CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 11-15
Yobu Sankakayikira Kuti Akufa Adzauka
Yobu anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Mulungu adzamuukitsa
Yobu anagwiritsa ntchito chitsanzo cha mtengo, mwina wa maolivi, pofuna kusonyeza chikhulupiriro chimene anali nacho chakuti Mulungu angathe kumuukitsa
Mizu ya mtengo wa maolivi imakhala yambiri komanso imakafika patali. Zimenezi zimachititsa kuti chitsa chake chiziphukirabe ngakhale thunthu lake litadulidwa
Ngakhale kutachita chilala mpaka chitsa cha mtengowu kuuma, kukagwa mvula, nthambi zina zimaphukiranso kuchokera ku mizu yake