‘Ndidzazungulira Guwa la Nsembe Lanu, Yehova’
“NDIDZASAMBA manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova.” (Salmo 26:6) Potchula mawu ameneŵa Mfumu Davide wakaleyo anasonyeza kudzipereka kwake kwa Yehova. Komano, n’chifukwa chiyani anafuna ‘kuzungulira’ guwa la nsembe la Yehova, ndipo analizungulira motani?
Kwa Davide, likulu la kulambira Yehova linali chihema chomwe chinali ndi guwa la nsembe lokutidwa ndi mkuwa, chimene m’nthaŵi ya ulamuliro wake chinali ku Gibeoni, kumpoto kwa Yerusalemu. (1 Mafumu 3:4) Mbali zonse zinayi, guwa la nsembe limeneli linali la mamitala 2.2, laling’ono kwambiri poliyekerezera ndi guwa la nsembe lalikululo limene linadzamangidwa m’bwalo la kachisi wa Solomo.a Ngakhale ndi choncho, Davide anasangalalabe ndi chihema ndi guwa lake la nsembe, lomwe linali likulu la kulambira koyera m’Israyeli.—Salmo 26:8.
Nsembe zopsereza, nsembe zoyamika, ndi nsembe zopalamula zinali kuperekedwa paguwalo, ndipo chaka ndi chaka pa Tsiku la Chitetezo nsembe zinali kuperekedwa m’malo mwa mtundu wonsewo. Guwalo ndi nsembe zake zili ndi tanthauzo kwa Akristu lerolino. Mtumwi Paulo analongosola kuti guwalo linaimira chifuniro cha Mulungu, chimene chinam’pangitsa kulandira nsembe yoyenera yowombola mtundu wa anthu. Paulo anati: “Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.”—Ahebri 10:5-10.
Akafuna kupereka nsembe paguwalo, ansembe mwamwambo anali kusamba m’manja ndi madzi kuti akhale oyera. Ndiye chifukwa chaketu Mfumu Davide anasamba m’manja “mosalakwa” ‘asanazungulire guwa la nsembelo.’ Anachita zinthu “ndi mtima woona ndi wolungama.” (1 Mafumu 9:4) Akanati asasambe m’manja m’njira imeneyi, kulambira kwake, kapena kuti ‘kuzungulira’ kwake guwa la nsembe, kukanakhala kosalandirika. Zoonadi, Davide sanali Mlevi chotero analibe mwayi wochita ntchito yaunsembe paguwa la nsembelo. Ngakhale kuti anali mfumu, sanali kuloledwa ngakhale kuloŵa m’bwalo la chihemacho. Komabe, monga Mwisrayeli wokhulupirika, iye anamvera Chilamulo cha Mose ndipo nthaŵi zonse anali kubweretsa nsembe zake kuti zidzaperekedwe paguwapo. Iye anazungulira guwa la nsembe m’lingaliro lakuti moyo wake wonse unali wokhudzana ndi kulambira koyera.
Kodi ifeyo tingatsanzire chitsanzo cha Davide lerolino? Inde. Ifenso tingasambe manja athu mosalakwa ndi kuzungulira guwa la nsembe la Mulungu ngati tisonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya Yesu ndi kutumikira Yehova ndi mtima wonse, tili ‘oyera m’manja, ndi oona m’mtima.’—Salmo 24:4.
[Mawu a M’munsi]
a Guwa la nsembe limenelo linali la mamitala 9 mbali zonse zinayi.
[Chithunzi patsamba 23]
Kachisiyo anaimira chifuniro cha Yehova, chimene chinam’pangitsa kulandira nsembe yoyenerera yowombola mtundu wa anthu