-
Anapemphera Kuchokera Pansi pa MtimaTsanzirani Chikhulupiriro Chawo
-
-
9. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Hana anachita popitabe ku Silo ngakhale kuti ankadziwa zoti mkazi mnzake azikamunyoza?
9 M’mawa wa tsiku la ulendoli, banja lonse la Elikana, linali pakalikiliki kukonzekera. Banja lalikululi linkakonzekera ulendo wa makilomita oposa 30 wopita ku Silo, kudutsa m’mapiri a ku Efraimu.b Kwa munthu woyenda pansi, ulendowu unali wa tsiku limodzi kapena masiku awiri. Hana ankadziwa kuti mkazi mnzake azikamunyoza, koma anapitabe. Pamenepatu iye anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu olambira Mulungu masiku ano. Si bwino kulola khalidwe loipa la anthu ena kutilepheretsa kulambira Mulungu. Ngati titachita zimenezi zingatilepheretse kulandira madalitso amene angatithandize kupirira mavuto.
-
-
Anapemphera Kuchokera Pansi pa MtimaTsanzirani Chikhulupiriro Chawo
-
-
b Mtunda umenewu tikutengera kuti mwina kwawo kwa Elikana kunali ku Rama, komwe m’nthawi ya Yesu kunkadziwika ndi dzina lakuti Arimateya.
-