Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?
    Nsanja ya Olonda—2007 | September 15
    • Baibulo limatiuza zimene zinachitika. Polankhula kudzera mwa njoka, Satana Mdyerekezi anafunsa Hava kuti: “Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Hava atauza Satana zimene Mulungu analamula, Satana anati: “Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” Ndipo Hava ataona kuti mtengowo unali wokoma m’maso, “anatenga zipatso zake, nadya.” Nkhaniyo imapitiriza kuti mkaziyo ‘anapatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso.’ (Genesis 3:1-6) Choncho, Adamu ndi Hava anagwiritsa ntchito molakwika ufulu wawo wosankha zochita ndipo anachimwa chifukwa sanamvere Mulungu.

      Kodi mukuona kuopsa kwa zimene zinachitikazi? Mdyerekezi anatsutsa zimene Mulungu anauza Adamu. Satana anasonyeza kuti Adamu ndi Hava sanafunikire kudalira Yehova pankhani yosankha chabwino ndi choipa. Mwa kutero, Satana anayambitsa kukayikira zoti Yehova ali ndi ufulu wolamulira anthu. Choncho, nkhani yaikulu imene Satana anayambitsa inali yakuti, Yehova si woyenera kulamulira anthu. Kodi Mulungu woonayo anatani kuti athetse nkhani imeneyi?

  • N’chifukwa Chiyani Zoipa Zikupitirirabe?
    Nsanja ya Olonda—2007 | September 15
    • Satana anauzanso Hava kuti: “Adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya [mtengo woletsedwawo], adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:5) Ndi mawu aukathyali amenewo, Satana ananyengerera anthu kuti atha kudzilamulira okha. Pofuna kuwasocheretsa, Satana anachititsa anthu kuganiza kuti zinthu zingawayendere bwino popanda kudalira Mulungu. Kodi nthawi imene yadutsayi yasonyeza kuti zimenezi n’zoona?

      Kuyambira kalekale, maufumu ambiri akhala akubwera ndi kupita. Anthu ayesera mitundu yosiyanasiyana ya maboma. Koma panthawi yonseyi, anthu akhala akukumana ndi zinthu zoipa. Zaka pafupifupi 3,000 zapitazo wolemba Baibulo wina ananena mwanzeru kuti: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Mneneri Yeremiya nayenso analemba kuti: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Mawu amenewa ndi olondolabe ngakhale kuti sayansi ndi luso la zopangapanga zapita patsogolo kwambiri masiku ano. Kupita kwa nthawi kwangotsimikizira kuti zimenezi ndi zoona.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena