-
Analimbikitsidwa ndi Mulungu WakeTsanzirani Chikhulupiriro Chawo
-
-
20, 21. (a) Fotokozani zimene Eliya anaona ataima pakhomo la phanga paphiri la Horebe. (b) Kodi zimene Yehova anasonyeza Eliya zinamuthandiza bwanji?
20 Eliya atafotokoza zinthu zimene zinkamuchititsa mantha ndiponso kumudetsa nkhawa, kodi Yehova anamuthandiza bwanji? Mngelo uja anauza Eliya kuti aimirire pakhomo la phanga limene anabisalako. Eliya anachitadi zimenezi ngakhale kuti sankadziwa kuti chichitike n’chiyani. Mwadzidzidzi pamalopo panawomba chimphepo. Payenera kuti panamveka chiphokoso chifukwa chimphepocho chinali champhamvu kwambiri moti chinang’amba mapiri ndi matanthwe. Ndiyeno yerekezerani kuti mukuona Eliya akuyesetsa kuphimba nkhope yake kwinaku atagwira mwamphamvu chovala chake chokhuthala chaubweya chomwe chinkauluzika ndi chimphepocho. Iye akuyesetsanso kuti aime bwinobwino n’cholinga chakuti asagwe chifukwa pamalo amene waimawo nthaka ikugwedezeka chifukwa cha chivomezi. Koma chimphepo ndiponso chivomezi chija chitangotha, pakubuka moto ndipo izi zikuchititsa Eliya kubwerera kuphanga pothawa kutentha kwa motowo.—1 Maf. 19:11, 12.
Yehova anagwiritsa ntchito mphamvu zake zochititsa mantha polimbikitsa Eliya
21 Nkhaniyi imafotokoza kuti Yehova sanali mu zinthu zachilengedwe monga mphepo, chivomezi ndiponso moto zimene Eliya anaonazi. Eliya ankadziwa kuti Yehova si mulungu wongoganiziridwa kuti alipo ngati mmene zinalili ndi Baala amene anthu omwe ankamulambira ankamutamanda kuti ndi woyendetsa mitambo, kapena kuti wobweretsa mvula. Mphamvu zochititsa mantha zimene zili m’zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe, zinachokera kwa Yehova. Koma iye ndi wamkulu kwambiri kuposa chilichonse chimene analenga. Ndipo ngakhale kumwamba kumene timaonaku, Yehova sangakwaneko. (1 Maf. 8:27) Ndiyeno kodi zimene Eliya anaonazi zinamuthandiza bwanji? Kumbukirani kuti Eliya anapezeka pamalo amenewa chifukwa chochita mantha. Popeza kuti Yehova Mulungu, yemwe ali ndi mphamvu zimenezi, anali kumbali ya Eliya, panalibe chifukwa chakuti iye aziopa Ahabu ndi Yezebeli.—Werengani Salimo 118:6.
22. (a) Kodi “mawu achifatse apansipansi” anatsimikizira bwanji Eliya kuti ndi munthu wofunika? (b) Kodi “mawu achifatse apansipansi” ayenera kuti anali a ndani? (Onani mawu a m’munsi.)
22 Moto uja utapita, pamalopo panakhala bata ndipo Eliya anamva “mawu achifatse apansipansi.” Mawuwo anali omupempha kuti anenenso zakukhosi kwake ndipo zimenezi zinachititsa kuti kachiwirinso Eliya afotokoze zinthu zomwe zinkamudetsa nkhawa.a Zimenezi ziyenera kuti zinamulimbikitsanso kwambiri. Komanso mosakayikira, Eliya analimbikitsidwa kwambiri ndi zimene “mawu achifatse apansipansi” aja anamuuza. Yehova anatsimikizira Eliya kuti ndi munthu wofunika. Kodi anachita bwanji zimenezi? Mulungu anamuuza kuti nkhondo yothetsa kulambira Baala mu Isiraeli ipitirizabe. Ndiyetu apa n’zoonekeratu kuti ntchito imene Eliya anagwira sinapite m’madzi chifukwa Mulungu anali akuyendetsabe zinthu kuti cholinga chake chikwaniritsidwe. Komanso, Yehova anali akugwiritsabe ntchito Eliya popeza anamupatsa malangizo omveka bwino n’kumuuza kuti abwerere akagwire ntchito yomweyi.—1 Maf. 19:12-17.
-
-
Analimbikitsidwa ndi Mulungu WakeTsanzirani Chikhulupiriro Chawo
-
-
a “Mawu achifatse apansipansi” amenewa ayenera kuti anali a mngelo amene anagwiritsidwanso ntchito kunena “mawu a Yehova” amene ali palemba la 1 Mafumu 19:9. Pa vesi 15 mngelo ameneyu anangotchulidwa kuti “Yehova.” Zimenezi zingatikumbutse mngelo yemwe Yehova anamugwiritsira ntchito kutsogolera Aisiraeli m’chipululu. Ponena za mngelo ameneyu, Mulungu anati: “Dzina langa lili mwa iye.” (Eks. 23:21) Ngakhale kuti Baibulo silinena mwatchutchutchu kuti mngelo amene analankhula ndi Eliya anali Yesu, mfundo yofunika kuidziwa ndi yakuti Yesu asanabwere padziko lapansi, Yehova ankamugwiritsa ntchito monga “Mawu,” kapena kuti Womulankhulira.—Yoh. 1:1.
-