Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Khalani Otsanzira Mulungu”
    Nsanja ya Olonda—2008 | October 1
    • Mawu a Mulungu amalimbikitsa Akhristu oona kuti: “Chifukwa chake, khalani otsanzira Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Mawu amenewa akusonyeza kuti Mulungu amakhulupirira kwambiri anthu amene amam’lambira. Kodi n’chifukwa chiyani amatero? Yehova Mulungu analenga munthu m’chifanizo Chake, monga mwa chikhalidwe Chake. (Genesis 1:26, 27) Motero Mulungu anapatsa anthu makhalidwe ofanana ndi makhalidwe ake.a Moti Baibulo likamalimbikitsa Akhristu kuti “khalani otsanzira Mulungu,” zili ngati kuti Yehova akuwauza kuti: ‘Sindimakukayikirani ngakhale pang’ono. Ngakhale kuti ndinu opanda ungwiro, ndikudziwa kuti mungathe ndithu kutsanzira makhalidwe anga.’

  • “Khalani Otsanzira Mulungu”
    Nsanja ya Olonda—2008 | October 1
    • a Lemba la Akolose 3:9, 10 limasonyeza kuti mawu akuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu amatanthauza kuti tili ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu. Anthu amene akufuna kukondweretsa Mulungu amalimbikitsidwa kuti avale “umunthu watsopano,” umene “ukukhalitsidwa watsopano, kukhala wogwirizana ndi chifaniziro cha [Mulungu] amene anaulenga.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena