Mose Wokhala ndi Nyanga—Chopeka cha Mmisiri
NGATI munapitapo ku Italy, mungakhale munawona fano lowumba lotchuka la Michelangelo la Mose wokhala pansi, tsopano loikidwa pa Tchalitchi cha St. Peter mu Chains, mu Rome. Chifano cha m’zaka za zana la 16 chimenecho chimawoneka chochititsa chidwi chotani nanga, popeza chimawonetsa Mose wokhala ndi nyanga zotulukira pamutu pake! Kwenikwenidi, amisiri ambiri asonyeza Mose ali ndi nyanga. Kodi nchifukwa ninji tero? Kodi Baibulo limapereka maziko aliwonse kaamba ka lingalirolo?
Matembenuzidwe a Baibulo Achilatin otchedwa Vulgate amatiuza kuti pambuyo pa kulankhula kwake ndi Mulungu pa Phiri la Sinai, nkhope ya Mose “inamera nyanga.” (Eksodo 34:29, 30, 35; yerekezerani ndi Douay Version.) Vulgate imeneyo inakondedwa mokulira m’mbali yaikulu ya Dziko Lachikristu ndipo motero inayambukira njira yomverera malemba.
Komabe, liwu Lachihebri lotembenuzidwa “kumera nyanga” lirinso ndi tanthauzo la ‘kutulutsa cheza’ kapena ‘kunyezima.’ (Onani mawu am’munsi a Douay Version pa Eksodo 34:29.) Mogwirizana ndi Theological Wordbook of the Old Testament, liwulo “likuimira mkhalidwe wa nyanga osati yeniyeniyo.” Ndipo kuwona mawonekedwe ake, cheza cha kuwala chimafananadi ndi nyanga.
Nsonga yakuti nkhope ya Mose inatulutsa cheza njolongosoleka, popeza kuti ulemerero wa Yehova unali utangomudutsa. (Eksodo 33:22; 34:6, 7) Paulo akutsimikizira zimenezi kukhala kamvetsetsedwe kolongosoka, polemba za “ulemerero” wa nkhope ya Mose, osati ponena za “nyanga” zake.—2 Akorinto 3:7.
Motero, kumvetsetsa kolongosoka kwa mawu Abaibulo kumatsogolera ku chidziŵitso chofika pamtima kwenikweni cha cholembedwa cha m’Baibulo. Moyenerera, nyanga za fano lowumba lotchuka la Michelangelo la Mose ziri kokha chopeka cha mmisiri chochokera ku cholakwa cha kutembenuza chimene chinawongoleredwa kalekale.
[Mawu a Chithunzi patsamba 7]
Chozikidwa pa Short History of Art