-
Kodi Dzikoli Lidzatha Bwanji?Nsanja ya Olonda—2012 | September 15
-
-
15. Kodi n’chiyani chidzachitikire Satana ndi ziwanda zake Aramagedo ikadzatha?
15 Choyamba, Satana adzaona dziko lakeli likuwonongedwa mpaka kutheratu. Kenako idzafika nthawi yoti nayenso aone zokhoma. Mtumwi Yohane anafotokoza zimene zidzachitike. (Werengani Chivumbulutso 20:1-3.) Yesu Khristu, yemwe ndi “mngelo” wokhala ndi “kiyi wa paphompho,” adzagwira Satana ndi ziwanda zake n’kuwaponya m’phompho kuti akhale m’menemo zaka 1,000. (Luka 8:30, 31; 1 Yoh. 3:8) Ichi chidzakhala chiyambi cha kuphwanya mutu wa njoka.d—Gen. 3:15.
-
-
Kodi Dzikoli Lidzatha Bwanji?Nsanja ya Olonda—2012 | September 15
-
-
d Adzamalizitsa kuphwanya mutu wa njoka zikadzatha zaka 1,000 zimenezi. Pa nthawiyi, Satana ndi ziwanda zake adzaponyedwa “m’nyanja yamoto ndi sulufule.”—Chiv. 20:7-10; Mat. 25:41.
-