Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 6/1 tsamba 23-27
  • Sukulu ya Gileadi—Ya Zaka 50 Ndipo Ikupitabe Patsogolo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sukulu ya Gileadi—Ya Zaka 50 Ndipo Ikupitabe Patsogolo!
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Nyumba Yatsopano Kaamba ka Sukulu ya Mishonale ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi Atenga Njira ya Moyo Yofupa
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi—“Amishonale Enieni!”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Amishonale Owonjezereka Kaamba ka Kututa Kwapadziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 6/1 tsamba 23-27

Sukulu ya Gileadi​—Ya Zaka 50 Ndipo Ikupitabe Patsogolo!

“PALI malo ambiri kumene umboni wonena za Ufumu sunaperekedwebe pamlingo wokulira,” anatero N. H. Knorr polankhula kwa kalasi la Gileadi loyamba pa February 1, 1943, tsiku limene anatsegulira sukuluyo. Iye anatinso: “Payenera kukhala anthu mazana zikwi zambiri amene akanafikiridwa ngati pakanakhala ogwira ntchito owonjezereka m’munda. Mwachisomo cha Mulungu, padzakhala owonjezereka.”

Ndipo pakhaladi antchito owonjezereka​—mamiliyoni owonjezereka! Ofalitsa Ufumu awonjezeka kuchokera pa 129,070 m’maiko 54 mu 1943 kufika pa 4,472,787 m’maiko 229 mu 1992! Sukulu ya Gileadi yachilikiza kwambiri umboni umene wachititsa chiwonjezekocho. Pambuyo pa zaka 50 ikupitirizabe kuchita mbali yaikulu m’kuphunzitsa antchito yaumishonale kukatumikira kulikonse kumene akufunika m’munda wa dziko.

Pa March 7, 1993, panali alendo oitanidwa 4,798 ndi ziŵalo za banja la Beteli ya United States amene anasonkhana m’Nyumba Yosonkhanira ku Jersey City, mu New Jersey, kudzaonerera dzoma la kumaliza maphunziro a kalasi la 94. Chochitika chapadera kwambiri chimenechi chinaperekanso mwaŵi wa kupenda zaka 50 zapitazo za Sukulu ya Gileadi. Kodi mungakonde kudziŵa pang’ono momwe programuyo inayendera?

Nyimbo yotsegulira itatha, George D. Gangas wa Bungwe Lolamulira anapereka pemphero logwira mtima. Ndiyeno, pambuyo pa mawu oyamba onenedwa ndi tcheyamani, Carey W. Barber, omaliza maphunzirowo​—ndi omvetsera onse​—anamvetsera mosamalitsa nkhani zazifupi zotsatizana.

Robert W. Wallen ndiye anayamba kulankhula, pamutu wakuti “Simuli Nokha.” Iyeyo mwaubwenzi, anati: ‘M’masiku alinkudzawo, padzakhala nthaŵi m’moyo mwanu pamene mudzadziona monga ngati kuti muli nokha, otalikirana kwambiri ndi banja lakwanu ndi mabwenzi.’ Nangano, tinganene motani kuti, “Simuli nokha”? Iye anafotokoza kuti: ‘Chifukwa chakuti aliyense wa inu nthaŵi zonse adzakhala ndi mwaŵi wa kukambitsirana ndi Yehova Mulungu.’ Anafulumiza omaliza maphunzirowo kusunga mwaŵi wa pemphero ndi kuugwiritsira ntchito tsiku ndi tsiku. Ndiyeno, mofanana ndi Yesu, adzakhala okhoza kunena kuti, “Sindikhala pa ndekha.” (Yohane 16:32) Mawu amenewo anali olimbikitsa chotani nanga kwa omaliza maphunzirowo!

Kenako, Lyman A. Swingle wa Bungwe Lolamulira pokamba mutu wakuti “Kugwiritsitsa Chiyembekezo Chathu” (wochokera palemba la tsiku la March 7), ananena za kufunika kwa mikhalidwe iŵiri​—chipiriro ndi chiyembekezo. ‘Chitonzo, nkhanza, udani, kuikidwa m’ndende, ngakhale imfa, ndizo zifukwa zimene chipiriro chimakhalira chofunika kwa Mkristu,’ iye anatero. ‘Palibe malire a nyonga yoposa yaumunthu amene Mboni yokhulupirika ya Yehova imadalirapo m’nthaŵi ya kusoŵa. Zimenezi nzolimbikitsadi, makamaka kwa omaliza maphunzironu.’ Bwanji za chiyembekezo? ‘Chiyembekezo nchofunika kwambiri,’ anafotokoza motero. ‘Monga momwe chisoti chimatetezera mutu wa wochivala, motero chiyembekezo cha chipulumutso chimasunga ndi kutetezera mphamvu za maganizo a Mkristu, kumkhozetsa kusunga umphumphu.’​—1 Atesalonika 5:8.

Wokamba nkhani wotsatira, Ralph E. Walls, anasankha mutu wankhani wokondweretsa wakuti, “Kodi Tingapulumuke Motani Kuloŵa mu ‘Malo Otakasuka’?” Kodi ‘malo otakasuka’ ameneŵa nchiyani? (Salmo 18:19) “Mkhalidwe wa kulanditsidwa umene umadzetsa mtendere wa maganizo ndi chisungiko mumtima,” anafotokoza motero wokamba nkhaniyo. Kodi timafuna kulanditsidwa kuchiyani? ‘Kwa inu mwini​—kuzophophonya zanu.’ Anawonjezeranso kuti: ‘Ndiponso, timafunikira kulanditsidwa kumikhalidwe yotizinga yosonkhezeredwa ndi Satana.’ (Salmo 118:5) Kodi ndimotani mmene tingapulumukire kuchisungiko cha malo otakasuka? ‘Mwa kufunafuna malamulo a Yehova m’zonse zomwe timachita ndi mwa kupempha Yehova mwa chikhulupiriro m’nkhaŵa zathu zonse.’

“Kodi Nchiyani Chimene Chikukuyembekezerani Mtsogolo?” ndiwo unali mutu wankhani wosankhidwa ndi Don A. Adams. Ndipo kodi nchiyani chimene chinayembekezera mtsogolo mwa amishonale atsopano ameneŵa? Nyengo ya kusintha, iye anafotokoza motero. “Palinso madalitso ambiri patsogolo panu.” Mwachitsanzo, iye anasimba za amishonale ena aŵiri okwatirana amene, atakhazikika kugawo lawo analemba kuti: “Ganizirani za tsiku labwino koposa munali nalo muutumiki, ndipo umu ndimo mmene tsiku lililonse lirili. Mabuku athu amapereŵera, ndipo anthu amangopemphabe kuti tiphunzire nawo.” Wokamba nkhaniyo anasimba mwachindunji kwa mabanja ndi mabwenzi a omaliza maphunzirowo kuti: ‘Simuyenera kudera nkhaŵa za omaliza maphunzirowa. Mungawathandize mwa kuwalembera makalata olimbikitsa.’​—Miyambo 25:25.

Kenako alangizi a sukuluyo anakamba nkhani. Jack D. Redford anasankha mutu wakuti “Musayembekezere Kalikonse kwa Munthu.” Vuto lina limene omaliza maphunziro adzayang’anizana nalo ndilo la kugwirizana ndi anthu, anafotokoza motero. Kodi chingathandize nchiyani? “Nyalanyazani zophophonya zawo. Musayembekezere zopambanitsa kwa anthu ena. Nthaŵi zonse musayembekezere zonse zimene mukulingalira kukhala zokuyenererani. Lolerani kusalungama kwa anthu ena, ndipo kukoma mtima kumeneku kudzakuthandizani kugwirizana ndi ena. Kukhoza kwanu kugwirizana ndi anthu ena kudzasonyeza mlingo wa uchikulire wanu.” (Miyambo 17:9) Ndithudi, kugwiritsira ntchito uphungu wanzeru umenewu kudzathandiza omaliza maphunziro kupanga masinthidwe achipambano a kukhala kwawo amishonale m’maiko achilendo!

“Tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi,” pamatero pa 2 Akorinto 4:7. Ulysses V. Glass, wosunga kaundula wa Sukulu ya Gileadi, anaperekera ndemanga palembali pamene anakamba nkhani ya mutu wakuti “Dalirani Abale Anu, Okhulupirika Enieni.” Kodi nchiyani chimene chili “zotengera zadothi”? “Zimenezi ziyenera kutanthauza ife monga anthu opanda ungwiro,” iye anatero. Kodi “chuma” nchiyani? “Ndicho utumiki wathu Wachikristu,” anafotokoza motero. (2 Akorinto 4:1) Ndipo kodi tiyenera kuchitanji ndi chumacho? “Chuma chimene Yehova watiikizira sichiyenera kungokundikidwa. Chotero, okondedwa inu oyembekezeredwa kukhala amishonale, gaŵirani chuma chimenecho kulikonse komwe mupita, ndipo phunzitsani ena ambiri mmene nawonso angachigaŵirire kwa ena.”

Inali nthaŵi yokumbutsa zakale pamene Albert D. Schroeder anapita papulatifomu, popeza kuti anali wosunga kaundula wa Sukulu ya Gileadi pamene inayamba. “Theka la Zaka Zana za Maphunziro Ateokratiki” ndiwo unali mutu wake. “Yehova amadziŵa mmene angaperekere maphunziro ogwira mtima, ndipo wachita zimenezi kumene,” iye anatero. Motani? Mbale Schroeder anasonyeza maphunziro olandiridwa kupyolera m’masukulu aŵiri okhazikitsidwa zaka 50 zapitazo​—Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi Sukulu ya Gileadi. Anasonyeza kuti chida cha mtengo wapatali m’kugaŵira chidziŵitso cholongosoka ndicho New World Translation. Iye anatsimikizira omaliza maphunzirowo kuti: “Mungathe kumka kumagawo anu achilendo ndi chidaliro chachikulu chakuti Sosaite idzakupatsani mokwanira chidziŵitso cholongosoka cha zifuno za Yehova.”

Milton G. Henschel, pulezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Soceity of Pennsylvania, anakamba mutu wakuti “Kuposa Pakukhala Olakika.” Mbale Henschel anatenga mutu wake wankhaniwo palemba la chaka la 1943: “Koma m’zonsezi, ife tilakatu, mwa iye amene anatikonda.” (Aroma 8:37) Linali lemba la chaka loyenera, iye anafotokoza motero, chifukwa chakuti mkati mwa Nkhondo Yadziko II, abale athu m’maiko ambiri anali kukumana ndi chizunzo chachikulu. Mbale Henschel anaŵerenga mawu ena ogwidwa m’kope la Nsanja ya Olonda limene linasimba za lemba la chakacho ndiyeno nafotokoza kuti: “Nkhani ya mu Nsanja ya Olonda imeneyi [ya January 15, 1943, Chingelezi] inaphunziridwa m’mwezi wa February ndi kalasi loyamba la Gileadi, ndipo inakonzekeretsa kalasili zimene zinali mtsogolo.” Omaliza maphunziro ambiri m’zaka zoposa 50 zapitazo adzisonyezadi kale kukhala olakika, iye anafotokoza motero. Bwanji za kalasi la 94? “Yandikirani kwa Yehova, yandikirani kuchikondi chake, ndipo chilakiko chanu chidzakhala chotsimikizirika.”

Pambuyo pa nkhani za mmaŵa, tcheyamani anapereka malonje ochokera kumaiko osiyanasiyana. Ndiyeno nthaŵi imene mabanja 24 anali kuyembekezera mwachidwi inafika​—kuperekedwa kwa madipuloma. Eya, ophunzira a ku Gileadi amenewo tsopano anali omaliza maphunziro awo a Gileadi mwalamulo! Iwo anachokera kumaiko 5, koma magawo awo anali a kumaiko 17, kuphatikizapo Hong Kong, Taiwan, Mozambique, ndi maiko ena a Kummaŵa kwa Ulaya.

Pambuyo pa kupuma, programu yamasana inayamba ndi chidule cha Phunziro la Nsanja ya Olonda, yotsogozedwa ndi Robert L. Butler. Ndiyeno omaliza maphunzirowo anasonyeza paplatifomu zokumana nazo zina zapadera zimene anali nazo pochitira umboni pafupi ndi Wallkill, New York. Programuyo inasonyeza chimodzi cha zinthu zimene mosakayikira chinawadzetsa ku Gileadi​—chikondi chawo chachikulu cha utumiki wakumunda.

Motsatira programu ya ophunzirawo, omvetsera ambiri anadabwa kaya ngati programuyo ikakhala ndi kanthu kena kapadera kukumbukira zaka 50 za Sukulu ya Gileadi. Sanagwiritsidwe mwala!​—Onani bokosilo, “Kupenda Zaka 50 za Sukulu ya Gileadi.”

Zaka 50 zapitazo, Mbale Knorr anasonyeza kuti anali mwamuna wachikhulupiriro ndi wowona zinthu patali. Kukhutiritsidwa kwake maganizo kuti Sukulu ya Gileadi idzakhala yopambana kunasonyezedwa m’mawu ake otsegulira onenedwa kwa kalasi loyamba, pamene anati: “Tikhulupirira kuti, mogwirizanadi ndi dzina lake, ‘mulu wa umboni’ udzamka kumbali zonse za dziko ndi kuti umboni wotero udzaima monga chizindikiro cha kulemekeza Mulungu chimene sichingawonongedwe konse. Inu monga atumiki oikidwa mudzadalira kotheratu Wammwambamwambayo, mukumadziŵa kuti adzakutsogolerani m’nthaŵi zonse za kusoŵa, ndipo mudzadziŵanso kuti ndiyenso Mulungu wodalitsa.”a

Zaka 50 pambuyo pake, Sukulu ya Gileadi ikali kupita patsogolo! Omaliza maphunziro a kalasi la 94 tsopano ali ndi mwaŵi wa kutsatira chitsanzo cha omaliza maphunziro oposa 6,500 amene anawayambirira. Aiketu chidaliro chawo chotheratu mwa Wammwambamwambayo pamene akuchita mbali yawo m’kusonkhanitsa “mulu wa umboni” umene udzaima monga chizindikiro kuulemerero wa Yehova Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

a M’Chihebri liwulo “Gileadi” limatanthauza “Mulu wa Umboni.”​—Genesis 31:47, 48, NW.

[Bokosi patsamba 25]

Ziŵerengero za Kalasi

Chionkhetso cha ophunzira: 48

Chiŵerengero cha maiko kumene anachokera: 5

Chiŵerengero cha maiko ogaŵiridwako: 17

Avareji ya zaka zakubadwa: 32

Avareji ya zaka m’chowonadi: 15.3

Avareji yazaka muutumiki wanthaŵi yonse: 9:6

[Bokosi pamasamba 26, 27]

KUPENDA ZAKA 50 ZA SUKULU YA GILEADI

Kodi pali njira yabwino kwambiri yotani kuposa mwa kupenda mbiri ya Gileadi kupyolera mwa zokumana nazo za awo amene anaphatikizidwamo​—omaliza maphunziro oyambirira, alangizi, ndi ena amene anathandizira kuikhazikitsa? Omvetsera anali okondwa pamene anamvetsera mbali yakuti “Kupenda Zaka 50 za Sukulu ya Gileadi,” nkhani yokambidwa ndi Theodore Jaracz.

Kodi ndimikhalidwe yotani imene inapangitsa kuti sukuluyo ikhazikitsidwe? Mbale Schroeder anafotokoza kuti iye ndi alangizi ena aŵiri anangopatsidwa miyezi inayi chabe ya kulinganiza sukuluyo. “Koma pofika Lolemba, February 1, 1943, tinali okonzekera kuipereka.”

Kodi zinthu zinali motani kwa amishonale oyamba amene anatumizidwa? Mbale Henschel anakumbukira kuti: “Tinalinganiza kuti dipatimenti ya Sosaite yotumiza katundu ikhomere katundu m’mabokosi a matabwa amene amishonalewo anafuna kutenga. Pamene mabokosiwo anafika kumene anali kupita, amishonalewo anawatsegula mosamala nachotsamo zinthu zawo. Koma anagwiritsira ntchito matabwa a mabokosiwo kupangira mipando.” Potsirizira, iye ananena kuti, Sosaite inalinganiza kumanga nyumba za amishonale zokonzedwa bwino ndiponso zachikatikati.

Ndiyeno zokumana nazozo zitatha, omaliza maphunziro a Gileadi oyambirira ena amene tsopano ali ziŵalo za banja la Beteli la United States anasimba zimene anakumbukira, malingaliro awo, ndi zokumana nazo zawo. Ndemanga zawo zinakhudzadi mitima ya omvetsera.

“Nditaitanidwa kukaloŵa kalasi loyamba, ndinamva kuti amayi anali ndi kansa. Koma popeza kuti anayamba upainiya ali ndi zaka 16 ndipo sanalekeze, anandilangiza mwamphamvu kuvomereza chiitanocho. Chotero nditazunguzika maganizo komabe modalira Yehova, ndinanyamuka ulendo kumka ku South Lansing. Ndinasangalaladi ndi kuyamikira kwambiri maphunziro a ku Gileadi. Amayi anamaliza ntchito yawo ya padziko lapansi patapita nthaŵi yaifupi nditamaliza maphunziro.”​—Charlotte Schroeder, amene anatumikira ku Mexico ndi El Salvador.

“Popeza kuti Yehova anali atandisamalira kale kumbali ya dziko kumene ndinali, ndinatsimikizira kuti kulikonse kumene ndikamka linali dziko lake, ndipo akandisamalira. Chotero ndinali wachimwemwe poitanidwa kukaloŵa kalasi loyamba.”​—Julia Wildman, amene anatumikira ku Mexico ndi El Salvador.

“Inali ntchito yokondweretsa! Tinkalankhula pakhomo lililonse. M’mwezi woyamba, ndinagaŵira mabuku 107 ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo 19. Mwezi wachiŵiri ndinali ndi maphunziro a Baibulo 28. Zowona, panali zinthu zina zimene tinafunikira kuzoloŵera​—kutentha, chinyontho, tizirombo toluma. Koma unali mwaŵi wosangalatsa kukhala kumeneko. Ndiko kanthu kena kamene ndidzakumbukira nthaŵi zonse.”​—Mary Adams, wa kalasi lachiŵiri, posimba za gawo lake ku Cuba.

“Kachedwe kakunja kanali limodzi la mavuto aakulu amene tinalimbana nawo ku Alaska. Kumpoto kunali kozizira kwambiri, tempilichala ikumatsika kufika pa [50 digirii Celsius] pansi pa mlingo woundanitsa madzi ndi kuposa pamenepo. Midzi ya Amwenye ndi midzi ina yaing’ono yakutali kummwera koma cha kummaŵa kwa Alaska inafikidwa ndi bwato kapena ndi ndege.”​—John Errichetti, wa kalasi lachitatu.

“Kwa ine Gileadi inali chiitano chochokera kwa Yehova kupyolera m’gulu lake la padziko lapansi kuti litilimbikitse mwauzimu ndi kutisonyeza njira yodabwitsa yomka kumoyo.”​—Mildred Barr, wa kalasi la 11, amene anatumikira ku Ireland.

Kufunsidwa kwina kosangalatsa kunalondola​—Lucille Henschel (wa kalasi la 14, amene anatumikira ku Venezuela), Margareta Klein (wa kalasi la 20, amene anatumikira ku Bolivia), Lucille Coultrup (wa kalasi la 24, amene anatumikira ku Peru), Lorraine Wallen (wa kalasi la 27, amene anatumikira ku Brazil), William ndi Sandra Malenfant (a kalasi la 34, amene anatumikira ku Morocco), Gerrit Lösch (wa kalasi la 41, amene anatumikira ku Austria), ndi David Splane (wa kalasi la 42, amene anatumikira ku Senegal).

Bwanji za abale amene anatumikira monga alangizi? Angapo a iwo anafunsidwanso​—Russell Kurzen, Karl Adams, Harold Jackson, Fred Rusk, Harry Peloyan, Jack Redford, ndi Ulysses Glass. Anafotokoza za mwaŵi wawo umenewo, akumanena mmene wawayambukirira kufikira lerolino.

Umboni wokondweretsa wosonyeza kugwira mtima kwa amishonale ophunzitsidwa ku Gileadi unaperekedwa ndi Lloyd Barry, amene anatumikira ku Japan. Mu 1949, pamene amishonale 15 anatumizidwa kumeneko, kunali ofalitsa osafikira 10 mu Japan yense. Komano patapita zaka 44, muli ofalitsa Ufumu oposa 175,000 m’dziko limenelo! Ndiyeno Robert Wallen anasimba za chipambano chapadera chimene amishonale ena anali nacho m’kuthandiza anthu kuloŵa m’chowonadi, kuphatikizapo mlongo wina amene ali mmishonale amene wakhala ku Panama kwa zaka zoposa 45 ndi amene wathandiza anthu 125 kufika pakudzipatulira ndi ubatizo.

Kaindeinde wa programu yonseyo anafikiridwa pamene onse amene anali omaliza maphunziro mwa omvetsera anapemphedwa kupita paplatifomu. Inalidi nthaŵi yochititsa chidwi. Mzere wa abale ndi alongo womatuluka pang’onopang’ono​—okwanira 89 m’banja la Beteli kuwonjezera ndi omaliza maphunziro odzacheza​—akumayenda mondondozana m’madanga oyendamo kukwera paplatifomu. Iwowa anagwirizana ndi abale amene anali atatumikira monga alangizi kwazaka zambiri, ndiponso ndi a kalasi la 94​—onse pamodzi analipo 160!

“Kodi ntchito ya Sukulu ya Gileadi m’kuphunzitsa amishonale kukagwira ntchito kumaiko achilendo yakhala ndi chipambano?” anafunsa motero Mbale Jaracz. “Umboni wa zaka 50 zapitazo umapereka yankho lamphamvu lakuti inde!”

[Chithunzi patsamba 25]

Kalasi la 94 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.

(1) De La Garza, C.; Borg, E.; Arriaga, E.; Chooh, E.; Purves, D.; Fosberry, A.; Delgado, A.; Drescher, L. (2) Scott, V.; Fridlund, L.; Kettula, S.; Copeland, D.; Arriaga, J.; Thidé, J.; Olsson, E.; Widegren, S. (3) Delgado, F.; Keegan, S.; Leinonen, A.; Finnigan, E.; Fosberry, F.; Halbrook, J.; Berglund, A.; Jones, P. (4) Watson, B.; Frias, C.; Chooh, B.; Halbrook, J.; Purves, J.; Finnigan, S.; Jones, A.; Cuccia, M. (5) Scott, G.; Copeland, D.; Drescher, B.; De La Garza, R.; Leinonen, I.; Keegan, D.; Watson, T.; Kettula, M. (6) Widegren, J.; Borg, S.; Cuccia, L.; Berglund, A.; Olsson, B.; Frias, J.; Fridlund, T.; Thidé, P.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena