuti mwamuna wangwiro alekere nkhani yonseyo mwa Mulungu, popeza kuti mwamsanga pambuyo pake iye anapeza kuti Mulungu anali atapanga malekezero a Iyemwini ponena za mkhalidwewo. Ponena za ichi ndi chimene tsopano chinachitika, cholemberacho chikutiwuza kuti:
9 “Koma kwa Adamu sanapezedwa womthangatira iye. Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikuru, ndipo anagona: ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake: ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu. Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzatchedwa Mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna. Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi. Onse aŵiri ndipo anali amaliseche, mwamuna ndi mkazi wake, ndipo analibe manyazi.”—Genesis 2:20-25.
-