Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Maso Anu Amayang’ana kwa Ndani?
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | July
    • 9. Kodi Yehova anapatsa Mose malangizo otani, koma iye anachita chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)

      9 Kodi Mose anachita zotani pa nthawi imeneyi? Iye anayang’ananso kwa Yehova kuti amupatse malangizo. Koma ulendo umenewu Yehova sanamuuze kuti amenye mwala. Iye anauza Mose kuti atenge ndodo yake, kuuza anthu kuti asonkhane pafupi ndi mwala, kenako alankhule ndi mwalawo. (Num. 20:6-8) Koma Mose sanalankhule ndi mwalawo. M’malomwake analankhula ndi anthu amene anasonkhanawo mokwiya kuti: “Tsopano tamverani anthu opanduka inu! Kodi tichite kukutulutsirani madzi m’thanthweli?” Kenako iye anamenya mwalawo osati kamodzi, koma kawiri.​—Num. 20:10, 11.

  • Kodi Maso Anu Amayang’ana kwa Ndani?
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | July
    • KODI CHIMENE MOSE ANALAKWITSA N’CHIYANI?

      12. Kodi n’kutheka kuti Yehova anakwiyira Mose ndi Aroni pa chifukwa china chiti?

      12 Koma pali chifukwa chinanso chomveka chimene chinachititsa kuti Yehova akwiyire Mose ndi Aroni. Kumbukirani kuti Mose anauza anthu aja kuti: “Kodi tichite kukutulutsirani madzi m’thanthweli?” Ponena kuti “tichite” kukutulutsirani, Mose ayenera kuti ankatanthauza iyeyo ndi Aroni. Ponena zimenezi, iye sanalemekeze Yehova monga wochititsa zozizwitsazo. Tikhoza kutsimikizira kuti mfundoyi ndi yoona tikaganizira zimene lemba la Salimo 106:32, 33 limanena. Paja limati: “Iwo anaputa mkwiyo pa madzi a ku Meriba, moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa. Iwo anamukwiyitsa ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalira bwino.”c (Num. 27:14) Kaya zinthu zinali bwanji, koma zimene Mose anachitazi zinachititsa kuti anthu asapereke ulemu woyenerera kwa Yehova. Choncho Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Amuna inu munapandukira malangizo anga.” (Num. 20:24) Apa zikuonekeratu kuti tchimo lawoli linali lalikulu kwambiri.

      13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chiweruzo chimene Yehova anapereka kwa Mose chinali choyenera komanso chachilungamo?

      13 Popeza Mose ndi Aroni anali ndi udindo wotsogolera anthu a Yehova, iwo ankayenera kuyankha pamaso pa Yehovayo. (Luka 12:48) Yehova anali atanena kale kuti m’badwo wonse wa Aisiraeli sudzalowa m’dziko la Kanani chifukwa chosamumvera. (Num. 14:26-30, 34) Choncho Yehova anachita zinthu moyenera komanso mwachilungamo popereka chiweruzo chomwecho kwa Mose pamene nayenso sanamumvere. Mofanana ndi Aisiraeli ena osamverawo, iye sanaloledwe kulowa m’Dziko Lolonjezedwa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena