Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Udindo Wapadera wa Yesu Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2008 | December 15
    • “Mbewu” Yolonjezedwa

      18. Kodi ndi ulosi uti umene unanenedwa Adamu atachimwa, ndipo ndi zinthu ziti zokhudza ulosiwo zimene zinavumbulidwa pambuyo pake?

      18 Anthu atachimwa mu Edeni, zinaoneka ngati palibe chabwino chifukwa anataya ubwenzi wawo ndi Mulungu, moyo wosatha, chimwemwe komanso Paradaiso. Koma Yehova Mulungu analosera za Mpulumutsi. Yehova anatchula mpulumutsi ameneyu kuti “mbewu.” (Gen. 3:15) Kwa nthawi yaitali maulosi ambiri a m’Baibulo anatchula za Mbewu. Komabe nthawi imeneyo mbewuyo inali isanadziwike kuti adzakhala ndani. Mbewuyo inali kudzachokera ku mbadwa ya Abulahamu, Isake ndi Yakobo komanso mu mzere wa Mfumu Davide.​—Gen. 21:12; 22:16-18; 28:14; 2 Sam. 7:12-16.

      19, 20. (a) Kodi ndani amene ali Mbewu yolonjezedwa? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mbewu yolonjezedwa si Yesu yekha?

      19 Kodi Mbewu yolonjezedwa imeneyi inali ndani? Yankho la funso limeneli lili pa Agalatiya 3:16. (Werengani.) Komabe kumapeto kwa chaputala chomwechi, mtumwi Paulo anauza Akhristu odzozedwa kuti: “Ndiponso, ngati muli a Khristu, mulidi mbewu ya Abulahamu, olandira cholowa malinga ndi lonjezolo.” (Agal. 3:29) Popeza kuti Yesu ndi amene ali Mbewu yolonjezedwa, zikutheka bwanji kuti ena akhalenso mbewu imeneyi?

      20 Mamiliyoni ambiri amanena kuti ndi mbadwa za Abulahamu ndipo ena afika pochita zinthu ngati aneneri. Zipembedzo zina zimanena motsimikiza kuti aneneri awo ndi mbadwa za Abulahamu. Koma kodi onsewo ndi Mbewu yolonjezedwadi? Ayi. Monga mmene mtumwi Paulo ananenera mouziridwa, si mbadwa zonse za Abulahamu zimene zingakhale Mbewu yolonjezedwa. Ndipo ndi zoona kuti si mbadwa zonse za Abulahamu zimene zinagwiritsidwa ntchito kuti anthu adalitsidwe. Mbewu yodalitsa anthu imeneyi ikanachokera kwa Isake yekha. (Aheb. 11:18) Pamapeto pake zinadziwika kuti Yesu Khristu amene anali mbadwa ya Abulahamu, ndiye anali mbali yoyamba ya mbewu yolonjezedwa.b Ndipo anthu onse amene anali m’gulu la makolo ake analembedwa m’Baibulo. Ena onse anadzakhala mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu chifukwa chakuti ndi ake “a Khristu.” Choncho udindo wa Yesu pokwaniritsa ulosi umenewo ndi wapaderadi.

  • Udindo Wapadera wa Yesu Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2008 | December 15
    • Kodi Mukukumbukira?

  • Udindo Wapadera wa Yesu Pokwaniritsa Cholinga cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2008 | December 15
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena