Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Pangani Manja Osatha a Yehova Kukhala chichirikizo Chanu
    Nsanja ya Olonda—1991 | October 1
    • 15. Kodi ndimfundo yaikulu yotani yokhala m’mawu a Davide pa Salmo 19:7-13?

      15 Ngakhale kuti timakonda lamulo la Yehova, nthaŵi zina timalakwa. Mosakaikira chimenechi chimatipsinja, monga momwe Davide anachitira, amene anawona malamulo a Mulungu, zikumbutso, zitsogozo, ndi ziweruzo kukhala zokhumbirika kuposa golidi. Iye anati: ‘Kapolo wanu achenjezedwa nazo: M’kuzisunga izo muli mphotho yaikulu. Adziŵitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika. Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine: pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.’ (Salmo 19:7-13) Tiyeni tiwapende mawuŵa.

  • Pangani Manja Osatha a Yehova Kukhala chichirikizo Chanu
    Nsanja ya Olonda—1991 | October 1
    • 17. Kodi kubisa machimo kungamyambukire motani munthu, komabe kodi ndimotani mmene angapezere chikhululukiro ndi mpumulo?

      17 Machimo obisidwa angachititse kupsinjika. Malinga ndi Salmo 32:1-5, Davide anayesa kubisa tchimo lake, koma anati: ‘Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; Uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.’ Kuyesa kudidikiza chikumbumtima cha liŵongo kunamtopetsa Davide, ndipo kuvutika mtima kunamfooketsa monga momwe mtengo umataira chinyontho choupatsa moyo m’nthaŵi ya chilala kapena m’kutentha kwa chirimwe. Mwachiwonekere iye anavutika ndi ziyambukiro zamaganizo ndi zakuthupi ndipo anataya chimwemwe chifukwa cha kulephera kuulula. Kuululira Mulungu ndiko kokha kukabweretsa chikhululukiro ndi mpumulo. Davide anati: ‘Wodala munthuyo wokhululukidwa chimo lake; Wokwiriridwa choipa chake. . . . Ndinavomera choipa changa kwa inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.’ Chithandizo chachikondi chochokera kwa akulu Achikristu chikhoza kutithandiza kuchira mwauzimu.​—Miyambo 28:13; Yakobo 5:13-20.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena