Analidziŵa Dzina la Mulungu
BUKHU loyambirira lodziŵika kukhala lolembedwa ndi kufalitsidwa kumaiko a ku Amereka olamuliridwa ndi Mangalande linali lotchedwa Bay Psalm Book. Kope lake loyamba linasindikizidwa ndi Stephen Daye ku Massachusetts Bay Colony m’chaka cha 1640. Bukhu loyambirira limenelo linali ndi bukhu la Baibulo la Masalmo, lotembenuzidwa kuchokera m’Chihebri kuika m’Chingelezi, chinenero cholankhulidwa ndi kulembedwa panthaŵiyo.
Chapadera ndi Bay Psalm Book chinali kutchula kwake dzina la Mulungu m’mavesi ena. Chifukwa chake, aliyense woŵerenga bukhulo kalelo pafupifupi zaka 350 zapitazo anali wokhoza kulidziŵa dzina la Mlengi wathu. Mwachitsanzo, m’kopelo Salmo 83:17, 18 limati: “Awopetu kosatha, nasokonezeke: inde, achititsidwe manyazi, nawonongeke. Kuti anthu adziŵe; kuti inu nokha amene dzina lanu ndilo IEHOVAH, ndinu wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi kosatha.”
Ndithudi, Mulungu wam’mwambamwamba samangofuna kuti ife tidziŵe kuti dzina lake ndi Yehova (Iehovah) basi. Mu Bay Psalm Book, Salmo 1:1, 2 limati “munthu wodala” samayenda muuphungu wa oipa, “koma chilamulo cha Iehovah, nchimene amalakalaka mokondwera.” New England Psalms yokonzedwanso ya mu 1648 imati: “Koma chikondwerero chake chonse amachisumika pachilamulo cha Yehova.”
Panopo New World Translation of the Holy Scriptures ya m’zaka za zana lino la 20 imati: “Wachimwemwe ali munthuyo amene sayenda muuphungu wa oipa, ndi amene saima m’njira ya ochimwa, ndi amene samakhala pabwalo la otonza. Koma chikondwerero chake chiri m’chilamulo cha Yehova, ndipo chilamulo chake nchimene iye amalingiliramo usana ndi usiku.”
Kuti akhaledi wachimwemwe, munthu ayenera kukana uphungu wa oipa. Sayenera kutsanzira chitsanzo cha ochimwa ndipo sayenera kuyanjana ndi otonza osapembedza. Zina zimene ayenera kupeŵa ndizo kuyanjana ndi anthu amene uphungu ndi mkhalidwe wawo zingamkopere m’kuchita chisembwere, kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka, ndi machitachita ena owombana ndi chilamulo cha Mulungu. Inde, chimwemwe chenicheni chimadalira pakuphunzira za Mulungu, amene dzina lake ndilo Yehova, ndi kugwiritsira ntchito chilamulo chake chovumbulidwa m’Baibulo.