Mkwiyo Wanga Kapena Thanzi Langa?
KODI ndani amene samakwiya? Kumachitika kwa tonsefe. Panthaŵi zina mlingo wakutiwakuti wa mkwiyo ungakhale woyenerera. Komatu, kunena zowona, kodi sizowona kuti kaŵirikaŵiri mkwiyo wathu (kapena ukulu wake) umakhala wosayenerera?
Baibulo limatiuza kuti: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: usavutike mtima ungachite choipa.” (Salmo 37:8) Kodi uphungu wotero ngwanzeru motani? Kodi ungayambukire kukhalitsa kwa thanzi lathu?
M’chigawo chake cha “Za Thanzi,” The New York Times inati:
“Anthu amene amakalipakalipa kapena amangokhala amtima wapachala pachinthu chilichonse angakhale akuchita zoipa kwambiri kuposa kudzipangitsa iwo eni kukhala osakondweretsa. Angakhale akudzipha.
“Ofufuza asonkhanitsa umboni wochuluka posachedwapa wosonyeza kuti mkwiyo wosatha ngwovulaza kwambiri kuthupi kwakuti ukuikidwa m’gulu limodzi ndi, ndipo mwinamwake ngakhale kuposa, kusuta fodya, kunenepetsa ndi chakudya cha mafuta ambiri monga wodzetsa imfa ya mwamsanga yaupandu waukulu.
“‘Kufufuza kwathu kukusonyeza kuti udani, mkwiyo wa kukayikira ena ngwofanana ndi maupandu ena a thanzi amene timadziŵa,’ anatero Dr. Redford Williams, wofufuza za mankhwala okhudza mkhalidwe pa Duke University Medical Center.”
Zofufuzidwazo zikusonyeza kuti awo amene amakwiya ndi mavuto a moyo amatulutsa mahomoni ambiri a kupsinjika. Kukalipakalipa kwawo kungachititse kusiyana m’milingo ya cholesterol yotetezera ndi yaupandu, kukumawaika paupandu wa nthenda ya mtima.
Ena anganene kuti, ‘Komatu ndimo mmene ndiliri’ kapena, ‘Ndimmene ndinakulira.’ Komabe, zimenezo sizikutanthauza kuti simungasinthe, mwakuyesayesa mowona mtima kugwiritsira ntchito uphungu wa Mulungu. M’Baibulo lanu, pendani uphungu wake wonena za kukwiya ndi ukali wolembedwa pa Miyambo 14:29, 30; 22:24, 25; Aefeso 4:26; Yakobo 1:19, 20.
Kugwiritsira ntchito nzeru yaumulungu imeneyo kungawongolere thanzi lanu ndi kutalikitsa moyo wanu. Times imeneyo inati: “Ofufuza ambiri anati anthu okwiyakwiya akhoza kuchepetsa kuthekera kwa kufa msanga mwa kusintha mkhalidwe womakwiyakwiyawo.”