Yang’anani kwa Yehova kaamba ka Chidziŵitso
“Ine ndizakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo.”—Salmo 32:8.
1. Nziti zomwe ziri zochititsa zina zomwe zimatsimikizira kaya ngati zigamulo zimene timapanga zidzakhala zanzeru? (Yerekezani ndi Deuteronomo 32:7, 29.)
TSIKU lirilonse timayang’anizana ndi zigamulo—zina za izo zowoneka zazing’ono, zina mwachidziŵikire zofunika. Kodi zigamulo zathu zidzakhala zanzeru? Chimenecho chimadalira mokulira pa kaya ngati timachita mwansontho kapena timalingalira tisanalankhule kapena kuchita. Pali nkhani zambiri, ngakhale kuli tero, m’zimene kupanga zigamulo zanzeru kumafunikira kuti tikhale okhoza kuwona kupyola pa chomwe chiri chodziŵikiratu. Ichi chingafunikire kuti tidziŵe chimene chidzakhala chotulukapo cha mkhalidwe wa dziko womwe ulipo, ngakhale kuti tizindikire za zimene zikuchitika m’malo a mizimu. Kodi tingachite chimenecho? Kodi chiri chothekera kwa munthu aliyense kuchita tero mu mkhalidwe umene suli kokha wongolota?
2. Kuti titsogoze njira ya chipambano mkati mwa moyo, ndi thandizo lotani limene timafunikira, ndipo nchifukwa ninji? (Miyambo 20:24)
2 Anthu anakonzekeretsedwa ndi mphamvu ya malingaliro yozizwitsa yowonadi, koma sanapangidwe ndi kuthekera kwa kupititsa patsogolo njira ya chipambano mkati mwa moyo popanda modzichepetsa kulandira thandizo kuchokera kwa Mulungu. Monga mmene mneneri wowuziridwa Yeremiya analembera kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu siri mwa iyemwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
3. Ngati tilephera kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka chitsogozo, nchiyani chomwe chikakhala chotulukapo? (Yerekezani ndi Genesis 3:4-6, 16-24.)
3 Nchiyani chomwe chiri chotulukapo ngati tinyalanyaza nsonga imeneyo ndi kudalira kaya pa ife eni kapena pa anthu ena kaamba ka zigamulo ponena za chimene chiri chanzeru kapena chopanda nzeru, chabwino kapena cholakwa? Chifukwa cha kutsogozedwa ndi kulingalira kwa umunthu, pakakhala nthaŵi zimene tikakhoza kuwona kukhala zabwino zimene Mulungu amanena kuti ziri zoipa, pamene tingalingalire kukhala yanzeru njira imene Mulungu amaitcha kukhala yopusa. (Yesaya 5:20) Ngakhale ngati tingachite chimenechi mosafuna, tingakhale chochititsa kukhumudwitsa kwa ena. (Yerekezani ndi 1 Akorinto 8:9.) Ponena za chotulukapo chotsirizira kwa awo omwe amawumirira m’kulephera kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka chitsogozo, Mawu ake amalongosola kuti: “Iripo njira yowoneka kwa mwamuna ngati yowongoka; Koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.”—Miyambo 14:12.
4. Ndi thandizo lotani limene Yehova mowoloŵa manja akulonjeza atumiki ake? (Yerekezani ndi Yeremiya 10:21.)
4 M’chiyang’aniro cha ichi, nchiyani chomwe timafunikira? Kuchiika mopepuka, timafunikira thandizo lomwe Yehova amapereka. Molimbikitsa, iye akunena kuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; Ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.”—Salmo 32:8.
Chimene Chidziŵitso Chimaphatikiza
5. Kodi “chidziŵitso” nchiyani?
5 Kodi nchiyani kokha chimene chiri “chidziŵitso” monga momwe chalozeredwako m’Malemba? Icho chiri kuthekera kwa kuwona mkhalidwe, kuyang’ana kupyola pa chodziŵikiratu. Mogwirizana ndi Theological Wordbook of the Old Testament, kalongosoledwe ka Chihebri koikidwa kukhala “chidziŵitso” kamalozera ku “kuzindikira kwa luntha kwa chifukwa” kaamba ka zinthu. Chiri mtundu wa kuzindikira umene umatheketsa munthu kuchita mwanzeru ndi kukhala ndi chipambano. M’chigwirizano ndi lingaliro lokulira limenelo ndipo kuti ipereke kumvekera bwino kwa verebu la Chihebri limodzimodzilo, New World Translation, m’kuwonjezera ku kalembedwe kakuti ‘khalani ndi chidziŵitso,’ imagwiritsira ntchito kalongosoledwe koteroko konga ngati ‘chitani mwanzeru,’ ‘chitani mochenjera,’ndi ‘khalani ndi chipambano.’—Salmo 14:2.
6. Nchifukwa ninji “wokhala chete” anganenedwe kukhala akuchita mwanzeru, kapena ndi chidziŵitso?
6 Chotero, “wokhala chete” akunenedwa kukhala “wochita mwanzeru,” kapena ndi chidziŵitso. (Miyambo 10:19) Iye amalingalira asanalankhule, akumaŵerengera mmene ena adzamvetsetsa chomwe wanena, ndiponso kaya ngati chimene anganene ponena za munthu wina chingakhale cha nzeru, cha chikondi, kapena choyenerera. (Miyambo 12:18; Yakobo 1:19) Chifukwa chakuti iye amafulumizidwa ndi chikondi kaamba ka njira za yehova ndi chikhumbo chowona mtima cha kuthandiza munthu mnzake, chimene amanena chimakhala chomangirira kwa ena.—Miyambo 16:23.
7. Nchiyani chomwe chinatheketsa Davide kupeza kutchuka kwa kukhala yemwe anachita mochenjera?
7 Ponena za Davide mwana wa Jese, kwalembedwa kuti: “Anatuluka kumka kulikonse Sauli anamtumako, nakhala wochenjera,” uko ndiko kunena kuti, ndi chidziŵitso. Davide anazindikira kuti mu ntchito yake zochulukira zinaphatikizidwa koposa kokha kukanthana pakati pa ankhondo aumunthu. Iye anazindikira kuti iye ndi amuna omwe anali naye anali kumenya nkhondo za Yehova. Chotero, Davide anayang’ana kwa Yehova kaamba ka chitsogozo ndi dalitso. (1 Samueli 17:45; 18:5; 2 Samueli 5:19) Monga chotulukapo chake, maulendo a Davide anapeza chipambano.
8. M’malemba Achikristu Achigriki, ndi malingaliro ena ati omwe akuperekedwa ndi verebu lomwe limatanthauzidwa ‘khalani ndi chidziŵitso’?
8 M’malemba Achikristu Achigriki, verebu lotembenuzidwa ‘kukhala ndi chidziŵitso’ limalembedwanso, ‘peza nzeru ya’ ndi, ‘zindikira.’ (Aroma 3:11; Mateyu 13:13-15; Aefeso 5:17, NW) Chimene Mulungu akulonjeza atumiki ake chiri kuthekera kwa kuchita zinthu zimenezi. Koma kodi ndimotani mmene iye amaperekera chidziŵitso choterocho kwa iwo?
Mmene Yoswa Anafikira Kukhala ndi Chidziŵitso
9. Mu Israyeli wakale, ndimotani mmene Yehova anapatsira anthu chidziŵitso?
9 Mu Israyeli wakale, Yehova anatuma Alevi kulangiza mtunduwo m’Chilamulo chake. (Levitiko 10:11; Deuteronomo 33:8, 10) Chilamulo chinali chowuziridwa ndi Mulungu, ndipo mzimu wa Yehova unali kugwira ntchito m’makonzedwe a gulu omwe anagawiridwa kuphunzitsa icho. (Malaki 2:7) Kupyolera mwanjirayi, Yehova ‘anapangitsa Aisrayeli kukhala ochenjera,’ kapena kuwapatsa iwo chidziŵitso, monga momwe kwasonyezedwera pa Nehemiya 9:20, NW.
10, 11. (a) Monga momwe kwasonyezedwera pa Yoswa 1:7, 8, nchiyani chomwe chikatheketsa Yoswa kuchita ndi chidziŵitso? (b) Ndi makonzedwe otani kaamba ka chilangizo omwe anali ofunika kwa Yoswa kuwayamikira? (c) Ndi kuyesayesa kwaumwini kotani kumene kunafunikiranso ku mbali ya Yoswa?
10 Koma kodi munthu payekha mkati mwa mtunduwo anachita ndi chidziŵitso? Ngati iwo akanayenera kuchita tero, chinachake chinafunikira kumbali yawo. Pa nthaŵi imene Yoswa anaikizidwa thayo la kutsogoza Israyeli kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anamuwuza iye kuti: “Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipambukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako. Bukhu iri la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiliremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.” Liwu la Chihebri pano loikidwa “kuchita mwanzeru” limatanthauzanso “kuchita ndi chidziŵitso.”—Yoswa 1:7, 8.
11 Ndimotani mmene Yehova akaperekera chidziŵitso choterocho kwa Yoswa? Osati mwa kuloŵetsamo chozizwitsa. Mawu olembedwa a Mulungu anali mfungulo ku icho. Yoswa anafunikira kudzaza maganizo ake ndi mtima ndi iwo, kuŵerenga iwo ndi kusinkhasinkha pa iwo mokhazikika. Monga mmene Yoswa anadziŵira, Mawu a Mulungu ananena kuti chilangizo kuchokera ku Chilamulo chikaperekedwa ndi Alevi. Chotero, Yoswa anafunikira kuyamikira chimenechi, osati mwa kudzipatula yekha ngati kuti iye akanatha kumvetsera zonse payekha m’chiyang’aniro cha chenicheni chakuti iye anali ndi malo a thayo mu mtunduwo. (Miyambo 18:1) Chinali chofunika kwa Yoswa kukhala waluso m’kuphunzira Mawu olembedwa a Mulungu. Ngati iye anachita chimenecho, osanyalanyaza mbali iriyonse ya ilo, ndipo ngati iye anamvera ilo, chotero iye akachita ndi chidziŵitso.—Yerekezani ndi 1 Mafumu 2:3.
Mmene Yehova Amaperekera Chidziŵitso Lerolino
12. Kuti tipindule kuchokera ku chidziŵitso chimene Yehova akuchipangitsa kukhala chothekera kwa ife, ndi zinthu zitatu ziti zimene ziri zofunikira?
12 Kufika m’nthaŵi yathu, Yehova wapitirizabe kupatsa atumiki ake chitsogozo chimene amachifunikira ndi cholinga chakuti achite mwanzeru. Kuti tipindule kuchokera ku chitsogozo chimenecho, zinthu zingapo ziri zofunikira kwa ife monga aliyense payekha: (1) Tifunikira kuyamikira gulu la Yehova, monga mmene Yoswa anachitira. M’nkhani yathu, chiyamikiro choterocho chimaphatikizapo kugwirizana ndi mpingo Wachikristu wa odzozedwa, “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” ndi Bungwe Lolamulira lake. (Mateyu 24:45-47, NW; yerekezani ndi Machitidwe 16:4.) Ndipo chiyamikiro chimenechi chimaphatikizapo kukhazikika m’kupezeka pa misonkhano. (Ahebri 10:24, 25) (2) Tiyenera kukhala akhama m’phunziro laumwini la Mawu a Mulungu ndi la zofalitsidwa zoperekedwa ndi gulu la “kapolo,” zomwe zimatithandiza ife kutenga nthaŵi ya kusinkhasinkha pa mmene zinthu zomwe timaphunzira zingagwiritsidwire ntchito m’miyoyo yathu ndi kugwiritsidwa ntchito kuthandiza ena.
13. Nchiyani chomwe chiri tanthauzo la lonjezo lolembedwa pa Yeremiya 3:15?
13 Ponena za mtundu wa kuyang’anira ndi kudyetsa kwauzimu kumene iye akapereka kaamba ka ife m’tsiku lathu, Yehova ananena, pa Yeremiya 3:15 kuti: “Ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi [chidziŵitso, NW].” Ndithudi, programu yodyetsa mwauzimu imeneyi ikatipatsa ife kuthekera kozizwitsa kwa kuwona mikhalikwe ndi kuzindikira njira imene tikatenga ndi cholinga chokhala ndi chipambano. Kodi ndani amene ali magwero a chidziŵitso chimenecho? Yehova Mulungu.
14. Nchifukwa ninji gulu la ‘kapolo wokhulupirika’ liri ndi chidziŵitso?
14 Nchifukwa ninji gulu la ‘kapolo wokhulupirika’ liri ndi chidziŵitso choterocho? Chifukwa iwo apanga Mawu a Mulungu kukhala chodera nkhaŵa chawo cha khama ndipo amatsatira chitsogozo chake. M’kuwonjezerapo, chifukwa chakuti iwo agonjera ku chitsogozo cha Yehova, iye waika mzimu wake pa iwo, kuwagwiritsira ntchito iwo m’chigwirizano ndi chifuno chake. (Luka 12:43, 44; Machitidwe 5:32) Monga mmene wamasalmo wowuziridwa wakaleyo analembera kuti: “Ndiri nacho chidziŵitso cha kuposa aphunzitsi anga onse, chifukwa zokumbutsa zanu ziri zodera nkhaŵa zanga.”—Salmo 119:99, NW.
15. (a) Ndi iti yomwe iri nsonga ya uphungu umene gulu la “kapolo” limatipatsa mosasintha? (b) Zaka zambiri zapitazo, ndimotani mmene chinaliri chotheka kwa gulu la “kapolo” kupereka “nzeru ndi chidziŵitso” zofunikira ponena za kawonedwe Kachikristu ka kuthiridwa mwazi?
15 M’kuyankha mafunso onena za chomwe chiri chinthu cholondola kuchita, “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” nthaŵi zonse walangiza kuti: ‘Gwiritsirani ntchito zomwe zalembedwa m’Baibulo. Khulupirirani mwa Yehova.’ (Salmo 119:105; Miyambo 3:5, 6) Pamene kuthiridwa kwa mwazi kunadzafikira kuwonedwa monga muyezo wa thandizo la mankhwala ndipo kunakhala nkhani yoyang’anizana ndi Mboni za Yehova, Nsanja ya Olonda ya July 1, 1945, (Chingelezi) inalongosola kawonedwe ka Chikristu ponena za kupatulika kwa mwazi. Iyo inasonyeza kuti mwazi wa ponse paŵiri zinyama ndi anthu unaphatikizidwa pa chiletso chaumulungu. (Genesis 9:3, 4; Machitidwe 15:28, 29) Ziyambukiro za pambali za kuthupi sizinakambitsiridwe m’nkhaniyo; chidziŵitso cha zoterozo chinali chochepera kwambiri pa nthaŵiyo. Nkhani yeniyeni inali chimvero ku lamulo la Mulungu, ndipo idakali tero. Lerolino, anthu ambiri amazindikira nzeru yothandiza ya kukana kuthiridwa mwazi ndipo akuchita tero m’ziŵerengero zomakulakula. Koma kwa nthaŵi yonseyi, Mboni za Yehova zakhala zokhoza kuchita ndi chidziŵitso chifukwa zimakhulupirira Mlengi, yemwe amadziŵa zochulukira koposa ponena za mwazi kuposa mmene munthu aliyense amachitira.
16. Nchifukwa ninji uphungu wa mu Nsanja ya Olonda pa nkhani zoterozo zonga mkhalidwe woipa wa chisembwere, mabanja a kholo limodzi, ndi kupsyinjika unatsimikizira kukhala kokha womwe unafunikira?
16 Pamene mikhalidwe yolekelera ponena za mkhalidwe woipa wa chisembwere yakhala yowonekera mowonjezerekawonjezereka, Nsanja ya Olonda, m’malo mopititsa patsogolo njira yotchuka, yapereka chitsogozo chomvekera cha m’Malemba. Ichi chikuthandiza ambiri kuchinjiriza unansi wawo wa mtengo wake ndi Yehova ndi kusumika pa chimwemwe chosatha m’malo mwa kokha chisangalatso chopita. Mofananamo, nkhani za Nsanja ya Olonda zolunjikitsidwa kwa mabanja a kholo limodzi ndi kwa awo omwe akulimbana ndi kupsyinjika zawunikira chidziŵitso chomwe chiri chothekera kokha kwa awo amene malingaliro a Yehova ali a mtengo wake ndi amene mowona mtima amapemphera kuti: “Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga.”—Salmo 143:10; 139:17.a
17. (a) Zaka makumi pasadakhale, nchiyani chimene atumiki a Yehova anadziŵa ponena za chaka cha 1914? (b) Ngakhale kuti panali tsatanetsatane ponena za amene anthu a Mulungu anali adakali ndi mafunso itapita 1914, nchiyani chomwe iwo anadziŵa chomwe chinawapatsa iwo chitsogozo chomvekera ku miyoyo yawo?
17 Kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera,” Yehova anathandizanso atumiki ake kuzindikira, zaka makumi angapo pasadakhale, kuti chaka cha 1914 chikazindikiritsa mapeto a Nthaŵi za Akunja. (Luka 21:24, King James Version) Pamene iwo analoŵa m’nyengo yotsatira Nkhondo ya Dziko ya I, panali, ndithudi, mafunso omwe anawazizwitsa iwo. Koma chomwe anadziŵa chinali chokwanira kaamba ka iwo kuchita mwanzeru. Iwo anadziŵa kuchokera m’Malemba kuti nthaŵi yoikika ya Mulungu inali pafupi kaamba ka dongosolo la kachitidwe kakale kuwonongedwa; chotero chikakhala chopusa kuika chiyembekezo chawo mwa ilo kapena kulola miyezo ya chipambano chake ya kukondetsa zinthu zakuthupi kulamulira miyoyo yawo. Iwo anadziŵanso kuti Ufumu wa Yehova uli yankho lenileni ku mavuto onse okantha mtundu wa anthu. (Danieli 2:44; Mateyu 6:33) Iwo anawona mowonekera kuti liri thayo la Akristu owona onse kubukitsa Mfumu yodzozedwa ya Yehova, Yesu Kristu, ndi Ufumu Wake. (Yesaya 61:1, 2; Mateyu 24:14) Mu 1925, kupyolera mwa nkhani ya mu Nsanja ya Olonda “Birth of the Nation” (Kubadwa kwa Mtundu), iwo analimbikitsidwa ndi kumvetsetsa kowonekera kwa Chibvumbulutso mutu 12: chotero tsopano anamvetsetsa chomwe chinkachitika m’mwamba, chosawoneka ku maso aumunthu. Chidziŵitso choterocho chinapereka chitsogozo chotsimikizirika ku miyoyo yawo.
18. Ndi mwaŵi wotani ndi thayo zimene tiri nazo tsopano, ndipo ndi funso lotani limene tiyenera kudzifunsa ife eni?
18 Akumachita m’chikhulupiriro, chikwi chochepera cha omwe pa nthaŵiyo ankatumikira Yehova monga mboni zake chinapititsa patsogolo kulalikira kwa mbiri yabwino ya Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu m’mbale zonse za dziko. Monga chotulukapo chake, mamiliyoni a anthu afikira pa kudziŵa ndi kukonda Yehova ndipo ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Tonsefe amene talandira chowonadi monga chotulukapo cha ntchito zawo zachikondi tasonyezedwa kuti ifenso tiri ndi mwaŵi ndi thayo la kugawanamo mu ntchitoyo, kupereka umboni wokwanira kwa aliyense amene tingafikire ndi kupitiriza kuchita tero kufikira Yehova anena kuti ntchito yachitidwa. (Chibvumbulutso 22:17; yerekezani ndi Machitidwe 20:26, 27.) Kodi njira mu imene mukugwiritsira ntchito moyo wanu imapereka umboni wakuti mumayamikira chidziŵitso chimene Yehova wapereka kupyolera m’gulu lake?
19. (a) Perekani chitsanzo cha mmodzi amene moyo wake umawunikira chiyamikiro kaamba ka chidziŵitso chimene Yehova akupereka kupyolera m’gulu lake. (b) Nchiyani chomwe tingaphunzire kuchokera ku chitsanzo chimenecho?
19 Miyoyo ya khamu lalikulu aliyense payekha m’mbali zonse za dziko lapansi imatsimikizira kuti ku mbali yawo yankho liri inde. Mwachitsanzo, lingalirani John Cutforth. Zaka zina 48 zapitazo, iye anatenga ku mtima uphungu wa Malemba ku umene gulu la ‘kapolo wokhulupirika’ linali kulunjikitsa chisamaliro pa nthaŵiyo monga mmene likuchitira tsopano, chotchedwa: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu. Chifukwa chake musadere nkhaŵa za mawa.” (Mateyu 6:33, 34) Pambuyo pa zaka za kuzoloŵera mu utumiki wa Yehova, Mbale Cutforth ananena kuti: ‘Chimodzi cha zinthu chomwe chasindikizidwa mwamphamvu m’malingaliro anga chiri chakuti Yehova ali ndi gulu pa dziko lapansi limene iye akulitsogoza, kuti ine monga pandekha ndingagwire ntchito ndi gulu limenelo, ndipo kuti ngati ine ndikatsatira kotheratu zilozero ndi zitsogozo zake, likandibweretsera ine mtendere, kukwaniritsidwa, chikhutiritso, ndi mabwenzi ambiri, kuwonjezerapo madalitso ena ambiri olemera.’ Chitsimikiziro chimenecho chalimbikitsidwa mobwerezabwereza pamene iye wasangalala ndi moyo wolemera ndi madalitso auzimu mu United States, Canada, Australia, ndi Papua New Guinea.b Zowonadi, kwa tonsefe njira ya nzeru iri ija yomwe imawunikira chiyamikiro kaamba ka njira imene Yehova akuperekera chidziŵitso pa anthu ake.—Mateyu 6:19-21.
Dzichinjirizeni Molimbana ndi Kutayika kwa Chidziŵitso
20, 21. (a) Ndimotani mmene anthu ena atayira chidziŵitso chaumulungu chomwe iwo pa nthaŵi ina anali nacho? (b) Nchiyani chomwe chidzathandiza kutichinjiriza ife molimbana ndi njira yovulaza?
20 Chidziwitso chimene Yehova akupereka chiri chuma choyenera kuchinyadira. Tiyenera kukhala ozindikira, ngakhale kuli tero, kuti ngati sitipitiriza m’njira imene yatitheketsa ife kupeza chidziŵitso chaumulungu, tingachitaye icho. Momvetsa chisoni, ena akhala kwenikweni ndi chokumana nacho choterocho. (Miyambo 21:16; Danieli 11:35) Akumakana chilango chomwe chinawakhudza iwo mwaumwini, iwo anayesera kulungamitsa chomwe anali kuchita. Kunyada kunakhala msampha kwa iwo. Iwo anayamba kuwona monga chabwino chimene Mawu a Mulungu amasonyeza kukhala choipa, ndipo iwo anadzikokera kutali ndi gulu la Yehova. Nchomvetsa chisoni chotani nanga!
21 Mikhalidwe ya munthu woteroyo iri monga yomwe yalongosoledwa pa Salmo 36:1-3 (NW), kumene timaŵerenga kuti: “Mawu olakwa kwa woipayo ali mkati mwa mtima wake.” Kumeneko ndiko kuti, malingaliro ndi zikhumbo zake zadyera zimamtsogoza iye m’kulakwa. “Palibe kuwopa Mulungu pamaso pake,” Wamasalmoyo akupitiriza tero. “Pakuti adzidyoletsa yekha m’kuwona kwake kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho. Mawu a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga.” Ndipo nchiyani chomwe chiri chotulukapo kwa iye? Iye ‘waleka kukhala ndi chidziŵitso cha kuchita zabwino.’ Iye m’chenicheni amadzitsimikizira iyemwini kuti chomwe akuchita chiri chabwino, ndipo amanyenga ena kumtsatira iye. Chotero, nchofunika chotani nanga, kuti tisakhale kokha ndi chidziŵitso komanso kuchichinjiriza icho mwa kuyamikira njira imene Yehova watitheketsera ife kuchipeza icho!
[Mawu a M’munsi]
a Onani Watch Tower Publications Index 1930-1985, pansi pa “Marriage,” “Families,” “Moral Breakdown,” ndi “Depression (Mental).”
b Onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1958, (Chingelezi) masamba 333-6.
Kodi Nchiyani Chomwe Mukukumbukira?
◻ Nchiyani chomwe chidzatithandiza ife kupanga zigamulo zanzeru?
◻ Nchiyani chomwe chikuphatikizidwamo mu “chidziŵitso”?
◻ Ndimotani mmene Yehova amaperekera chidziŵitso kwa atumiki ake mu nthaŵi yathu?
◻ Nchiyani chomwe chikufunikira ku mbali yathu ngati titi tipindule kotheratu kuchokera ku chidziŵitso chimene Yehova akupereka?
[Chithunzi patsamba 16]
Kuti tipindule ndi chidziŵitso chomwe Yehova akupereka, tiyenera kuyamikira gulu lake, kukhala akhama m’phunziro laumwini, ndi kusinkhasinkha pa mmene tingagwiritsire ntchito zomwe taphunzira