Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Onani Ena Monga Momwe Yehova Amawaonera
    Nsanja ya Olonda—2003 | March 15
    • Onani Ena Monga Momwe Yehova Amawaonera

      “Yehova saona monga aona munthu.”​—1 SAMUELI 16:7.

      1, 2. Kodi mmene Yehova anaonera Eliabu zinasiyana bwanji ndi mmene Samueli anamuonera, ndipo tikuphunzirapo chiyani pamenepa?

      M’ZAKA za m’ma 1000 B.C.E., Yehova anatuma mneneri Samueli kuti akagwire ntchito yachinsinsi. Anauza mneneriyo kupita kunyumba ya munthu wina, dzina lake Jese kukadzoza mmodzi mwa ana ake aamuna kuti adzakhale mfumu ya Israyeli. Samueli ataona mwana woyamba wa Jese, dzina lake Eliabu, anakhulupirira kuti anapeza munthu amene Mulungu anasankha. Koma Yehova anati: “Usayang’ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza ine ndinam’kana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:6, 7) Samueli analephera kuona Eliabu monga momwe Yehova anali kumuonera.a

  • Onani Ena Monga Momwe Yehova Amawaonera
    Nsanja ya Olonda—2003 | March 15
    • a Patapita nthaŵi zinaonekeratu kuti Eliabu yemwe anali wokongolayo, analibe makhalidwe a mfumu yoyenera ya Israyeli. Pamene chimphona chachifilisiti, Goliati, chinaderera Aisrayeli kunkhondo, Eliabu ndi amuna ena achiisrayeli anachita mantha.​—1 Samueli 17:11, 28-30.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena