Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 2/15 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Okalamba Adzakhalanso Achinyamata
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Mphotho ya Yobu—Magwero a Chiyembekezo
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mwamuna Wachitsanzo Chabwino Amene Anavomera Kum’langiza
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Phunziro pa Kusamalira Mavuto
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 2/15 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Yobu 33:24 akulankhula za “dipo” kukhala litapezeka kaamba ka Yobu, kumulola kupeŵa imfa. Kodi ndani anayenera kukhala dipo la Yobu?

Panalibe nsembe yadipo yamunthu yomwe inaperekedwa kaamba ka Yobu kalelo, koma Mulungu anaphimba, kapena kukhululuka, cholakwa cha Yobu.

Satana anapangitsa mavuto ambiri kwa Yobu, kuphatikizapo ‘zironda zowawa, kuyambira ku phazi lake kufikira pakati pa mutu pake.’ Mkhalidwe wa Yobu unali woipa kwenikweni kwakuti mkazi wake anamsonkhezera ‘kuchitira Mulungu mwano ndikufa.’ Ngakhale Yobu analingalira kaya ngati imfa inali yabwinoko kuposa kuvutika koteroko.​—Yobu 2:7-9; 3:11.

Pamene zinawoneka kuti Yobu angamwalire, Elihu anasanthula mkhalidwe womvetsa chisoni wa Yobu naika maziko a chiyembekezo akumati: ‘Mnofu wake udatha, kuti sungapenyeke . . . Inde wasendera kufupi ndi ku manda, ndi moyo wake kwa akuononga. Akakhala kwa iye mthenga, womasulira mawu mmodzi mwa chikwi, kuonetsera munthu chomuyenera; pamenepo Mulungu amchitira chifundo, nati, Mlanditse, angatsikire kumanda, Ndampezera dipo. Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana.’​—Yobu 33:21-25.

Tikudziŵa kuti Yesu Kristu anapereka moyo wake wangwiro waumunthu monga dipo lolinganira kaamba ka anthu opanda ungwiro. Nsembe yake imalingana ndendende ndi chimene Adamu anataya, kupereka mtengo wofunikira kumasula anthu ku tchimo. (Aroma 5:12-19; 1 Timoteo 2:5, 6) Komabe, kumeneku sindiko kugwiritsira ntchito “dipo” kumodzi kokha m’Baibulo. Liwu Lachihebri lopezeka pa Yobu 33:24 kwakukulukulu limatanthauza “chophimba.” (Eksodo 25:17, NW) Pamene Mulungu ankachita ndi Israyeli wakale, iye anali ndi kakonzedwe kakuphimba, kapena kupereka chotetezera kaamba ka machimo​—nsembe zomwe zinaphimba machimo, kulungamitsa zinthu pakati pa anthu ndi Mulungu.​—Eksodo 29:36; Levitiko 16:11, 15, 16; 17:11.

Komabe, kuchiyambiyambi Mulungu anali wofunitsitsa kulandira nsembe monga chisonyezero cha chiyamikiro kapena pempho la kukhululukidwa ndi chivomerezo. (Genesis 4:3, 4; 8:20, 21; 12:7; 31:54) Yobu anamvetsetsa phindu la nsembe zimenezo. Tikuŵerenga motere: ‘Anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuŵerenga kwa [ana ake] onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m’mtima mwawo. Anatero Yobu masiku onse.’ (Yobu 1:5) Popeza kuti anayesayesa kukondweretsa Mulungu ndipo mwachiwonekere anali ndi mzimu wamantha, nsembe zake zinali zaphindu pamaso pa Mulungu.​—Salmo 32:1, 2; 51:17.

Koma Yobu pambuyo pake anadwala matenda omwe anawoneka kuti anawopseza moyo wake. Iye analingaliranso molakwa za chilungamo chake, chotero anafunikira chiwongolero, chimene Elihu anachipereka. (Yobu 32:6; 33:8-12; 35:2-4) Elihu ananena kuti Yobu sanafunikire kupitiriza ndi mkhalidwe wachisoni kufikira imfa ndi kumanda (Shelo, kapena manda wamba). Ngati Yobu akalapa, “dipo” likapezeka.​—Yobu 33:24-28.

Sitifunikira kuganiza kuti mwakunena kuti “dipo” Elihu anatanthauza munthu kalelo yemwe akafera Yobu. Polingalira nsembe zimene alambiri owona ankapereka, mtundu wa dipo limene Elihu ankasonyako m’nkhani ya Yobu lingakhale linali nsembe yanyama. Mosangalatsa, pambuyo pake Mulungu anauza mabwenzi atatu osuliza a Yobu kuti: “Mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu.” (Yobu 42:8) Mulimonse mmene linaliri dipolo, mfundo yaikulu ya Elihu inali yakuti cholakwa cha Yobu chikanaphimbidwa ndikupeza mapindu otulukapo.

Chimenechi ndicho chinachitika. Yobu ‘anadzinyansa nalapa.’ Chinatsatira nchiyani? ‘Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu . . . Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake . . . Ndipo zitatha izi, Yobu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi mphambu makumi anayi, nawona ana ake ndi zidzukulu zake mibadwo inayi.’ Zowonadi, dipo limenelo silinammasule Yobu ku tchimo, chotero m’kupita kwa nthaŵi anamwalira. Komabe, kutalikitsidwa kwa moyo wake kumatsimikizira kuti, kwenikwenidi, ‘mnofu wake unakhala se, woposa wa mwana; anabwerera ku masiku a ubwana wake.’​—Yobu 33:25; 42:6, 10-17.

Madalitso amenewo amene anadza kuchokera ku kugwiritsira ntchito dipo pa Yobu kokhala ndi polekezera kumatumikira monga kalirole wamtsogolo wa dziko latsopano. Kenaka, madalitso enieni a nsembe yadipo ya Yesu adzakhalapo, kuchotseratu ziyambukiro zatsoka za tchimo ndi kupanda ungwiro. Ha, ndichifukwa chotani nanga chimene tidzakhala nacho ‘chakukondwera,’ monga momwe anatchulira Elihu!​—Yobu 33:26.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena