Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bm gawo 2 tsamba 5
  • Anataya Mwayi Wokhala M’Paradaiso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anataya Mwayi Wokhala M’Paradaiso
  • Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Moyo Unali Wotani m’Paradaiso?
    Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Mulungu ndi Wamkulu Kuposa Aliyense
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Adamu ndi Hava Sanamvere Mulungu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Tingaphunzire ku Banja Loyamba la Anthu
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
bm gawo 2 tsamba 5
Hava wagwira chipatso choletsedwa

GAWO 2

Anataya Mwayi Wokhala M’Paradaiso

Mngelo wopanduka anakopa Adamu ndi Hava, mwamuna ndi mkazi oyamba, kuti akane ulamuliro wa Mulungu. Chifukwa cha zimenezi anthu onse anachimwa ndipo anayamba kufa

KALE kwambiri Mulungu asanalenge anthu, analenga angelo ambirimbiri omwe sitingathe kuwaona. M’munda wa Edeni, mngelo wopanduka, amene anadzakhala Satana Mdyerekezi, mochenjera anayesetsa kunyengerera Hava kuti adye chipatso cha mtengo umene Mulungu anawaletsa.

Polankhula kudzera mwa njoka, Satana ananena kuti Mulungu anabisira mwamuna ndi mkazi wakeyo zinthu zabwino kwambiri. Mngeloyo anauza Hava kuti iye ndi mwamuna wake sangafe atadya chipatso chimene Mulungu anawaletsacho. Choncho pamenepa Satana anaimba Mulungu mlandu woti ananamiza Adamu ndi Hava, omwe anali ana ake. Satana ananama kuti ngati anthu atapanda kumvera Mulungu, zinthu zidzawayendera bwino kwambiri ndiponso adzadziwa zinthu zochuluka komanso adzakhala ndi ufulu. Koma limeneli linali bodza lamkunkhuniza, ndipotu linali bodza loyamba kunenedwa padziko lapansi. Nkhani yaikulu pamenepa inali yokhudza ulamuliro umene Mulungu ali nawo pa chilengedwe chonse. Satana anakayikira zoti Mulungu ndi woyenera kulamulira, zoti amalamulira mwachilungamo komanso mokomera anthu.

Hava anakhulupirira bodza la Satanalo. Iye anayamba kusirira chipatsocho, ndipo anadya. Kenako anapatsa mwamuna wake ndipo nayenso anadya. Atachita zimenezi anachimwa. Zimene anachitazi, ngakhale kuti zingaoneke ngati nkhani yaing’ono, zinasonyeza kusamvera Mulungu. Posankha mwadala kusamvera lamulo la Mulungu, Adamu ndi Hava anakana ulamuliro wa Mlengi amene anawapatsa chilichonse, ngakhalenso moyo wangwiro.

Mbewu “idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.”—Genesis 3:15

Mulungu anaweruza opandukawo chifukwa cha zimene anachitazo. Iye ananeneratu kuti kudzabwera Mbewu yolonjezedwa, kapena kuti Mpulumutsi, amene adzawononge Satana yemwe akuimiridwa ndi njoka. Mulungu anapereka chilango cha imfa kwa Adamu ndi Hava, koma sanawaphe nthawi yomweyo. Pamenepa Mulungu anachitira chifundo ana awo amene anali asanabadwe. Ana amenewo anali ndi chifukwa choyembekezera zabwino m’tsogolo popeza Mulungu analonjeza kuti adzatumiza winawake amene adzachotse mavuto amene anayambika m’munda wa Edeni chifukwa cha kupandukako. Pamene ntchito yolemba Baibulo inkapitirira, zinadziwika mmene Mulungu adzakwaniritsire cholinga chake chokhudza Mpulumutsi wam’tsogoloyu komanso kuti Mpulumutsi ameneyo adzakhala ndani.

Mulungu anapitikitsa Adamu ndi Hava m’Paradaiso, ndipo iwo anafunika kugwira mwakhama ntchito yolima, kunja kwa munda wa Edeni, kuti apeze chakudya. Kenako Hava anakhala ndi pakati ndipo anabereka Kaini, mwana wawo woyamba. Adamu ndi Hava anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi, ndipo ena mwa iwo anali Abele ndiponso Seti, agogo ake a Nowa.

​—Nkhaniyi yachokera m’buku la Genesis chaputala 3 mpaka 5 ndi pa Chivumbulutso 12:9.

  • Kodi bodza loyamba linali lotani, ndipo ndani amene analinena?

  • Kodi chinachitika n’chiyani kuti Adamu ndi Hava ataye mwayi wokhala m’Paradaiso?

  • Poweruza opandukawo, kodi Mulungu anatchula mfundo iti yomwe ndi yopatsa chiyembekezo?

KUPANDA UNGWIRO NDIPONSO IMFA

Mulungu analenga Adamu ndi Hava ali angwiro, ndipo anali ndi mwayi wokhala m’Paradaiso kosatha. Koma iwo sanamvere Mulungu ndipo anachimwa. Choncho Adamu ndi Hava sanakhalenso angwiro ndipo ubwenzi wawo ndi Yehova amene anawapatsa moyo, unatha. Kuyambira nthawi imeneyo iwo anakhala ochimwa ndipo kenako anafa. Zimenezi ndi zimene zimachitikiranso anthu onse obadwa kuchokera mwa iwo.—Aroma 5:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena