Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lff phunziro 58 mfundo 1-5
  • Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Yehova
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • FUFUZANI MOZAMA
  • ZOMWE TAPHUNZIRA
  • ONANI ZINANSO
  • Kupambana Chiyeso cha Kukhulupirika
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Zipembedzo Zonyenga Zimaphunzitsa Zabodza Zokhudza Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • ‘Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika’
    Yandikirani Yehova
  • Pewani Kulambira Konyenga!
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff phunziro 58 mfundo 1-5
Phunziro 58. Banja likudutsa gulu la anthu ampatuko omwe akukuwiza anthu amene akufika pamsonkhano wa Mboni za Yehova.

PHUNZIRO 58

Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Yehova

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

Akhristu oona salola kuti munthu kapena chinthu chilichonse chiwalepheretse kulambira Yehova. Sitikukayikira kuti nanunso mumaona choncho. Yehova amasangalala kwambiri akamaona kuti mukupitiriza kukhala okhulupirika kwa iye. (Werengani 1 Mbiri 28:9.) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingakulepheretseni kukhala wokhulupirika kwa Yehova? Nanga n’chiyani chingakuthandizeni kuti musasiye kukhala wokhulupirika kwa Yehova?

1. Kodi anthu ena angachititse bwanji kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova?

Anthu ena amafuna titasiya kutumikira Yehova. Kodi anthu amenewa angakhale ndani? Anthu ena amene anasiya kutumikira Yehova amanena mabodza okhudza gulu la Mulungu n’cholinga choti ifenso tisiye kutumikira Yehova. Anthu amenewa amatchedwa ampatuko. Komanso atsogoleri achipembedzo ena amafalitsa mabodza n’cholinga chofuna kusokoneza anthu omwe amangotengeka ndi zilizonse kuti asiye kutumikira Yehova. Tiyenera kupeweratu kutsutsana ndi anthu ampatuko, kuwerenga mabuku awo kapena zimene amalemba pa intaneti, kutsegula mawebusaiti awo kapenanso kuonera mavidiyo awo. Ponena za anthu amene amachititsa ena kuti asiye kutumikira Yehova mokhulupirika, Yesu anati: “Alekeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu. Chotero ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera m’dzenje.”​—Mateyu 15:14.

2. Kodi zimene timasankha pa moyo wathu zingachititse bwanji kuti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova?

Ngati timakonda Yehova tidzapewa kuchita chilichonse chokhudzana ndi chipembedzo chonyenga. Tidzapewa kukhala kapena kugwira ntchito m’gulu linalake lachipembedzo kapenanso kuchita chilichonse chokhudzana ndi chipembedzo chonyenga. Yehova amatichenjeza kuti: “Tulukani [mu Babulo Wamkulu] anthu anga.”​—Chivumbulutso 18:2, 4.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zimene mungachite kuti aliyense asakulepheretseni kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Muonanso mmene mungasonyezere kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova potuluka mu Babulo Wamkulu.

3. Samalani ndi aphunzitsi abodza

Kodi tiyenera kutani tikamva ena akunena zinthu zoipa zokhudza gulu la Yehova? Werengani Miyambo 14:15, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kuti tisamangokhulupirira zilizonse zomwe tamva?

Werengani 2 Yohane 9-11, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Malinga ndi lembali, kodi tizitani ndi anthu ampatuko?

  • Ngakhale kuti sitingacheze mwachindunji ndi anthu ampatuko, kodi tingasokonezedwe bwanji ndi zimene amaphunzitsa?

  • Kodi mukuganiza kuti Yehova angamve bwanji tikamamvetsera zinthu zabodza zokhudza iyeyo kapenanso gulu lake?

4. Muzikhalabe okhulupirika kwa Mulungu munthu wina akachita tchimo

Kodi tiyenera kuchita chiyani tikadziwa kuti munthu wina mumpingo wachita tchimo lalikulu? Onani mfundo yomwe ikupezeka mulamulo lomwe Mulungu anapereka kwa Aisiraeli. Werengani Levitiko 5:1.

Mogwirizana ndi vesili, tikadziwa kuti munthu wina wachita tchimo lalikulu, tiyenera kuuza akulu zomwe tikudziwa pa nkhaniyo. Komabe tisanachite zimenezi, tiyenera kuuza munthu wochimwayo kuti akaulule yekha kwa akulu za tchimo lakelo. Ndiyeno akakanika kuchita zimenezi, ifeyo tiyenera kusonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Yehova pokanena kwa akulu. Kodi tikachita zimenezi timasonyeza bwanji kuti tili ndi chikondi chokhulupirika kwa . . .

  • Yehova Mulungu?

  • munthu yemwe wachimwayo?

  • anthu ena onse mumpingo?

Zithunzi: M’bale akuthandiza m’bale mnzake yemwe wachita zoipa. 1. M’baleyo wakhudzidwa kwambiri ndi zimene waona pafoni yake. 2. Akuonetsa mnzakeyo zimene waonazo koma mnzakeyo sakugwirizana ndi zimene wachita pomuthandiza. 3. Akuonetsa akulu awiri zomwe anaona pafoni zija.

Ngati Mkhristu mnzanu wachita zoipa, muyenera kumuthandiza

5. Tulukani mu Babulo Wamkulu

Onerani VIDIYO.

VIDIYO: Tulukani mu Babulo Wamkulu! (5:06)

Chithunzi chamuvidiyo yakuti, ‘Tulukani mu Babulo Wamkulu!’ Wophunzira Baibulo akuchoka pamaso pa wansembe atasiya kugwira ntchito patchalitchi

Werengani Luka 4:8 ndi Chivumbulutso 18:4, 5, kenako muyankhe mafunso awa:

  • Kodi sindinafufutitse dzina langa kuchipembedzo chonyenga?

  • Kodi ndili m’bungwe lomwe limachita zinthu zogwirizana ndi chipembedzo chinachake?

  • Kodi ntchito yomwe ndimagwira imathandizira zochita za chipembedzo chonyenga?

  • Kodi pali zinthu zinanso zomwe ndingachite kuti ndisiyiretu kuchita zinthu zogwirizana ndi chipembedzo chonyenga?

  • Ngati funso linalake ndaliyankha kuti inde, kodi ndiyenera kusintha zinthu ziti?

Pa zinthu zonse zomwe takambiranazi muzionetsetsa kuti zomwe mungasankhe zizikuthandizani kukhala ndi chikumbumtima choyera komanso zizisonyeza kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova.

Mlongo ndi mwana wake akutuluka mushopu. Akudutsa mzimayi wina yemwe akupemphetsa ndalama zothandizira pa ntchito zachifundo za chipembedzo chinachake.

Kodi mungatani mutapemphedwa kuti mupereke ndalama zothandizira pa ntchito zachifundo za chipembedzo chinachake?

ZIMENE ENA AMANENA: “Ndikufunika kudziwa zimene ampatuko amanena zokhudza Mboni za Yehova kuti nditeteze choonadi.”

  • Kodi mukuona kuti ndi nzeru kuchita zimenezi? N’chifukwa chiyani mukutero?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Kuti tipitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova tiyenera kupewa kugwirizana ndi anthu amene amafuna kutisocheretsa.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kumvetsera zimene ampatuko amaphunzitsa?

  • Ngati tadziwa kuti m’bale kapena mlongo wachita tchimo lalikulu, kodi tiyenera kuchita chiyani?

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikumvera chenjezo lakuti tituluke m’chipembedzo chonyenga?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani zimene muyenera kuchita anthu ena akamanena zinthu zabodza zokhudza Mboni za Yehova.

“Kodi Mukudziwa Nkhani Yonse?” (Nsanja ya Olonda, August 2018)

Kodi mungadziwe bwanji kuti mabungwe kapena zinthu zinazake zikugwirizana ndi Babulo Wamkulu?

“Tizitumikira Yehova Mwakhama Kumapeto kwa ‘Masiku Otsirizawa’” (Nsanja ya Olonda, October 2019, ndime 16-18)

Kodi ndi zinthu ziti zimene anthu ena otsutsa achita pofuna kufooketsa chikhulupiriro chathu?

Samalani Ndi Anthu Achinyengo (9:32)

Munkhani yakuti, “Kuyambira Ndili Mwana Ndinkafunitsitsa Kudziwa Mulungu,” werengani nkhani ya wansembe wachipembedzo cha Chishinto yemwe anatuluka m’chipembedzo chonyenga.

“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, July 1, 2011)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena