Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 8/15 tsamba 5-7
  • Tingayambenso Kudalirana!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tingayambenso Kudalirana!
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zotsatira Zake? Kusokonezeka kwa Maunansi
  • Kodi Tingakhulupirire Yani?
  • Kuyambanso Kudalirana
  • Nchifukwa Ninji Kudalirana Kukuvuta?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kulimbitsa Chidaliro Chathu mwa Chilungamo cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Timakalamba Komanso Kufa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Tiyenera Kudalira Yehova
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 8/15 tsamba 5-7

Tingayambenso Kudalirana!

NGAKHALE kuti kusadalirana kumene kulipoku ndi chizindikiro cha “masiku otsiriza,” kusoŵeka kwa chidaliro kunaonekeranso zaka zikwi zambiri zapitazo. (2 Timoteo 3:1) Kunayambira m’malo osayembekezereka kuti kukanayamba​—m’paradaiso. Ponena za malowo Baibulo limati: “Mulungu anabzala m’munda ku Edene chakummaŵa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo. Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pa mundapo, ndi mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa.”​—Genesis 2:8, 9.

Mavesi otsatira amatisonyeza mmene izi zinakhudzira kusoŵeka kwa chidaliro lerolino. Timaŵerenga kuti: “Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Kodi Adamu anali ndi chifukwa chilichonse chokayikirira zimene Yehova anali atanena?

Timaŵerengabe kuti: “Ndipo njoka inali yakuchenjera yoposa zamoyo zonse za m’thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu? Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m’mundamu tidye. Koma zipatso za mtengo umene uli mkati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe. Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai; chifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa. Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m’maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya nayenso.”​—Genesis 3:1-6.

Mwakunyalanyaza chenjezo lomveka bwino la Mulungu, Adamu ndi Hava anasonyeza kuti sanali kumdalira Yehova. Anatsanzira mdani wa Mulungu Satana, amene anayankhula ndi Hava kupyolera mwa njoka yeniyeni. Satana anasoŵa chidaliro mu ulamuliro wa Yehova. Chifukwa cha zimenezi ndiponso chifukwa cha mtima wonyada ndi wosirira, anapandukira Mulungu nasokeretsanso anthu kuti apanduke. Anawasonkhezera kuganiza kuti Mulungu ngwosayenera kumkhulupirira.

Zotsatira Zake? Kusokonezeka kwa Maunansi

Mwina inu mwaonapo kuti anthu amene sakhulupirira anzawo sagwirizana ndi anthu kwanthaŵi yaitali. Wolemba nkhani wachilatini wa m’zaka za zana loyamba B.C.E., Publilius Syrus, analemba kuti: “Ubwenzi umalimba ngati pali kudalirana.” Mwakupanduka kwawo, Adamu ndi Hava anasonyeza kuti sanali kudalira Mulungu. Motero Mulungu analibenso chifukwa chakuti aziwadalira. Chifukwa cha kuleka kukhulupirirana, kapena kudalirana, anthu oyambawo sanakhalenso mabwenzi a Mulungu. Sitipeza paliponse pamene Yehova analankhula nawonso atawaimba mlandu wompandukira.

Unansi wa Adamu ndi Hava nawonso unasokonezeka. Yehova anachenjeza Hava kuti: ‘Udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.’ (Genesis 3:16) The Jerusalem Bible limati: “Adzachita umbuye pa iwe.” Mmalo mosonyeza umutu wachikondi kwa mkazi wake monga mmene Mulungu anafunira, tsopano Adamu anakhala womlamulira, akumachita umbuye pa iye.

Atachimwa, Adamu anayesa kukankhira mlanduwo kwa mkazi wake. Iye analingalira kuti anawatulutsa m’munda wabwino nkuwapititsa m’dziko losatha kukonzedwa, kuweruzidwira ku ukapolo m’mikhalidwe yovuta asanabwerere kufumbi, chifukwa cha zimene mkaziyo anachita. (Genesis 3:17-19) Sitingalakwe kulingalira kuti zimenezi zinkawapangitsa kukangana. Mwina Adamu anakalipa kwambiri, akumati sadzamumveranso Hava. Angakhale ataona kuti kunali koyenera kumuuza kuti, ‘Kuyambira tsopano mpaka mtsogolo, ndizilamulira ndine!’ Nayenso Hava angakhale ataona kuti Adamu walephera kusonyeza kuti ndi mutu wabanja, nampangitsa kuti asamdalirenso. Mulimonse mmene zinalili, anthu sanakhalenso paubwenzi ndi Mulungu ndipo anasokoneza unansi wawo chifukwa cha kusadalira Mulungu.

Kodi Tingakhulupirire Yani?

Si aliyense amene timafunika kumdalira, monga taonera za Adamu ndi Hava. Kodi tingadziŵe bwanji amene tifunikira kumdalira ndi amene sitifunikira kumdalira?

Salmo 146:3 limatilangiza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” Ndipo pa Yeremiya 17:5-7 timaŵerenga kuti: “Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nuchoka kwa Yehova mtima wake.” Mosiyana ndi zimenezo, “wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova.”

Nzoona kuti si nthaŵi zonse pamene kuli kolakwika kudalira anthu. Malembawo akungosonyeza kuti nthaŵi zonse nkolondola kudalira Mulungu, pamene kukhulupirira anthu nthaŵi zina kungabweretse mavuto. Mwachitsanzo, anthu amene amakhulupirira kuti anthu akwaniritse zimene Mulungu yekha ndiye angakwaniritse​—kuwapatsa chipulumutso ndi kubweretsa mtendere weniweni ndi chisungiko​—adzakhumudwa.​—Salmo 46:9; 1 Atesalonika 5:3.

Kwenikweni, anthu ndi mabungwe awo amafunika kuwakhulupirira kokha ngati akuchita mogwirizana ndi zifuno za Mulungu ndipo akusonyeza mapulinsipulo aumulungu. Chotero ngati titi tipangitse ena kutikhulupirira, tiyenera kumalankhula choonadi, tikumakhala oona mtima ndi odalirika. (Miyambo 12:19; Aefeso 4:25; Ahebri 13:18) Pokhapokha ngati tichita zinthu mogwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo, chikhulupiriro chimene anthu amakhala nacho mwa ife chikakhala choyenereradi ndipo padzakhaladi kulimbikitsana.

Kuyambanso Kudalirana

Mboni za Yehova zili ndi chifukwa chokwanira chodalira Mulungu ndi kulimbikitsa ena kumdaliranso. Yehova ndi wokhulupirika, amene nthaŵi zonse tingamdalire kuti adzachita zimene wanena chifukwa “Mulungu sakhoza kunama.” Palibe amene adzakhumudwa chifukwa choika chidaliro chake mwa Mulungu wachikondiyo.​—Ahebri 6:18; Salmo 94:14; Yesaya 46:9-11; 1 Yohane 4:8.

Anthu onse amene ali ndi chidaliro mwa Yehova ndipo amakhala ndi moyo wogwirizana ndi malamulo ake, amasonkhezeredwa mwamphamvu kuti azidalirana. Nkosangalatsa chotani nanga kuti m’dziko limene kudalirana kukuvuta tingapezemo anthu odalirika! Talingalirani mmene dziko likanasinthira chikhala kuti timadalira kotheratu zimene wina aliyense akunena kapena akuchita! Ndi mmene zidzakhalira m’dziko latsopano likudzalo limene Mulungu walonjeza. Sikudzakhalanso kovuta kumadalirana!

Kodi mungakonde kudzakhalamo? Ngati mungakonde, Mboni za Yehova zikukupemphani kulimbitsa chidaliro chanu mwa Mulungu ndi m’malonjezo ake mwa kuphunzira zochuluka ponena za zimene iye amafuna pamoyo. Phunziro la Baibulo limapereka chitsimikiziro chakuti Mulungu alipo, kuti ndi wosangalatsidwa ndi mmene anthu akukhalira, ndi kuti posachedwapa adzachitapo kanthu kuti akonze mavuto a dziko lapansi kupyolera mwa Ufumu wake. Anthu mamiliyoni ambiri aphunzira kuika chidaliro chawo mwa Mulungu ndi m’Mawu ake, Baibulo. Mwachimwemwe, Mboni za Yehova zidzakusonyezani mmene zimathandizira anthu ndi kosi ya phunziro la Baibulo imene zimapereka kwaulere. Kapena lemberani ofalitsa magazini ino kuti mudziŵe zambiri.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Kusadalira Mulungu kumasokoneza maunansi a anthu

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Anthu amafunika kuwakhulupirira kokha ngati achita mogwirizana ndi malamulo a Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena