Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/15 tsamba 10-15
  • Chenjerani ndi Miseche Yovulaza!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chenjerani ndi Miseche Yovulaza!
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Zimasiyanira
  • Mmene Miseche Imakhalira Kusinjirira
  • Pamene Mavuto Abuka
  • Kodi Nkuchenjereranji?
  • Kodi Ndiko Kusinjirira?
  • Miseche Kodi Nchifukwa Ninji Imasangalatsa?
    Galamukani!—1991
  • Kujeda—Nchiyani Chomwe Chiri Chivulazo mu Iko?
    Galamukani!—1989
  • Mmene Miseche Yovulaza Ingathetsedwere
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Miseche ndi Yoipa Bwanji?
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/15 tsamba 10-15

Chenjerani ndi Miseche Yovulaza!

“Pochuluka mawu zolakwa sizisoŵeka; koma wokhala chete achita mwanzeru.”​—MIYAMBO 10:19.

1. Kodi miseche yanjiru, kapena kusinjirira njovulaza motani?

PALIBE chimene chingasinthe paizoni yakupha kukhala chakumwa chabwino. Kudyera miseche kwanjiru, kapena kusinjirira, kwayerekezeredwa bwino lomwe ndi paizoni, kumene kungaberenso munthu wopanda liwongo dzina lake labwino. Wolemba ndakatulo Wachiroma Juvenal anatcha kusinjirira kukhala “paizoni yoipitsitsa koposa ena onse.” Ndipo wolemba madrama Wachingelezi William Shakespeare anatchula mawu otsatirawa kukhala atanenedwa ndi mmodzi wa oseŵera ake: “Iye wondilanda dzina langa labwino akundibera chinthu chimene sichidzamlemeretsa ndipo andichititsa kukhala mphaŵi weniweni.”

2. Kodi ndi mafunso otani ofunikira kupendedwa?

2 Koma kodi miseche nchiyani? Kodi ingasiyane bwanji ndi kusinjirira? Kodi nkuchenjereranji ndi miseche yovulaza? Ndipo kodi zimenezi zingachitidwe motani?

Mmene Zimasiyanira

3. Kodi nchiyani chimene chiri kusiyana pakati pa miseche ndi kusinjirira?

3 Miseche ndiyo “kulankhula mphekesera, zimene nthaŵi zonse siziri zowona, ponena za anthu ena ndi zochitika zawo.” Ndiyo “nkhani wamba, yozoloŵereka kapena yolembedwa.” Popeza tonsefe timakondwerera anthu, nthaŵi zina timalankhula zinthu zabwino, zolimbikitsa ponena za ena. Kusinjirira kuli kosiyana. Ndiko “nkhani yabodza yolinganizidwira kuvulaza dzina labwino ndi mbiri za munthu winayo.” Kaŵirikaŵiri kulankhula za munthuyo kumakhala njiru ndi kosagwirizana ndi Chikristu.

4. Mogwirizana ndi wolemba wina, kodi kusinjirira kungayambe motani, ndipo kodi kumachokera ku magwero otani?

4 Miseche wamba ingatembenuzidwe kukhala kusinjirira kwankhalwe. Wolemba wina Arthur Mee anati: “Kaŵirikaŵiri kwambiri kusinjirira kumene kumavulaza munthu, ndi kumene kungamupweteke, kumayamba ndi kudyera miseche, mwinamwake, poyambapo miseche ingakhale mawu a mphekesera. Ndiwo mphulupulu zoipa koposa m’dziko, koma kaŵirikaŵiri, imachokera m’kusadziŵa. Kwakukulukulu timaipeza pakati pa anthu okhala ndi zochita zochepa kwambiri, ndipo opanda chifuno chenicheni m’moyo.”

5. Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la uphungu wa Paulo pa 1 Timoteo 5:11-15?

5 Popeza kuti mphekesera ingatsogolere kukusinjirira, mtumwi Paulo analankhula motsutsana ndi amiseche ena. Pambuyo pa kutchula akazi amasiye oyeneretsedwa kupeza chithandizo cha mpingo, iye analemba kuti: “Amasiye ang’ono uwakane, pakuti pamene zilakolako zawo za kugonana zikhala pakati pawo ndi Kristu, . . . aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera. Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye ang’ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira; pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsata Satana.”​—1 Timoteo 5:11-15.

6. Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa kugonjetsa chofooka cha munthu cha kuchita miseche imene ingatsogolere ku kusinjirira?

6 Popeza kuti Paulo adalemba mwachiuziro cha Mulungu, iye sanali kulankhula mawu osayenera ponena za akazi amenewo. Zimene iye adanena nzoyenera kuzilingalira mwamphamvu ndithu. Palibe mkazi wopembedza amene amafuna ‘kupatuka ndi kutsata Satana.’ Komabe, bwanji ngati mkazi Wachikristu apeza kuti ali ndi chofooka cha kulankhula nkhani imene ingamchititse kukhala ndi liwongo la kusinjirira? Pamenepo modzichepetsa ayenera kulabadira uphungu wa Paulo wakuti: “Akazi akhale olemekezeka, osadyerekeza.” Iye anatinso: “Akazi okalamba akhale nawo makhalidwe oyenera anthu oyera, osadyerekeza.” (1 Timoteo 3:11; Tito 2:3) Nawonso abale ayenera modzichepetsa kugwiritsira ntchito uphungu wanzeru umenewo.

7. Mogwirizana ndi Malemba, kodi nchifukwa ninji munganene kuti tonsefe tiyenera kulamulira zimene timanena?

7 Ndithudi, nthaŵi zina, tonsefe timalankhula za anthu ena, zokumana nazo zawo mu uminisitala, ndi zina zotero. Komabe, ‘tisakhale pansi konse ndi kulankhula motsutsana ndi mbale wathu.’ (Salmo 50:19, 20) Ndithudi, kuli kwanzeru kusalankhula zambiri chifukwa chakuti “pochuluka mawu zolakwa sizisoŵeka; koma wokhala chete achita mwanzeru.” (Miyambo 10:19) Chotero tiyenera kuchenjera ndi kuchita miseche, ngakhale ngati sikuoneka kukhala yovulaza. Palibe kufunika kwakuti tilankhule za anthu nthaŵi zonse, popeza kuti pali nkhani zabwino kwambiri zochuluka ngati tilingalira zinthu zolungama, zoyera, zokondedwa, zabwino, ndi zoyenera kutamandidwa.​—Afilipi 4:8.

Mmene Miseche Imakhalira Kusinjirira

8. Kodi nchifukwa ninji sikuli nthaŵi zonse kulakwa kulankhula za Akristu anzathu?

8 Palibe chivulazo ngati tilankhula za uminisitala wakumunda ndi ntchito zina zaumulungu za okhulupirira anzathu ngati sitinawonjezere ndipo ngati palibe zotulukapo zovulaza pa zimene tinena. Kwenikweni, mawu otero ngati ali oyamikira angalimbikitse ena. (Yerekezani ndi Machitidwe 15:30-33.) Akristu ena analankhula za mkulu wina wokhulupirika Gayo, amene mtumwi Yohane adalembera kuti: “Wokondedwa, uchita chokhulupirika nacho chirichonse, uwachitira abale ndi alendo omwe; amene anachita umboni za chikondi chako pamaso pa mpingo.” (3 Yohane 5, 6) Chotero sikuli nthaŵi zonse kulakwa kulankhula za Akristu anzathu.

9. (a) Kodi mphekesera ingasandulike motani kukhala kusinjirira wosalakwayo? (b) Kodi ndi mafunso otani amene moyenerera tingadzifunse?

9 Komabe, mphekesera zingasanduke kusinjirira anthu abwino ngati tisuzumira m’zochitika zawo zobisika, kukaikira zolinga zawo, kapena kudzutsa zikaikiro ponena za kudzisungira kwawo. Tingathe kuloŵa m’chizoloŵezi cha kudzifunsa mafunso, monga akuti: Kodi kalankhulidwe kanga kakavulaza mbiri ya munthu winayo? Kodi zimene ndikunena nzowona? (Chibvumbulutso 21:8) Kodi ndikananena chinthu chofananachi iye alipo? Kodi zikafesa kusagwirizana mumpingo? Kodi mawu anga akamchititsa kutayikiridwa mwaŵi wake wa utumiki? Kodi kungakhale kwakuti ndiri ndi kaduka mu mtima mwanga? (Agalatiya 5:25, 26; Tito 3:3) Kodi zotulukapo za zolankhula zanga zidzakhala zabwino kapena zoipa? (Mateyu 7:17-20) Kodi ndikadanena mawu ofananawo ponena za atumwi? (2 Akorinto 10:10-12; 3 Yohane 9, 10) Kodi nkhani yotero njoyenerera anthu amene amalemekeza Yehova?

10, 11. Mogwirizana ndi Salmo 15:1, 3, kodi sitidzachitanji ngati tifuna kukhala alendo a Mulungu?

10 Posonya kwa olemekeza Mulungu, Salmo 15:1 limafunsa kuti: “Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu? Adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika?” Ponena za munthu wotero, wamasalmo Davide akuyankha kuti: “Amene sasinjirira ndi lilime lake, sachitira mnzake choipa, ndipo satola mseche pa mnansi wake.” (Salmo 15:3) Panopa liwu lakuti “kusinjirira” lachokera ku mneni Wachihebri wotanthauza “kupita nacho ndi miyendo” ndipo motero kutanthauza “kuderukaderuka.” Aisrayeli analamulidwa kuti: “Musamaderukaderuka kufalitsa kusinjirira pakati pa anthu anu.” (Levitiko 19:16, New International Version) Aliyense ‘woderukaderuka nafalitsa kusinjirira’ sali mlendo ndi bwenzi la Mulungu.

11 Mabwenzi a Mulungu samachita choipa kwa atsamwali awo ndipo sadzawona, kapena kuvomereza za mkutu zotonza atsamwali awo osalakwa kukhala zowona. M’malo mwa kuwanditsa mabodza ponena za okhulupirira anzathu ndi kuwonjezera mitonzo ya nkhanza yochitidwa ndi osapembedza imene iwo akupirira nayo kale, tiyenera kulankhula zabwino ponena za iwo. Sitikafuna kuwonjezera zothodwetsa za abale ndi alongo athu okhulupirika mwa kulankhula zinthu zopereka mtonzo zonena za iwo.

Pamene Mavuto Abuka

12. Kodi Machitidwe 15:36-41 angatithandize motani ngati tayesedwa kudyera miseche ponena za wina amene takangana naye?

12 Pokhala opanda ungwiro, tingayesedwe kulankhula motsutsana ndi munthu amene tinakangana naye kwambiri pa mfundo ina. Koma lingalirani zimene zinachitika pamene mtumwi Paulo anali pafupi kuyamba ulendo wake wachiŵiri wa umishonale. Ngakhale kuti Barnaba anali wotsimikiza kuti Marko apitire nawo limodzi, Paulo sanavomereze, “amene [Marko] anawasiya nabwerera pa Pamfuliya paja osamuka nawo ku ntchito.” Pamenepo, “kupsyetsana mtima” kunayambika, ndipo analekana. Barnaba anatenga Marko kumka naye ku Kupro, pamene Paulo anatenga Sila kumka naye ku Suriya ndi Kilikiya. (Machitidwe 15:36-41) Pambuyo pake, mwachiwonekere kusagwirizana kumene kunali pakati pa Paulo, Barnaba, ndi Marko kunathetsedwa, chifukwa chakuti Marko anali ndi mtumwiyo m’Roma, ndipo Paulo analankhula mawu omyamikira. (Akolose 4:10) Ngakhale kuti panali mkangano, palibe umboni wakuti Akristu amenewo anamka namachita miseche pakati pa okhulupirira anzawo.

13. Kodi ndi mikhalidwe yotani yophatikizapo Petro imene Paulo anapeŵa kuthekera kwa kuyesedwa kudyera miseche Mkristu mnzake?

13 Ndiponso Paulo anapeŵa chiyeso chothekera cha kuchita miseche yosakaza pamene anadzudzula Kefa (Petro), amene adachita manyazi kudya ndi okhulupirira Akunja ndi kuyanjana nawo chifukwa cha kukhalapo kwa Akristu ena Achiyuda ochokera ku Yerusalemu. M’malo mwa kulankhula za Petro atachokapo, Paulo ‘anatsutsana naye pamaso pake,’ akumalankhula momveka “pamaso pa onse.” (Agalatiya 2:11-14) Nayenso Petro sanadyere miseche womdzudzulayo. Kwenikweni, pambuyo pake anamtcha “mbale wathu wokondedwa Paulo.” (2 Petro 3:15) Chotero ngakhale ngati wokhulupirira mnzathu angafunikire kuwongoleredwa, zimenezo sizimapereka chifukwa chodzikhululukira cha kumdyera miseche. Pali zifukwa zabwino kwambiri za kuchenjerera ndi kulankhula koteroko ndi kukaniza chiyeso cha kuwanditsa miseche yovulaza.

Kodi Nkuchenjereranji?

14. Kodi nchiti chimene chiri chifukwa chachikulu cha kusamvetserera kapena kuwanditsa miseche yovulaza?

14 Chifukwa chachikulu chimene sitiyenera kumvetserera miseche yovulazayo kapena kukhala ndi phande m’kuiwanditsa chiri chakuti timafuna kukondweretsa Yehova, amene amatsutsa kusinjirira. Monga momwe kwasonyezedwera, njira imene Mulungu amawonera mawu otero inamveketsedwa bwino pamene Aisrayeli analamulidwa kuti: “Usamayendayenda ndi osinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; ine ndine Yehova.” (Levitiko 19:16) Pamenepa, ngati titi tikhale ndi chiyanjo chaumulungu, sitiyenera kusinjirira aliyense amene tingatchule m’makambitsirano athu.

15. Kodi ndani amene ali wosinjirira wamkulu koposa, ndipo ndi chiyambukiro chotani chimene kudziloŵetsa m’miseche yovulaza chiri nako pa unansi wathu ndi Mulungu?

15 Chifukwa china chosachitira miseche yovulazayo chiri chakuti kuteroko kungatsogolere ku kutsanzira Satana, wosinjirira wamkulu koposa wa Yehova. Moyenerera mdani wamkulu wa Mulungu ameneyu anapatsidwa dzina lakuti “Mdyerekezi” (Chigriki, di·aʹbo·los), limene limatanthauza “wosinjirira.” Pamene Hava anamvetsera ku zolankhula zosinjirira za Satana motsutsana ndi Mulungu nazimvera, aŵiri oyambirira aumunthu analekanitsidwa ndi Bwenzi lawo labwino koposa. (Genesis 3:1-24) Chifukwa chake, tisagonjere konse ku zolinganiza za Satana ndi kuphatikizidwa m’kulankhula kovulaza kumene kungatibweretsere mkwiyo wa Mulungu, ndi kumene kungatilekanitse ndi Bwenzi lathu labwino koposa, Yehova Mulungu.

16. Kodi ndimotani mmene wosinjirira ‘amalekanitsira mabwenzi’?

16 Sitiyenera kumvetsera kwa odyera miseche anjiru, chifukwa chakuti amalekanitsa mabwenzi. Kaŵirikaŵiri, osinjirirawo amakuza zinthu ndi malovu, kuimira molakwa, kunama, ndi kukulitsa mbuto ya kalulu ndi dzawoneni mwa mawu osyasyalika. M’malo mwa kulankhula ndi munthuyo maso ndi maso, amanong’ona munthuyo palibe. Kaŵirikaŵiri kunyumwilana popanda pake kumadzutsidwa. Motero, “kazitape afetsa ubwenzi.”​—Miyambo 16:28.

17. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchenjera motsutsana ndi kukhala wophatikizidwa kwambiri m’miseche wamba?

17 Tiyenera kuchenjera kuti tisakhale ophatikizidwa kwambiri ngakhale m’miseche wamba. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mawu osalinganizidwira kuvulaza munthu aliyense angafikire kukhala ovulaza pamene abwerezedwa. Angakhoze kukometseredwa kapena kupotozedwa kufikira avulaza mbiri ya munthu wa Mulungu, kumbera dzina lake labwino. Ngati zimenezo zinachitika, kodi mukadzimva bwanji ngati inu munali magwero a nkhaniyo kapena ngati munaipitiriziradi kwa wina? Anthu angakuwoneni monga woperekadi chivulazo, ndicho chifukwa chake iwo sangakonde kuyanjana nanu.​—Yerekezani ndi Miyambo 20:19.

18. Kodi ndimotani mmene miseche ingapangitsire munthu kukhala wabodza?

18 Chifukwa china chakukhalira wochenjera ndicho chakuti miseche yosakaza ingakuchititseni kukhala wabodza. “Mawu a [wosinjirira ali ngati zakudya zomezedwa mwadyera, zimene, NW] zitsikira mkati mwa mimba.” (Miyambo 26:22) Bwanji ngati mungamve mabodza ndiyeno muwabwereza? Eya, ngakhale ngati muganiza kuti mabodzawo ali owona, inu mukunama pamene muwawanditsa. Pamene chinyengo chawo chavumbulutsidwa, mungalingaliridwe kukhala wabodza. Kodi mumafuna kuti zimenezo zichitike? Kodi Mulungu samawawona kukhala ndi thayo aphunzitsi onyenga kaamba ka mabodza achipembedzo? Inde, ndipo iye adzaimbanso mlandu osinjirira onama. Yesu anachenjeza kuti: “Mawu opanda pake alionse amene anthu adzalankhula adzawaŵerengera mlandu pa tsiku la chiweruzo; pakuti mudzapezeka wopanda mlandu mwa mawu anu ndi kugwidwa ndi mlandu mwa mawu anu.” (Mateyu 12:36, 37, Byington) Popeza “munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu,” kodi mukafuna kuti akupezeni ndi mlandu monga wosinjirira wabodza?​—Aroma 14:12.

19. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti miseche yovulaza ingathe kukhala yochititsa mbanda?

19 Ndiponso chifukwa china cha kusawanditsira miseche yovulaza chiri chakuti iyo ingakhale yochititsa mbanda. Inde, ingathe kukhala yakupha, yowononga mbiri yabwino ya munthu wosalakwa. Malilime ena ali ‘malupanga akuthwa,’ ndipo mawu owawa ngofanana ndi mivi yolunjikitsidwa kwa osalakwa atabisaliridwa. Davide anapemphera kuti: “Ndibiseni [Yehova] pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa; pa phokoso la ochita zopanda pake: Amene anola lilime lawo ngati lupanga, napiringiza mivi yawo ndiyo mawu akuwawitsa; kuponyera wangwiro mobisika.” (Salmo 64:2-4) Kodi inu mungafune kukhala ndi liwongo la zinthu zoipa zotero ponena za munthu mnzanu kufikira pa mfundo yakuti anakakamizika kupemphera kwa Mulungu kaamba ka mpumulo, monga momwe adachitira wamasalmo? Kodi mumafuna kukhala ndi liwongo la kuchita mbanda?

20. (a) Ponena za mpingo wa Mulungu, kodi nchiyani chimene chingachitike kwa wosinjirira wosalapa? (b) Kodi ndi kuchenjera kotani kumene akulu ayenera kukhala nako ponena za miseche ndi kusinjirira?

20 Kusinjirira kungatsogolere ku kuchotsedwa m’gulu la Mulungu; wosinjirira angachotsedwe, mwinamwake monga wabodza wosalapa. Komabe, chochitika chotero sichiyenera kuchitidwa kwa awo okha la ndi liwongo la miseche wamba. Akulu ayenera kupenda zochitikazo mwapemphero, akumasonyeza kusiyana kowoneka bwino pakati pa miseche wamba ndi kusinjirira kwankhalwe. Kuti wochita zoipa achotsedwe, akafunikira kukhala wosinjirira wanjiru, wosalapa. Akulu alibe ulamuliro wa kuchotsa aliyense kaamba ka miseche yaing’ono yosonkhezeredwa ndi chikondwerero cha anthu koma imene siiri yabodza kapena yanjiru. Zochitikazo siziyenera kukuzidwa kuposa milingo yoyenerera, ndipo payenera kukhala mboni zokhala ndi zochitika zenizeni kutsimikizira kuti wosinjirirayo akuphatikizidwa popanda chikaikiro. (1 Timoteo 5:19) Osinjirira osalapa amachotsedwa kwakukulukulu kuti miseche yanjiru ithetsedwe, ndipo mpingo udzapulumutsidwa ku kutupitsidwa ndi uchimo. (1 Akorinto 5:6-8, 13) Koma akulu sayenera kukhala ofulumira konse kotero kuti akuchotsa munthu pa zifukwa zosagwirizana ndi Malemba. Kaŵirikaŵiri kupyolera mwa pemphero ndi uphungu, iwo adzakhoza kuthandiza munthuyo kulapa, kupepesa kapena kusintha, ndi kupanga kupita patsogolo m’kulamulira lilime.

Kodi Ndiko Kusinjirira?

21. M’malo mwa kudyera miseche ponena za wochimwa, kodi muyenera kuchitanji?

21 Mwambi wanzeru umati: “Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi; koma wokhulupirika mtima abisa mawu.” (Miyambo 11:13) Kodi izi zidzatanthauza kuti ngati inu mudziŵa munthu wina amene akuchita chimo lalikulu mobisa, kukakhala kusinjirira kunena kanthu kalikonse ka chimolo? Ayi. Ndithudi, simuyenera kuchita miseche ponena za nkhaniyo. Muyenera kulankhula kwa wochita cholakwayo, mukumamlimbikitsa kufunafuna chithandizo cha akulu. (Yakobo 5:13-18) Ngati iye sachita zimenezo pambuyo pa nthaŵi yakutiyakuti, kudera nkhaŵa chiyero cha mpingo kuyenera kukusonkhezerani kuulula nkhaniyo kwa akulu.​—Levitiko 5:1.

22. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti 1 Akorinto 1:11 samapereka chilolezo cha kudyera miseche?

22 Kuulula kotero kungatulukire m’kulangidwa kwa wochita choipayo, ndipo zimenezo zingawonekere kukhala zosakondweretsa. Komabe, munthu wophunzitsidwa ndi chilango amapeza chipatso cha chilungamo. (Ahebri 12:11) Cholakwa chiyenera kuululidwa kwa oikidwa kusamalira nkhani yoteroyo, osati kwa akazitape amene angamke nafalitsa. Paulo anauza Akristu mu Korinto kuti: “Zinamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Kloe, kuti pali makani pakati pa inu.” (1 Akorinto 1:11) Kodi ziŵalo za banja limenelo zinali kuchita miseche ponena za okhulupirira anzawo? Ayi, ripotilo linachitidwa kwa mkulu wokhala ndi thayo amene anachitapo kanthu kuthandiza ofunikira chithandizowo kuti mapazi awo abwererenso pa njira yakumoyo.

23. Kodi ndi funso lotani limene liti lipendedwe?

23 Ngati tithandiza munthu wina kuti achenjere ndi kudziphatikiza m’miseche yovulaza, tikakhala tikuchita chinthu chomkomera. Mwambi wanzeru umati: “Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake; koma woyasamula milomo yake adzawonongeka.” (Miyambo 13:3) Pamenepa, mwachiwonekere, pali zifukwa zabwino za kuchenjerera kusachita miseche yovulaza ndi kusinjirira oipa. Komabe, kodi miseche yovulaza ingathetsedwa motani? Nkhani yotsatira idzatiuza.

Kodi Mayankho Anu Ndi Ati?

◻ Kodi nchiyani chimene chiri kusiyana pakati pa miseche wamba ndi kusinjirira?

◻ Kodi miseche ingakhale motani kusinjirira?

◻ Kodi ndi ziti zimene ziri zifukwa zina za kukhalira wochenjera motsutsana ndi kudyera miseche yovulaza?

◻ Kodi nchifukwa ninji sikuli kusinjirira pamene tipereka ripoti la cholakwa chachikulu cha munthu wina?

[Chithunzi patsamba 14]

Tsimikizirani kuti inu simuli ndi liwongo konse la kulasa munthu kumbuyo mwa kum’dyera miseche

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena