Posachedwapa—Dziko Lopanda Zopweteka!
DZIKO lopanda zopweteka kudza posachepa? Imeneyo ingakhale nkhani yabwino chotani nanga kwa odwala matenda osachiritsika—kaya akudwala kuthupi, maganizo, kapena malingaliro! Mwachitsanzo, mamiliyoni akasangalala koposa atamva za kuchotsedwa kwa zopweteka zazikulu zakuthupi zochititsidwa ndi mitundu ina ya khensa, nthenda yachisoma, ndi yamtima. Odwala matenda oopsa a maganizo angasangalale kuchotseredwa mavuto awo osaneneka. Ndipo mamiliyoni ena angasangalale ngati zopweteka zawo za malingaliro zochititsidwa ndi mavuto onga mantha, chisoni, liwongo, nkhaŵa, ndi kugwiritsidwa mwala zithetsedwa. Koma kodi tifunadi kuwona mapeto a zopweteka zonsezi?
“Kusamva kupweteka kulikonse ndiko ngozi,” akutero katswiri wa mpangidwe wa thupi Allan Basbaum wa pa Yunivesite ya California ku San Francisco. Anali ndi chifukwa chabwino chonenera motero. Monga dongosolo lochenjezera, kupweteka kwakuthupi kumatidziŵitsa kuti chinachake chovulaza chikuchitika.
Kusakhoza kumva kupweteka kwakuthupi kungakhaledi kwangozi. Izi zikufotokozedwa mwafanizo m’lipoti la magazini a Time lakuti: “Kumwetulira kosangalatsa kwa mnyamata wa zaka khumi ndi ziŵiri zakubadwa kumapanga kusiyana kotheratu ndi mawonekedwe ake ochititsa chisoni. Mikono yake ndi miyendo njopunduka ndi yokhota, monga ngati anadwala mazukumira. Zala zingapo zinaduka. Ali ndi chironda chachikulu chotseguka pabondo lina, ndipo miromo yomwetulirayo njazironda kaamba koziluma. Amawoneka kukhala mwana wochitiridwa nkhanza . . . Iye anabadwa ndi ulema waukulu wamajini womwe umampangitsa kusamva kupweteka. Zala zake zinaphwanyidwa kapena kutenthedwa chifukwa chakuti sanachotse manja ake pazinthu zotentha kapena zaupandu. Mafupa ake ndi mfundo zinachoka m’malo ake kaamba ka kuzimenyetsa mwamphamvu kopambanitsa pamene ankayenda kapena kuthamanga. Mawondo ake anachita zironda kaamba kokwaŵa pazinthu zakuthwa zimene sanakhoze kuzimva. Akathyoka fupa kapena kuguluka fupa lansukunyu, sakamva ululu wokwanira kuti nkulira kotero kuti amvedwe ndi kuthandizidwa.”
Anthu ena amafulumira kupatsa Mulungu mlandu kaamba ka matenda otero ndi masoka amene mamiliyoni ambiri amakumana nawo. Komabe, kodi tingapatse Mulungu mlandu moyenerera kaamba ka kuvutika kowawitsa kwa mtundu wa anthu?
Kodi Tiyenera Kupatsa Mulungu Mlandu?
Kwazaka zokwanira 6,000 tsopano, anthu akhala mu ukapolo wazopweteka zakuthupi, zamaganizo, ndi zamalingaliro. Kwenikweni, zaka mazana 19 zapitazo, mtumwi Wachikrsitu Paulo molondola anati: “Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.” (Aroma 8:22) Mosasamala kanthu za mibulu yakupha ululu yambirimbiri yopezedwa m’nyumba zamankhwala ndi zoyesayesa za asing’anga ndi akatswiri a nthenda zamaganizo, ukapolo wofalikira wazopweteka zamitundumitundu ukupitirizabe. Eya, ena atukwana Mulungu chifukwa cha kuvutuka kwawo, monga momwedi mkazi wa mwamuna wotchedwa Yobu anamsonkhezerera kuchita zaka mazana ambiri zapitazo! Komabe, monga momwe iye mwini anazindikirira, mzimu woterowo ndiwo kupusa ndi wosayenera.—Yobu 2:9, 10.
Mulungu sangapatsidwe mlandu moyenerera kaamba ka ukapolo wazopweteka wamakonowu wa anthu. Mmalo mwake, liwongo liri pa wonama wosawonekayo ndi makolo athu oyambirira. Motani?
Malemba akusonyeza kuti ngakhale chinali cholungama poyambirira, cholengedwa chauzimu chinachita umbombo wokhumba ulamuliro ndi kutchuka. Kuchiyambiyambi kwa anthu padziko lapansi, icho chinawoneratu fuko la anthu pa dziko lapansi laparadaiso, onse akudzipereka kotheratu kwa Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova. Mosonkhezeredwa ndi mtima umene unafikira kukhala wanjiru, cholengedwa chauzimu chimenechi chinapandukira Mlengi, chikumafuna kulambira kwa munthu ndi kudzipereka kupita kwa icho. Zolinga zake zoipa zinawonekera pamene chinanena bodza lamkunkhuniza. Limene pambuyo pake, linabweretsa uchimo m’dziko.
Yehova Mulungu adauza mwamuna woyamba, Adamu, kuti kudya chipatso cha mtengo wa kudziŵitsa zabwino ndi zoipa kukamdzetsera imfa. (Genesis 2:15-17) Koma mkazi wa Adamu, Hava, adanyengedwa kusamvera. Mogwiritsira ntchito njoka monga cholankhulira, Wonyengayo wauzimu anauza mkaziyo kuti: “Kufa simudzafai; chifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu [a Hava ndi a mwamuna wake], ndipo [aŵirinu] mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:1-5) Limenelo linali bodza loyamba, ndipo linadziŵikitsa cholengedwa chauzimu chimenechi kukhala ‘atate wa mabodza.’ (Yohane 8:44) Kugwiritsira ntchito kwake njoka pachochitikacho m’munda wa Edene kumayenerana ndi kuzindikiritsidwa kwake Kwam’malemba kukhala “njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.”—Chivumbulutso 12:9.
Uchimo unabweretsa kuusa moyo ndi ukapolo pa anthu. Mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, patsiku lenilenilo la kuchimwa kwa Adamu, Mulungu anapereka chiweruzo cha imfa pa ochimwawo. Mwachiweruzo, m’lingaliro la Yehova, Adamu ndi Hava adafa tsiku lomwelo. (Yerekezerani ndi Luka 20:37, 38.) Mu Edene, Yehova anauza mkazi woyamba amene panthaŵiyo anali wochimwa kuti: “Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala.” (Genesis 3:16) Adamu akayamba kukhala ndi moyo wamavuto kunja kwa munda wa Edene m’malo a dziko lapansi osiyana kutalitali ndi mkhalidwe wauparadaiso. Yehova adati: “M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m’menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:17-19) Ndimo mmene ukapolo wazopweteka unayambira pafuko la anthu.
Pamenepa, ukapolo wazopweteka ukugwirizanitsidwa ndi kupanda ungwiro, uchimo, ndi imfa zacholoŵa kuchokera kwa Adamu. Monga mmene mtumwi Paulo akunena kuti: “Chifukwa chake, monga uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Komabe Mawu a Mulungu amatithandiza kupirira zopweteka, popeza amatiuza chifukwa chake Yehova wazilolera ndipo akutitsimikizira kuti posachedwapa zidzatha. Mulungu analola ‘atate wa mabodza’ wonga njokayo, Satana Mdyerekezi, kuvutitsa Yobu wolungamayo kuti ayese umphumphu wake. Mtutso wa Mdyerekezi unali wakuti Yobu anatumikira Mulungu chifukwa cha dyera, sichikondi ayi. (Yobu 1:8-12) Koma Yobu anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu, kutsimikizira kuti anthu opanda ungwiro angamtumikire Iye chifukwa cha chikondi ndikuti angachirikize ufumu Wake mosasamala kanthu za ziyeso zadzaoneni za chikhulupiriro chawo. Chipiriro cha Yobu monga wosunga umphumphu chinathandizira kulemekezedwa kwa dzina la Yehova, chinatsimikizira Satana kukhala wonama, ndipo chinabweretsa mphotho zolemerera kwa khololo lopereka chitsanzo chabwino. (Yobu 42:12-17; Yakobo 5:11) Kuchokera ku chokumana nacho cha Yobu, tinganene kuti pamene chifuniro cha Mulungu chidzakhala chitachitidwa, ukapolo wa anthu ku zopweteka udzatha. Koma kodi tingatsimikizire motani za chimenecho?
Mmene Zopweteka Zidzathera
Kwenikweni, Yehova wapereka njira yogwira mtima kotheratu yothetsera ukapolo wazopweteka wa anthu. Iye wachita chimenechi pamaziko a nsembe yadipo ya Mwana wake, Yesu Kristu. Yesu ali “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!” (Yohane 1:29) Iye sanadze kudziko lapansi, “kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake [moyo wake wangwiro waumunthu] dipo la ambiri.” (Mateyu 20:28) Mwa kusamvera kwake, Adamu anataya moyo wangwiro waumunthu, ndi zoyenerera zake zonse ndi ziyembekezo. Ndipo zimenezo ndizo zimenedi zikuwomboledwa ndi nsembe yadipo ya Yesu. (1 Timoteo 2:5, 6; Ahebri 7:26) Ndithudi, “Mulungu anakonda dziko lapansi [la mtundu wa anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Mulungu walonjezanso mwachindunji kuti ukapolo wazopweteka udzatha. Akumaneneratu za nthaŵi pamene zopweteka zogwirizanitsidwa ndi uchimo zidzachotsedwa, mtumwi Wachikristu Yohane anauziridwa ndi Mulungu kulemba kuti:
“Ndipo ndinawona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja . . . ndinamva mawu aakulu ochokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. Ndipo iye [Yehova Mulungu] wakukhala pampando wachifumu anati, Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi owona.”—Chivumbulutso 21:1-5.
Anthu omvera posachedwapa adzalandira phindu lokwanira la nsembe yadipo ya Yesu. Izi zidzachitika pansi pa kulamulira kwa Ufumu umene olungama mtima akhala akuwupempherera kwanthaŵi yaitali, kumati: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Mu Ufumu wakumwamba, Yesu Kristu adzalamulira kufikira ataika adani ake onse pansi pa mapazi ake, kuphatikizapo ukapolo wazopweteka ndi mdani womalizira, imfa.—1 Akorinto 15:25, 26.
Inde, ponena za anthu omvera, posachedwapa Mulungu ‘adzawapukutira misozi yonse, ndipo sipadzakhalanso imfa, maliro, kulira kapena zopweteka zirizonse.’ (Chivumbulutso 21:4) Pamenepo mawu a ulosi otsatiraŵa amene tsopano ali ndi tanthauzo lauzimu adzakwaniritsidwa m’chenicheni: “Lemekeza Yehova, moyo wanga; . . . amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse.” “Wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.”—Salmo 103:1-3; Yesaya 33:24.
Mapeto a Zopweteka, Liti?
Mapeto a ukapolo wazopweteka ayandikira. Inde, adzachitika m’tsiku lathu, ndipo mbadwo womwe uno udzawawona. Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo kukusonyeza kuti tikukhala chakotsirizira kwa dongosolo la zinthu loipa iri. Nkhondo zosayerekezereka, njala, ndi zivomezi, limodzinso ndi kulalikidwa kwa mbiri yabwino kuzungulira padziko lonse lapansi kochitidwa ndi Mboni za Yehova, ziri mbali ya chiungwe cha “chizindikiro” cha ‘kukhalapo’ kosawoneka kwa Yesu muulemerero wa Ufumu wakumwamba.—Mateyu 24:3-14, 21, 34.
Posachedwapa, “m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba,” dongosolo la zinthu lolinganizidwa la Satana Mdyerekezi limodzi ndi mpangidwe wake wamaboma, zidzapita. “Nyanja” yoŵinduka ya anthu oipa idzachoka. Motero tikuima pamphembenu pa “miyamba yatsopano” ya boma lodalitsidwa ndi Mulungu pa “dziko latsopano,” chitaganya cha anthu olungama. Mwa amenewa “mukhalitsa chilungamo.”—Chivumbulutso 21:1; 2 Petro 3:13.
Ndi madalitso oterowo pansi pa boma latsopano—Ufumu wa Mulungu—oyandikira motero, limbikani. Funafunani chidziŵitso chowonjezereka cha dziko latsopano lopanda zopweteka ndi imfa. Ndithudi, yang’anani kutsogolo kutsiku lodalitsika limene tsopano liri pafupi pamene onse okonda ndi kumvera Yehova Mulungu adzakhala m’dziko lopanda zopweteka.