Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 6/1 tsamba 7-12
  • Yehova—Mulungu Wovumbula Zinsinsi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova—Mulungu Wovumbula Zinsinsi
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wamphamvuyonse Koma Wachikondi
  • Kulemekeza Anthu Amene Yehova Akuwagwiritsira Ntchito
  • Tisunge Kapena Tisasunge Chinsinsi?
  • Tiulule Kapena Tisaulule?
  • Chinsinsi Chimene Akristu Sayenera Kusunga!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Mungam’dziwe Bwanji Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2006
  • ‘Nzeru ya Mulungu Imaonekera mu Chinsinsi Chopatulika’
    Yandikirani Yehova
  • Kuvundukula Chinjokacho
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 6/1 tsamba 7-12

Yehova​—Mulungu Wovumbula Zinsinsi

“Kuli Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi.”​—DANIELI 2:28.

1, 2. (a) Kodi Yehova amasiyana motani ndi Mdani wake wamkulu? (b) Kodi anthunso amaonetsa motani kusiyana kumeneko?

YEHOVA, Mulungu wa chilengedwe chonse, wam’mwambamwamba ndi wachikondi, Mlengi yekhayo, ali Mulungu wanzeru ndi chilungamo. Sadzibisa iye yekha, kubisa ntchito zake, kapena zifuno zake. Panthaŵi yakeyake ndipo modzifunira, amadzivumbula iye yekha. Nzimene zimamsiyanitsa ndi Mdani wake, Satana Mdyerekezi, amene amayesa kudzibisa yekha, ndi kubisa zolinga zake.

2 Kusiyana kwa Yehova ndi Satana kulinso pa olambira awo. Amene amatsata Satana ali akatangale ndi onyenga. Amayesa kudzionetsa ngati abwino, pamene amachita ntchito zamdima. Akristu a ku Korinto anauzidwa kuti asadabwe nazo zimenezo. “Pakuti otere ali atumwi onyenga, ochita ochenjerera, odzionetsa ngati atumwi a Kristu. Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.” (2 Akorinto 11:13, 14) Koma Akristu amayang’ana kwa Kristu Mtsogoleri wawo. Pamene iye anali padziko lapansi, anaonetsa mwangwiro umunthu wa Atate wake, Yehova Mulungu. (Ahebri 1:1-3) Chotero, mwa kutsatira Kristu, Akristu amatsanza Yehova, Mulungu wa choonadi, wosabisa zinthu, ndi wa kuunika. Iwonso samadzibisa ayi, kubisa ntchito zawo, kapena zolinga zawo.​—Aefeso 4:17-19; 5:1, 2.

3. Kodi tingatsutse motani chinenezo chakuti anthu amene amakhala Mboni za Yehova amachita kuwakakamiza kuloŵa “m’kagulu kampatuko kachinsinsi”?

3 Panthaŵi yabwino kwa iye, Yehova amavumbula mwatsatanetsatane zifuno zake ndi zinthu za mtsogolo zimene anthu sanadziŵepo konse. Mwanjira imeneyi iye ali Mulungu wovumbula zinsinsi. Ndiye chifukwa chake anthu ofuna kumtumikira amawapempha​—inde kuwalimbikitsa​—kuphunzira chidziŵitso chovumbulidwa chimenecho. Mboni zoposa 145,000 zomwe anazifunsa mu 1994 m’dziko lina ku Ulaya zinanena kuti aliyense wa izo payekha anayamba wafufuza ziphunzitso za Mboni za Yehova zaka ngati zitatu asanasankhe kukhala Mboni. Anadzisankhira okha mwaufulu, sanawakakamize ayi. Ndipo anapitiriza ndi ufulu wawo wodzisankhira zinthu ndi kuzichita. Mwachitsanzo, popeza kuti ena angapo anayamba kutsutsa makhalidwe abwino a Akristu, amenewo pambuyo pake anasankha kusiya kukhala Mboni. Zosangalatsa nzakuti pazaka zisanu zapitazi, ambiri mwa amene kale anali Mboni ameneŵa anayambanso kugwirizana ndi Mboni ndi kugwira nawo ntchito.

4. Kodi Akristu okhulupirika sayenera kuvutika maganizo ndi chiyani, ndipo chifukwa ninji?

4 Inde, si onse omwe kale anali Mboni amene amabwerera, ndipo ena a iwo anali ndi udindo mumpingo wachikristu. Sitiyenera kudabwa nazo zimenezi, pakuti ngakhale mmodzi wa otsatira a Yesu apamtima, mtumwi Yudasi, anapanduka. (Mateyu 26:14-16, 20-25) Koma kodi chimenechi chingakhale chifukwa chovutikira maganizo ndi Chikristu? Kodi zimenezi zimachititsa njira yabwino imene Mboni za Yehova zimayendetsera ntchito yawo yophunzitsa kukhala yachabe? Ayi, pakutinso ngakhale chinyengo cha Yudasi Isikariote sichinaimitse zifuno za Mulungu.

Wamphamvuyonse Koma Wachikondi

5. Kodi tidziŵa bwanji kuti Yehova ndi Yesu amakonda anthu, ndipo achisonyeza motani chikondicho?

5 Yehova ali Mulungu wachikondi. Amawasamala anthu. (1 Yohane 4:7-11) Ngakhale kuti ali wokwezeka, amakonda kukhala mabwenzi ndi anthu. Za mmodzi wa atumiki ake akale, timaŵerenga kuti: “Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudaŵerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.” (Yakobo 2:23; 2 Mbiri 20:7; Yesaya 41:8) Monga momwe mabwenzi amauzirana zinsinsi, iyenso Yehova amatero kwa mabwenzi ake. Pankhani imeneyi Yesu anatsanzira Atate wake, pakuti anakhala mabwenzi ndi ophunzira ake ndipo anawauza zinsinsi. “Sinditchanso inu akapolo,” anawauza tero, “chifukwa kapolo sadziŵa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziŵitsani.” (Yohane 15:15) Chidziŵitso chobisika, kapena kuti “chinsinsi,” chimene Yehova, Mwana wake, ndi mabwenzi awo omwe akudziŵa chimawagwirizanitsa paunansi wachikondi ndi wodzipereka.​—Akolose 3:14.

6. Nchifukwa ninji Yehova samabisa zolinga zake?

6 Tanthauzo la dzina la Yehova lakuti, “Amachititsa Kukhalako,” limasonyeza mphamvu yake yokhala chilichonse chimene iye akufuna kuti akwaniritse chifuno chake. Kusiyana ndi anthu, Yehova samabisa zolinga zake kuopa kuti mwina ena angamlepheretse kuzikwaniritsa. Iye salephera konse, choncho amavumbula poyera m’Mawu ake, Baibulo, zochuluka zimene akufuna kuchita. Amalonjeza kuti: “Mawu anga . . . sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:11.

7. (a) Kodi Yehova analoseranji m’Edene, ndipo kodi Satana anasonyeza motani kuti Mulungu ngwoona? (b) Kodi ndi motani mmene mawu a pa 2 Akorinto 13:8 amakhalira oona nthaŵi zonse?

7 Chipanduko chitangochitika m’Edene, Yehova anavumbula mwatsatanetsatane zotsatira zake zomaliza za mkangano womwe ulipo pakati pa iye ndi Mdani wake, Satana. Mbewu ya Mulungu imene analonjeza anati adzainzunzunda kwa kanthaŵi, pamene Satanayo adzamnzunzunda kotheratu, kumpheratu. (Genesis 3:15) Mu 33 C.E., Mdyerekezi ananzunzundadi Mbewuyo, Kristu Yesu, mwa kumphetsa. Mwanjira imeneyo, Satana anakwaniritsa Lembalo ndiyeno motero anasonyeza kuti Yehova ali Mulungu wa choonadi, ngakhale kuti iye Satana sizimene anali kufuna zimenezi ayi. Kuda kwake choonadi ndi chilungamo, ndiponso mzimu wake wonyada ndi wosalapa, zinamchititsadi zinthu zimene Mulungu analosera kuti iyeyo adzachita. Inde, kwa onse otsutsa choonadi, ngakhale kwa Satana, mawu awa ngoona akuti: “Sitikhoza kanthu pokana choonadi, koma povomereza choonadi.”​—2 Akorinto 13:8.

8, 9. (a) Kodi Satana akudziŵa chiyani, koma kodi kudziŵa kwakeko kumasokoneza kukwaniritsika kwa zifuno za Yehova? (b) Kodi ndi chenjezo lotani lomveka limene otsutsa Yehova akulinyalanyaza, ndipo chifukwa ninji?

8 Popeza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa mosaoneka mu 1914, Chivumbulutso 12:12 chakwaniritsidwa, chomwe chimati: “Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” Koma kodi kudziŵa kwake Satana kuti kamtsalira kanthaŵi kumamsinthitsa zochita zake? Ngati Satana angachite zimenezo, angakhale akuvomera kuti Yehova ali Mulungu wa choonadi ndi kuti pokhala Wolamulira Wam’mwambamwamba, ndi yekhayo woyenera kumlambira. Komabe, Mdyerekezi safuna kugonja, ngakhale akudziŵa.

9 Yehova amavumbula poyera zimene zidzachitika pamene Kristu adzabwera kudzapereka chiweruzo padziko la Satana. (Mateyu 24:29-31; 25:31-46) Pankhani imeneyi, Mawu ake amanena za olamulira a dziko kuti: “Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka [“chisungiko,” NW], pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zoŵaŵa mkazi wa pakati.” (1 Atesalonika 5:3) Amene amatsata Satana amanyalanyaza chenjezo lomveka limeneli. Ali akhungu chifukwa cha mitima yawo yoipa, ndipo zimenezo zawaletsa kulapa pantchito zawo zoipa ndi kusintha zolingalira zawo ndi machenjera awo oyesa kusokoneza zifuno za Yehova.

10. (a) Kodi 1 Atesalonika 5:3 angakhale atakwaniritsidwa pamlingo wotani, koma kodi anthu a Yehova ayenera kutani? (b) Kodi nchifukwa ninji anthu opanda chikhulupiriro angadzalimbe mtima kwambiri mtsogolo potsutsa anthu a Mulungu?

10 Makamaka kuyambira 1986, pamene United Nations inalengeza Chaka cha Mtendere wa Dziko Lonse, kwakhala zolankhulalankhula zambiri za mtendere ndi chisungiko padziko lonse. Anthu achita zinthu zotsimikizika kuti adzetse mtendere wa dziko lonse, ndipo nthaŵi zina akhoza pang’ono. Kodi zimenezi ndizo kukwaniritsika konse kwa ulosi umenewo, kapena kodi tingayembekezere kumva chilengezo china chake chachikulu mtsogolo? Yehova adzaimveketsa bwino mfundoyo panthaŵi yake. Pakali pano, tiyeni tigalamuke mwauzimu, “akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” (2 Petro 3:12) Pamene nthaŵi ikupita ndiponso zolankhulalankhula za mtendere ndi chisungiko nkumawonjezeka, anthu ena odziŵa chenjezo limeneli, nasankha kulinyalanyaza, angadzakhale amwano kwambiri poganiza kuti Yehova sadzakwaniritsa kapena kuti sangathe kukwaniritsa mawu ake. (Yerekezerani ndi Mlaliki 8:11-13; 2 Petro 3:3, 4.) Koma Akristu oona amadziŵa kuti Yehova adzachita chifuno chake!

Kulemekeza Anthu Amene Yehova Akuwagwiritsira Ntchito

11. Kodi Danieli ndi Yosefe anaphunziranji za Yehova?

11 Pamene Mfumu Nebukadinezara, wolamulira mu Ufumu watsopano wa Babulo, analota maloto ovutitsa maganizo omwe sanathe kukumbukira, anafuna omthandiza. Ansembe ake, openduza, ndi aula analephera kumuuza lotolo ngakhale tanthauzo lake. Komabe, Danieli mtumiki wa Mulungu anakhoza, ngakhale ananena nthaŵi yomweyo kuti kuvumbula kwake lotolo ndi tanthauzo lake sikunali chifukwa cha nzeru zake ayi. Danieli anati: “Kuli Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziŵitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza.” (Danieli 2:1-30) Zaka mazana ambiri zimenezo zisanachitike, Yosefe, mneneri wina wa Mulungu, anaona kuti Yehova ndiye Wovumbula zinsinsi.​—Genesis 40:8-22; Amosi 3:7, 8.

12, 13. (a) Kodi mneneri wa Mulungu woposa onse anali yani, ndipo mwayankhiranji tero? (b) Ndani lero amene ali “adindo a zinsinsi za Mulungu,” ndipo tiyenera kuwaona motani?

12 Mneneri wa Yehova woposa onse amene anatumikira padziko lapansi anali Yesu. (Machitidwe 3:19-24) Paulo anafotokoza kuti: “Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m’manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana, koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika woloŵa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am’mwamba omwe.”​—Ahebri 1:1, 2.

13 Yehova analankhula kwa Akristu oyambirira mwa Mwana wake, Yesu, amene anawauza zinsinsi za Mulungu. Yesu anawauza kuti: “Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:10) Pambuyo pake Paulo analankhula za Akristu odzozedwa kuti ndiwo “atumiki a Kristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.” (1 Akorinto 4:1) Lero, Akristu odzozedwa adakali otero, ndipo ndiwo kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene kupyolera mwa Bungwe lake Lolamulira akukonza chakudya chauzimu panthaŵi yake. (Mateyu 24:45-47) Ngati timalemekeza kwambiri aneneri akale ouziridwa a Mulungu, ndipo makamaka Mwana wa Mulungu, kodi sitiyeneranso kulemekeza anthu amene Yehova akuwagwiritsira ntchito lero povumbula chidziŵitso cha m’Baibulo chofunika kwambiri kwa anthu nthaŵi zino zoŵaŵitsa?​—2 Timoteo 3:1-5, 13.

Tisunge Kapena Tisasunge Chinsinsi?

14. Kodi ndi liti pamene Akristu amachita ntchito yawo mwachinsinsi, akamatero amatsatira chitsanzo cha yani?

14 Kodi kumasuka kwa Yehova povumbula zinthu kumatanthauza kuti Akristu nthaŵi zonse ayenera kuvumbula zonse zimene akudziŵa zivute zitani? Chabwino, Akristu amatsatira uphungu wa Yesu kwa atumwi ake wakuti akhale “ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.” (Mateyu 10:16) Wina akawauza kuti safunikira kulambira Mulungu malinga ndi kufuna kwa chikumbumtima chawo, Akristu amapitiriza “kumvera Mulungu,” pakuti adziŵa kuti kulibe munthu aliyense amene ali ndi mphamvu yowaletsa kulambira Yehova. (Machitidwe 5:29) Yesu mwiniyo anasonyeza kuti zimenezo nzoyenera. Timaŵerenga kuti: “Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda m’Galileya; pakuti sanafuna kuyendayenda m’Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye. Koma phwando la Ayuda, phwando la misasa, linayandikira. Chifukwa chake Yesu ananena nawo [achibale ake osakhulupirira], . . . Kwerani inu kumka kuphwando; sindikwera Ine ku phwando ili tsopano apa; pakuti nthaŵi yanga siinakwanire. Ndipo mmene adanena nawo zimenezi anakhalabe m’Galileya. Koma pamene abale ake adakwera kumka kuphwando, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika.”​—Yohane 7:1, 2, 6, 8-10.

Tiulule Kapena Tisaulule?

15. Kodi Yosefe anasonyeza motani kuti kusunga chinsinsi nthaŵi zina ndiko chikondi?

15 Nthaŵi zina, kusunga chinsinsi sikumangokhala kwanzeru komanso kwachikondi. Mwachitsanzo, kodi Yosefe, atate wa Yesu womlera, anatani atadziŵa kuti mkwatibwi wake, Mariya, yemwe anapalana naye chibwenzi anali ndi pakati? Timaŵerenga kuti: ‘Koma Yosefe, mwamuna wake, anali wolungama, ndiponso sanafuna kunyazitsa iye, nayesa m’mtima kumleka iye m’tseri.’ (Mateyu 1:18, 19) Kumnyazitsa iye poyera kukanasonyeza kupanda chifundo kwakukulu!

16. Kodi akulu, ngakhalenso onse mumpingo, ali ndi ntchito yotani pankhani zachinsinsi?

16 Zinsinsi zomwe zingamvetse manyazi kapena kupweteka wina siziyenera kuvumbulidwa kwa anthu osayenera. Akulu achikristu amakumbukira zimenezi popereka uphungu kwa munthu payekha kapena potonthoza Akristu anzawo kapena mwina ndi powalanga pomwe atamchimwira kwambiri Yehova. Nkhani zimenezi zimafunika kuzisamalira mwa Malemba; kuvumbula zinsinsi kwa osakhudzidwa nkosafunika ndipo nkupanda chikondi. Inde, a mumpingo wachikristu samayesa kufunsitsa akulu kuti awauze nkhani zachinsinsi koma amalemekeza ntchito ya akulu yosavumbula zinthu zachinsinsi. Miyambo 25:9 imati: “Nena mlandu wako ndi mnzako, osaulula zinsinsi za mwini.”

17. Nchifukwa ninji Akristu nthaŵi zambiri amasunga chinsinsi, nanga nchifukwa ninji sangatero nthaŵi zina?

17 Pulinsipulo limeneli limakhudzanso banja kapena mabwenzi apamtima. Chinsinsi chimafunika kwambiri pazinthu zina kuti pasakhale kusamvana ndi kuti maunansi asasweke. “Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula; chomwecho lilime losinjirira [“lovumbula chinsinsi,” NW] likwiyitsa nkhope.” (Miyambo 25:23) Zoona, kukhulupirika kwathu kwa Yehova ndi mapulinsipulo ake olungama, ndiponso kukonda kwathu olakwawo, nthaŵi zina kungafune kuti tiulule ngakhale nkhani zachinsinsi kwa makolo, akulu achikristu, kapena ena omwe ali ndi udindo.a Koma nthaŵi zambiri, Akristu amasunga chinsinsi pankhani za ena, monga amachisungira pankhani za iwo eni.

18. Kodi ndi mikhalidwe itatu iti yachikristu imene ingatithandize kudziŵa zimene tingaulule ndi zimene sitingaulule?

18 Mwachidule, Mkristu amatsanzira Yehova mwa kusunga chinsinsi pankhani zina pamene kuli kofunika, ndi kuchivumbula kokha pamene kuli koyenera kutero. Pofuna kudziŵa zimene angaulule ndi zimene sangaulule, amatsogozedwa ndi kudzichepetsa, chikhulupiriro, ndi chikondi. Kudzichepetsa kumamletsa kudzitukumula, kuyesa kukondweretsa ena mwa kuwauza zonse zomwe akudziŵa kapena kuwakopa chidwi ndi zinsinsi zimene sayenera kuwauza. Kukhulupirira Mawu a Yehova ndi mpingo wachikristu kumamsonkhezera kulalikira chidziŵitso chaumulungu chopezeka m’Baibulo, pamene akusamala kuti sakunena zinthu zimene zingakwiyitse ena pachiyambi penipeni. Inde, chikondi chimamsonkhezera kulankhula poyera zinthu zolemekeza Mulungu zimenenso anthu afunika kudziŵa kuti apeze moyo. Koma nkhani zaumwini zachinsinsi samaziulula, pozindikira kuti nthaŵi zambiri angamasonyeze kuti alibiretu chikondi ngati azivumbula.

19. Kodi ndi njira iti imene imathandiza kudziŵa Akristu oona, ndipo ili ndi zotsatirapo zotani?

19 Njira yabwino imeneyi imathandiza kudziŵa Akristu oona. Samabisa Mulungu mwa kunena kuti alibe dzina kapena mwa kulandira chiphunzitso chachinsinsi chosafotokozeka cha Utatu. Milungu yosadziŵika njachipembedzo chonyenga, osati choona ayi. (Onani Machitidwe 17:22, 23.) Mboni zodzozedwa za Yehova zimauyamikiradi mwaŵi wokhala “adindo a zinsinsi za Mulungu.” Mwa kuwavumbulira ena zinsinsi zimenezi poyera, zimathandizira kukopa oona mtima kuti amfunefune Yehova nakhale mabwenzi ake.​—1 Akorinto 4:1; 14:22-25; Zekariya 8:23; Malaki 3:18.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Musakhale ndi Mbali m’Machimo a Ena” mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 1986.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Nchifukwa ninji Yehova samabisa zolinga zake?

◻ Kodi Yehova amavumbulira yani zinsinsi zake?

◻ Kodi Akristu ali ndi ntchito yotani pankhani zachinsinsi?

◻ Kodi ndi mikhalidwe itatu iti imene idzathandiza Akristu kudziŵa zimene angaulule ndi zimene sangaulule?

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Yehova amavumbula zinsinsi mwa Mawu ake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena