Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Anapemphera Kuchokera Pansi pa Mtima
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
    • 15, 16. (a) Kodi chinachitika n’chiyani Hana atapita kuchihema komanso atauza Yehova zakukhosi kwake? (b) Kodi tingatsatire bwanji chitsanzo cha Hana tikamavutika maganizo ndi zinazake?

      15 Kodi chinachitika n’chiyani Hana atapita kuchihema komanso atamuuza Yehova zakukhosi kwake? Baibulo limati: “Mkaziyo anachoka ndi kupita kukadya, ndipo sanakhalenso ndi nkhawa.” (1 Sam. 1:18) Ndipo Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu limati: “Nkhope yake siinakhalanso yachisoni.” Hana atauza Yehova nkhawa zake, mtima wake unakhala m’malo. Zinali ngati ankalemedwa ndi katundu winawake, ndiyeno watulira katunduyo Atate wakumwamba amene ndi wamphamvu kwambiri kuposa iye. (Werengani Salimo 55:22.) Kodi pali vuto limene Mulungu angalephere kulisenza? Ayi, palibe ngakhale limodzi.

      16 Tikaona kuti mavuto atikulira, ndi bwino kutsatira chitsanzo cha Hana. Tiyenera kulankhula momasuka kwa Mulungu amene Baibulo limamutchula kuti “Wakumva pemphero.” (Sal. 65:2) Tikamapemphera tili ndi chikhulupiriro, nafenso tidzaona kuti nkhawa zathu zatha ndipo tapeza “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—Afil. 4:6, 7.

  • Anapemphera Kuchokera Pansi pa Mtima
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
    • 18 Kodi Penina anazindikira liti kuti Hana sakukhumudwanso ndi zimene akumuchitira? Baibulo silinena, koma mawu akuti “sanakhalenso ndi nkhawa” akusonyeza kuti Hana atangopemphera, anayamba kuoneka wosangalala. Mulimonse mmene zinalili, pasanapite nthawi Penina anazindikira kuti zochita zake zofuna kukwiyitsa Hana sizikugwiranso ntchito. Kuyambira pamenepa, Baibulo silitchulanso dzina la Penina.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena