Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chingalawa cha Nowa Chinapangidwa Mwaluso
    Galamukani!—2007 | January
    • Nkhani ya mu Genesis imati Mulungu anaganiza zoyeretsa dziko lapansi n’cholinga chothetsa kuipa, ndipo anatero mwa kuwononga dziko ndi madzi. Mulungu anauza Nowa kupanga chingalawa kuti iyeyo pamodzi ndi banja lake apulumukiremo komanso kuti apulumutsiremo mitundu yosiyanasiyana ya zinyama za padziko lapansi panthawi ya Chigumula chachikulu. Mulungu anauza Nowa kupanga chingalawa chotalika mikono 300 m’litali mwake, mikono 50 m’lifupi ndi mikono 30 kupita m’mwamba. (Genesis 6:15) M’kuwerengera kwina, chingalawachi chinali chachikulu mamita 134 m’litali, 22 m’lifupi ndi mamita 13 kupita m’mwamba.a Zimenezi zikutanthauza kuti chimatenga malo okwana makyubiki mita 40,000, ndipo chimasuntha madzi ambiri pamene chaima, ofanana ndithu ndi madzi osunthidwa ndi sitima yapamadzi ya Titanic, yomwe inali sitima yapamwamba.

  • Chingalawa cha Nowa Chinapangidwa Mwaluso
    Galamukani!—2007 | January
    • Chinkakhazikika Bwino Pamadzi

      Mtunda wa m’litali mwa chingalawachi, unali waukulu mowirikiza maulendo 6 poyerekezera ndi mtunda wa m’lifupi mwake ndipo unali wowirikiza maulendo 10 poyerekezera ndi mtunda wochoka pansi pake n’kukafika pamwamba pake. Sitima zapamadzi zambiri zamakono, zimapangidwanso motsatira masamu amenewa, ngakhale kuti masiku ano kusiyana kwa m’litali ndi m’lifupi mwa sitima kumatengeranso mphamvu ya injini ya sitimayo. Kungoti chingalawa cha Nowa anangochipanga kuti chiziyandama, osati kuti chiziyenda ayi. Koma kodi kuyandama kwa chingalawachi kunali kwabwino motani?

      Kuti sitima izitha kukhazikika bwino pamadzi, ngakhale kutachita mphepo kapena mafunde bwanji, zimayenderananso ndi mmene anasiyanitsira kutalika kwa m’litali ndi m’lifupi mwa sitimayo. Baibulo limafotokoza kuti madzi anakhuthuka n’kuchititsa Chigumula ndipo potsirizira pake Mulungu anachititsa mphepo kuwomba. (Genesis 7:11, 12, 17-20; 8:1) Malemba sanena kuti mafunde komanso mphepo imeneyo inali ya mphamvu bwanji, koma n’zosachita kufunsa kuti zinthu zimenezi zinali zamphamvu ndi zosinthasintha kwambiri ngati mmene zilili masiku ano. Mphepo ikawomba kwa nthawi yayitali komanso mwamphamvu, mafunde amakhala aakulu kwambiri komanso otalikiranatalikirana. Ngati kunachitikanso chivomerezi chilichonse, ndiye kuti chinayambitsanso mafunde amphamvu kwambiri.

      Masamu a kutalika kwa mbali zosiyanasiyana za chingalawa cha Nowa, ndi amene anachititsa kuti chikhale chokhazikika pamadzi, n’kuchiteteza kuti chisagubuduke. Chinapangidwanso kuti chisamakankhidwekankhidwe ngati chitakumana ndi mphepo kapena mafunde. Ngati chikadamatero, makamaka ngati mafunde atanyamula mbali yake imodzi kenaka n’kuisiya kuti imenyetseke pamadzi, sibwenzi anthu ndi nyama atakhalamo bwinobwino m’chingalawamo. Ndipo kukankhidwakankhidwa kukanachititsa kuti chingalawacho chisweke. Thunthu lake linayeneranso kukhala lolimba kwambiri kuti chisathifuke pakati, ngati mafunde atapikula mbali zonse ziwiri za kumapeto kwa chingalawacho panthawi imodzi. Komanso, ngati mafunde aakulu kwambiri akanachinyamula mwamphamvu cha pakatikati pake, chingalawachi chikanatha kuthifuka. Mulungu anauza Nowa kuti kukula kwa chingalawachi, m’mbali yake yopita m’mwamba, kukhale gawo limodzi mwa magawo khumi a m’litali mwake. M’kupita kwa nthawi, anthu opanga sitima zapamadzi anadzaphunzira, koma mochedwa, kuti masamu amenewa n’ngofunika kwambiri kuti sitima isasweke ikakumana ndi mafunde kapena mphepo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena