Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 8/1 tsamba 29
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Maliro
    Nsanja ya Olonda—2007
  • “Ndaika Mawu Anga M’kamwa Mwako”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Yehova Amapereka Chiyembekezo Pakati pa Chisoni
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Yehova Wachita Zimene Anali Kuganiza”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 8/1 tsamba 29

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi nchifukwa ninji Maliro 4:10 amalozera kwa amayi omwe anadya ana awo kukhala “akazi achisoni”?

Akulongosola mkhalidwe wosoŵa chochita wa Ayuda mkati mwa kuzingidwa kwa Chibabulo pa Yerusalemu mu 607 B.C.E., Yeremiya analemba kuti: “Manja a akazi achisoni anaphika ana awo awo; anali chakudya chawo poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.”​—Maliro 4:10.

Mazana angapo kumbuyoko, Mose anali atachenjeza Aisrayeli kuti mtsogolo mwawo mukazindikiritsidwa ndi “dalitso” kapena “temberero.” Iwo akasangalala ndi madalitso ngati akasunga malamulo a Mulungu, koma akabweretsa kuvutika pa iwo eni ngati anakana njira zake zolungama. Chimodzi cha zotulukapo zowopsya chinali chakuti Aisrayeli akachepetsedwa ku kudya ana awo awo. (Deuteronomo 28:1, 11-15, 54, 55; 30:1; Levitiko 26:3-5, 29) Ichi m’chenicheni chinachitika pambuyo pakuti Yehova anakana mtundu wosakhulupirikawo, wosamvera kuupereka m’dzanja la Ababulo.

Pa Maliro 4:10 mneneri Yeremiya analozera pa nsonga yodziŵika bwino koposa yakuti mayi mwachibadwa amakhala wofewa mtima, wachisoni, ndi wotetezera kulinga kwa ana ake. (1 Mafumu 3:26, 27; 1 Atesalonika 2:7) Komabe, njala yomwe inali mu Yerusalemu wozingidwa inali yokulira kwenikweni ndipo kusoŵa chakudya kotulukapo kunali kokakamiza kotero kuti amayi omwe mwachibadwa akanakhala achisoni anaphika ndi kudya mbadwa zawo.​—Yerekezani ndi Maliro 2:20.

Mkhalidwe wofananawo unachitika pambuyo pakuti Ayuda anakana Mesiya, yemwe anachenjeza za kudza kwa kuzingidwa kwa Yerusalemu. (Mateyu 23:37, 38; 24:15-19; Luka 21:20-24) Katswiri wa mbiri yakale Josephus analongosola chimodzi cha zowopsya za kuzingidwa kwa mu 70 C.E.: “Mary mwana wamkazi wa Eleazar . . . anapha mwana wake wamwamuna, kenaka kumuwotcha iye ndi kudya theka limodzi, kubisa ndi kusunga mbali yotsalayo.”​—The Jewish War, lotembenuzidwa ndi G. A. Williamson, mutu 20, tsamba 319.

Zowonadi, kukana malamulo ndi njira za Mulungu siiri njira yanzeru.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena