Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?
    Nsanja ya Olonda—2007 | September 15
    • Baibulo limatiuza zimene zinachitika. Polankhula kudzera mwa njoka, Satana Mdyerekezi anafunsa Hava kuti: “Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Hava atauza Satana zimene Mulungu analamula, Satana anati: “Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” Ndipo Hava ataona kuti mtengowo unali wokoma m’maso, “anatenga zipatso zake, nadya.” Nkhaniyo imapitiriza kuti mkaziyo ‘anapatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso.’ (Genesis 3:1-6) Choncho, Adamu ndi Hava anagwiritsa ntchito molakwika ufulu wawo wosankha zochita ndipo anachimwa chifukwa sanamvere Mulungu.

      Kodi mukuona kuopsa kwa zimene zinachitikazi? Mdyerekezi anatsutsa zimene Mulungu anauza Adamu. Satana anasonyeza kuti Adamu ndi Hava sanafunikire kudalira Yehova pankhani yosankha chabwino ndi choipa. Mwa kutero, Satana anayambitsa kukayikira zoti Yehova ali ndi ufulu wolamulira anthu. Choncho, nkhani yaikulu imene Satana anayambitsa inali yakuti, Yehova si woyenera kulamulira anthu. Kodi Mulungu woonayo anatani kuti athetse nkhani imeneyi?

  • N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?
    Nsanja ya Olonda—2007 | September 15
    • Papita zaka pafupifupi 6,000 kuchokera pamene Satana anatsutsa zoti Mulungu ali ndi ufulu wolamulira anthu. Kodi nthawi imeneyi yasonyeza chiyani? Taganizirani zinthu ziwiri zimene Satana ananena potsutsa Mulungu. Satana anauza Hava mopanda mantha kuti: “Kufa simudzafai.” (Genesis 3:4) Ponena kuti Adamu ndi Hava saafa akadya zipatso zoletsedwa, kwenikweni Satana ankanena kuti Yehova ndi wabodza. Imeneyi inali nkhani yaikulu kwabasi! Ngati Mulungu ananamadi, kodi tingam’khulupirire bwanji pa zinthu zina zonse? Komano kodi nthawi yonse imene yadutsayi yasonyeza chiyani?

      M’kupita kwa nthawi, Adamu ndi Hava anayamba kudwala, kuvutika, kukalamba ndipo anafa. Baibulo limati: “Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anayi, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira.” (Genesis 3:19; 5:5) Ndipo Adamu anapatsira anthu onse mavuto amenewa. (Aroma 5:12) Nthawi yonseyi yatsimikizira kuti Satana ndi “wabodza komanso tate wake wa bodza” ndiponso kuti Yehova ndi “Mulungu wa choonadi.”​—Yohane 8:44; Salmo 31:5.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena