Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Tikufunika Kupulumutsidwa
    Nsanja ya Olonda—2008 | March 1
    • Sikuti ambirife tingatsekerezedwe mu mgodi ngati mmene anachitira anthu 9 aja, ndipo mwina sitingafe pa ngozi. Komabe, m’pofunika kuti tipulumutsidwe ku mavuto osapeweka monga matenda, ukalamba ndi imfa. Ndipotu Yobu ananena kuti: “Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto. Atuluka ngati duwa, nafota; athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.” (Yobu 14:1, 2) Mawu amenewa adakali oona masiku ngakhale kuti tsopano papita zaka pafupifupi 3,500 kuchokera pamene ananenedwa. Izi zili choncho chifukwa palibe amene angazembe imfa. Motero, kaya tikukhala kuti kapena tikusamalira bwanji moyo wathu, tifunikira kupulumutsidwa ku mavuto monga ukalamba ndi imfa.

  • Tikufunika Kupulumutsidwa
    Nsanja ya Olonda—2008 | March 1
    • Kaya mukugwirizana ndi maganizo a Yobu pankhani ya moyo ndi imfa kapena ayi, simungapewe mfundo yakuti pamene zaka zikutha inunso ‘mudzathawa ngati mthunzi’ kapena kuti mudzafa. Mudzasiya anzanu, banja lanu, nyumba yanu ndiponso zinthu zanu zonse. Ndipotu Solomo, mfumu yanzeru ya Isiraeli wakale, inalemba kuti: “Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.”​—Mlaliki 9:5.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena