Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 10/1 tsamba 10-15
  • Kodi muli Okhutiritsidwa ndi Makonzedwe Auzimu a Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi muli Okhutiritsidwa ndi Makonzedwe Auzimu a Yehova?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tsoka Limabwera kwa Osakhutiritsidwa
  • Chakudya Chauzimu Chochuluka
  • Kuchokera ku Chipululu Chauzimu Kupita ku Paradaiso Wauzimu
  • Mtengo ‘Umene Tsamba Lake Silifota’
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Madalitso Oti Mudzasowa Powalandirira”
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
  • Kodi Ndani Adzapulumuka Tsiku la Yehova?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Zinthu Zonse Zimene Yehova Amatipatsa Zimakuthandizani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 10/1 tsamba 10-15

Kodi muli Okhutiritsidwa ndi Makonzedwe Auzimu a Yehova?

“‘Ndipo mundiyese nako tsono,’ ati Yehova wa makamu, ‘ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.’”​—MALAKI 3:10.

1. Kodi ndi makonzedwe otani amene zolengedwa zamoyo zambiri zimakhutiritsidwa nawo?

NGATI muleka kupuma mpweya, mudzafa m’timphindi tochepa. Ngati muleka kumwa madzi, mudzafa m’masiku ochepa. Ngati muleka kudya, mudzafa m’milungu yochepa. Ngati muleka kudya pa makonzedwe auzimu a Yehova, ndiye kuti mudzafa ndipo mudzafa kotheratu. Yehova amapereka mpweya, madzi, ndi chakudya zimene zolengedwa zonse zimafuna. Chotero, kwa Yehova wamasalmo ananena kuti: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsa zamoyo zonse chokhumba chawo.” (Masalmo 145:16) Chokhumba cha zamoyo zambiri chimakwaniritsidwa ndi zopereka zakuthupi. Koma ichi sichiri chowona ponena za zolengedwa zaumunthu.

2. Nchiyani chimene chiri chikhumbo cha mtima wa munthu, ndipo kodi ndi makonzedwe otani amene ali ofunikira kaamba ka kukwaniritsidwa kwake?

2 Yesu anachiloza icho pamene ananena kuti: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa [Yehova, NW.]” (Mateyu 4:4) Zolengedwa zapansi ziribe chiyembekezo cha moyo wosatha, koma munthu ali nawo, monga mmene Mlaliki 3:11 amanenera: “Ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo.” Kapena monga mmene Revised Standard Version imachiperekera icho: “Iye waika zamuyaya m’malingaliro a munthu.” Chotero, chikhumbo chochokera mu mtima wa munthu chiri kukhala kunthaŵi zosatha, ngakhale kwamuyaya. Mpweya, madzi, ndi mkate wokha, siziri zokwanira kaamba ka chimenecho. Kuti mukhale ndi moyo kosatha kumafunikira makonzedwe auzimu ozikidwa pa “mawu onse otuluka m’kamwa mwa [Yehova, NW.]” Lerolino, iwo akupezeka m’bukhu limodzi Baibulo, ndipo zoperekedwa ziri zosatha​—zonse zimene mufuna, zoposa zimene mungathe kusunga. Kabathi imeneyi siikhala yopanda kanthu.

3. Nchiyani chimene Yesu anachiika pambali monga chofunika koposa, ndipo ndi chinsinsi chotani chimene Paulo anaphunzira?

3 Yesu anatiphunzitsa ife kupemphera kaamba ka chakudya chakuthupi chofunika: “Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.” Koma mwamsanga pambuyo pake iye anaika zakudya zauzimu pa malo oyamba pamene iye ananena kuti: “Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake.” (Mateyu 6:11, 33) Chakudya chakuthupi chimatipangitsa ife kukhala a moyo tsiku limodzi panthaŵi imodzi; kudya kwauzimu kopitiriza kungachite icho kwa nthaŵi yonse ya moyo, ndipo ngakhale kosatha. Chotero musakhale odera nkhaŵa ponena za zinthu zakuthupi. Paulo sanali wotero. Iye analankhula za zinthu zauzimu zomwe zinamutheketsa iye kukhala wokhutiritsidwa mosasamala kanthu za mikhalidwe yakuthupi, akumanena kuti: “Ndadziŵa [chinsinsi, NW] cha kukhala wokhuta, ndiponso wakumva njala, wakusefukira, ndiponso wakusowa. Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:12, 13.

Tsoka Limabwera kwa Osakhutiritsidwa

4. Ndi makonzedwe otani amene sanali okwanira kwa anthu aŵiri oyambirira, ndipo nchiyani chowonjezereka chimene anafuna?

4 Ambiri, ngakhale kuli tero, sali okhutiritsidwa ndi makonzedwe a Yehova. Makolo athu oyambirira sanali otero. Iwo anakhala m’munda wa paradaiso​—malo owoneka bwino anasangalatsa maso awo, maluŵa onunkhira bwino omwe anadzaza mpweya anali kupuma ndi fungo labwino, zakudya zosangalatsa zinatsitsimula mbali zokhoza kulawa za lilime lawo, nyimbo za mbalame zinalemekeza makutu awo. M’kuwonjezerapo, iwo anali ndi ntchito yosangalatsa ya kusamalira munda umenewo, kuwonjezerapo dalitso la kudzaza dziko lapansi ndi mbadwa zangwiro. Koma iwo anali odzikonda. Chimene Mulungu anali atapereka sichinali chokwanira. Iwo anafuna zowonjezereka. Iwo anafuna kudzisankhira kaamba iwo eni chomwe chinali chabwino ndi chomwe chinali choipa. Chotero iwo anatero, ndipo chosankha choyambirira chimenecho chimene iwo anachipanga chinali chobweretsa tsoka, kutulukapo m’kutaika kwa chirichonse, kwa iwo eni ndi kwa mbadwa zawo.​—Genesis 3:1-7, 16-19.

5. Kodi ndi makonzedwe otani amene Yehova anadalitsa nawo Aisrayeli, ndipo nchiyani chimene chinali chivomerezo chawo?

5 Aisrayeli anatsanzira chitsanzo chawo choipa. Mulungu anawapulumutsa kuchokera ku ukapolo mu Igupto, kuwapanga iwo kukhala mtundu, kuwapatsa iwo Lamulo langwiro, anawatsogoza iwo m’maulendo a m’chipululu, kuwapatsa iwo zovala zomwe sizinathe, ndipo mozizwitsa kuwadyetsa iwo ndi mana omwe anagwa kuchokera kumwamba ndi madzi omwe anatuluka m’thanthwe. Koma iwo sanali okhutiritsidwa ndi makonzedwe a Yehova. (1 Akorinto 10:1-5) Pamene iwo anayenda kupyola m’chipululu, iwo anadandaula kwa nthaŵi ndi nthaŵi.​—Eksodo 13:21, 22; Numeri 11:1-6; Deuteronomo 29:5.

6. Kodi ndi njira yotani imene inabweretsa chiwonongeko pa Aisrayeli monga mtundu?

6 Iwo anang’ung’udzabe pambuyo pa kukhazikitsidwa m’Dziko Lolonjezedwa​—dziko lachonde, la madzi abwino “loyenda mkaka ndi uchi.” Osayamikirabe, osakhutiritsidwabe ndi makonzedwe a Yehova, iwo anasiya kulambira kwake, kutembenukira ku kulambira mafano kwa mkhalidwe woipa wa kugonana, kupereka ana awo nsembe kwa Moleki, ndi kubweretsa chiwonongeko pa iwo eni monga mtundu. Obwezeretsedwa kuchokera ku ukapolo ku Babulo, iwo anatsatira miyambo ya pakamwa yomwe inapangitsa Mawu a Mulungu kukhala achabe. Iwo anafikira kupha Mesiya wolonjezedwa, Kristu Yesu.​—Deuteronomo 6:3; 8:7-9; Oweruza 10:6; 1 Mafumu 14:22-24; 2 Mafumu 21:1-16; Yesaya 24:1-6; Mateyu 15:3-9; 27:17-26.

7. Kodi ndimotani mmene atsogoleri achipembedzo a Dziko la Chipembedzo lerolino akupitirizira m’njira yofanana ndi ansembe osakhulupirika a m’tsiku la Malaki?

7 Kufikira ku tsiku lino mtundu wa anthu mwachisawawa wapitirizabe kukonda nthanthi zonyenga za chipembedzo. Atsogoleri achipembedzo anyazitsa dzina la Yehova, samaligwiritsira ntchito nkomwe. Iwo samamulemekeza iye ndi ziphunzitso zosakhala za m’malemba zoterozo zonga ngati Utatu, kusafa kwa moyo, ndi kuzunzidwa kosatha m’moto wa helo. Ziphunzitso zawo siziri kokha zoipitsidwa ndi kunyenga kochokera ku Babulo wakale ndi Igupto komanso, m’nkhani zambiri, zoikidwa ululu ndi kukana kwa nsembe ya dipo ya Kristu ndi kulandiridwa kwa chisinthiko. Iwo amalanda Yehova chilemekezo chimene amafunikira, monga mmene anachitira ansembe m’tsiku la Malaki.​—Malaki 1:6-8; 3:7-9.

8. (a) Ndi chiitano chotani chimene ansembe a m’tsiku la Malaki ndi atsogoleri achipembedzo a lerolino anakana? (b) Ndi andani amene anavomereza ku chiitanocho, ndipo ndi zotulukapo zotani?

8 M’nthaŵi imeneyo Aisrayeli analimbikitsidwa kudziyeretsa ndi kubwerera kwa Yehova. “Bwererani kudza kwa ine, ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,” anatero Yehova. Iye mowonjezereka anaitana iwo: “‘Ndipo mundiyese nako tsono,’ ati Yehova wa makamu, ‘ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.’” (Malaki 3:7, 10) Kokha otsalira a mtundu wa Chiyuda anabwerera; lerolino, otsalira okhulupirika a Israyeli wauzimu atuluka m’zipembedzo zonyenga zadziko lino. Iwo, limodzi ndi alambiri achiŵerengero chomakulakula cha khamu lalikulu la onga nkhosa zina, amalemekeza Yehova monga Mboni zake. (Yohane 10:16) Kwa iwo, Yehova wasunga lonjezo lake ndipo ‘watsegula mazenera a kumwamba ndi kutsanulira mdalitso wakuti asoweka malo akuulandira’​—phwando la chakudya chosiyanasiyana chauzimu!​—Yesaya 25:6.

Chakudya Chauzimu Chochuluka

9. Kodi ndi makonzedwe auzimu otani amene alipo lerolino, kupyolera m’njira yotani, ndipo ndi zotulukapo zotani?

9 “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene Yesu ananeneratu kaamba ka tsiku lathu ali wotanganitsidwa kupereka chakudya chauzimu chochuluka. (Mateyu 24:45) Chaka chatha chokha, m’maiko 208 ndi zisumbu za m’nyanja, ndi m’zinenero 200, Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni atatu zinapanga makonzedwe auzimu amenewo kukhalapo kupyolera m’maulendo a kunyumba ndi nyumba ndi kugawira mazana a mamiliyoni a mabukhu, magazini, ndi maBaibulo. Ambiri anadyako chakudya chauzimu chimenechi ndipo anali okhutiritsidwa: Achatsopano oposa 225,000 anabatizidwa m’chaka chimodzi chimenecho!

10. Kodi ndi makonzedwe otani amene alipo kaamba ka kulabadira chenjezo la Paulo ku kusonkhana pamodzi?

10 Makonzedwe auzimu a Yehova apangidwanso kukhalapo kupyolera mwa misonkhano yachigawo, misonkhano yadera, ndi misonkhano isanu ya mlungu ndi mlungu yopangidwa mokhazikika m’mipingo 52,000 ya Mboni za Yehova​—onse omvera ku chenjezo la Paulo pa Ahebri 10:25 ‘osaleka kusonkhana kwathu pamodzi.’

11. Nchiyani chimene chimachitira chitsanzo njira yokhumbirika ya mmene chakudya chauzimu chimakonzekeretsedwera?

11 Pamene mkazi aitana alendo ku chakudya, iye samangowiritsa chabe nthuli ya nyama ndi kuiika iyo pa mbale. Iye amagwiritsira ntchito zonunkhiritsa ndi nsuzi kuwonjezera ku kununkhira kosangalatsa ndi kukongoletsa kwina kuipangitsa iyo kukhala yosangalatsa m’maso. Kokha kawonekedwe kake ndi fungo zimakhala zokwanira kupangitsa mkawa kukha mate ndi kupangitsa madzi a m’mimba othandizira kugaya zakudya kuyenda. Mmenemo ndi mmene makonzedwe auzimu a Yehova akonzekeretsedwera​—osati ouma, amtundu wa kalembedwe ka bukhu la nazonse, koma ali m’njira yokoma yosangalatsa malingaliro ndi kukhudza mtima. Mkristu aliyense payekha ayenera kutsatira chitsanzo chimenecho. “M’khutumu simuyesa mawu, koma monga m’kamwa mulawa chakudya chake?”​—Yobu 12:11.

12. Ndi zitsanzo zotani zimene tiri nazo za chakudya chauzimu kukhala chokonzekeretsedwa modzutsa chilakolako?

12 Bukhu Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokratiki mu phunziro lake loyamba limagogomezera kugwiritsira ntchito mawu osangalatsa. Solomo anagwiritsira ntchito osati kokha mawu olondola komanso mawu osangalatsa. (Mlaliki 12:10) Masalmo 45:2 ananeneratu za Mesiya, Yesu Kristu: “Anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu.” Chinatsimikizira kukhala tero. Amvetseri ake anazizwa “ndi mawu a chisomo akutuluka m’kamwa mwake.” Iwo anapitiriza kulendewera kwa iye kuti amve, anabwera mofulumira ku kachisi kuti amve iye, anamvetsera kwa iye ndi chisangalalo, anazizwitsidwa panjira yake ya kuphunzitsa. Nduna zotumizidwa kudzamugwira iye zinalalikira: “Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.” (Luka 4:22; 19:48; 21:38; Marko 12:37; Mateyu 7:28; Yohane 7:46) Bukhu Lolangiza linaperekedwa kuthandiza ife kulankhula mawu osangalatsa a chowonadi. Kodi mumaligwiritsira ntchito ilo kotheratu?

13. Kodi Aefeso 5:15-17 amagogomezera motani ponena za ‘kumadzipezera nthaŵi,’ ndipo nchifukwa ninji pali chigogomezo chotero?

13 Aefeso 5:15-17, NW amatichenjeza ife kuti: “Yang’anitsitsani kuti mmene muyendera simuli monga opanda nzeru koma monga anthu anzeru, mukumadzipezera nthaŵi yabwino, chifukwa chakuti masiku ali oipa. Chifukwa cha ichi lekani kukhala opanda nzeru, koma pitirizani kuzindikira chimene chiri chifuniro cha Yehova.” Liwu la Chigriki pano lotembenuzidwa “nthaŵi” silimatanthauza nthaŵi m’lingaliro lofala komanso limasonyeza nthaŵi yoikika, nthaŵi yoyenera kaamba ka chifuno chapadera. Verebu la Chigriki lotanthauzidwa “kumadzipezera” liri mu mpangidwe wochita chinthu mopitirira muyezo, ndipo “m’lemba iri mwinamwake limatanthauza ‘kumadzipezera mofunitsitsa’; kunena kuti, kutenga mwaŵi uliwonse womwe ungabwere.”a Kodi inu mumadzipezera nthaŵi kuchokera ku ndandanda yanu kudzipanga inu eni anzeru mwakutenga makonzedwe auzimu a Yehova? Muyenera kutero. Tonsefe tiyenera kutero. Chifukwa ninji? “Chifukwa masiku ali oipa.”

Kuchokera ku Chipululu Chauzimu Kupita ku Paradaiso Wauzimu

14. Ndi versi liti la Baibulo limene limatumikira monga chitsanzo cha mbali yathu ya New World Translation Reference Bible ya chinenero cha Chingelezi?

14 Makonzedwe auzimu owoneka kwambiri ali New World Translation of the Holy Scriptures​—With References yathu, yotulutsidwa mu 1984. Iyo iri ndi mbali zambiri zimene zingachipangitse kukhala chothekera kugwiritsira ntchito ‘nthaŵi yopezedwa’ kuwonjezera chidziŵitso chathu.b Chitsanzo chimodzi chiri zilozero zake. Tengani Masalmo 1:3, lomwe limanena za mkhalidwe wa munthu amene amasinkhasinkha pa malamulo a Mulungu usana ndi usiku. Versi limenelo limanena kuti: “Ndi iye akunga mtengo wowoka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” Pali zambiri, zowonjezereka zambiri, ku versi limeneli kuposa zofikira za diso la woŵerenga yemwe amangoŵerenga mofulumira ndi kupitirira.

15. Ndi mafunso otani amene amadzutsidwa ponena za mtengo wa pa Masalmo 1:3, ndipo ndi kuwunikira kotani kumene Yesaya 44:4 amapereka?

15 Chonde dziwani: Mtengowo wabzyalidwa. Ndani waubzyala iwo? Iwo uli pafupi ndi mitsinje, pulula. Kodi mtengo umodzi umamera m’magombe a mitsinje yambiri? Ayi. Chotero khalani ofunitsitsa kudziŵa. Kodi mtengo umenewo nchiyani? Zilozero zimatsegula maso a maganizo athu. Izo ziri Yesaya 44:4, 61:3 ndi Yeremiya 17:8. Yesaya 44:4 amanena kuti anthu ake adzakhala ngati mitengo “[m’mphepete mwa magwero amadzi, NW.]” M’mphepete mwa magwero a madzi ambiri? Nkulekelanji, inde! Mitsinje iri magwero otsirira omwe amatsirira mitengo m’munda wa zipatso!

16. Ndi kumveketsa kowonjezereka kotani kumene kukuperekedwa pa Yesaya 61:3 ndi Yeremiya 17:8?

16 Yesaya 61:3 amatcha ina ya mitengo imeneyi “mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.” Yehova ali mmodzi yemwe amabzyala ndi kutsirira iyi, ndipo iye amalemekezedwa ndi zipatso zimene mitengoyo imabala! Yeremiya 17:8 amafanizira munthu yemwe amasinkhasinkha pa malamulo a Mulungu usana ndi usiku ku “mtengo wowoka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, osawopa kufika nyengo yadzuŵa, koma tsamba lake likhala laliŵisi, ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.” Tsamba lake silifota; chirichonse chimene umachita chimapambana!

17. Ndi chithunzi chotani tsopano chimene chimabuka ponena za Masalmo 1:3, ndipo kodi ndi mbali yotani imene timaichita mu icho?

17 Tsopano mamba akugwa m’maso athu! Masalmo 1:3 akupaka utoto chithunzi chokongola. Awo amene amasinkhasinkha pa malamulo a Yehova usana ndi usiku ali monga mitengo yobzyalidwa pa magwero osatha a madzi. Iwo salinso mbali ya magulu osakhutira mwauzimu a dziko koma tsopano ali oyanjana ndi gulu la Mulungu lomwe limagawiridwa mochuluka ndi madzi opatsa mpumulo a chowonadi. Ndithudi, iwo ali m’paradaiso wauzimu, iwo amatsitsimulidwa mwauzimu, ndipo akubala zipatso zauzimu ku chilemekezo cha Yehova. Ndipo tangolingalirani! Mulungu akugwiritsira ntchito Mboni zake kutsogoza anthu kuchokera ku magulu a dziko osakhutira, oikidwa nsanza, kupita ku paradaiso wauzimu wopatsa mpumulo, othiriridwa bwino.

18. Kodi ndimotani mmene ena amachitira pamene awona ena akupeza chipambano m’kuchitira umboni, ndipo nchifukwa ninji iwo angalephere?

18 Kuti tikwaniritse ntchito imeneyi mokhutiritsa, tiyenera kulanga malingaliro athu ndi mitima yathu kotero kuti tigwiritsire ntchito makonzedwe auzimu onse a Yehova. Ena amamva ena akulongosola malemba a Baibulo ndipo kenaka nkunena kuti: “Ndikukhumba ndikanadziŵa Baibulo monga mmene iye amachitira!” Koma ngati oterowo adzilanga iwo eni kuphunzira Baibulo, iwo nawonso angawonjezere chidziŵitso chawo cha Baibulo. Ena amamva ena akuchitira umboni pa makomo ndipo kenaka nkunena kuti: “Ndikukhumba ndikanakhoza kuchitira umboni pa makomo monga mmene iye amachitira!” Koma ngati iwo atadzilanga iwo eni kugawanamo mobwerezabwereza mu utumiki wa m’munda, kugwiritsira ntchito bukhu la Reasoning From the Scriptures, iwo nawonso angakhale Mboni zaluso lowonjezereka. Ena amamva ena akupereka nkhani za Baibulo ndipo kenaka nkunena kuti: “Ndikukhumba kuti ndikanapereka nkhani monga mmene iye amachitira.” Koma, kachiŵirinso, ngati awa akanadzilanga iwo eni kukonzekera magawo awo akulankhula bwino lomwe, kumwerekera m’maphunziro a mu Bukhu Lolangiza la Sukulu la Utumiki Wateokratiki, nawonso akakhoza kupita patsogolo m’kuthekera kwawo kwa kulankhula.

19. Nchiyani chimene chiri mfungulo ya kukulitsa kuthekera kwathu kwa kuchitira umboni?

19 Tsopano, kukhumba kuli kwabwino, koma kukhumba kokha kopanda ntchito sikumapangitsa ntchitoyo kuchitika. Iri ntchito imene imapangitsa chikhumbo kukhala chowona. Dzilangeni inu eni mwa kudzipezera nthaŵi, ndipo chitani ntchito imene imapangitsa chikhumbo kukhala chowona. Ngati simugwiritsira ntchito minofu yanu, iyo idzafota. Ngati simugwiritsira ntchito luso lanu, ilo lidzazimiririka. Ngati simugwiritsira ntchito malingaliro anu, kuthekera kwanu kwa kulingalira kudzafota. Ngati simugwiritsira ntchito chidziŵitso chanu, mudzachitaya icho. Mu chirichonse ndi mbali zonse, lamulo liri lakuti, “Gwiritsirani ntchito icho kapena chitayeni icho.” Chiri ‘kupyolera m’kugwiritsira ntchito kuti mphamvu za kulingalira zimaphunzitsidwa.’ Kenaka “kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakuchinjiriza.”​—Ahebri 5:14; Miyambo 2:11.

20. Mwakutenga mwaŵi wa makonzedwe auzimu a Yehova, kodi nchiyani chimene tidzapewa, ndipo nchiyani chimene tidzapeza?

20 Chotero gwiritsirani ntchito makonzedwe auzimu a Yehova. Sangalalani ndi anthu ake okhutiritsidwa. Thaŵani ku njala yonenedweratu ndi Amosi: “‘Tawonani! akudza masiku,’ ati [Mfumu, NW] Ambuye Yehova, ‘akuti ndidzatumiza njala m’dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova.’” (Amosi 8:11) Gawanani ndi awo amene amadya ndi kusangalala, osati awo amene amakana chakudya ndi kuvutika ndi manyazi: “Chifukwa chake atero [Mfumu, NW] Ambuye Yehova: ‘Tawonani! Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala. Tawonani! Atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu. Tawonani! Atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi.”​—Yesaya 65:13.

[Mawu a M’munsi]

a Onani The New International Dictionary of New Testament Theology, volyumu 1, tsamba 268, ya Colin Brown.

b Mwinamwake pakali pano mulibe m’chinenero chanu koma mosakaikira mungapeze chikondwerero m’chitsanzo chiri pamwambapo cha kugwiritsira ntchito kwake.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi ndimotani mmene mtundu wa Israyeli unasonyezerera kusakhutiritsidwa kwake ndi makonzedwe a Yehova?

◻ Ndimotani mmene Malaki 3:10 wakwaniritsidwira pa Mboni za Yehova?

◻ Kodi ndi liti limene liri tanthauzo lenileni la Masalmo 1:3?

◻ Nchifukwa ninji chiri choyenera kugwiritsira ntchito zinthu zophunziridwa kupyolera m’makonzedwe auzimu a Yehova?

[Chithunzi patsamba 15]

Awo amene amasinkhasinkha pa malamulo a Yehova ali monga mitengo yobzyalidwa m’mphepete mwa magwero osatha a madzi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena