Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 31 tsamba 76-tsamba 77 ndime 2
  • Anabudula Ngala za Tirigu pa Tsiku la Sabata

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anabudula Ngala za Tirigu pa Tsiku la Sabata
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Kubudula Ngala pa Sabata
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kubudula Ngala pa Sabata
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Akhristu Ayenera Kusunga Sabata?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Sabata
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 31 tsamba 76-tsamba 77 ndime 2
Ophunzira a Yesu akubudula ndi kudya ngala za tirigu pa tsiku la Sabata

MUTU 31

Anabudula Ngala za Tirigu pa Tsiku la Sabata

MATEYU 12:1-8 MALIKO 2:23-28 LUKA 6:1-5

  • OPHUNZIRA ANABUDULA NGALA ZA TIRIGU PA TSIKU LA SABATA

  • YESU NDIYE “MBUYE WA SABATA”

Yesu ndi ophunzira ake anayamba ulendo wolowera kumpoto cha ku Galileya. Ayenera kuti anayenda ulendowu m’mwezi wa March kapena April chifukwa pa nthawiyi tirigu anali atacha. Ophunzira a Yesu anali ndi njala ndipo anayamba kubudula tirigu n’kumadya. Koma limeneli linali tsiku la Sabata ndipo Afarisi anaona zimene ophunzira a Yesuwo ankachita.

Kumbukirani kuti Ayuda ena a ku Yerusalemu ankafuna kupha Yesu pomuganizira kuti waphwanya Sabata. Koma pa nthawiyi, Afarisi anayamba kumuimba Yesu mlandu chifukwa cha zimene ophunzira ake anachita. Iwo ananena kuti: “Taona! Ophunzira ako akuchita zosayenera kuzichita pa sabata.”—Mateyu 12:2.

Afarisi ankanena kuti kubudula ngala n’kuzitikita m’manja n’cholinga choti udye, kunali ngati kugwira ntchito yokolola ndi kupuntha. (Ekisodo 34:21) Tsiku la Sabata linakhazikitsidwa kuti likhale tsiku losangalala komanso loti anthu azilimbikitsidwa akamaganizira zinthu zauzimu.Koma tsikuli linali lolemetsa chifukwa cha malamulo okhwima amene Afarisi anakhazikitsa okhudza ntchito zimene anthu ankayenera kugwira. Yesu anatsutsa maganizo awo olakwikawo powafotokozera zitsanzo zosonyeza kuti zimene ankachitazo zinali zosiyana ndi zimene Yehova Mulungu ankafuna kuti anthu azichita potsatira lamulo la Sabata.

Chitsanzo choyamba chimene Yesu anawauza ndi cha Davide ndi anyamata ake. Pa nthawi ina ali ndi njala, Davide ndi anyamata ake anakalowa mu chihema n’kudya mkate wachionetsero. Mikateyo inali itachotsedwa kale pamaso pa Yehova ndipo anali ataikapo ina yatsopano koma amene ankayenera kudya mikate yochotsedwayo anali ansembe okha. Koma chifukwa cha mmene zinthu zinalili, Davide ndi anyamata ake sanaimbidwe mlandu chifukwa chodya mikateyi.—Levitiko 24:5-9; 1 Samueli 21:1-6.

Pofotokoza chitsanzo chachiwiri, Yesu anati: “Kapena simunawerenge m’Chilamulo, kuti pa sabata ansembe m’kachisi anali kuchita zinthu mosalabadira kupatulika kwa tsiku la sabata koma anakhalabe osalakwa?” Ponena mawu amenewa Yesu ankatanthauza kuti ansembe ankapha nyama zoti apereke nsembe komanso ankagwira ntchito zina za pakachisi pa tsiku la Sabata. Kenako Yesu ananena kuti: “Koma ndikukuuzani kuti wamkulu kuposa kachisi ali pano.”—Mateyu 12:5, 6; Numeri 28:9.

Pofuna kuwathandiza kumvetsa bwino mfundo yake, Yesu anagwiritsa ntchito Malemba ndipo ananena kuti: “Ngati mukanamvetsa tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe,’ simukanaweruza anthu osalakwa.” Kenako anamaliza ndi kuti: “Pakuti Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa sabata.” Pamenepa Yesu ankanena za Ufumu wake womwe udzalamulire mwamtendere kwa zaka 1000.—Mateyu 12:7, 8; Hoseya 6:6.

Kwa zaka zambiri, anthu akhala akuvutika kwambiri ndi nkhondo komanso zinthu zankhanza zomwe zimachitika chifukwa chakuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli. Zimenezi zidzakhalatu zosiyana kwambiri ndi zimene zidzachitike tikadzalowa mu Sabata lalikulu, lomwe ndi ulamuliro wa Khristu. Pa nthawi imeneyi tidzapumula ku mavuto athu onse. Zimenezi ndi zimene takhala tikuziyembekezera kwa nthawi yaitali.

  • Kodi Afarisi anaimba mlandu wotani ophunzira a Yesu ndipo n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?

  • Kodi Yesu anathandiza bwanji Afarisi kuti akhale ndi maganizo abwino?

  • N’chifukwa chiyani Yesu amatchedwa “Mbuye wa Sabata”?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena