-
Anauza Mulungu Zakukhosi KwakeNsanja ya Olonda—2010 | July 1
-
-
PANTHAWI ina Hana anali kalikiliki kukonzekera ulendo ndipo zimenezi zinathandiza kuti aiwaleko mavuto ake. Ulendowu unali wosangalatsa kwambiri. Chaka chilichonse, mwamuna wake Elikana ankakonda kupita ndi banja lake lonse kukalambira kuchihema ku Silo. Yehova ankafuna kuti zochitika zimenezi zizikhala zosangalatsa. (Deuteronomo 16:15) Ndipo ziyenera kuti Hana kuyambira ali mwana wamng’ono ankasangalala kukachita nawo misonkhano imeneyi. Koma zinthu pamoyo wake zinali zisakuyenda bwino.
-
-
Anauza Mulungu Zakukhosi KwakeNsanja ya Olonda—2010 | July 1
-
-
M’mamawa tsiku la ulendoli, banja lonse la Elikana, ndi ana omwe, linali pakalikiliki kukonzekera ulendo. Banjali limene linali lalikulu linali kukonzekera kuyenda ulendo wa makilomita oposa 30 wopita ku Silo, kudutsa m’mapiri a ku Efraimu.c Kwa munthu woyenda pansi, ulendowu unali wa tsiku limodzi kapena masiku awiri. Hana ankadziwa kuti mkazi mnzakeyo azimunyoza pa ulendowo, koma Hana anapitabe. Choncho, iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu olambira Mulungu masiku ano. Si bwino kuti khalidwe loipa la anthu ena litilepheretse kulambira Mulungu. Ngati titasiya kulambira Mulungu, ndiye kuti sitingalandire madalitso amene angatithandize kupirira mavuto.
-
-
Anauza Mulungu Zakukhosi KwakeNsanja ya Olonda—2010 | July 1
-
-
c Mtunda umenewu tikutengera kuti mwina kwawo kwa Elikana kunali ku Rama, komwe m’nthawi ya Yesu kunkadziwika ndi dzina lakuti Arimateya.
-