Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 4/15 tsamba 5-8
  • Kodi Tsogolo Lanu Lidzakhala Lotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tsogolo Lanu Lidzakhala Lotani?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tsogolo Lolembedweratu
  • Kodi Mulungu Amadziŵiratu Chilichonse?
  • Zoikidwiratu Ziŵiri za Munthu
  • Kodi Tsogolo Lanu Linalembedweratu?
    Galamukani!—2009
  • Kodi Kuikiratu za Mtsogolo Kungagwirizanitsidwe ndi Chikondi cha Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Abwino Nawonso Amakumana Ndi Mavuto?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Yehova Amalalikira ‘za Chimaliziro Kuchokera Pachiyambi’
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 4/15 tsamba 5-8

Kodi Tsogolo Lanu Lidzakhala Lotani?

NGATI Mulungu Wamphamvuyonse ngwodziŵa chilichonse, wodziŵa zonse zakale, zalero, ndiponso zamtsogolo, kodi sitinganene kuti zinthu zonse zidzachitika mofanana ndi mmene Mulunguyo anazioneratu? Ngati Mulungu anaoneratu ndi kusankhiratu njira ya moyo ndiponso mapeto a munthu aliyense, kodi zingakhaledi zoona kuti tili ndi ufulu wosankha njira yathu ya moyo, kusankha tsogolo lathu?

Anthu akhala akukambitsirana za mafunso ameneŵa kwa zaka mazana ambiri. Mkangano umenewu ukupangitsabe magaŵano m’zipembedzo zikuluzikulu. Kodi kudziŵiratu zamtsogolo kwa Mulungu kungakhale kogwirizana ndi ufulu wa munthu wa kusankha? Kodi mayankho ake tingawapeze kuti?

Anthu mamiliyoni ambiri kuzungulira dziko lonse lapansi angavomereze kuti Mulungu walankhula ndi anthu mwa Mawu ake olembedwa amene ananenedwa ndi omlankhulira ake, aneneri. Mwachitsanzo, Koran imati zivumbulutso zinachokera kwa Mulungu: Taurāh (Torah, Chilamulo, kapena kuti mabuku asanu a Mose), Zabūr (Masalmo), ndi Injīl (Uthenga Wabwino, Malemba Achigiriki Achikristu, kapena kuti “Chipangano Chatsopano”), ndiponso zimene zinavumbulidwa kwa aneneri a Israyeli.

M’Malemba Achigiriki Achikristu, timaŵerenga kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero.” (2 Timoteo 3:16) Mwachionekere, chitsogozo kapena malangizo alionse amene timalandira ziyenera kuchokeradi kwa Mulungu iyemwini. Choncho, kodi sikungakhale kwanzeru kupenda zolemba za aneneri oyambirira a Mulungu? Kodi zimanenanji za tsogolo lathu?

Tsogolo Lolembedweratu

Aliyense amene anaŵerengapo Malemba Opatulika amadziŵa kuti iwo ali ndi maulosi ambirimbiri. Zochitika za m’mbiri monga kugwa kwa Babulo wakale, kumangidwanso kwa Yerusalemu (m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi mpaka zana lachisanu B.C.E.), ndiponso kukhalapo ndi kugwa kwa mafumu akale a Amedi ndi Aperisi ndiponso mafumu a Grisi zonse zinanenedweratu mwatsatanetsatane. (Yesaya 13:17-19; 44:24–45:1; Danieli 8:1-7, 20-22) Kukwaniritsidwa kwa maulosi ameneŵa ndi umodzi mwa maumboni amphamvu kwambiri akuti Malemba Opatulika alidi Mawu a Mulungu, popeza kuti ndi Mulungu yekha amene ali ndi mphamvu yochita zonse ziŵiri kuona zamtsogolo ndiponso kulinganiza zimene zidzachitika mtsogolo. M’lingaliro limeneli, Malemba Opatulika amanenadi za tsogolo lolembedweratu.

Mulungu iyemwini anati: “Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofanana ndi Ine; ndilalikira za chimariziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthaŵi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse . . . Inde, ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.” (Yesaya 46:9-11; 55:10, 11) Dzina lenilenilo limene Mulungu anadzidziŵikitsira nalo kwa aneneri akale ndilo Yehova, limene kwenikweni limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako.”a (Genesis 12:7, 8; Eksodo 3:13-15; Salmo 83:18) Mulungu amadzidziŵikitsa kuti Ndiye amene ali Wokwaniritsa mawu ake, Ndiye amene nthaŵi zonse amapangitsa kuti zifuno zake zichitike.

Choncho, Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu yake ya kudziŵiratu zamtsogolo pofuna kukwaniritsa zifuno zake. Iye wakhala akuigwiritsira ntchito pochenjeza anthu oipa za chiweruzo chimene chikudza ndi kupatsa atumiki ake chiyembekezo cha chipulumutso. Koma kodi Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu imeneyi popanda malire ake? Kodi pali umboni uliwonse m’Malemba Opatulika wonena za zinthu zimene Mulungu anasankha kuti asamazidziŵiretu?

Kodi Mulungu Amadziŵiratu Chilichonse?

Mawu onse ochirikiza chiphunzitso cha choikidwiratu amazikidwa pa malingaliro akuti popeza kuti nzachidziŵikire kuti Mulungu ali ndi mphamvu ya kudziŵiratu ndi kulinganiza zochitika zamtsogolo, iye ayenera kuti amadziŵiratu chilichonse, kuphatikizapo zochita zamtsogolo za munthu aliyense. Komabe, kodi malingaliro ameneŵa nganzeru? Zimene Mulungu amavumbula m’Malemba ake Opatulika zikusemphana ndi zimenezo.

Mwachitsanzo, Malemba amanena kuti “Mulungu anamuyesa Abrahamu” mwa kumlamulira kuti apereke mwana wake wamwamuna Isake monga nsembe yopsereza. Pamene Abrahamu anali pafupi kupereka Isakeyo, Mulungu anamletsa nanena: ‘Tsopano ndidziŵa kuti iwe umuopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.’ (Genesis 22:1-12) Ngati Mulungu anadziŵiratu kuti Abrahamu anali kudzamvera lamulo lake, kodi iye akananena mawu ameneŵa? Kodi chikanakhala chiyeso chanzeru?

Ndiponso, aneneri akale amanena kuti Mulungu anadzilankhulira mobwerezabwereza kuti ‘anachita chisoni’ ndi chinthu chinachake chimene anachita kapena chimene anali kulingalira kuchichita. Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti ‘anachita chisoni [kuchokera ku mawu achihebri akuti na·chamʹ] kuti anaika Sauli akhale mfumu ya Israyeli.’ (1 Samueli 15:11, 35; yerekezerani ndi Yeremiya 18:7-10; Yona 3:10.) Popeza kuti Mulungu ali wangwiro, mavesi ameneŵa sakutanthauza kuti Mulungu analakwitsa posankha Sauli kukhala mfumu yoyamba ya Israyeli. M’malo mwake, ayenera kuti akusonyeza kuti Mulungu anamva chisoni chifukwa chakuti Sauli anakhala wosakhulupirika ndiponso wosamvera. Mawu amenewo a Mulungu onena za iyemwini akanasonyeza kupanda nzeru zikanakhala kuti iye anadziŵiratu ntchito za Sauli.

Mawu amodzimodziwo akupezekanso m’Malemba akale koposa, amene ponena za masiku a Nowa, amati: “Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu padziko lapansi, ndipo anavutika m’mtima mwake. Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga padziko lapansi . . . pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga [iwo].” (Genesis 6:6, 7) Pamenepanso, zimenezi zikusonyeza kuti zochita za munthu sizilinganizidwiratu ndi Mulungu. Mulungu anamva chisoni, ndipo ngakhale kuvutika mtima, osati chifukwa chakuti ntchito zake zomwezo zinali zolakwa ayi, koma chifukwa chakuti machimo a munthu anachuluka. Mlengiyo anamva chisoni kwambiri kuti kunali kofunika kuwononga anthu onse kupatulapo Nowa ndi banja lake. Mulungu akutitsimikizira kuti: “Sindikondwera nayo imfa ya woipa.”​—Ezekieli 33:11; yerekezerani ndi Deuteronomo 32:4, 5.

Choncho, kodi Mulungu anadziŵiratu ndipo ngakhale kulinganiziratu za kuchimwa kwa Adamu, pamodzi ndi mavuto amene zimenezi zinali kudzachititsa m’banja la munthu? Zimene takambitsiranazi zikusonyeza kuti zimenezi sizingakhale zoona. Ndiponso, chikhala Mulungu anadziŵiratu zinthu zonsezi, ndiye kuti akanakhala mlengi wa uchimo pamene analenga munthu ndiponso akanakhala kuti ndiye akuchititsa mwadala makhalidwe onse oipa a anthu ndi mavuto awo. Mwachionekere, zimenezi nzosiyana ndi zimene Mulungu anavumbula za iyemwini m’Malemba. Iye ndi Mulungu wachikondi ndi wachilungamo amene amadana ndi zoipa.​—Salmo 33:5; Miyambo 15:9; 1 Yohane 4:8.

Zoikidwiratu Ziŵiri za Munthu

Malemba Opatulika savumbula kuti tsogolo la aliyense wa ife linalinganizidwiratu, kapena kuti linaikidwiratu, ndi Mulungu. M’malo mwake, zimene iwo amavumbula nzakuti Mulungu ananeneratu za zoikidwiratu ziŵiri zokha basi za munthu. Mulungu anapatsa munthu aliyense ufulu wa kusankha choikidwiratu chake. Kalekale mneneri Mose anauza Aisrayeli kuti: ‘Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, . . . potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kummamatira iye, pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka.’ (Deuteronomo 30:19, 20) Yesu mneneri wa Mulungu anachenjezeratu kuti: “Loŵani pachipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Misewu iŵiri, zoikidwiratu ziŵiri. Tsogolo lathu limadalira pa zochita zathu. Kumvera Mulungu kumapatsa moyo, kusamumvera kumadzetsa imfa.​—Aroma 6:23.

Mulungu “alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima; chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo.” (Machitidwe 17:30, 31) Monga anthu ambiri a m’tsiku la Nowa amene anasankha kusamvera Mulungu nawonongeka, zidzateronso ndi anthu ambiri osamvera malamulo a Mulungu lerolino. Komabe, Mulungu sanalinganiziretu anthu amene adzawonongeka ndiponso amene adzapulumuka. Ndithudi, Mawu a Mulungu amanena kuti iye ‘safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Petro 3:9) Ngakhale anthu oipa kwambiri angalape, kukhala omvera, ndiponso kupanga masinthidwe oyenerera kuti apeze chiyanjo cha Mulungu.​—Yesaya 1:18-20; 55:6, 7; Ezekieli 33:14-16; Aroma 2:4-8.

Anthu omvera, Mulungu akuwalonjeza moyo wosatha m’paradaiso wamtendere, dziko lapansi losakhalanso ndi kuipa, upandu, ndi nkhondo, m’dziko limene simudzakhalanso njala, mavuto, matenda, ndi imfa. (Salmo 37:9-11; 46:9; Yesaya 2:4; 11:6-9; 25:6-8; 35:5, 6; Chivumbulutso 21:4) Ngakhale akufa adzaukitsidwa ndi kupatsidwa mwaŵi wotumikira Mulungu.​—Danieli 12:2; Yohane 5:28, 29.

“Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima!” akutero wamasalmo, “pakuti kumatsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere. Koma olakwa adzawonongeka pamodzi: matsiriziro a oipa adzadulidwa.” (Salmo 37:37, 38) Kodi tsogolo lanu lidzakhala lotani? Zonse zili kwa inu. Ofalitsa magazini ino ngokondwa kukuuzani zowonjezereka pofuna kukuthandizani kuti mukhaledi ndi tsogolo lachimwemwe ndiponso lamtendere.

[Mawu a M’munsi]

a Dzina lakuti Yehova limapezeka nthaŵi zoposa 7,000 m’Malemba Opatulika; onani nkhani yakuti “Kuthetsa Chinsinsi cha Dzina Lalikulu Koposa” ya mu Nsanya ya Olonda ya November 1, 1993, masamaba 3-5, yofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu yake ya kudziŵiratu zamtsogolo pofuna kukwaniritsa zifuno zake

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Mulungu ‘safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’​—2 Petro 3:9

[Chithunzi patsamba 7]

Ngati Mulungu anadziŵiratu kuti Abrahamu anali wofunitsitsa kupereka nsembe mwana wake, kodi chimenecho chikanakhala chiyeso chanzeru?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena