Kuyamikira Misonkhano Yachikristu
“Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi.”—AHEBRI 10:24, 25.
1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji ndi mwaŵi kupezeka pamsonkhano wa Akristu oona? (b) Kodi Yesu amakhalapo motani pamisonkhano ya otsatira ake?
ULI mwaŵi waukulu chotani nanga kupezeka pamsonkhano wachikristu, kaya ukhale wa alambiri a Yehova osakwanira khumi kapena akhale zikwi zingapo, popeza Yesu anati: “Kumene kuli aŵiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndili komweko pakati pawo.” (Mateyu 18:20) Nzoona kuti popanga lonjezo limenelo, Yesu anali kunena za nkhani zachiweruzo zofunika kusamaliridwa bwino ndi amene akutsogolera mumpingo. (Mateyu 18:15-19) Koma kodi mawu a Yesu angagwirenso ntchito monga pulinsipulo lokhudza misonkhano yonse yachikristu imene imatsegulidwa ndi kutsekedwa ndi pemphero m’dzina lake? Inde. Kumbukirani kuti pamene Yesu anatuma otsatira ake kukachita ntchito yopanga ophunzira, iye analonjeza kuti: “Onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”—Mateyu 28:20.
2 Sitingakayikire kuti Mutu wa mpingo wachikristu, Ambuye Yesu Kristu, amasamala kwambiri za misonkhano yonse ya otsatira ake okhulupirika. Ndiponso, ndife otsimikizira kuti amakhala nawo mwa mzimu woyera wa Mulungu. (Machitidwe 2:33; Chivumbulutso 5:6) Nayenso Yehova Mulungu amasamala za kusonkhana kwathu pamodzi. Chifuno chachikulu cha misonkhano imeneyi ndicho kupereka chitamando kwa Mulungu “m’masonkhano.” (Salmo 26:12) Kufika kwathu pamisonkhano yampingo kuli umboni wakuti timamkonda.
3. Kodi timayamikira misonkhano yachikristu pazifukwa zofunika ziti?
3 Pali zifukwa zinanso zabwino zimene timayamikirira misonkhano yachikristu. Yesu Kristu asanachoke padziko lapansi, anaika ophunzira ake odzozedwa kukhala monga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wopereka chakudya chauzimu panthaŵi yake ku banja lachikhulupiriro. (Mateyu 24:45) Kudyetsedwa kwauzimu kumeneku kumachitika makamaka pamisonkhano yampingo pamodzinso ndi pamisonkhano yaikulu—masiku a msonkhano wapadera, misonkhano yadera, ndi misonkhano yachigawo. Ambuye Yesu Kristu amatsogoza kapolo wokhulupirika ameneyu popereka chidziŵitso chofunika kwambiri pamisonkhano imeneyi kwa onse amene akufuna kupulumuka mapeto a dongosolo loipali ndi kupeza moyo m’dziko latsopano lolungama la Mulungu.
4. Kodi ‘nchizoloŵezi’ changozi chiti chimene chinatchulidwa m’Baibulo, ndipo nchiyani chimene chidzatithandizira kuchipeŵa?
4 Choncho, palibe Mkristu amene angafune kuyamba chizoloŵezi changozi chotchulidwa ndi mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Kusinkhasinkha ponena za mwaŵi ndi mapindu a kupezeka pamisonkhano yachikristu kudzatithandiza kuchirikiza misonkhano imeneyi mokhulupirika ndiponso ndi mtima wonse.
Misonkhano Yomangirira
5. (a) Kodi zolankhula zathu pamisonkhano ziyenera kuchititsa chiyani? (b) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuzengereza kuitanira okondwerera kumisonkhano?
5 Popeza kuti Akristu amapempherera mzimu woyera wa Yehova kuti uzigwira ntchito pamisonkhano yachikristu, munthu aliyense wopezekapo amayenera kuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi mzimuwo ndi ‘kusamvetsa chisoni mzimu woyera wa Mulungu.’ (Aefeso 4:30) Pamene mtumwi Paulo analemba mawu ouziridwa amenewo, iye anali kunena za kufunika kwa kulankhula zinthu zabwino. Zolankhula zathu nthaŵi zonse ziyenera kukhala ‘zomangirira monga mofunika ndizo, kuti zipatse chisomo kwa iwo akumva.’ (Aefeso 4:29) Zimenezi nzofunika kwambiri makamaka pamisonkhano yachikristu. M’kalata yake yopita kwa Akorinto, Paulo anagogomezera kuti misonkhano iyenera kukhala yomangirira, yolangiza, ndiponso yolimbikitsa. (1 Akorinto 14:5, 12, 19, 26, 31) Onse opezekapo amapindula nayo misonkhano imeneyo, kuphatikizapo opezekapo atsopano, amene pomalizira pake anganene kuti: “Mulungu ali ndithu mwa inu.” (1 Akorinto 14:25) Pachifukwa chimenechi, sitiyenera kuzengereza kuitanira okondwerera kuti adzasonkhane nafe, popeza kuteroko kudzawathandiza kupita patsogolo mwauzimu mwamsanga.
6. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zimathandizira misonkhano kukhala yomangirira?
6 Onse amene amapatsidwa nkhani, kufunsa ena papulatifomu, kapena zitsanzo pamsonkhano wachikristu amayenera kuonetsetsa kuti zimene akulankhula nzomangirira ndiponso nzogwirizana ndi Mawu olembedwa a Mulungu, Baibulo. Kuwonjezera pa kulankhula zinthu zolongosoka, tiyenera kusonyeza malingaliro ndi kukhudzika mtima zimene zili zogwirizana ndi mikhalidwe yachikondi ya Mulungu ndi Kristu. Ngati onse amene amakhala ndi mbali paprogramu ya msonkhano amadziŵa kuti ayenera kusonyeza ‘chipatso cha mzimu wa Mulungu,’ monga chimwemwe, kuleza mtima, ndi chikhulupiriro, ndiye kuti onse opezekapo adzamvadi kukhala omangiriridwa.—Agalatiya 5:22, 23.
7. Kodi opezekapo onse angathandizire motani kuti msonkhano ukhale womangirira?
7 Ngakhale kuti ndi ochepa okha amene angakhale ndi mbali m’programu pamisonkhano yampingo, onse opezekapo angachititse msonkhanowo kukhala womangirira. Kaŵirikaŵiri pamakhala mpata woti omvetsera ayankhe mafunso. Imeneyi imakhala nthaŵi yolengeza chikhulupiriro chathu poyera. (Aroma 10:9) Sitiyenera kuigwiritsira ntchito monga mpata wochirikizira malingaliro athu aumwini, kudzitukumula ponena za zimene takwaniritsa, kapena kusuliza wokhulupirira mnzathu. Kodi zimenezo sizingachititse chisoni mzimu wa Mulungu? Kusiyana maganizo ndi okhulupirira anzathu kumasamalidwa bwino mwamtseri ndiponso mwachikondi. Baibulo limati: “Mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.” (Aefeso 4:32) Ndi mpata waukulu chotani nanga umene misonkhano yachikristu imatipatsa kuti tigwiritsire ntchito uphungu wabwinowu! Pofuna kuchita zimenezi, ambiri amafika msanga pamisonkhano ndipo sachoka msanga misonkhanoyo itatha. Zimenezi zimathandizanso okondwerera achatsopano, amene amafunitsitsa kumva kukhala olandiridwa bwino. Chotero Akristu onse odzipatulira ali ndi udindo wopangitsa misonkhano kukhala yomangirira mwa ‘kuganizirana wina ndi mnzake ndi kufulumizana kuchikondano ndi ntchito zabwino.’
Konzekerani Bwino
8. (a) Kodi nkuvutikira kotani koyamikirika kumene ena amapanga kuti apezeke pamisonkhano? (b) Kodi Yehova amapereka chitsanzo chotani monga mbusa?
8 Ngakhale kuti ena amapezeka pamisonkhano yachikristu mosavutikira, ena amavutikira nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, mayi wina wachikristu amene amagwira ntchito yolembedwa kuti azithandiza kupeza zosoŵa za banja lake, nthaŵi zambiri amakhala wotopa atachoka kuntchitoko. Kenako mwina amayenera kukonza chakudya ndi kuthandiza ana ake kukonzekera kupita kumsonkhano. Akristu ena mwina amayenda ulendo wautali kuti afike kumisonkhano, kapena angakhale ndi zofooka za m’thupi kapena ukalamba. Ndithudi, Yehova Mulungu amadziŵa bwino za mkhalidwe wa aliyense wopezeka pamsonkhano, monga momwe mbusa wachikondi amamvetsetsera zofunika zapadera za nkhosa iliyonse ya m’gulu lake la nkhosa. Baibulo limati: “Iye [Yehova] adzadyetsa zoŵeta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake, nadzawatengera pachifuŵa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.”—Yesaya 40:11.
9, 10. Kodi ndi motani mmene tingapindulire kwambiri ndi misonkhano?
9 Awo amene nthaŵi zonse amavutikira kwambiri kuti azipezeka pamisonkhano angamakhale ndi nthaŵi yochepa yoti akonzekere nkhani zimene zidzakambidwa. Kutsatira ndandanda ya mlungu ndi mlungu ya kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kumachititsa kupezeka pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki kukhala kopindulitsa kwambiri. Momwemonso, kukonzekera pasadakhale misonkhano inanso, monga Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi Phunziro la Buku la Mpingo, kumapangitsa misonkhanoyi kukhala yopindulitsa kwambiri. Mwa kuŵerenga pasadakhale nkhani zokaphunziridwa ndiponso mwa kusinkhasinkha pa ena mwa malemba a m’Baibulo osonyezedwa, awo amene ali ndi maudindo apabanja ofuna nthaŵi yaikulu adzakhala okonzekera bwino kukatengamo mbali mokwanira pamakambitsirano ofunika a Baibulo ameneŵa.
10 Ena amene sakhala otanganika kwambiri, angakhale ndi nthaŵi yaikulu yokonzekerera misonkhano. Mwachitsanzo, akhoza kufufuza mfundo zowonjezereka zokhudza malemba amene asonyezedwa koma amene sanagwidwe mawu. Chotero onse angakonzekere kuti akapindule koposa pamisonkhano ndiponso kuti akatengemo mbali mokwanira pomangirira mpingo mwa nkhani ndi ndemanga zawo. Mwa kukhala okonzekera bwino, akulu ndi atumiki otumikira adzapereka chitsanzo chabwino cha kupereka mayankho aafupi ndiponso olunjika. Chifukwa chakuti amalemekeza makonzedwe a Yehova, opezekapowo adzapeŵa kuchita kalikonse komwe kangasokoneze misonkhano pamene ikuchitika.—1 Petro 5:3.
11. Kodi nchifukwa ninji kudzilanga nkofunika kuti tikonzekere misonkhano?
11 Zochita ndiponso zosangulutsa zosafunika kwenikweni pathanzi lathu lauzimu zingatidyere nthaŵi kwambiri. Ngati zili choncho, tiyenera kudzifufuza ndi ‘kusakhala opusa’ ponena za mmene timagwiritsirira ntchito nthaŵi yathu. (Aefeso 5:17) Cholinga chathu chiyenera kukhala ‘kuombola nthaŵi’ pazinthu zosafunika kwenikweni kuti tithere nthaŵi yaikulu paphunziro laumwini la Baibulo ndi kukonzekera misonkhano, ndiponso mu utumiki wa Ufumu. (Aefeso 5:16, NW) Zoonadi, si nthaŵi zonse pamene zimenezi zimakhala zapafupi ndipo zimafuna kudzilanga. Achinyamata amene amasamala za zimenezi akuyala maziko abwino kaamba ka kupita patsogolo kwamtsogolo. Paulo analembera mnzake wachinyamatayo Timoteo kuti: “Izi [uphungu wa Paulo kwa Timoteo] uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.”—1 Timoteo 4:15.
Zitsanzo za m’Mawu a Mulungu
12. Kodi nchitsanzo chabwino kwambiri chiti chimene banja la Samueli linapereka?
12 Talingalirani za chitsanzo chabwino choperekedwa ndi banja la Samueli, limene nthaŵi zonse linali kutengamo mbali m’makonzedwe a kusonkhana ndi okhulupirira anzawo pamene chihema cha Mulungu chinali ku Silo. Amuna okha ndiwo anali kufunikira kupita kumadyerero apachaka amenewo. Koma atate ake a Samueli, Elikana, anali kutenga banja lake lonse pamene ‘anakwera chaka ndi chaka kutuluka m’mudzi mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Mulungu wa makamu m’Silo.’ (1 Samueli 1:3-5) Mudzi wakwawo kwa Samueli, Ramatayimu Zofimu, uyenera kuti unali pafupi ndi gombe la ku Rentis wamakono mtsinde mwa mapiri ku “dziko la mapiri la Efraimu.” (1 Samueli 1:1) Choncho ulendo wopita ku Silo uyenera kuti unali ulendo wamakilomita 30, ulendo wotopetsa kwambiri masikuwo. Ndizo zimene banja la Elikana linachita mokhulupirika “chaka ndi chaka, popita [iwo] ku nyumba ya Yehova.”—1 Samueli 1:7.
13. Kodi Ayuda okhulupirika panthaŵi imene Yesu anali padziko lapansi anapereka chitsanzo chotani?
13 Yesu nayenso anakulira m’banja lalikulu. Chaka chilichonse banjalo linali kuyenda ulendo wamakilomita pafupifupi 100 kuchokera ku Nazarete kuloŵera chakummwera ku Yerusalemu kukapezeka pamadyerero a Paskha. Pali njira ziŵiri zimene mwina anatsata. Njira yolunjika kwambiri inali kutsetserekera m’Chigwa cha Megido ndiyeno kukwera chitunda cha mamita pafupifupi 600 kudutsa m’chigawo cha Asamariya ndiyeno kupitirizabe kufika ku Yerusalemu. Njira inanso yotchuka ndiyo ija imene Yesu anatsata paulendo wake womaliza wa ku Yerusalemu mu 33 C.E. Poyenda m’njira imeneyi iwo anali kutsetserekera m’Chigwa cha Yordano chakuya kuposa pa sea level mpaka atafika “ku maiko a ku Yudeya . . . kutsidya lija la Yordano.” (Marko 10:1) Kuchokera pamenepa, ‘njira yokwera kumka ku Yerusalemu’ ndiyo mtunda wamakilomita pafupifupi 30, ndipo penapake pali chitunda cha mamita 1,100. (Marko 10:32) Nthaŵi zonse, makamu a anthu okhulupirika okapezeka pamadyerero anali kuyenda ulendo wovutawo kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu. (Luka 2:44) Ndi chitsanzo chabwino chotani nanga kwa atumiki a Yehova m’maiko otukuka lerolino, ambiri amene amafika pamisonkhano yachikristu mosavutikira chifukwa cha mitundu yamakono ya zoyendera!
14, 15. (a) Kodi Ana anapereka chitsanzo chotani? (b) Kodi tingaphunzirenji pa mzimu wabwino umene achatsopano opezeka pamisonkhano amasonyeza?
14 Chitsanzo china ndi chija cha Ana, mkazi wamasiye wazaka 84 zakubadwa. Baibulo limanena kuti “sanachoka ku Kachisi.” (Luka 2:37) Komanso, Ana anali ndi chikondi pa ena. Ataona Yesu wakhandayo ndipo atamva kuti ndiye Mesiya wolonjezedwayo, kodi iye anachitanji? Anayamika Mulungu “nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu.” (Luka 2:38) Ndi mzimu wabwino chotani nanga, chitsanzo kwa Akristu lerolino!
15 Inde, kupezeka pamisonkhano ndi kutengamo mbali kuyenera kukhala kosangalatsa kwambiri kwakuti, monga Ana, tizifuna kupezekapo nthaŵi zonse osaphonya. Ndi mmene achatsopano ambiri amamverera. Pokhala atatuluka mumdima kuloŵa m’kuunika kwakukulu kwa Mulungu, iwo amafuna kuphunzira zonse zimene angaphunzire, ndipo ambiri amasonyeza changu chachikulu pamisonkhano yachikristu. Komanso, amene akhala m’choonadi kwa nthaŵi yaitali amayenera kudzitetezera kuti ‘asataye chikondi chawo choyamba.’ (Chivumbulutso 2:4) Matenda aakulu kapena zinthu zina zosapeŵeka zingachititse munthu kusapezeka pamisonkhano nthaŵi zina. Koma sitiyenera konse kulola kukonda chuma, zosangulutsa, kapena kusoŵa chidwi kutichititsa kuti tikhale osakonzeka, amphwayi, kapena osonkhana modumphadumpha.—Luka 8:14.
Chitsanzo Chabwino Koposa
16, 17. (a) Kodi Yesu anali ndi mzimu wotani ponena za misonkhano yauzimu? (b) Kodi nchizoloŵezi chabwino chiti chimene Akristu onse amayenera kutsatira?
16 Yesu anapereka chitsanzo chabwino koposa posonyeza chiyamikiro cha misonkhano yauzimu. Pamene anali wamng’ono, wazaka 12 zakubadwa, iye anasonyeza kukonda kwake nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Iye anasoŵa koma pambuyo pake makolo ake anampeza akukambitsirana za Mawu a Mulungu ndi aphunzitsi m’kachisi. Ataona kuti makolo ake anali ndi nkhaŵa, Yesu anawafunsa mwaulemu kuti: “Simunadziŵa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m’zake za Atate wanga?” (Luka 2:49) Mogonjera, Yesu wachinyamatayo anabwerera ndi makolo ake ku Nazarete. Kumeneko anapitirizabe kusonyeza kukonda kwake misonkhano ya kulambira mwa kupezeka pa sunagoge nthaŵi zonse. Choncho, atayamba utumiki wake, Baibulo limasimba kuti: ‘Anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analoŵa m’sunagoge, monga anazoloŵera, naimiriramo kuŵerenga m’kalata.’ Yesu ataŵerenga ndi kufotokoza Yesaya 61:1, 2, omvetsera ‘anazizwa ndi mawu achisomo akutuluka mkamwa mwake.’—Luka 4:16, 22.
17 Misonkhano yachikristu lerolino imatsatira makonzedwe ofunika ameneŵa. Msonkhano utatsegulidwa ndi nyimbo yachitamando ndi pemphero, mavesi a m’Baibulo (kapena mavesi ogwidwa mawu m’phunziro la Baibulo) amaŵerengedwa ndi kufotokozedwa. Akristu oona ayenera kutsatira chizoloŵezi chabwino cha Yesu Kristu. Monga momwe mikhalidwe yawo ikuwalolera, iwo amasangalala kupezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse.
Zitsanzo Zamakono
18, 19. Kodi abale m’maiko osatukuka kwenikweni apereka zitsanzo zabwino kwambiri zotani ponena za misonkhano yampingo ndi misonkhano yaikulu?
18 M’maiko osatukuka kwenikweni a dziko lapansi, abale ndi alongo athu ambiri amapereka chitsanzo chabwino cha kuyamikira misonkhano yachikristu. Ku Mozambique woyang’anira chigawo, Orlando, ndi mkazi wake Amélia, anatenga maola 45 akumayenda pansi mtunda wa makilomita pafupifupi 90 kukwera phiri lina lalitali kuti akatumikire pamsonkhano wina waukulu. Ndiyeno anayenera kuyendanso mtunda womwewo pobwerera kuti akatumikire pamsonkhano waukulu wotsatira. Orlando modzichepetsa anasimba kuti: “Tinaona monga kuti palibe chimene tachita titakumana ndi abale ochokera ku Mpingo wa Bawa. Kuti afike pamsonkhanowo ndi kubwereranso kwawo anayenera kuyenda ulendo wapansi wa masiku asanu ndi limodzi wamakilomita pafupifupi 400, ndipo pakati pawo panali mbale wazaka 60 zakubadwa!”
19 Bwanji ponena za kuyamikira misonkhano yampingo ya mlungu ndi mlungu? Kashwashwa Njamba ndi mlongo wathanzi lofooka wazaka zakubadwa za m’ma 70. Iye amakhala m’mudzi waung’ono wa Kaisososi, pamtunda wamakilomita pafupifupi asanu kuchokera ku Nyumba ya Ufumu ku Rundu, Namibia. Kuti apezeke pamisonkhano, amayenda ulendo wamakilomita khumi kupita ndi kubwera ndipo amatsata njira ya m’thengo. Ena afwambidwa poyenda m’njira imeneyi, koma Kashwashwa amafikabe pamisonkhano. Misonkhano yambiri imachitidwa m’zinenero zimene sazidziŵa. Choncho kodi amapindula motani atapezekapo? “Mwa kutsatira malemba,” akutero Kashwashwa, “ndimayesa kuona kuti nkhaniyo ikunena za chiyani.” Koma sadziŵa kuŵerenga, choncho amawatsatira motani malemba? “Ndimatchera khutu ku malemba amene ndimawadziŵa pamtima,” akuyankha motero. Ndipo kwazaka zambiri, iye waloŵeza malemba ambiri ndithu pamtima. Kuti awongolere luso lake la kugwiritsira ntchito Baibulo, amapita kusukulu yophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga yolinganizidwa ndi mpingo. “Kusonkhana kumandisangalatsa,” iye akutero. “Nthaŵi zonse timaphunzira zinthu zatsopano. Ndimasangalala kwambiri kuyanjana ndi abale ndi alongo. Ngakhale kuti si onse amene ndingalankhule nawo, nthaŵi zonse amandipatsa moni. Ndipo chofunika kwambiri nchakuti ndikudziŵa kuti mwa kupezeka pamisonkhano, ndimasangalatsa mtima wa Yehova.”
20. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuleka kusonkhana kwathu kwachikristu?
20 Monga Kashwashwa, alambiri a Yehova mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi amayamikira chifukwa cha misonkhano yachikristu. Pamene dziko la Satana likupita kuchiwonongeko chake, sitiyenera kusiya kusonkhana kwathu pamodzi. M’malo mwake, tiyeni tikhalebe ogalamuka mwauzimu ndipo tisonyeze kuti timaiyamikira kwambiri misonkhano yampingo, ndi misonkhano yaikulu. Zimenezo sizidzangosangalatsa mtima wa Yehova wokha komanso zidzatipindulitsa kwambiri pamene tilandira nawo maphunziro a Mulungu otsogolera ku moyo wamuyaya.—Miyambo 27:11; Yesaya 48:17, 18; Marko 13:35-37.
Mafunso Obwereza
◻ Kodi nchifukwa ninji ndi mwaŵi kupezeka pamisonkhano yachikristu?
◻ Kodi onse opezekapo angathandizire motani kuti msonkhano ukhale womangirira?
◻ Kodi Yesu Kristu anapereka chitsanzo chabwino koposa chotani?
◻ Kodi tingaphunzirepo phunziro lotani pa abale a m’maiko osatukuka kwenikweni?
[Bokosi patsamba 17]
Amayamikira Misonkhano ya Mlungu ndi Mlungu
Anthu mamiliyoni ambiri amakhala m’mizinda yodzala ndi umphaŵi ndi upandu. Mosasamala kanthu za mikhalidwe imeneyi, Akristu oona amene ali pakati pawo amasonyeza kuti amayamikira zedi misonkhano yachikristu. Mkulu wina amene akutumikira mu umodzi wa mipingo ya m’Soweto ku Gauteng, South Africa, anasimba kuti: “Mumpingo mmene muli Mboni ndi ofalitsa osabatizidwa 60, timakhala ndi anthu opezeka pamisonkhano yathu pakati pa 70 ndi 80, ndipo nthaŵi zina kuposa pamenepo. Ngakhale kuti abale ndi alongo samachokera kutali, mkhalidwe m’mbali imeneyi ya Soweto ngwoipa kwambiri. Mbale wina anambaya kumsana pamene anali kupita kumsonkhano. Alongo aŵiri anagwidwa ncholinga chowalanda katundu. Koma zimenezi sizimawaletsa kufika pamisonkhano. Lamlungu lililonse titatseka msonkhano ndi pemphero, timayeseza nyimbo kwa mphindi zochepa. Pafupifupi 95 peresenti ya opezekapo amatsalira ndi kuimba nyimbo zonse zodzaimba pamisonkhano ya mlungu wotsatira. Zimenezi zimathandiza achatsopano kuphunzira nyimbozo ndi kuimba nawo.”
Okhala kumidzi ali ndi zopinga zina, monga mitunda yaitali imene amayenda kuti akapezeke pamisonkhano katatu pamlungu. Banja lina lokondwerera limakhala pamtunda wa makilomita 15 kuchokera ku Nyumba ya Ufumu ku Lobatse, Botswana. Kwa chaka chonse chathachi, iwo akhala akupezeka pamisonkhano mokhazikika pamodzi ndi ana awo aŵiri. Mwamuna amasoka nsapato kuti achirikize banja. Mkazi wake amagulitsa iti ndi iti kuti athandizire kupeza ndalama za banja zolipirira ulendo wopita kumisonkhano ndi kubwerako.
Madzulo ena m’dzinja chaposachedwapa, pambuyo pa msonkhano wa woyang’anira dera, banja limeneli linapeza kuti pasiteshoni panalibe mabasi nthaŵi ya 9 koloko madzulo. Mabasi anali atasiya msanga kuyenda chifukwa cha mkuntho. Wapolisi wina anaima ndi galimoto lake ndi kuwafunsa zimene anali kuchita. Atamva za vuto lawo, anawachitira chifundo ndipo anawanyamula mpaka kunyumba kwawo, ulendo wa makilomita 15 umenewo. Mkaziyo, amene ali wofalitsa wosabatizidwa, anati kwa mwamuna wake: “Mwaonatu, ngati tiika misonkhano patsogolo, nthaŵi zonse Yehova amathandiza.” Tsopano mwamuna wake wanena kuti nayenso akufuna kukhala mlaliki wa uthenga wabwino.
[Chithunzi patsamba 18]
Mboni monga izi za ku Romania zimapereka chitsanzo chabwino cha kuyamikira misonkhano yachikristu